A A A A A

Khalidwe Labwino: [Kusamalira]


1 TIMOTEO 5:4
Koma ngati mkazi wamasiye ali ndi ana ndi zidzukulu, anawo ayambe aphunzira kukwaniritsa udindo wawo pa banja lawo moopa Mulungu, potero akubweza zabwino kwa makolo awo ndi agogo awo. Pakuti zimenezi ndiye zimakondweretsa Mulungu.

1 TIMOTEO 3:15
Ine zina zikandichedwetsa kubwera, mudziwe za mmene anthu ayenera kukhalira mʼNyumba ya Mulungu, imene ndi mpingo wa Mulungu wamoyo, mzati ndi maziko achoonadi.

YOHANE 8:32
Tsono mudzadziwa choonadi, ndipo choonadicho chidzakumasulani.”

CHIVUMBULUTSO 17:5
Pa mphumi pake panalembedwa dzina lodabwitsa: BABULONI WAMKULU MAYI WA AKAZI ADAMA NDI WAZOYIPITSA ZA DZIKO LAPANSI.

YAKOBO 1:27
Chipembedzo chimene Mulungu Atate athu amachivomereza kuti ndi changwiro ndi chopanda zolakwika ndi ichi: kusamalira ana amasiye ndi akazi amasiye pa mavuto awo, ndi kudzisunga bwino kuopa kudetsedwa ndi dziko lapansi.

YOHANE 6:54
Aliyense amene adya thupi langa ndi kumwa magazi anga ali ndi moyo wosatha ndipo Ine ndidzamuukitsa kwa akufa pa tsiku lomaliza.

MARKO 6:3
Kodi uyu si mpalamatabwa uja? Kodi uyu si mwana wa Mariya ndi mʼbale wa Yakobo, Yose, Yudasi ndi Simoni? Kodi alongo ake si ali ndi ife?” Ndipo anakhumudwa naye.

YOHANE 14:6
Yesu anayankha kuti, “Ine ndine njira, choonadi ndi moyo. Palibe munthu angafike kwa Atate popanda kudzera mwa Ine.

GENESIS 1:1-7
[1] Pachiyambi Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi.[2] Dziko lapansi linali losakonzedwa ndi lopanda kanthu. Mdima wandiweyani unakuta nyanja ndipo Mzimu wa Mulungu unkayendayenda pamwamba pa madziwo.[3] Pamenepo Mulungu anati, “Kuwale” ndipo kunawaladi.[4] Mulungu anaona kuti kuwalako kunali bwino ndipo Iye analekanitsa kuwala ndi mdima.[5] Mulungu anatcha kuwalako “usana” ndipo mdima anawutcha “usiku.” Ndipo panali madzulo ndiponso mmawa pa tsiku loyamba.[6] Kenaka Mulungu anati, “Pakhale thambo pakati pa madzi kuti lilekanitse madzi a mʼmwamba ndi madzi a pansi.”[7] Ndipo Mulungu anapanga thambo nalekanitsa madzi amene anali pansi ndi pamwamba pa thambo lija, ndipo zinachitikadi.

1 TIMOTEO 5:8
Ngati wina sasamalira abale ake, makamaka a mʼbanja mwake mwenimweni, ameneyo wakana chikhulupiriro ndipo ndi woyipa kuposa wosakhulupirira.

AGALATIYA 1:19
Ine sindinaonane ndi atumwi enawo koma Yakobo yekha, mʼbale wa Ambuye.

MALAKI 1:11
Dzina langa lidzalemekezedwa pakati pa mitundu ya anthu, kuchokera kummawa mpaka kumadzulo. Mʼmalo monse adzapereka nsembe zofukiza ndi zopereka zangwiro mʼdzina langa, chifukwa dzina langa lidzakhala lalikulu pakati pa mitundu ya anthu,” akutero Yehova Wamphamvuzonse.

GENESIS 2:7
Tsono Yehova Mulungu anawumba munthu kuchokera ku dothi nawuziramo mpweya wamoyo mʼmphuno mwake ndipo munthuyo anakhala wamoyo.

YOHANE 3:3-5
[3] Poyankha Yesu ananena kuti, “Zoonadi, Ine ndikukuwuza kuti, ngati munthu sabadwanso mwatsopano sangathe kuona ufumu wa Mulungu.”[4] Nekodimo anati, “Kodi munthu angabadwenso bwanji atakalamba? Kodi angalowe kachiwiri mʼmimba ya amayi ake kuti abadwenso?”[5] Yesu anayankha kuti, “Zoonadi, Ine ndikukuwuza kuti ngati munthu sabadwa mwa madzi ndi Mzimu Woyera, sangalowe mu ufumu wa Mulungu.

AHEBRI 12:14
Yesetsani kukhala pa mtendere ndi anthu onse ndi kukhala oyera mtima, pakuti popanda chiyero palibe ndi mmodzi yemwe adzaona Ambuye.

CHIVUMBULUTSO 17:18
Mkazi unamuonayo ndi mzinda waukulu umene ulamulira mafumu a dziko lapansi.”

MATEYU 16:18
Ndipo Ine ndikuwuza iwe kuti ndiwe Petro ndipo pa thanthwe ili Ine ndidzamangapo mpingo wanga ndipo makomo a ku gehena sadzawugonjetsa.

GENESIS 1:1
Pachiyambi Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi.

EKSODO 15:3
Yehova ndi wankhondo; Yehova ndilo dzina lake.

CHIVUMBULUTSO 17:9
“Zimenezi zikufunika kuganizira mwanzeru. Mitu isanu ndi iwiriyo ndi mapiri asanu ndi awiri pomwe mkazi uja amakhalirapo. Yomweyonso ndi mafumu asanu ndi awiri.

AFILIPI 4:6-7
[6] Musade nkhawa ndi kanthu kalikonse, koma pa china chilichonse, mwa pemphero ndi chidandaulo pamodzi ndi chiyamiko, perekani zopempha zanu kwa Mulungu.[7] Ndipo mtendere wa Mulungu, umene upambana nzeru zonse udzasunga bwino mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.

AGALATIYA 4:19
Ana anga okondedwa, inu amene ine ndikukumveraninso zowawa za kubereka kufikira Khristu atawumbidwa mwa inu,

1 PETRO 3:15
Koma lemekezani Khristu mʼmitima mwanu ngati Ambuye wanu. Khalani okonzeka nthawi zonse kuyankha aliyense amene akufunsani za chiyembekezo chimene muli nacho.

CHIVUMBULUTSO 17:1
Mmodzi wa angelo asanu ndi awiri aja amene anali ndi mbale zisanu ndi ziwiri anadza nati kwa ine, “Bwera ndikuonetse chilango cha mkazi wadama wotchuka uja amene akukhala pambali pa madzi ambiri.

MATEYU 18:15-18
[15] “Ngati mʼbale wako akuchimwira, pita kamuwuze cholakwa chake pa awiri. Ngati akumvera, wamubweza mʼbale wakoyo.[16] Koma ngati sakumvera, katenge wina mmodzi kapena ena awiri, ‘kuti nkhani itsimikizike ndi umboni wa anthu awiri kapena atatu.’[17] Ngati iye akana kuwamvera iwo, kaneneni ku mpingo; ndipo ngati sakamvera ngakhale mpingo, muchite naye monga mukanachitira ndi wakunja kapena wolandira msonkho.[18] “Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti chilichonse chimene muchimanga pa dziko lapansi, chidzamangidwanso kumwamba, ndipo chilichonse chimene muchimasula pa dziko chidzamasulidwanso kumwamba.

AEFESO 1:22-23
[22] Ndipo Mulungu anayika zinthu zonse pansi pa mapazi ake ndi kumusankha Iyeyo kukhala mutu pa chilichonse chifukwa cha mpingo,[23] umene ndi thupi lake, chidzalo cha Iye amene adzaza chilichonse mu njira iliyonse.

AEFESO 5:23
Pakuti mwamuna ndi mutu wa mkazi monga momwe Khristu ali mutu wa mpingo, thupi lake, limene Iyeyo ndi Mpulumutsi wake.

MACHITIDWE A ATUMWI 4:32
Okhulupirira onse anali a mtima umodzi, ndi maganizo amodzi. Palibe munthu amene amati zomwe anali nazo zinali zake zokha, koma amagawana chilichonse chimene anali nacho.

1 AKORINTO 1:10
Ndidandaulira inu, abale, mʼdzina la Ambuye athu Yesu Khristu kuti nonsenu muvomerezane wina ndi mnzake kuti pasakhale kugawikana pakati panu ndi kuti mukhale amodzi kwenikweni mu nzeru ndi mʼmaganizo.

YOHANE 12:48
Iye amene akana Ine ndipo salandira mawu anga ali ndi womuweruza. Tsiku lomaliza mawu amene ndiyankhulawa adzamutsutsa.

YOHANE 14:28
“Inu munamva Ine ndikunena kuti, ‘Ine ndikupita ndipo ndidzabweranso kwa inu.’ Mukanandikonda, mukanasangalala kuti Ine ndikupita kwa Atate, pakuti Atate ndi wamkulu kuposa Ine.

AHEBRI 1:14
Kodi angelo onse si mizimu yotumikira odzalandira chipulumutso?

MATEYU 18:10
“Onetsetsani kuti musanyoze mmodzi wa anawa. Pakuti ndikuwuzani kuti angelo awo kumwamba amakhala pamaso pa Atate anga akumwamba nthawi zonse.”

AEFESO 6:12
Pakuti sitikulimbana ndi thupi ndi magazi, koma tikulimbana ndi maufumu, maulamuliro, mphamvu za dziko la mdima, ndi mphamvu zoyipa kwambiri zauzimu zamlengalenga.

YOHANE 3:16
“Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi, kotero anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira Iye asatayike koma akhale ndi moyo wosatha.

YOHANE 17:17
Ayeretseni ndi choonadi chanu. Mawu anu ndiye choonadi.

CHIVUMBULUTSO 2:9
Ine ndimadziwa masautso ako ndi umphawi wako, chonsecho ndiwe wolemera! Ndikudziwa zimene amakusinjirira anthu amene amati ndi Ayuda pamene sizili choncho, koma ndi a mpingo wa Satana.

MASALIMO 68:5
Atate wa ana amasiye, mtetezi wa akazi amasiye, ndiye Mulungu amene amakhala mʼmalo oyera.

MASALIMO 146:9
Yehova amasamalira alendo ndipo amathandiza ana ndi akazi amasiye, koma amasokoneza njira za anthu oyipa.

AGALATIYA 2:10
Chimene iwo anapempha ndi chakuti ife tipitirize kukumbukira osauka, chinthu chimene ine ndinali okonzeka kuchichita.

AROMA 3:23
pakuti onse anachimwa naperewera pa ulemerero wa Mulungu

Chewa Bible 2016
Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.®