AKOLOSE 3:8 |
Koma tsopano tayani inunso zonsezi: mkwiyo, kupsa mtima, dumbo, mwano, zonyansa zotuluka m'kamwa mwanu: |
|
AKOLOSE 4:6 |
Mau anu akhale m'chisomo, okoleretsa, kuti mukadziwe inu mayankhidwe anu a kwa yense akatani. |
|
AEFESO 4:29 |
Nkhani yonse yovunda isatuluke m'kamwa mwanu, koma ngati pali ina yabwino kukumangirira monga mofunika ndiyo, kuti ipatse chisomo kwa iwo akumva. |
|
AEFESO 5:4 |
kapena chinyanso, ndi kulankhula zopanda pake, kapena zopusa zimene siziyenera; koma makamaka chiyamiko. |
|
EKSODO 20:7 |
Usatchule dzina la Yehova Mulungu wako pachabe; chifukwa Yehova sadzamuyesa iye wosachimwa, amene atchula pachabe dzina lakelo. |
|
YAKOBO 1:26 |
Ngati wina adziyesera ali wopembedza Mulungu, ndiye wosamanga lilime lake, koma adzinyenga mtima wake, kupembedza kwake kwa munthuyu nkopanda pake. |
|
YAKOBO 3:10 |
Mochokera m'kamwa momwemo mutuluka chiyamiko ndi temberero. Abale anga, izi siziyenera kutero. |
|
YAKOBO 3:5-12 |
[5] Kotero lilimenso lili chiwalo chaching'ono, ndipo lidzikuzira zazikulu. Taonani, kamoto kakang'ono kayatsa nkhuni zambiri![6] Ndipo lilime ndilo moto; ngati dziko la chosalungama mwa ziwalo zathu laikika lilime, ndili lodetsa thupi lonse, niliyatsa mayendedwe a chibadwidwe, ndipo liyatsidwa ndi Gehena.[7] Pakuti mtundu uliwonse wa nyama ndi wa mbalamenso, wa zokwawa, ndi wa zam'nyanja, zimazoloweretsedwa, ndipo zazoloweretsedwa ndi anthu;[8] koma lilime palibe munthu akhoza kulizoloweretsa; lili choipa chotakataka, lodzala ndi ululu wakupha.[9] Timayamika Ambuye ndi Atate nalo; nalonso timatemberera anthu, okhala monga mwa mafanizidwe a Mulungu;[10] Mochokera m'kamwa momwemo mutuluka chiyamiko ndi temberero. Abale anga, izi siziyenera kutero.[11] Kodi kasupe atulutsira pa uno womwewo madzi okoma ndi owawa?[12] Kodi mkuyu ukhoza kubala azitona, abale anga, kapena mpesa kubala nkhuyu? Kotero madzi amchere sakhoza kutulutsa okoma. |
|
LEVITIKO 20:9 |
Pakuti aliyense wakutemberera atate wake kapena mai wake azimupha ndithu; watemberera atate wake kapena amai wake; mwazi wake ukhale pamutu pake. |
|
LUKA 6:28 |
dalitsani iwo akutemberera inu, pemphererani iwo akuchitira inu chipongwe. |
|
MATEYU 5:22 |
koma Ine ndinena kwa inu, kuti yense wokwiyira mbale wake wopanda chifukwa adzakhala wopalamula mlandu; ndipo amene adzanena ndi mbale wake, Wopanda pake iwe, adzakhala wopalamula mlandu wa akulu: koma amene adzati, Chitsiru iwe: adzakhala wopalamula Gehena wamoto. |
|
1 PETRO 3:10 |
Pakuti, Iye wofuna kukonda moyo, ndi kuona masiku abwino, aletse lilime lake lisanene choipa, ndi milomo yake isalankhule chinyengo; |
|
MATEYU 15:11 |
si chimene chilowa m'kamwa mwake chiipitsa munthu; koma chimene chituluka m'kamwa mwake, ndicho chiipitsa munthu. |
|
MIYAMBO 18:21 |
Lilime lili ndi mphamvu pa imfa ndi moyo; wolikonda adzadya zipatso zake. |
|
MASALIMO 109:17 |
Inde, anakonda kutemberera, ndipo kudamdzera mwini; sanakondwere nako kudalitsa, ndipo kudamkhalira kutali. |
|
AROMA 12:14 |
Dalitsani iwo akuzunza inu; dalitsani, musawatemberere. |
|
2 MAFUMU 2:23-24 |
[23] Ndipo anachokako kukwera ku Betele, ndipo iye ali chikwerere m'njiramo, munatuluka anyamata ang'ono m'mudzimo, namseka, nati kwa iye, Takwera wadazi, takwera wadazi![24] Ndipo anacheuka, nawaona, nawatemberera m'dzina la Yehova. Ndipo kuthengo kunatuluka zimbalangondo ziwiri zazikazi, ndi kupwetedza mwa iwo ana makumi anai mphambu awiri. |
|
MATEYU 15:10-11 |
[10] Ndipo Iye anaitana makamuwo nati kwa iwo, Imvani, nimudziwitse;[11] si chimene chilowa m'kamwa mwake chiipitsa munthu; koma chimene chituluka m'kamwa mwake, ndicho chiipitsa munthu. |
|
YAKOBO 3:8-10 |
[8] koma lilime palibe munthu akhoza kulizoloweretsa; lili choipa chotakataka, lodzala ndi ululu wakupha.[9] Timayamika Ambuye ndi Atate nalo; nalonso timatemberera anthu, okhala monga mwa mafanizidwe a Mulungu;[10] Mochokera m'kamwa momwemo mutuluka chiyamiko ndi temberero. Abale anga, izi siziyenera kutero. |
|
MATEYU 15:18-20 |
[18] Koma zakutuluka m'kamwa zichokera mumtima; ndizo ziipitsa munthu.[19] Pakuti mumtima muchokera maganizo oipa, zakupha, zachigololo, zachiwerewere, zakuba, za umboni wonama, zamwano;[20] izi ndizo ziipitsa munthu, koma kudya osasamba manja sikuipitsa munthu ai. |
|
Chewa Bible 2014 |
Bible Society of Malawi |