A A A A A

Khalidwe Loipa: [Mkwiyo]


AEFESO 4:26-31
[26] Kwiyani koma musachimwe. Dzuwa lisalowe mukanali chikwiyire.[27] Musamupatse mpata Satana.[28] Iye amene wakhala akuba asabenso, koma agwire ntchito ndi kuchita kenakake kaphindu ndi manja ake, kuti akhale ndi kenakake kogawana ndi amene akusowa.[29] Mʼkamwa mwanu musatuluke mawu aliwonse onyansa, koma okhawo amene ndi othandiza kulimbikitsa ena molingana ndi zosowa zawo, kuti athandize amene akawamve.[30] Ndipo musamvetse chisoni Mzimu Woyera wa Mulungu amene mwasindikizidwa naye chizindikiro cha tsiku la kuwomboledwa.[31] Chotsani kuzondana, ukali ndi kupsa mtima, chiwawa ndi kuyankhula zachipongwe, pamodzi ndi choyipa chilichonse.

YAKOBO 1:19-20
[19] Abale anga okondedwa, gwiritsitsani mawu awa: munthu aliyense azifulumira kumva, koma asamafulumire kuyankhula, ndipo asamafulumirenso kupsa mtima.[20] Pakuti mkwiyo wa munthu subweretsa chilungamo chimene amafuna Mulungu.

MIYAMBO 29:11
Munthu wopusa amaonetsa mkwiyo wake, koma munthu wanzeru amadzigwira.

MLALIKI 7:9
Usamafulumire kukwiya mu mtima mwako, pakuti mkwiyo ndi bwenzi la zitsiru.

MIYAMBO 15:1
Kuyankha kofatsa kumathetsa mkwiyo, koma mawu ozaza amautsa ukali.

MIYAMBO 15:18
Munthu wopsa mtima msanga amayambitsa mikangano, koma munthu woleza mtima amathetsa ndewu.

AKOLOSE 3:8
Koma tsopano mukuyenera kuzichotsa zinthu zonsezi monga: mkwiyo, ukali, dumbo, chipongwe ndi mawu onyansa.

YAKOBO 4:1-2
[1] Nʼchiyani chimene chimayambitsa ndewu ndi mapokoso pakati panu? Kodi sizichokera ku zilakolako zimene zimalimbana mʼkati mwanu?[2] Mumalakalaka zinthu koma simuzipeza, choncho mumapha. Mumasirira zinthu koma simutha kuzipeza zimene mukufuna, choncho mumakangana ndi kumenyana. Mulibe zinthuzo chifukwa simupempha kwa Mulungu.

MIYAMBO 16:32
Munthu wosapsa mtima msanga amaposa munthu wankhondo, munthu wowugwira mtima wake amaposa amene amalanda mzinda.

MIYAMBO 22:24
Usapalane naye ubwenzi munthu wosachedwa kupsa mtima ndipo usayanjane ndi munthu amene sachedwa kukwiya

MATEYU 5:22
Koma Ine ndikukuwuzani kuti aliyense wokwiyira mʼbale wake adzapezeka wolakwa ku bwalo la milandu. Ndiponso aliyense amene wonena mʼbale wake kuti, ‘Ndiwe wopanda phindu,’ adzapezeka wolakwa ku bwalo la milandu lalikulu. Ndipo aliyense amene anganene mnzake ‘wopandapake’ adzatengeredwa ku bwalo la milandu. Ndiponso aliyense amene angamunene mnzake kuti, ‘Chitsiru iwe,’ adzaponyedwa ku gehena.

MASALIMO 37:8-9
[8] Pewa kupsa mtima ndipo tembenuka kuchoka ku ukali, usavutike chifukwa zimenezi zimatsogolera ku zoyipa.[9] Pakuti anthu oyipa adzachotsedwa, koma iwo amene amayembekeza mwa Yehova adzalandira dziko.

MASALIMO 7:11
Mulungu amaweruza molungama, Mulungu amene amaonetsa ukali wake tsiku ndi tsiku.

2 MAFUMU 11:9-10
[9] Atsogoleri olamulira asilikali 100 aja anachitadi zonse monga analamulira wansembe Yehoyada. Aliyense anatenga anthu ake, iwo amene amakagwira ntchito pa tsiku la Sabata ndi amene amapita kukapuma ndipo anabwera kwa wansembe Yehoyada.[10] Ndipo wansembeyo anawapatsa asilikaliwo mikondo ndi zishango zimene zinali za mfumu Davide ndipo zinali mʼNyumba ya Yehova.

2 MAFUMU 17:18
Choncho Yehova anakwiya nawo kwambiri Aisraeli ndipo anawachotsa pamaso pake. Palibe amene anatsala kupatula fuko la Yuda lokha.

MIYAMBO 14:29
Munthu wosapsa mtima msanga amamvetsa zinthu kwambiri, koma munthu wopsa mtima msanga amaonetsa uchitsiru wake.

Chewa Bible 2016
Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.®