A A A A A

Machimo: [Kuledzera]


1 AKORINTO 10:13-14
[13] Sichinakugwerani inu chiyeso koma cha umunthu; koma Mulungu ali wokhulupirika, amene sadzalola inu kuyesedwa koposa kumene mukhoza; koma pamodzi ndi chiyeso adzaikanso populumukirapo, kuti mudzakhoze kupirirako.[14] Chifukwa chake, okondedwa anga, thawani kupembedza mafano.

1 YOHANE 2:16
Pakuti chilichonse cha m'dziko lapansi, chilakolako cha thupi ndi chilakolako cha maso, matamandidwe a moyo, sizichokera kwa Atate, koma kudziko lapansi.

1 AKORINTO 15:33
Musanyengedwe; mayanjano oipa aipsa makhalidwe okoma.

YAKOBO 4:7
Potero mverani Mulungu; koma kanizani mdierekezi, ndipo adzakuthawani inu.

1 AKORINTO 6:12
Zinthu zonse ziloledwa kwa ine; koma si zonse zipindula. Zinthu zonse ziloledwa kwa ine, koma sindidzalamulidwa nacho chimodzi.

1 PETRO 5:10
Ndipo Mulungu wa chisomo chonse, amene adakuitanani kulowa ulemerero wake wosatha mwa Khristu, mutamva zowawa kanthawi, adzafikitsa inu opanda chilema mwini wake, adzakhazikitsa, adzalimbikitsa inu.

MASALIMO 50:15
Ndipo undiitane tsiku la chisautso, ndidzakulanditsa, ndipo iwe udzandilemekeza.

AROMA 5:3-5
[3] Ndipo si chotero chokha, komanso tikondwera m'zisautso; podziwa ife kuti chisautso chichita chipiriro; ndi chipiriro chichita chizolowezi;[4] ndi chizolowezi chichita chiyembekezo:[5] ndipo chiyembekezo sichichititsa manyazi; chifukwa chikondi cha Mulungu chinatsanulidwa m'mitima mwathu mwa Mzimu Woyera, amene wapatsidwa kwa ife.

1 AKORINTO 6:9-11
[9] Kapena simudziwa kuti osalungama sadzalandira ufumu wa Mulungu? Musasocheretsedwe; adama, kapena opembedza mafano, kapena achigololo, kapena olobodoka ndi zoipa, kapena akudziipsa ndi amuna,[10] kapena ambala, kapena osirira, kapena oledzera, kapena olalatira, kapena olanda, sadzalowa Ufumu wa Mulungu.[11] Ndipo ena a inu munali otere; koma munasambitsidwa, koma munayeretsedwa, koma munayesedwa olungama, m'dzina la Ambuye Yesu Khristu, ndi mwa Mzimu wa Mulungu wathu.

TITO 2:12
ndi kutiphunzitsa ife kuti, pokana chisapembedzo ndi zilakolako za dziko lapansi, tikhale ndi moyo m'dziko lino odziletsa, ndi olungama, ndi opembedza;

YAKOBO 1:2-3
[2] Muchiyese chimwemwe chokha, abale anga, m'mene mukugwa m'mayesero a mitundumitundu;[3] pozindikira kuti chiyesedwe cha chikhulupiriro chanu chichita chipiriro.

AHEBRI 4:15-16
[15] Pakuti sitili naye mkulu wa ansembe wosatha kumva chifundo ndi zofooka zathu; koma wayesedwa m'zonse monga momwe ife, koma wopanda uchimo.[16] Potero tilimbike mtima poyandikira mpando wachifumu wachisomo, kuti tilandire chifundo ndi kupeza chisomo cha kutithandiza nthawi yakusowa.

YOHANE 3:16-17
[16] Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakhulupirira Iye asatayike, koma akhale nao moyo wosatha.[17] Pakuti Mulungu sanatume Mwana wake kudziko lapansi, kuti akaweruze dziko lapansi, koma kuti dziko lapansi likapulumutsidwe ndi Iye.

AFILIPI 4:13
Ndikhoza zonse mwa Iye wondipatsa mphamvuyo.

MASALIMO 95:8
Musaumitse mitima yanu, ngati ku Meriba, ngati tsiku la ku Masa m'chipululu.

MATEYU 6:13
Ndipo musatitengere kokatiyesa, koma mutipulumutse kwa woipayo.

MATEYU 26:41
Chezerani ndi kupemphera, kuti mungalowe m'kuyesedwa: mzimutu uli wakufuna, koma thupi lili lolefuka.

Chewa Bible 2014
Bible Society of Malawi