A A A A A

Zowonjezera: [Fahavetavetana]


DANIELE 11:31
Ary hisy miaramila hitsangana noho ny teniny ka handoto ny fitoerana masina, dia ny fiarovana mafy, ary hampitsahatra ny fanatitra isan'andro sady hampiditra ny fahavetavetana mahatonga fandravana.[Heb. sandry]

DANIELE 12:11
“Kuyambira pamene nsembe ya tsiku ndi tsiku idzathetsedwa ndi kukhazikitsa kwa chonyansa chobweretsa chisokonezo chija, padzapita masiku 1,290.

DEUTERONOMO 22:5
Akazi asavale zovala za amuna, kapena mwamuna kuvala zovala za akazi, pakuti Yehova Mulungu wanu amanyansidwa ndi aliyense wochita izi.

DEUTERONOMO 23:18
Musabweretse malipiro a wachiwerewere wamkazi kapena wamwamuna Mʼnyumba ya Yehova Mulungu wanu kudzapereka za malumbiro aliwonse, chifukwa Yehova Mulungu wanu amadana ndi zimenezi.

DEUTERONOMO 24:4
mwamuna wake woyamba uja, amene anamuleka saloledwanso kumukwatira kachiwiri popeza mkaziyo wadetsedwa. Chimenechi ndi chonyansa pamaso pa Yehova. Musalowetse tchimo mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani ngati cholowa chanu.

YESAYA 1:13
Siyani kubweretsa nsembe zachabechabezo! Nsembe zanu zofukiza zimandinyansa Ine. Sindingapirire misonkhano yanu yoyipa, kapenanso zikondwerero za Mwezi Watsopano ndi Masabata.

LEVITIKO 7:18
Ngati munthu adya nyama yachiyanjano pa tsiku lachitatu, nsembeyo sidzalandiridwa. Amene wayipereka nsembeyo Mulungu sadzamulandira ndipo nsembeyo idzakhala yonyansa pamaso pa Mulungu, yosamupindulira kanthu woperekayo.

LEVITIKO 18:22
“ ‘Usagonane ndi mwamuna ngati mkazi; chimenecho ndi chinthu chonyansa.

MIYAMBO 11:1
Muyeso wachinyengo Yehova umamunyansa, koma amakondwera ndi muyeso woyenera.

MIYAMBO 11:20
Yehova amanyansidwa ndi anthu a mtima wokhotakhota koma amakondwera ndi anthu a makhalidwe angwiro.

MIYAMBO 12:22
Pakamwa pa bodza pamamunyansa Yehova, koma amakondwera ndi anthu oyankhula zoona.

MIYAMBO 15:8
Nsembe za anthu oyipa zimamunyansa Yehova, koma amakondwera ndi pemphero la anthu owona mtima.

MIYAMBO 15:26
Maganizo a anthu oyipa amamunyansa Yehova, koma mawu a anthu oyera mtima amamusangalatsa.

MIYAMBO 16:5
Munthu aliyense wodzikuza amamunyansa Yehova. Koma dziwani izi: Iwo sadzakhala osalangidwa.

MIYAMBO 17:15
Kumasula munthu wolakwa kapena kumanga munthu wosalakwa, zonse ziwirizi Yehova zimamunyansa.

MIYAMBO 20:10
Masikelo ndi miyeso ya zinthu imene ili yachinyengo zonsezi Yehova zimamunyansa.

MIYAMBO 20:23
Miyeso yosintha imamunyansa Yehova; ndipo masikelo onyenga si abwino.

MIYAMBO 28:9
Wokana kumvera malamulo ngakhale pemphero lake lomwe limamunyansa Yehova.

CHIVUMBULUTSO 21:27
Kanthu kosayeretsedwa sikadzalowamo, kuphatikizanso aliyense wochita zinthu zochititsa manyazi ndi zachinyengo, koma okhawo amene mayina awo alembedwa mʼbuku lamoyo la Mwana Wankhosa.

MARKO 13:14
“Mukadzaona ‘chinthu chonyansa chosakaza’ chitayima pa malo amene si ake, owerenga azindikire. Pamenepo amene ali ku Yudeya athawire kumapiri.

MATEYU 24:15
“Tsono mukadzaona chinthu chonyansa chosakaza chitayima pamalo oyera chimene anayankhula mneneri Danieli, owerengayo azindikire.

AROMA 1:26-27
[26] Chifukwa cha ichi, Mulungu anawasiya kuti azitsata zilakolako zochititsa manyazi. Ngakhale akazi omwe anasiya machitidwe achibadwidwe pa za ukwati, namachita machitidwe ena otsutsana ndi chibadwa chawo.[27] Chimodzimodzinso amuna analeka machitidwe a ukwati ndi akazi nʼkumakhumbana amuna okhaokha. Amuna ankachita zochitisa manyazizi ndi amuna anzawo, ndipo analandira chilango choyenera molingana ndi zochita zawo zachitayikozo.

LEVITIKO 20:12-13
[12] “ ‘Ngati munthu agonana ndi mkazi wa mwana wake, awiriwo ayenera kuphedwa. Iwo achita chinthu chonyansa kwambiri. Magazi awo adzakhala pa mitu pawo.[13] “ ‘Ngati munthu agonana ndi mwamuna mnzake ngati akugonana ndi mkazi, ndiye kuti onsewo achita chinthu cha manyazi. Choncho aphedwe. Magazi awo adzakhala pa mitu pawo.

MIYAMBO 6:16-20
[16] Pali zinthu zisanu ndi chimodzi zimene Yehova amadana nazo, zinthu zisanu ndi ziwiri zimene zimamunyansa:[17] maso onyada, pakamwa pabodza, manja akupha munthu wosalakwa,[18] mtima wokonzekera kuchita zoyipa, mapazi othamangira msanga ku zoyipa,[19] mboni yonama yoyankhula mabodza komanso munthu amene amayambitsa mikangano pakati pa abale.[20] Mwana wanga, usunge malamulo a abambo ako; ndipo usataye zimene anakuphunzitsa amayi ako.

Chewa Bible 2016
Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.®