A A A A A

Moyo: [Kukongola]


1 PETRO 3:3-4
[3] Kudzikongoletsa kwanu kusakhale kwa maonekedwe akunja, monga kuluka tsitsi ndi kuvala zokometsera zagolide ndi zovala zamberewere.[4] Mʼmalo mwake kudzikongoletsa kwanu kukhale kwa munthu wa mʼkatimo, kukongola kosatha kwa mtima ofatsa ndi mzimu wachete, zimene ndi za mtengowapatali pamaso pa Mulungu.

2 AKORINTO 4:16
Nʼchifukwa chake ife sititaya mtima. Ngakhale thupi lathu likunka lifowokerafowokera, koma mʼkatimu tikulimbikitsidwa mwatsopano tsiku ndi tsiku.

AEFESO 2:10
Pakuti ndife ntchito ya Mulungu, olengedwa mwa Khristu Yesu kuti tichite ntchito zabwino, zimene Mulungu anazikonzeratu kale kuti tizichite.

GENESIS 1:27
Ndipo Mulungu analenga munthu mʼchifanizo chake. Anawalengadi mʼchifanizo cha Mulungu; analenga iwo, mwamuna ndi mkazi.

YESAYA 40:8
Udzu umanyala ndipo maluwa amafota, koma mawu a Mulungu wathu adzakhalapo mpaka muyaya.”

AFILIPI 4:8
Potsiriza, abale, muziyika mtima wanu pa zinthu zilizonse zabwino ndi zotamandika monga, zinthu zoona, zinthu zolemekezeka, zinthu zolungama, zinthu zoyera, zinthu zokongola ndi zinthu zosiririka.

MASALIMO 139:14
Ndimakuyamikani chifukwa ndinapangidwa mochititsa mantha ndi modabwitsa; ntchito zanu ndi zodabwitsa, zimenezi ndimazidziwa bwino lomwe.

AROMA 8:6
Kuyika mtima pa zathupi ndi imfa koma kuyika mtima pa za Mzimu ndi moyo ndi mtendere.

NYIMBO YA SOLOMONI 4:7
Ndiwe wokongola kwambiri wokondedwa wanga; palibe chilema pa iwe.

MATEYU 6:28-29
[28] “Ndipo bwanji inu mudera nkhawa za zovala? Onani makulidwe a maluwa akutchire. Sagwira ntchito kapena kuwomba nsalu.[29] Ndikukuwuzani kuti angakhale Solomoni mu ulemerero wake sanavale mofanana ndi limodzi la maluwa amenewa.

1 TIMOTEO 2:9-10
[9] Ndikufunanso kuti amayi azivala mwaulemu, modzilemekeza ndi moyenera. Adzikongoletse koma osati ndi tsitsi loluka mowonjeza muyeso kapena zokongoletsa zagolide kapena mikanda yamtengowapatali kapena ndi zovala zamtengowapatali.[10] Koma adzikongoletse ndi ntchito zabwino zoyenera mayi wopembedza Mulungu.

1 SAMUELE 16:7
Koma Yehova anati kwa Samueli, “Usaone maonekedwe ake kapena msinkhu wake, pakuti ndamukana iyeyu. Yehova sapenya zimene munthu amapenya. Anthu amapenya zakunja, koma Mulungu amapenya za mu mtima.”

MLALIKI 3:11
Iye anapanga chinthu chilichonse kuti chikhale chabwino pa nthawi yake. Anayika nzeru zamuyaya mʼmitima ya anthu; komabe anthuwo sangathe kuzindikira zomwe Mulungu wachita kuyambira pa chiyambi mpaka chimaliziro.

AGALATIYA 3:26-27
[26] Nonse ndinu ana a Mulungu kudzera mʼchikhulupiriro mwa Khristu Yesu,[27] pakuti nonse amene munalumikizana ndi Khristu mu ubatizo munavala Khristu.

MIYAMBO 3:15-18
[15] Nzeru ndi yoposa miyala yamtengowapatali; ndipo zonse zimene umazikhumba sizingafanane ndi nzeru.[16] Mʼdzanja lake lamanja muli moyo wautali; mʼdzanja lake lamanzere muli chuma ndi ulemu.[17] Njira zake ndi njira zosangalatsa, ndipo mu njira zake zonse muli mtendere.[18] Nzeru ili ngati mtengo wopatsa moyo kwa oyigwiritsitsa; wodala munthu amene amayigwiritsa kwambiri.

EZEKIELE 28:17-18
[17] Unkadzikuza mu mtima mwako chifukwa cha kukongola kwako, ndipo unayipitsa nzeru zako chifukwa chofuna kutchuka. Kotero Ine ndinakugwetsa pansi kuti ukhala chenjezo pamaso pa mafumu.[18] Ndi malonda ako achinyengo unachulukitsa machimo ako. Motero unayipitsa malo ako achipembedzo. Choncho ndinabutsa moto pakati pako, ndipo unakupsereza, ndipo unasanduka phulusa pa dziko lapansi pamaso pa anthu onse amene amakuona.

YAKOBO 1:23
Munthu aliyense amene amangomva mawu koma osachita zimene mawuwo amanena, ali ngati munthu amene amayangʼana nkhope yake pa galasi.

MATEYU 23:28
Chimodzimodzinso, kunja mumaoneka kwa anthu kuti ndinu olungama koma mʼkatimo ndinu odzaza ndi chinyengo ndi zoyipa zina.

MIYAMBO 31:30
Nkhope yachikoka ndi yonyenga, ndipo kukongola nʼkosakhalitsa; koma mkazi amene amaopa Yehova ayenera kutamandidwa.

Chewa Bible 2016
Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.®