A A A A A

Zinsinsi: [Ma Dinosaurs]


YESAYA 27:1
Tsiku limenelo, Yehova ndi lupanga lake lakuthwa, lalikulu ndi lamphamvu, adzalanga Leviyatani chinjoka chothawa chija, Leviyatani chinjoka chodzikulunga; adzapha chirombo choopsa cha mʼnyanja.

GENESIS 1:21
Choncho Mulungu analenga zamoyo zikuluzikulu za mʼnyanja ndi chamoyo chamtundu uliwonse chokhala mʼmadzi ndi mbalame iliyonse ya mapiko monga mwa mtundu wake. Mulungu anaona kuti zinali bwino.

MASALIMO 104:26
Kumeneko sitima zapamadzi zimayenda uku ndi uku, ndiponso Leviyatani amene munamulenga kuti asewere kumeneko.

AROMA 1:18
Mkwiyo wa Mulungu ukuonekera kuchokera kumwamba. Ukutsutsana ndi kusapembedza konse ndi kuyipa kwa anthu amene amapondereza choonadi mwa chikhalidwe chawo choyipa.

GENESIS 1:24-31
[24] Kenaka Mulungu anati, “Dziko lapansi litulutse zolengedwa zamoyo monga mwa mitundu yawo: ziweto, zolengedwa zokwawa ndi nyama zakuthengo, iliyonse monga mwa mtundu wake.” Ndipo zinaterodi.[25] Mulungu anapanga nyama zakuthengo monga mwa mitundu yawo, nyama zoweta monga mwa mitundu yawo ndi nyama zokwawa monga mwa mitundu yawo. Ndipo Mulungu anaona kuti zinali bwino.[26] Zitatha izi Mulungu anati, “Tipange munthu mʼchifanizo chathu, mofanana ndi ife kuti alamulire nsomba za mʼnyanja, mbalame zamlengalenga, nyama zonse zoweta ndi zonse zokwawa za pa dziko lapansi ndi zamoyo zonse zakutchire.”[27] Ndipo Mulungu analenga munthu mʼchifanizo chake. Anawalengadi mʼchifanizo cha Mulungu; analenga iwo, mwamuna ndi mkazi.[28] Mulungu anawadalitsa nati kwa iwo, “Muberekane, muchulukane, mudzaze dziko lapansi ndipo muligonjetse. Mulamulire nsomba zamʼnyanja, mbalame zamlengalenga ndi cholengedwa chamoyo chilichonse chimene chimayenda mokwawa pa dziko lapansi.”[29] Kenaka Mulungu anati, “Ine ndakupatsani chomera chilichonse cha pa dziko lapansi chimene chili ndi mbewu komanso mtengo uliwonse wobala zipatso zokhala ndi mbewu mʼkati mwake kuti zikhale chakudya chanu.[30] Ndaperekanso msipu kwa nyama zonse za pa dziko lapansi ndi kwa mbalame zamlengalenga ndi kwa cholengedwa chamoyo chilichonse chimene chimakwawa, chilichonse chimene chili ndi moyo.” Ndipo zinachitikadi.[31] Mulungu anaona zonse zimene anazilenga kuti zinali zabwino kwambiri. Ndipo panali madzulo ndiponso mmawa, tsiku lachisanu ndi chimodzi.

YOBU 40:15-24
[15] “Taganiza za mvuwu, imene ndinayipanga monga momwe ndinapangira iwe, ndipo imadya udzu ngati ngʼombe.[16] Mphamvu zake ndi zazikulu kwambiri, thupi lake ndi lanyonga kwambiri![17] Mchira wake umayima tolotolo ngati mtengo wamkungudza; mitsempha ya ntchafu zake ndi yogwirana bwino.[18] Mafupa ake ali ngati mapayipi amkuwa, nthiti zake zili ngati mipiringidzo yachitsulo.[19] Mvuwuyo ndi yayikulu mwa zolengedwa za Mulungu, komatu mlengi wake amatha kuyiopseza ndi lupanga lake.[20] Imapeza chakudya chake ku mtunda ndipo nyama zakuthengo zonse zimasewera pambali pake.[21] Imagona pa tsinde pa zitsamba za mipeta, imabisala mʼbango ndiponso pa thawale.[22] Imaphimbika ndi mthunzi wazitsamba za mipeta; imazunguliridwa ndi misondozi ya mu mtsinje.[23] Madzi a mu mtsinje akakokoma, sichita mantha, iyo sitekeseka, ngakhale madzi a mu Yorodani afike mʼkhosi mwake.[24] Kodi alipo amene angathe kukola mvuwu ndi mbedza kapena kuyikola mu msampha?

YOBU 41:1-10
[1] “Kodi ungathe kukoka ngʼona ndi mbedza ya nsomba kapena kukanikiza lilime lake pansi ndi chingwe?[2] Kodi ungathe kumanga chingwe mʼmphuno mwake, kapena kubowola nsagwada zake ndi mbedza?[3] Kodi ngʼonayo idzakupempha kuti uyichitire chifundo? Kodi idzakuyankhula ndi mawu ofatsa?[4] Kodi idzachita nawe mgwirizano kuti uyisandutse kapolo wako mpaka muyaya?[5] Kodi udzasewera nayo ngati mbalame, kapena kuyimangirira kuti atsikana ako asewere nayo?[6] Kodi anthu adzayitsatsa malonda? Nanga amalondawo nʼkugawanagawana nyama yake kuti akagulitse?[7] Kodi chikopa chake ungathe kuchilasa ndi zisonga, kapena kubowola mutu wake ndi nthungo zophera nsomba?[8] Ukayiputa udziwe kuti pali nkhondo, ndipo iweyo sudzabwereranso.[9] Chiyembekezo choti nʼkuyigonjetsa ndi chabodza; kungoyiona kokha, ndithu iwe kumangodzigwera wekha.[10] Palibe wolimba mtima kuti ndi kuyiputa. Ndani angalimbe mtima kulimbana ndi Ine?

YOSWA 10:1-10
[1] Adoni-Zedeki mfumu ya ku Yerusalemu inamva kuti Yoswa wagonjetsa ndi kuwononga kotheratu mzinda wa Ai pamodzi ndi mfumu yake, monga anachitira ndi Yeriko ndi mfumu yake. Inamvanso kuti anthu a ku Gibiyoni anachita pangano la mtendere ndi Israeli ndipo amakhala pakati pawo.[2] Choncho iye ndi anthu ake anachita mantha aakulu, chifukwa Gibiyoni unali mzinda waukulu kwambiri, monga mzinda uliwonse wokhala ndi mfumu. Unali waukulu ndipo ankhondo ake anali olimba mtima.[3] Chotsatira chake Adoni-Zedeki mfumu ya Yerusalemu inatuma uthenga kwa Hohamu mfumu ya Hebroni, Piramu mfumu ya Yarimuti, Yafiya mfumu ya Lakisi ndi Debri mfumu ya Egiloni.[4] Iye anatumiza mawu kuti, “Bwerani mudzandithandize kumenyana ndi Gibiyoni, chifukwa anthu ake achita pangano la mtendere ndi Yoswa ndi Aisraeli.”[5] Mafumu asanu a Aamori aja, mfumu ya Yerusalemu, mfumu ya Hebroni, mfumu ya Yarimuti, mfumu ya Lakisi ndi mfumu ya Egiloni, anagwirizana. Iwo anasonkhanitsa ankhondo awo nazungulira mzinda wa Gibiyoni ndi kuwuthira nkhondo.[6] Koma anthu a ku Gibiyoni anatumiza uthenga kwa Yoswa ku misasa ya ku Giligala nati, “Musawataye anthu anu! Bwerani msanga mudzatipulumutse! Dzatithandizeni chifukwa mafumu a Aamori ochokera ku dziko la ku mapiri agwirizana kuti adzatithire nkhondo.”[7] Choncho Yoswa ananyamuka kuchoka ku Giligala ndi gulu lake la ankhondo pamodzi ndi anthu ake olimba mtima.[8] Yehova anati kwa Yoswa, “Usawaope, Ine ndawapereka mʼdzanja lako. Palibe ndi mmodzi mwa amenewa amene adzalimbe.”[9] Atayenda usiku wonse kuchokera ku Giligala, Yoswa anawathira nkhondo mwadzidzidzi.[10] Yehova anachititsa mantha adani aja atangoona gulu lankhondo la Israeli. Choncho Aisraeli anagonjetsa Aamori ku Gibiyoni ndipo anawathamangitsa mu msewu wopita ku Beti-Horoni ndi kuwapha njira yonse yopita ku Azeka ndi Makeda.

Chewa Bible 2016
Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.®