A A A A A

Mulungu: [Dalitso]

LUKA ๖:๓๘
Perekani ndipo mudzapatsidwa. Adzakupatsani mʼthumba mwanu muyeso wabwino, wotsenderezeka, wokhutchumuka ndi wosefukira. Pakuti muyeso umene mumagwiritsa ntchito, ndi omwewo adzakuyeserani.”

MATEYU ๕:๔
Odala ndi amene ali achisoni, chifukwa adzatonthozedwa.

AFILIPI 4:19
Ndipo Mulungu wanga adzakwaniritsa zosowa zanu monga mwa chuma chake chaulemerero mwa Khristu Yesu.

MASALIMO ๖๗:๗
Mulungu atidalitse kuti pamenepo malekezero onse a dziko lapansi apembedze Iyeyo.

NUMERI 6:24-25
[24] “ ‘Yehova akudalitse ndi kukusunga;[25] Yehova awalitse nkhope yake pa iwe, nakuchitira chisomo;

AFILIPI ๔:๖-๗
[๖] Musade nkhawa ndi kanthu kalikonse, koma pa china chilichonse, mwa pemphero ndi chidandaulo pamodzi ndi chiyamiko, perekani zopempha zanu kwa Mulungu.[๗] Ndipo mtendere wa Mulungu, umene upambana nzeru zonse udzasunga bwino mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.

YAKOBO ๑:๑๗
Mphatso iliyonse yabwino ndi yangwiro imachokera kumwamba, kwa Atate mwini kuwala, amene sasintha ngati mthunzi woyendayenda.

YEREMIYA 17:7-8
[7] “Koma ndi wodala munthu amene amadalira Yehova, amene amatsamira pa Iye.[8] Adzakhala ngati mtengo wodzalidwa mʼmphepete mwa madzi umene umatambalitsa mizu yake mʼmbali mwa mtsinje. Mtengowo suopa pamene kukutentha; masamba ake amakhala obiriwira nthawi zonse. Suchita mantha pa chaka cha chilala ndipo sulephera kubereka chipatso.”

YESAYA 41:10
Tsono usaope, pakuti Ine ndili nawe; usataye mtima chifukwa Ine ndine Mulungu wako. Ndidzakupatsa mphamvu ndipo ndidzakuthandiza, ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.

YOHANE ๑:๑๖
Kuchokera mʼkuchuluka kwa chisomo chake ife tonse talandira madalitso pamwamba pa madalitso.

GENESIS 22:16-17
[16] ndipo anati, “Ndikulumbira mwa Ine ndekha kuti popeza wachita zimenezi, wosandikaniza mwana wako mmodzi yekhayu,[17] ndidzakudalitsa ndithu ndipo ndidzakupatsa zidzukulu zochuluka ngati nyenyezi zamlengalenga komanso ngati mchenga wa mʼmphepete mwa nyanja. Zidzukulu zako zidzalanda mizinda ya adani awo,

GENESIS 27:28-29
[28] Mulungu akugwetsere mame akumwamba ndipo minda yako ibale tirigu wambiri ndi vinyo watsopano.[29] Mitundu ya anthu ikutumikire iwe ndipo anthu akugwadire iwe. Ukhale wolamula abale ako, ndipo ana aamuna a amayi ako akugwadire. Amene akutemberera iwe atembereredwe ndipo amene adalitsa iwe adalitsike.”

MASALIMO 1:1-3
[1] Wodala munthu amene satsatira uphungu wa anthu ochimwa, kapena kuyima mʼnjira ya anthu oyipa, kapena kukhala mʼmagulu a anthu onyoza.[2] Koma chikondwerero chake chili mʼmalamulo a Yehova ndipo mʼmalamulo akewo amalingaliramo usana ndi usiku.[3] Iye ali ngati mtengo wodzalidwa mʼmbali mwa mitsinje ya madzi, umene umabereka zipatso zake pa nyengo yake ndipo masamba ake safota. Chilichonse chimene amachita amapindula nacho.

MASALIMO ๒๓:๑-๔
[๑] Salimo la Davide. Yehova ndiye mʼbusa wanga, sindidzasowa kanthu.[๒] Amandigoneka pa msipu wobiriwira, amanditsogolera ku madzi akumwa abwino,[๓] amatsitsimutsa moyo wanga. Amanditsogolera mʼnjira zachilungamo chifukwa cha dzina lake.[๔] Ngakhale ndiyende mʼchigwa cha mdima wakuda bii, sindidzaopa choyipa, pakuti Inu muli ndi ine; chibonga chanu ndi ndodo yanu zimanditonthoza.

2 SAMUELE 22:3-4
[3] Mulungu wanga ndiye thanthwe langa, mʼmene ndimathawiramo, chishango changa ndi ndodo yachipulumutso changa. Iye ndi linga langa, pothawirapo panga ndi mpulumutsi wanga. Munandipulumutsa mʼmanja mwa anthu ankhanza.[4] “Ndimayitana Yehova amene ndi woyenera matamando, ndipo ndapulumutsidwa kwa adani anga.

1 YOHANE 5:18
Tikudziwa kuti aliyense amene ndi mwana wa Mulungu sachimwirachimwirabe. Yesu, Mwana wa Mulungu, amamusunga ndipo woyipa uja sangamukhudze.

MASALIMO 138:7
Ngakhale ndiyende pakati pa masautso, mumasunga moyo wanga; mumatambasula dzanja lanu kutsutsana ndi mkwiyo wa adani anga, mumandipulumutsa ndi dzanja lanu lamanja.

2 AKORINTO ๙:๘
Ndipo Mulungu akhoza kukudalitsani kwambiri, kuti inuyo nthawi zonse mukhale ndi zinthu zokukwanirani, ndiponso ndi zina zochuluka kuti muthandize pa ntchito zonse zabwino.

AFILIPI 4:7
Ndipo mtendere wa Mulungu, umene upambana nzeru zonse udzasunga bwino mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.

Chewa Bible 2016
Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.®