A A A A A

Mulungu: [Madalitso Azachuma]


1 SAMUELE 2:7
Yehova amasaukitsa ndipo amalemeretsa, amatsitsa ndipo amakweza.

2 AKORINTO 8:9
Pakuti mukudziwa chisomo cha Ambuye athu Yesu Khristu, kuti ngakhale anali wolemera, koma chifukwa cha inuyo anasanduka wosauka, kuti umphawi wakewo, inuyo mulemere.

3 YOHANE 1:2
Wokondedwa, ndimakupempherera kuti zako zonse zikuyendere bwino, ndikuti ukhale bwino mʼthupi mwako, monga momwe ulili moyo wako wauzimu.

MLALIKI 9:10
Ntchito iliyonse imene ukuyigwira, uyigwire ndi mphamvu zako zonse, pakuti ku manda kumene ukupita kulibe kugwira ntchito, kulibe malingaliro, chidziwitso ndiponso nzeru.

AGALATIYA 6:9
Tisatope nʼkuchita zabwino, pakuti pa nthawi yoyenera tidzakolola ngati sititopa.

GENESIS 13:2
Abramu anali wolemera kwambiri; anali ndi ziweto ndiponso siliva ndi golide.

HOSEYA 4:6
Anthu anga akuwonongeka chifukwa chosadziwa. “Pakuti mwakana kudziwa, Inenso ndidzakukanani monga ansembe anga; chifukwa mwayiwala lamulo la Mulungu wanu, Inenso ndidzayiwala ana anu.

YAKOBO 5:12
Koposa zonse, abale anga, musamalumbire. Polumbira osamatchula kumwamba kapena dziko lapansi, kapena china chilichonse. “Inde” wanu azikhala “Inde,” ndipo “Ayi” wanu azikhala “Ayi,” kuopa kuti mungadzapezeke olakwa.

YOHANE 6:12
Ndipo atakhuta, Iye anati kwa ophunzira ake, “Tolani zotsala kuti pasawonongeke kanthu.”

LUKA 6:38
Perekani ndipo mudzapatsidwa. Adzakupatsani mʼthumba mwanu muyeso wabwino, wotsenderezeka, wokhutchumuka ndi wosefukira. Pakuti muyeso umene mumagwiritsa ntchito, ndi omwewo adzakuyeserani.”

LUKA 12:34
Popeza kumene kuli chuma chanu, mtima wanunso udzakhala komweko.”

MIYAMBO 10:22
Mdalitso wa Yehova ndiwo umabweretsa chuma, ntchito za munthu siziwonjezerapo kanthu.

MIYAMBO 11:14
Pakasoweka uphungu mtundu wa anthu umagwa; koma pakakhala aphungu ambiri pamakhalanso chipulumutso.

MIYAMBO 19:17
Amene amakomera mtima osauka amachita ngati wakongoletsa Yehova, ndipo Yehovayo ndiye adzamubwezere.

MIYAMBO 21:17
Aliyense wokonda zisangalalo adzasanduka mʼmphawi, ndipo wokonda vinyo ndi mafuta sadzalemera.

MIYAMBO 22:9
Amene ali ndi diso lachifundo adzadalitsika, pakuti iye amagawana chakudya chake ndi anthu osauka.

MIYAMBO 28:22-27
[22] Munthu wowumira amafunitsitsa kulemera koma sazindikira kuti umphawi udzamugwera.[23] Amene amadzudzula mnzake potsiriza pake mnzakeyo adzamukonda kwambiri, kupambana amene amanena mawu oshashalika.[24] Amene amabera abambo ake kapena amayi ake namanena kuti “kumeneko sikulakwa,” ndi mnzake wa munthu amene amasakaza.[25] Munthu wadyera amayambitsa mikangano, koma amene amadalira Yehova adzalemera.[26] Amene amadzidalira yekha ndi chitsiru, koma amene amatsata nzeru za ena adzapulumuka.[27] Amene amapereka kwa osauka sadzasowa kanthu, koma amene amatsinzina maso ake adzatembereredwa kwambiri.

MASALIMO 24:1
Salimo la Davide. Dziko lapansi ndi la Yehova ndi zonse zimene zili mʼmenemo, dziko ndi onse amene amakhala mʼmenemo;

MATEYU 6:33
Koma muyambe mwafuna ufumu wake ndi chilungamo chake ndipo zinthu zonsezi zidzapatsidwa kwa inu.

MATEYU 23:23
“Tsoka kwa inu, aphunzitsi amalamulo ndi Afarisi, achiphamaso! Mumapereka chakhumi cha timbewu tonunkhira ndi cha timbewu tokometsera chakudya. Koma mwasiya zofunikira kwambiri za mʼmalamulo monga chilungamo, chifundo ndi kukhulupirika. Muyenera kuchita zomalizirazi komanso osasiya zoyambazo.

MATEYU 25:21
“Ambuye ake anayankha nati, ‘Wachita bwino, wantchito wabwino ndi wokhulupirika iwe! Wakhala wokhulupirika pa zinthu zochepa; ndidzakuyika iwe kukhala woyangʼanira zinthu zambiri. Bwera, udzakondwere pamodzi ndi mbuye wako!’

AROMA 13:8
Musakhale ndi ngongole ndi wina aliyense kupatula ngongole ya kukondana wina ndi mnzake. Pakuti amene amakonda munthu mnzake wakwaniritsa lamulo.

MIYAMBO 3:9-10
[9] Uzilemekeza Yehova ndi chuma chako chonse; zokolola zonse zoyamba kucha uzilemekeza nazonso Yehova.[10] Ukatero nkhokwe zako zidzadzaza ndi zinthu zambiri, ndiponso mitsuko yako idzadzaza ndi vinyo.

MASALIMO 121:1-2
[1] Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. Ndikweza maso anga ku mapiri; kodi thandizo langa limachokera kuti?[2] Thandizo langa limachokera kwa Yehova, wolenga kumwamba ndi dziko lapansi.

MARKO 11:22-23
[22] Yesu anayankha kuti, “Khalani ndi chikhulupiriro mwa Mulungu.[23] Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti ngati wina aliyense angalamule phiri ili kuti, ‘Pita, kadziponye mʼnyanja,’ ndipo wosakayika mu mtima mwake koma kukhulupirira kuti chimene akunena chidzachitika, chidzachitikadi kwa iyeyo.

GENESIS 1:26-27
[26] Zitatha izi Mulungu anati, “Tipange munthu mʼchifanizo chathu, mofanana ndi ife kuti alamulire nsomba za mʼnyanja, mbalame zamlengalenga, nyama zonse zoweta ndi zonse zokwawa za pa dziko lapansi ndi zamoyo zonse zakutchire.”[27] Ndipo Mulungu analenga munthu mʼchifanizo chake. Anawalengadi mʼchifanizo cha Mulungu; analenga iwo, mwamuna ndi mkazi.

2 AKORINTO 9:6-8
[6] Takumbukirani mawu awa: Amene adzala pangʼono, adzakololanso pangʼono, ndipo amene adzala zochuluka, adzakololanso zochuluka.[7] Munthu aliyense apereke chimene watsimikiza mu mtima mwake kuti apereka, osati monyinyirika kapena mokakamizidwa, pakuti Mulungu amakonda wopereka mokondwera.[8] Ndipo Mulungu akhoza kukudalitsani kwambiri, kuti inuyo nthawi zonse mukhale ndi zinthu zokukwanirani, ndiponso ndi zina zochuluka kuti muthandize pa ntchito zonse zabwino.

LUKA 14:28-30
[28] “Taganizani, ngati wina mwa inu akufuna kumanga nsanja, kodi iye sayamba wakhala pansi ndi kuganizira za mtengo wake kuti aone ngati ali ndi ndalama zokwanira kuti atsirizire?[29] Pakuti ngati ayika maziko ndi kulephera kutsiriza, aliyense amene adzayiona adzamuseka,[30] nanena kuti, ‘Munthu uyu anayamba kumanga koma sanathe kutsiriza.’

LUKA 6:34-36
[34] Ndipo ngati mukongoza amene mukuyembekeza kuti abweza, mwapindula chiyani? Ngakhale ‘ochimwa’ amabwereketsa kwa ochimwa anzawo, ndipo amayembekezera kubwezeredwa zonse.[35] Koma kondani adani anu, achitireni zabwino, akongozeni koma osayembekezera kulandira kanthu. Pamenepo mphotho yanu idzakhala yayikulu ndipo inu mudzakhala ana a Wammwambamwamba, chifukwa ndi wokoma mtima kwa anthu osayamika ndi oyipa.[36] Khalani achifundo, monga momwe Atate anu ali achifundo.”

YAKOBO 5:1-3
[1] Tsono tamverani, inu anthu achuma, lirani ndi kufuwula chifukwa cha zovuta zimene zidzakugwereni.[2] Chuma chanu chawola ndipo njenjete zadya zovala zanu.[3] Golide ndi siliva wanu zachita dzimbiri. Dzimbirilo lidzakhala umboni wokutsutsani ndi kuwononga mnofu wanu ngati moto. Mwadziwunjikira chuma pa masiku ano otsiriza.

GENESIS 12:1-20
[1] Tsiku lina Yehova anamuwuza Abramu kuti, “Tuluka mʼdziko lako. Siya abale ako ndi banja la abambo ako ndipo pita ku dziko limene ndidzakusonyeza.[2] “Ndidzakusandutsa kholo la mtundu waukulu wa anthu ndipo ndidzakudalitsa; ndi kukusandutsa wotchuka kotero kuti udzakhala dalitso kwa anthu ambiri.[3] Ndidzadalitsa amene adzadalitsa iwe, ndi kutemberera amene adzatemberera iwe; ndipo mafuko onse a pa dziko lapansi adzadalitsika kudzera mwa iwe.”[4] Choncho Abramu ananyamuka monga momwe Yehova anamuwuzira, napita pamodzi ndi Loti. Pamene Abramu amachoka ku Harani nʼkuti ali ndi zaka 75.[5] Abramu anatenga mkazi wake Sarai, Loti, mwana wamngʼono wake, pamodzi ndi chuma chawo chimene anapeza ndi antchito amene anali nawo ku Harani. Iwo ananyamuka ulendo mpaka kukafika ku dziko la Kanaani.[6] Abramu anadutsa mʼdzikomo mpaka kukafika ku Sekemu pa mtengo wa thundu wa ku More. Nthawi imeneyo Akanaani analipobe mʼdzikomo.[7] Yehova anadza kwa Abramu nati, “Kwa zidzukulu zako ndidzapereka dziko limeneli.” Choncho Abramu anamangira Yehova amene anadza kwa iye, guwa lansembe.[8] Atachoka pamenepo analowera cha ku mapiri a kummawa kwa Beteli namangako tenti yake pakati pa Beteli chakumadzulo ndi Ai chakummawa. Kumeneko anamangira Yehova guwa lansembe napemphera mʼdzina la Yehovayo.[9] Kenaka Abramu ananyamuka kumalowera cha ku Negevi.[10] Kunagwa njala yayikulu mʼdzikomo, ndipo Abramu anapita ku Igupto kukakhala ngati mlendo kwa kanthawi kochepa popeza njalayo inakula kwambiri.[11] Atatsala pangʼono kulowa mu Igupto, Abramu anamuwuza mkazi wake Sarai kuti, “Ndimadziwa kuti ndiwe mkazi wokongola kwambiri.[12] Tsono Aigupto akakuona adzanena kuti ‘Ameneyu ndi mkazi wake.’ Tsono adzandipha ine nakusiya iwe ndi moyo.[13] Tsono udzikawawuza kuti iwe ndiwe mlongo wanga. Ukatero zidzandiyendera bwino ndipo ndidzapulumuka chifukwa cha iwe.”[14] Pamene Abramu anafika ku Igupto, Aigupto aja anaona kuti Sarai anali mkazi wokongoladi.[15] Pamene akuluakulu a ku nyumba ya Farao anamuona, anakamuyamikira pamaso pa Farao ndipo ananka naye ku nyumba ya Farao.[16] Abramu naye zinthu zinkamuyendera bwino chifukwa cha Sarai. Farao anamupatsa nkhosa, ngʼombe, abulu aamuna ndi abulu aakazi, antchito aakazi pamodzi ndi ngamira.[17] Koma Yehova anabweretsa matenda owopsa pa Farao pamodzi ndi banja lake lonse chifukwa cha Sarai mkazi wa Abramu.[18] Choncho Farao anayitanitsa Abramu namufunsa kuti, “Nʼchiyani wandichitirachi? Nʼchifukwa chiyani sunandiwuze kuti ameneyu ndi mkazi wako?[19] Nʼchifukwa chiyani unati ndi mlongo wako, mpaka ine ndinamutenga kukhala mkazi wanga? Eko mkazi wako. Mutenge uzipita!”[20] Farao analamula asilikali ake ndipo iwo anamutulutsa Abramu pamodzi ndi mkazi wake ndi zonse anali nazo.

MATEYU 6:1-34
[1] “Samalani kuti musachite ntchito zanu zolungama pamaso pa anthu kuti akuoneni. Popeza ngati mutero simudzalandira mphotho yochokera kwa Atate anu akumwamba.[2] “Pamene mupereka zachifundo, musachite modzionetsera monga amachita achiphamaso mʼmasunagoge ndi pa misewu kuti atamidwe ndi anthu. Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti iwowo alandiriratu mphotho yawo yonse.[3] Koma pamene mupereka zachifundo, dzanja lanu lamanzere lisadziwe chimene dzanja lanu lamanja likuchita,[4] kotero kuti kupereka kwanu kukhale mwachinsinsi. Ndipo Atate anu amene amaona zochitika mwachinsinsi, adzakupatsani mphotho.[5] “Pamene mupemphera, musakhale ngati achiphamaso, chifukwa iwo amakonda kupemphera choyimirira mʼmasunagoge ndi pa mphambano za mʼmisewu kuti anthu awaone. Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti iwo alandiriratu mphotho yawo yonse.[6] Koma pamene mupemphera, lowani mʼchipinda chanu chamʼkati, ndi kutseka chitseko ndipo mupemphere kwa Atate anu amene saoneka. Ndipo Atate anu, amene amaona zochitika mseri, adzakupatsani mphotho.[7] Ndipo pamene mukupemphera, musamabwerezabwereza monga akunja, pakuti iwo amaganiza kuti adzamveka chifukwa chochulutsa mawu.[8] Musakhale ngati iwo chifukwa Atate anu amadziwa zimene musowa musanapemphe.[9] “Chifukwa chake pempherani motere: “ ‘Atate athu akumwamba, dzina lanu lilemekezedwe,[10] Ufumu wanu ubwere, chifuniro chanu chichitike pansi pano monga kumwamba.[11] Mutipatse chakudya chathu chalero.[12] Mutikhululukire mangawa athu, monga ifenso tawakhululukira amangawa athu.[13] Ndipo musatitengere kokatiyesa; koma mutipulumutse kwa woyipayo.’[14] Ngati inu mukhululukira anthu pamene akuchimwirani, Atate anu akumwamba adzakukhululukirani.[15] Koma ngati inu simukhululukira anthu zolakwa zawo, Atate anunso sadzakukhululukirani machimo anu.[16] “Pamene mukusala kudya, musaonetse nkhope yachisoni monga achita achiphamaso, pakuti iwo amasintha nkhope zawo kuonetsa anthu kuti akusala kudya. Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti iwo alandiriratu mphotho yawo yonse.[17] Koma pamene ukusala kudya, samba mʼmaso nudzole mafuta kumutu,[18] kuti usaonekere kwa anthu kuti ukusala kudya koma kwa Atate ako ali mseri; ndipo Atate ako amene amaona za mseri adzakupatsa mphotho.[19] “Musadziwunjikire chuma pa dziko lapansi, pamene njenjete ndi dzimbiri zimawononga ndi pamene mbala zimathyola ndi kuba.[20] Koma mudziwunjikire chuma kumwamba kumene njenjete ndi dzimbiri siziwononga ndipo mbala sizithyola ndi kuba.[21] Pakuti kumene kuli chuma chako, mtima wako udzakhala komweko.[22] “Diso ndi nyale ya thupi. Ngati maso ako ali bwino, thupi lako lonse lidzakhala mʼkuwala.[23] Koma ngati maso ako sali bwino, thupi lako lonse lidzakhala mu mdima. Koma ngati kuwala kuli mwa iwe ndi mdima, ndiye kuti mdimawo ndi waukulu bwanji![24] “Palibe munthu angathe kukhala kapolo wa ambuye awiri. Pakuti pena adzamuda mmodzi ndi kukonda winayo kapena adzagwira ntchito mokhulupirika kwa mmodzi, nadzanyoza winayo. Simungathe kukhala kapolo wa Mulungu ndi wa chuma pa nthawi imodzi.[25] “Nʼchifukwa chake ndikuwuzani kuti musadere nkhawa za moyo wanu kuti mudzadya chiyani kapena mudzamwa chiyani; kapenanso za thupi lanu kuti mudzavala chiyani. Kodi moyo suposa chakudya? Kodi thupi siliposa zovala?[26] Onani mbalame zamlengalenga sizifesa kapena kukolola kapena kusunga mʼnkhokwe komabe Atate anu akumwamba amazidyetsa. Kodi inu simuziposa kwambiri?[27] Kodi ndani wa inu podandaula angathe kuwonjeza ora limodzi pa moyo wake?[28] “Ndipo bwanji inu mudera nkhawa za zovala? Onani makulidwe a maluwa akutchire. Sagwira ntchito kapena kuwomba nsalu.[29] Ndikukuwuzani kuti angakhale Solomoni mu ulemerero wake sanavale mofanana ndi limodzi la maluwa amenewa.[30] Ngati umu ndi mmene Mulungu avekera udzu wa kutchire umene ulipo lero ndipo mawa uponyedwa ku moto, kodi sadzakuvekani koposa? Aa! Inu a chikhulupiriro chochepa![31] Chifukwa chake musadere nkhawa ndi kuti, ‘Tidzadya chiyani?’ kapena ‘Tidzamwa chiyani?’ kapena ‘Tidzavala chiyani?’[32] Pakuti anthu akunja amazifuna zinthu zonsezi ndipo Atate anu akumwamba adziwa kuti musowa zimenezi.[33] Koma muyambe mwafuna ufumu wake ndi chilungamo chake ndipo zinthu zonsezi zidzapatsidwa kwa inu.[34] Chifukwa chake musadere nkhawa ndi za mawa, popeza tsiku lililonse lili ndi zovuta zake zokwanira.

DEUTERONOMO 28:1-68
[1] Ngati mumvera Yehova Mulungu wanu ndi kutsatira mosamalitsa malamulo ake onse amene ndikukupatsani lero lino, Yehova Mulungu wanu adzakukwezani pamwamba pa mitundu yonse ya pa dziko lapansi.[2] Madalitso awa adzabwera kwa inu ndi kuyenda nanu ngati mumvera Yehova Mulungu wanu:[3] Mudzadalitsika mʼmizinda yanu ndi kudalitsika mʼdzikolo.[4] Yehova adzadalitsa ana anu, zokolola za mʼdziko lanu, ngʼombe zanu pamodzi ndi ziweto zanu zonse.[5] Dengu lanu ndi chiwaya chanu cha buledi zidzadalitsika.[6] Mudzadalitsika pa kulowa kwanu ndi pa kutuluka kwanu.[7] Yehova adzaonetsetsa kuti adani anu amene adzakuwukirani agonjetsedwe pamaso panu. Iwo adzabwera kwa inu kuchokera mbali imodzi koma adzakuthawani ku mbali zisanu ndi ziwiri.[8] Yehova adzatumiza madalitso pa nkhokwe zanu ndi pa chilichonse chimene muchikhudza. Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani mʼdziko limene akukupatsani.[9] Yehova Mulungu wanu adzachititsa kuti mukhale anthu ake opatulika, monga momwe analonjezera pa malumbiro ake, ngati musunga malamulo ake ndi kuyenda mʼnjira zake.[10] Pamenepo anthu onse a dziko lapansi adzaona kuti mumadziwika ndi dzina la Yehova ndipo adzakuopani.[11] Yehova adzakupambanitsani kwambiri ndipo adzakupatsani ana ambiri, ziweto zambiri, ndi zokolola zochuluka, mʼdziko limene Yehova analumbira kwa makolo anu kuti adzakupatsani.[12] Yehova adzatsekula kumwamba kumene amasungirako chuma chake, kutumiza mvula mʼdziko lanu pa nthawi yake ndi kudalitsa ntchito yonse ya manja anu. Mudzakongoza mitundu yambiri koma inu simudzakongola kwa aliyense.[13] Yehova adzakuthandizani kukhala mutu osati mchira. Mukakhala ndi chidwi ndi malamulo a Yehova Mulungu wanu amene ndikukupatsani lero lino ndi kuwatsata mosamalitsa, inu mudzakhala apamwamba nthawi zonse osati apansi.[14] Musapatukire ku dzanja lamanja kapena lamanzere pa lamulo lina lililonse limene ndikukupatsani lero lino ndi kumatsatira kapena kuyitumikira milungu ina.[15] Koma ngati simumvera Yehova Mulungu wanu ndi kusatsata mosamalitsa malamulo ake ndi malangizo ake onse amene ndikukupatsani lero lino, matemberero awa adzabwera pa inu ndikukugonjetsani:[16] Mudzatembereredwa mu mzinda ndi kutembereredwa mʼmudzi.[17] Dengu lanu ndi chiwaya chanu cha buledi zidzatembereredwa.[18] Zipatso za mʼmimba mwanu zidzatembereredwa, ndiponso zomera za mʼdziko lanu, ana angʼombe zanu ndi ana ankhosa zanu zidzatembereredwa.[19] Mudzatembereredwa pa kulowa kwanu ndi pa kutuluka kwanu.[20] Yehova adzakutumizirani matemberero, chisokonezo ndi minyozo pa chilichonse chimene mudzachichita mpaka mudzawonongedwa ndi kukhala bwinja mofulumira chifukwa cha zoyipa zimene mwazichita pa kumutaya Yehova.[21] Yehova adzakugwetserani mliri wa matenda mpaka atakuwonongani mʼdziko limene mukulowa kukalitengali.[22] Yehova adzakukanthani ndi nthenda yowondetsa, ya malungo ndi ya zotupatupa, ndi kutentha kwakukulu ndi chilala, ndi chinsikwi ndi chiwawu zimene zidzakusautsani mpaka mutawonongeka.[23] Mitambo ya pamutu panu idzawuma ngati mkuwa ndipo sidzagwetsa mvula mpaka nthaka yanu idzawuma gwaa ngati chitsulo.[24] Mʼmalo mwa mvula Yehova adzakupatsani fumbi ndi dothi ndipo lidzakugwerani kuchokera kumwamba mpaka mutawonongeka.[25] Yehova adzalola kuti adani anu akugonjetseni. Mudzadzera njira imodzi pokalimbana ndi adani anu koma pothawa mudzabalalika mbali zisanu ndi ziwiri. Mudzakhala chinthu chochititsa mantha pakati pa maufumu onse a dziko lapansi.[26] Mitembo yanu idzadyedwa ndi mbalame zamumlengalenga ndi nyama zakutchire, ndipo palibe amene adzaziyingitse.[27] Yehova adzakusautsani ndi zithupsa za ku Igupto ndi zotupatupa, zipere, ndi mphere zimene simudzachiritsika nazo.[28] Yehova adzakusautsani inu ndi misala, khungu ndi chisokonekero cha maganizo.[29] Masanasana mudzayenda ngati muli mu mdima, kumafufuzira njira ngati wosaona. Mudzakhala olephera pa chilichonse mungachite. Tsiku ndi tsiku mudzaponderezedwa ndi kuberedwa wopanda wokupulumutsani.[30] Mudzachita chinkhoswe ndi mkazi, koma wina adzakulandani ndi kumukwatira. Mudzamanga nyumba koma simudzagonamo. Mudzalima munda wamphesa koma simudzadyako zipatso zake.[31] Ngʼombe yanu yamtheno idzaphedwa inu muli pomwepo koma simudzadyako. Bulu wanu adzalandidwa kwa inu mwamakani osabwera nayenso. Nkhosa zanu zidzapatsidwa kwa adani anu, ndipo palibe amene adzazipulumutsa.[32] Ana anu aamuna ndi aakazi adzaperekedwa kwa anthu a mitundu ina ndipo inu mudzafika potopa ndi kulefuka nʼkudikirira tsiku ndi tsiku kuti mwina anawo abwerako.[33] Anthu amene simukuwadziwa adzakudyerani zokolola zanu, ndipo mudzakhala mukuponderezedwa mwankhanza masiku onse.[34] Zimene muzidzaziona zidzakusokonezani mitu.[35] Yehova adzakusautsani ndi zithupsa zaululu ndi zosachiritsika za mʼmawondo ndi mʼmiyendo ndipo zidzafalikira kuchoka kuphazi mpaka kumutu.[36] Yehova adzakuthamangitsirani, inu ndi mafumu anu amene muwayika, ku dziko losadziwika kwa inu ndi kwa makolo anu. Kumeneko mudzakapembedza milungu ina, milungu ya mitengo ndi miyala.[37] Inu mudzakhala chinthu chochititsa mantha kuchisunga ndiponso chinthu chotukwanidwa ndi chonyozeka kwa anthu a mitundu yonse kumene Yehova adzakuthamangitsirani.[38] Mudzadzala mbewu zambiri ku munda koma mudzakolola pangʼono, chifukwa dzombe lidzaziwononga.[39] Mudzadzala mpesa ndi kulimirira koma vinyo wake simudzamumwa kapena kukolola mphesazo, chifukwa mphutsi zidzadya mphesazo.[40] Mudzakhala ndi mitengo ya olivi mʼdziko lanu lonse koma simudzagwiritsa ntchito mafuta ake, chifukwa zipatso zake zidzayoyoka.[41] Mudzabereka ana aamuna ndi aakazi koma sadzakhala anu, chifukwa adzapita ku ukapolo.[42] Magulumagulu a dzombe adzawononga mitengo yanu ndi mbewu za mʼdziko lanu.[43] Mlendo wokhala pakati panu adzatukuka kuposa inu, koma inuyo mudzaloweralowera pansi.[44] Iye adzakubwereketsani, koma inu simudzatha kubwereketsa. Iye adzakhala mutu ndipo inu mudzakhala mchira.[45] Matemberero onsewa adzabwera pa inu. Adzakulondolani ndi kukugonjetsani mpaka mutawonongeka, chifukwa simunamvere Yehova Mulungu wanu ndi kusunga malamulo ndi malangizo amene anakupatsani.[46] Matemberero amenewa adzakhala chizindikiro ndi chozizwitsa kwa inu ndi zidzukulu zanu mpaka kalekale.[47] Pakuti inu simunatumikire Yehova Mulungu wanu pa nthawi imene zinthu zinkakuyenderani bwino,[48] chomwecho pa nthawi ya njala ndi ludzu, ya maliseche ndi umphawi woopsa, mudzatumikira adani amene Yehova adzakutumizirani. Iye adzayika goli lachitsulo mʼkhosi mwanu kufikira atakuwonongani.[49] Yehova adzakutumizirani mtundu wa anthu kuchokera kutali kumapeto kwa dziko lapansi nudzachita ngati mphungu yowulukira pansi, mtundu wa anthu umene chiyankhulo chawo simudzachimva,[50] mtundu wooneka wochititsa mantha, wopanda ulemu kwa okalamba kapena chisoni kwa ana.[51] Iwo adzagwira ana a ziweto zanu, natenga zokolola za mʼdziko lanu kufikira mutawonongeka. Iwo sadzakusiyirani tirigu, vinyo watsopano kapena mafuta a olivi, kapena mwana wangʼombe aliyense kapena mwana wankhosa mpaka mutasanduka bwinja.[52] Iwo adzathira nkhondo mizinda yonse mʼdziko lanu lonse mpaka malinga anu ataliatali omwe mumadalira aja atagwa. Adzathira nkhondo mizinda yonse ya mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani.[53] Chifukwa cha zosautsa zimene mdani wanu adzabweretsa pa nthawi yokuthirani nkhondo, inu mudzadya ana anu, mnofu wa ana anu aamuna ndi aakazi amene Yehova Mulungu wanu wakupatsani.[54] Ngakhale munthu woleza mtima ndi wachifundo kwambiri pakati panu sadzakhala ndi chifundo pa mʼbale wake weniweni kapena mkazi wake amene iye amamukonda kapena ana ake otsalawo,[55] ndipo sadzagawirako aliyense wa iwo mnofu wa ana ake amene akudyawo. Kadzakhala kali komweko basi kamene kamutsalira chifukwa cha msautso umene mdani wanu adzagwetsa pa nthawi yothira nkhondo mizinda yanu yonse.[56] Mayi woleza mtima ndi wachifundo kwambiri pakati panu, uja woti sangayerekeze kuponda pansi, adzabisira mwamuna wake amene amamukonda ndi ana ake omwe aamuna ndi aakazi[57] zotsalira za uchembere zochoka mʼmimba mwake ndi ana amene wabereka. Pakuti adzafuna kuti adye zimenezi yekha mobisa pa nthawi yothiridwa nkhondo chifukwa cha masautso amene mdani wanu adzagwetsa pa inu mʼmizinda yanu.[58] Ngati simutsata mosamalitsa mawu onse a malamulo awa amene alembedwa mʼbuku lino, komanso ngati simuopa dzina la ulemerero ndi loopsa, dzina la Yehova Mulungu wanu,[59] Yehova adzatumiza pa inu ndi zidzukulu zanu miliri yoopsa, zosautsa zowawa ndi zokhalitsa, ndi matenda aakulu ndi ovuta kuchiritsika.[60] Adzakubweretserani matenda onse a ku Igupto aja mumawaopawa ndipo adzakukanirirani.[61] Yehova adzakubweretseraninso mtundu uliwonse wa matenda ndi zosautsa zimene sizinalembedwe mʼbuku la malamulo lino, mpaka mutawonongeka.[62] Inu aja munali ochuluka ngati nyenyezi zakumwamba mudzatsala ochepa chabe chifukwa simunamvere Yehova Mulungu wanu.[63] Monga kunamukomera Yehova kukulemeretsani ndi kukuchulukitsani, momwemonso kudzamukondweretsa kukunthani ndi kukuwonongani. Inu mudzazulidwa kukuchotsani mʼdziko limene mukulowa kukalitengali.[64] Kenaka Yehova adzakubalalitsani pakati pa anthu a mitundu yonse, kuchokera ku mapeto a dziko kufika ku mapeto ena. Kumeneko mudzapembedza milungu ina, milungu ya mitengo ndi ya miyala, imene inu eni kapena makolo anu sanayidziwepo.[65] Pakati pa mitundu ya anthu imeneyi simudzapeza mpata, popanda malo woti nʼkuyikapo phazi. Kumeneko Yehova adzakupatsani moyo wa nkhawa, maso otopa ndi chiyembekezo, ndi mtima wosakhazikika.[66] Inu mudzakhala osakhazikika mopitirira, odzazidwa ndi mantha usiku ndi usana womwe, osowa chitsimikizo cha pa moyo wanu.[67] Mmawa muzidzati, “Chikhala anali madzulo!” ndipo madzulo mudzati, “Chikhala unali mmawa!” Mudzanena zimenezi chifukwa cha mantha amene adzakhale mu mtima mwanu ndi chifukwa cha zomwe muzidzaziona.[68] Yehova adzakubwezani ku Igupto pa sitima zapamadzi paulendo umene Ine ndinati musawuyendenso. Kumeneko mudzadzitsatsa nokha kwa adani anu monga akapolo aamuna ndi aakazi, koma palibe amene adzakuguleni.

Chewa Bible 2016
Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.®