A A A A A

Zowonjezera: [Mtima Wosweka]


1 AKORINTO 13:7
Chimatchinjiriza nthawi zonse, chimakhulupirika nthawi zonse, chimakhala ndi chiyembekezo nthawi zonse, chimapirira nthawi zonse.

1 PETRO 5:7
Tayani pa Iye nkhawa zanu zonse chifukwa ndiye amakusamalani.

1 SAMUELE 16:7
Koma Yehova anati kwa Samueli, “Usaone maonekedwe ake kapena msinkhu wake, pakuti ndamukana iyeyu. Yehova sapenya zimene munthu amapenya. Anthu amapenya zakunja, koma Mulungu amapenya za mu mtima.”

2 AKORINTO 5:7
Ife timakhala mwachikhulupiriro, osati mwa zooneka ndi maso.

2 AKORINTO 12:9
Koma anandiwuza kuti, “Chisomo changa ndi chokukwanira, pakuti mphamvu zanga zimaoneka kwathunthu mwa munthu wofowoka.” Choncho ndidzadzitamandira mokondwera chifukwa cha zofowoka zanga, kuti mʼkutero mphamvu ya Khristu ikhale pa ine.

AHEBRI 13:5
Mtima wanu usakonde ndalama koma mukhutitsidwe ndi zimene muli nazo, chifukwa Mulungu anati, “Sadzakusiyani, kapena kukutayani konse.”

YESAYA 6:1
Chaka chimene mfumu Uziya anamwalira, ndinaona Ambuye atakhala pa mpando waufumu, wautali ndi wokwezedwa, ndipo mkanjo wawo unali wautali; kotero kuti unadzaza mʼNyumba ya Yehova.

YESAYA 41:10
Tsono usaope, pakuti Ine ndili nawe; usataye mtima chifukwa Ine ndine Mulungu wako. Ndidzakupatsa mphamvu ndipo ndidzakuthandiza, ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.

YESAYA 57:15
Pakuti Iye amene ali Wamkulu ndi Wopambanazonse, amene alipo nthawi zonse, amene dzina lake ndi Woyerayo, akunena kuti, “Ndimakhala pamalo aulemu ndi opatulika, koma ndimakhalanso ndi munthu wodzichepetsa ndi wosweka mtima kuti odzichepetsawo ndiwalimbitse ndi kuwachotsa mantha osweka mtima.

YEREMIYA 29:11
Pakuti Ine ndikudziwa zimene ndinakukonzerani,” akutero Yehova, “ndimalingalira zabwino zokhazokha za inu osati zoyipa, ayi. Ndimalingalira zinthu zokupatsani chiyembekezo chenicheni pa za mʼtsogolo.

YOHANE 3:16
“Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi, kotero anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira Iye asatayike koma akhale ndi moyo wosatha.

YOHANE 12:40
“Iye wachititsa khungu maso awo ndi kuwumitsa mitima yawo, kotero kuti iwo sangathe kuona ndi maso awo, kapena kuzindikira ndi mitima yawo, kapena kutembenuka kuti Ine ndikanawachiza.”

YOHANE 14:1
“Mtima wanu usavutike. Khulupirirani Mulungu; khulupirirani Inenso.

YOHANE 14:27
Ine ndikukusiyirani mtendere. Ndikukupatsani mtendere wanga. Ine sindikukupatsani monga dziko lapansi limaperekera. Mtima wanu usavutike ndipo musachite mantha.

YOHANE 16:33
“Ine ndakuwuzani izi kuti mwa Ine mukhale nawo mtendere. Mʼdziko lapansi mudzakhala nawo mavuto. Koma limbikani mtima! Ine ndaligonjetsa dziko lapansi.”

LUKA 24:38
Iye anawafunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani mukuvutika? Nʼchifukwa chiyani mukukayika mu mtima mwanu?

MARKO 11:23
Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti ngati wina aliyense angalamule phiri ili kuti, ‘Pita, kadziponye mʼnyanja,’ ndipo wosakayika mu mtima mwake koma kukhulupirira kuti chimene akunena chidzachitika, chidzachitikadi kwa iyeyo.

MATEYU 5:8
Odala ndi amene ali oyera mtima, chifukwa adzaona Mulungu.

MATEYU 11:28
“Idzani kwa Ine, inu nonse otopa ndi olemedwa ndipo Ine ndidzakupatsani mpumulo.

MIYAMBO 3:5
Uzikhulupirira Yehova ndi mtima wako wonse ndipo usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu.

MASALIMO 34:18
Yehova ali pafupi kwa osweka mtima ndipo amapulumutsa iwo amene asweka mu mzimu.

MASALIMO 51:17
Nsembe za Mulungu ndi mzimu wosweka; mtima wosweka ndi wachisoni Inu Mulungu simudzawunyoza.

MASALIMO 55:22
Tulani nkhawa zanu kwa Yehova ndipo Iye adzakulimbitsani; Iye sadzalola kuti wolungama agwe.

MASALIMO 147:3
Akutsogolera anthu osweka mtima ndi kumanga mabala awo.

CHIVUMBULUTSO 21:4
‘Mulungu adzapukuta misozi yonse mʼmaso mwawo. Sikudzakhalanso imfa kapena kukhuza maliro kapena kulira kapena ululu popeza zakale zapita.’ ”

AROMA 8:28
Ndipo ife tikudziwa kuti zinthu zonse zimathandizana kuwachitira ubwino amene amakonda Mulungu, amene anayitanidwa monga mwa cholinga chake.

AROMA 12:2
Musafanizidwenso ndi makhalidwe a dziko lino koma musandulike pokonzanso maganizo anu. Ndipo mudzadziwa ndi kuzindikira chifuniro chabwino cha Mulungu chomwe ndi chokondweretsa ndi changwiro.

MIYAMBO 4:23
Ndipotu mtima wako uziwuyangʼanira bwino ndithu pakuti ndiwo magwero a moyo.

MIYAMBO 3:5-6
[5] Uzikhulupirira Yehova ndi mtima wako wonse ndipo usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu.[6] Pa zochita zako zonse uvomereze kuti Mulungu alipo, ndipo Iye adzawongola njira zako.

1 AKORINTO 6:19-20
[19] Kodi simukudziwa kuti thupi lanu ndi Nyumba ya Mzimu Woyera, amene ali mwa inu, amene mwalandira kuchokera kwa Mulungu? Inu simuli panokha ayi.[20] Ndinu ochita kugulidwa. Nʼchifukwa chake lemekezani Mulungu mʼthupi lanu.

AFILIPI 4:6-7
[6] Musade nkhawa ndi kanthu kalikonse, koma pa china chilichonse, mwa pemphero ndi chidandaulo pamodzi ndi chiyamiko, perekani zopempha zanu kwa Mulungu.[7] Ndipo mtendere wa Mulungu, umene upambana nzeru zonse udzasunga bwino mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.

MATEYU 11:28-30
[28] “Idzani kwa Ine, inu nonse otopa ndi olemedwa ndipo Ine ndidzakupatsani mpumulo.[29] Senzani goli langa ndipo phunzirani kwa Ine, pakuti ndine wofatsa ndi wodzichepetsa. Ndipo inu mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu.[30] Pakuti goli langa ndi losavuta ndipo katundu wanga ndi wopepuka.”

MASALIMO 34:1-22
[1] Salimo la Davide. Pamene iye ananyengezera misala pamaso pa Abimeleki, amene anamupirikitsa, iyeyo nʼkuchoka. Ndidzayamika Yehova nthawi zonse; matamando ake adzakhala pa milomo yanga nthawi zonse.[2] Moyo wanga udzanyadira Yehova; anthu osautsidwa amve ndi kukondwera.[3] Lemekezani Yehova pamodzi ndi ine; tiyeni pamodzi tikuze dzina lake.[4] Ine ndinafunafuna Yehova ndipo Iye anandiyankha; anandilanditsa ku mantha anga onse.[5] Iwo amene amayangʼana kwa Iye, nkhope zawo zimanyezimira; nkhope zawo sizikhala zophimbidwa ndi manyazi.[6] Munthu wosauka uno anayitana, ndipo Yehova anamumva; Yehova anamupulumutsa ku mavuto ake onse.[7] Mngelo wa Yehova amatchinjiriza amene amakonda Iye ndi kuwalanditsa.[8] Lawani ndipo onani kuti Yehova ndi wabwino; wodala munthu amene amathawira kwa Iye.[9] Wopani Yehova inu oyera mtima ake, pakuti iwo amene amaopa Iye sasowa kanthu.[10] Mikango itha kulefuka ndi kumva njala koma iwo amene amafunafuna Yehova sasowa kanthu kalikonse kabwino.[11] Bwerani ana anga, mundimvere; ndidzakuphunzitsani kuopa Yehova.[12] Aliyense wa inu amene amakonda moyo wake ndi kukhumba kuti aone masiku abwino ambiri,[13] asunge lilime lake ku zoyipa ndi milomo yake kuti isayankhule zonama.[14] Tembenuka kuchoka ku zoyipa ndipo chita zabwino; funafuna mtendere ndi kuwulondola.[15] Maso a Yehova ali pa olungama ndipo makutu ake ali tcheru kumva kulira kwawo;[16] nkhope ya Yehova ikutsutsana ndi amene amachita zoyipa, kuwachotsa kuti asawakumbukirenso pa dziko lapansi.[17] Olungama amafuwula, ndipo Yehova amawamva; Iye amawalanditsa ku mavuto awo onse.[18] Yehova ali pafupi kwa osweka mtima ndipo amapulumutsa iwo amene asweka mu mzimu.[19] Munthu wolungama atha kukhala ndi mavuto ambiri, Koma Yehova amamulanditsa ku mavuto onsewo,[20] Iye amateteza mafupa ake onse, palibe limodzi la mafupawo limene lidzathyoledwa.[21] Choyipa chidzapha anthu oyipa; adani a olungama adzapezeka olakwa.[22] Yehova amawombola atumiki ake; aliyense amene amathawira kwa Iye sadzapezeka wolakwa.

Chewa Bible 2016
Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.®