A A A A A

Zowonjezera: [Kudya munthu wina]


YEREMIYA 19:9
Adani awo adzawuzinga mzindawo kufuna kuwapha motero kuti anthu a mʼkatimo adzafika pomadyana wina ndi mnzake. Adzadya ana awo aamuna ndi ana awo aakazi.’

EZEKIELE 5:10
Tsono pakati panu makolo adzadya ana awo, ndipo ana adzadya makolo awo. Ndidzakulanga ndipo otsala onse ndidzawabalalitsa ku mphepo zonse zinayi.

LEVITIKO 26:29
Mudzadya ana anu aamuna ndiponso mudzadya ana anu aakazi.

2 MAFUMU 6:28-29
[28] Pamenepo mfumuyo inafunsa mayiyo kuti, “Kodi chakuvuta nʼchiyani?” Iye anayankha kuti, “Mayi uyu anandiwuza kuti, ‘Bweretsa mwana wako kuti timudye lero, ndipo mawa tidzadya mwana wangayu.’[29] Choncho tinaphika mwana wanga ndi kumudya. Tsiku lotsatira lakelo ine ndinati, ‘Bweretsa mwana wako kuti timudye,’ koma iye anabisa mwana wakeyo.”

MALIRO 4:10
Amayi achifundo afika pophika ana awo enieni, ndiwo anali chakudya chawo pamene anthu anga anali kuwonongeka.

MALIRO 2:20
Inu Yehova, onani, ndipo ganizirani: kodi ndani amene mwamuchitirapo zinthu ngati izi? Kodi amayi adye ana awo, amene amawasamalira? Kodi ansembe ndi aneneri awaphere mʼmalo opatulika a Ambuye?

DEUTERONOMO 28:53-57
[53] Chifukwa cha zosautsa zimene mdani wanu adzabweretsa pa nthawi yokuthirani nkhondo, inu mudzadya ana anu, mnofu wa ana anu aamuna ndi aakazi amene Yehova Mulungu wanu wakupatsani.[54] Ngakhale munthu woleza mtima ndi wachifundo kwambiri pakati panu sadzakhala ndi chifundo pa mʼbale wake weniweni kapena mkazi wake amene iye amamukonda kapena ana ake otsalawo,[55] ndipo sadzagawirako aliyense wa iwo mnofu wa ana ake amene akudyawo. Kadzakhala kali komweko basi kamene kamutsalira chifukwa cha msautso umene mdani wanu adzagwetsa pa nthawi yothira nkhondo mizinda yanu yonse.[56] Mayi woleza mtima ndi wachifundo kwambiri pakati panu, uja woti sangayerekeze kuponda pansi, adzabisira mwamuna wake amene amamukonda ndi ana ake omwe aamuna ndi aakazi[57] zotsalira za uchembere zochoka mʼmimba mwake ndi ana amene wabereka. Pakuti adzafuna kuti adye zimenezi yekha mobisa pa nthawi yothiridwa nkhondo chifukwa cha masautso amene mdani wanu adzagwetsa pa inu mʼmizinda yanu.

GENESIS 1:26-27
[26] Zitatha izi Mulungu anati, “Tipange munthu mʼchifanizo chathu, mofanana ndi ife kuti alamulire nsomba za mʼnyanja, mbalame zamlengalenga, nyama zonse zoweta ndi zonse zokwawa za pa dziko lapansi ndi zamoyo zonse zakutchire.”[27] Ndipo Mulungu analenga munthu mʼchifanizo chake. Anawalengadi mʼchifanizo cha Mulungu; analenga iwo, mwamuna ndi mkazi.

2 AKORINTO 5:8
Inde, ife tikulimba mtima, ndipo tikanakonda kulekana nalo thupi lathu ndi kukhala ndi Ambuye.

LUKA 16:19-26
[19] “Panali munthu wachuma amene ankavala zovala zofiirira za mtengowapatali ndipo ankakhala moyo wachisangalalo tsiku lililonse.[20] Pa khomo la mpanda wake ankagonekapo munthu wopempha wotchedwa Lazaro, wazilonda thupi lonse[21] ndipo ankafunitsitsa atadya zomwe zinkagwa pansi kuchokera pamene munthu wolemerayo amadyerapo. Agalu ankabweranso ndi kumanyambita zilonda zake.[22] “Nthawi inafika imene wopemphayo anamwalira ndipo angelo anamunyamula nakamuyika mʼmanja mwa Abrahamu. Munthu wolemerayo anamwaliranso ndipo anayikidwa mʼmanda.[23] Ali mʼgehena kuzunzika, anakweza maso ake ndipo anaona Abrahamu ali ndi Lazaro pambali pake.[24] Ndipo anafuwula kwa iye kuti, ‘Abambo Abrahamu, mundimvere chisoni ine ndipo mutumeni Lazaroyo kuti aviyike msonga ya chala chake mʼmadzi kuti aziziritse lilime langa, chifukwa ndikumva ululu mʼmoto muno.’[25] “Koma Abrahamu anayankha kuti, ‘Mwanawe kumbukira kuti nthawi yamoyo wako unalandira zinthu zako zabwino, pamene Lazaro analandira zinthu zoyipa, koma tsopano akusangalatsidwa kuno ndipo iwe uli mʼmazunzo.[26] Ndipo kuwonjezera pa zonsezi, pakati pa inu ndi ife pali chiphompho chachikulu chimene chinayikidwa, kotero kuti amene akufuna kubwera kumeneko sangathe, kapena palibe amene angawoloke kuchokera kumeneko kudzafika kuno.’

CHIVUMBULUTSO 20:11-15
[11] Kenaka ndinaona Mpando Waufumu waukulu woyera ndi Iye amene anakhalapo. Dziko lapansi ndi kumwamba zinathawa pamaso pake ndipo panalibenso malo awo.[12] Ndipo ndinaona akufa, aakulu ndi aangʼono omwe atayimirira patsogolo pa Mpando Waufumu ndipo mabuku anatsekulidwa. Buku lina linatsekulidwa limene linali Buku Lamoyo. Akufa anaweruzidwa monga mwa zimene anachita monga mmene zinalembedwera mʼmabuku.[13] Nyanja inapereka amene anaferamo ndipo imfa ndi Hade zinapereka akufa ake ndipo munthu aliyense anaweruzidwa monga mwa ntchito zake.[14] Kenaka imfa ndi Hade zinaponyedwa mʼnyanja ya moto. Nyanja yamoto ndiyo imfa yachiwiri.[15] Ngati dzina la wina aliyense silinapezeke mʼBuku Lamoyo, anaponyedwa mʼnyanja yamoto.

DEUTERONOMO 28:53
Chifukwa cha zosautsa zimene mdani wanu adzabweretsa pa nthawi yokuthirani nkhondo, inu mudzadya ana anu, mnofu wa ana anu aamuna ndi aakazi amene Yehova Mulungu wanu wakupatsani.

1 AKORINTO 14:34-35
[34] Amayi akhale chete mʼmisonkhano ya mpingo. Iwo asaloledwe kuyankhula, koma azikhala omvera monga mmene lamulo linenera.[35] Ngati ali ndi mafunso, akafunse amuna awo ku nyumba. Nʼchochititsa manyazi kuti mkazi ayankhule mu msonkhano wa mpingo.

LUKA 1:37
Pakuti palibe chinthu chosatheka ndi Mulungu.”

YOHANE 1:1
Pachiyambi panali Mawu, ndipo Mawu anali kwa Mulungu, ndipo Mawu ndiye Mulungu.

DEUTERONOMO 28:57
zotsalira za uchembere zochoka mʼmimba mwake ndi ana amene wabereka. Pakuti adzafuna kuti adye zimenezi yekha mobisa pa nthawi yothiridwa nkhondo chifukwa cha masautso amene mdani wanu adzagwetsa pa inu mʼmizinda yanu.

1 TIMOTEO 2:11-15
[11] Amayi azikhala chete pophunzitsidwa ndi mtima ogonjera kwathunthu.[12] Ine sindikulola kuti amayi aziphunzitsa kapena kulamulira amuna; koma akhale chete.[13] Pakuti Adamu ndiye anayamba kupangidwa kenaka Hava.[14] Ndipo Adamu si amene ananyengedwa koma mkazi ndiye amene ananyengedwa nachimwa.[15] Ndipo mkazi adzapulumutsidwa pobereka mwana ngati apitiriza kukhala mʼchikhulupiriro, mʼchikondi ndi mʼkuyera mtima pamodzi ndi kudzichepetsa konse.

1 TIMOTEO 5:3-16
[3] Uziwachitira ulemu akazi amasiye amene ali okhaokha.[4] Koma ngati mkazi wamasiye ali ndi ana ndi zidzukulu, anawo ayambe aphunzira kukwaniritsa udindo wawo pa banja lawo moopa Mulungu, potero akubweza zabwino kwa makolo awo ndi agogo awo. Pakuti zimenezi ndiye zimakondweretsa Mulungu.[5] Mkazi wamasiye amene ali yekha ndi wopanda womuthandiza, ameneyo wayika chiyembekezo chake pa Mulungu, ndipo amapemphera kosalekeza usana ndi usiku kuti Mulungu azimuthandiza.[6] Koma mkazi wamasiye amene amangokhalira kuchita zosangalatsa moyo wake, wafa kale ngakhale akanali ndi moyo.[7] Pereka malangizo amenewa kwa anthu kuti akhale opanda zolakwa.[8] Ngati wina sasamalira abale ake, makamaka a mʼbanja mwake mwenimweni, ameneyo wakana chikhulupiriro ndipo ndi woyipa kuposa wosakhulupirira.[9] Mayi wamasiye aliyense amene sanakwanitse zaka 60 zakubadwa, asakhale mʼgulu la akazi amasiye. Akhale woti anakwatiwapo ndi mwamuna wake mmodzi yekha.[10] Akhale mayi woti amadziwika bwino pa ntchito zake zabwino monga kulera ana, kusamalira alendo, kusambitsa mapazi a anthu a Mulungu, kuthandiza amene ali pa mavuto ndi kudzipereka pa ntchito zonse zabwino.[11] Akazi amasiye achitsikana, usawayike mʼgulu limeneli. Pakuti zilakolako zawo zikayamba kuwavutitsa nʼkuwalekanitsa ndi Khristu, amafuna kukwatiwanso.[12] Zikatero amadziweruza okha chifukwa aphwanya lonjezo lawo loyamba.[13] Komanso amakhala ndi chizolowezi cha ulesi ndi kumangoyenda khomo ndi khomo. Ndipo sikungokhala aulesi kokha komanso kuchita miseche, kududukira za eni ake, kumangokamba zinthu zosayenera kukamba.[14] Kotero, ndikulangiza akazi amasiye achitsikana kuti akwatiwe, akhale ndi ana, asamalire makomo awo ndipo asamupatse mdani mpata wonyoza[15] Akazi amasiye ena apatuka kale nʼkumatsatira Satana.[16] Ngati mayi aliyense wokhulupirira ali ndi akazi amasiye amene akuwasamalira, apitirizebe kuwasamalira ndipo asalemetse mpingo, kuti mpingo uthandize akazi amasiye amene ali okhaokha.

1 AKORINTO 11:2-16
[2] Ndikukuyamikani chifukwa chondikumbukira pa zonse ndiponso posunga ziphunzitso monga ndinakuphunzitsirani.[3] Tsopano ndikufuna muzindikire kuti Khristu ndiye mutu wa munthu aliyense, ndipo mwamuna ndiye mutu wamkazi, ndipo mutu wa Khristu ndi Mulungu.[4] Mwamuna aliyense wopemphera kapena kunenera ataphimba mutu wake akunyoza mutu wakewo.[5] Ndipo mkazi aliyense wopemphera kapena kunenera asanaphimbe mutu wake sakulemekeza mutu wakewo. Kuli chimodzimodzi kumeta mutu wake.[6] Ngati mkazi saphimba kumutu kwake, ndiye kuti amete tsitsi lake. Ngati nʼchamanyazi kwa mkazi kungoyepula kapena kumeta mpala, ndiye kuti aphimbe kumutu kwake.[7] Mwamuna sayenera kuphimba kumutu popeza ndi chifaniziro ndi ulemerero wa Mulungu; pamene mkazi ndi ulemerero wa mwamuna.[8] Pakuti mwamuna sachokera kwa mkazi, koma mkazi kwa mwamuna.[9] Ndipo mwamuna sanalengedwe chifukwa cha mkazi, koma mkazi analengedwera mwamuna.[10] Pa chifukwa ichi, ndiponso pa chifukwa cha angelo, mkazi akuyenera kukhala ndi chizindikiro cha ulamuliro wake.[11] Komabe mwa Ambuye, mkazi amadalira mwamuna ndipo mwamuna amadalira mkazi.[12] Pakuti monga mkazi anachokera kwa mwamuna, momwemonso mwamuna anabadwa mwa mkazi. Koma zonse zichokera kwa Mulungu.[13] Dziweruzeni. Kodi nʼchabwino kuti mkazi apemphere kwa Mulungu wopanda chophimba kumutu?[14] Kodi chikhalidwe chathu sichitiphunzitsa kuti nʼchamanyazi kuti mwamuna akhale ndi tsitsi lalitali,[15] koma mkazi akakhala ndi tsitsi lalitali ndi ulemerero wake? Pakuti mkazi anapatsidwa tsitsi lalitali monga chophimba kumutu.[16] Ngati wina akufuna kutsutsapo pa zimenezi, ife ndiponso mipingo ya Mulungu tilibe machitidwe ena apadera koma ndi omwewa.

Chewa Bible 2016
Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.®