A A A A A

Zinsinsi: [Ma Dinosaurs]


YESAYA 27:1
Tsiku limenelo Yehova ndi lupanga lake lolimba ndi lalikulu ndi lamphamvu adzalanga Leviyatani njoka yothamanga, ndi Leviyatani njoka yopindikapindika; nadzapha ching'ona chimene chili m'nyanja.

GENESIS 1:21
Mulungu ndipo adalenga zinsomba zazikulu ndi zoyendayenda zamoyo zakuchuluka m'madzi mwa mitundu yao, ndi mbalame zamapiko, yonse monga mwa mtundu wake: ndipo anaona Mulungu kuti kunali kwabwino.

MASALIMO 104:26
M'mwemo muyenda zombo; ndi Leviyatani amene munamlenga aseweremo.

AROMA 1:18
Pakuti mkwiyo wa Mulungu, wochokera Kumwamba, uonekera pa chisapembedzo chonse ndi chosalungama cha anthu, amene akanikiza pansi choonadi m'chosalungama chao;

GENESIS 1:24-31
[24] Ndipo adati Mulungu, Dziko lapansi libale zamoyo monga mwa mitundu yao, ng'ombe, ndi zokwawa, ndi zinyama za dziko lapansi monga mwa mitundu yao: ndipo kunatero.[25] Ndipo Mulungu anapanga zinyama za dziko lapansi monga mwa mitundu yao; ndi ng'ombe monga mwa mtundu wake, ndi zonse zokwawa pansi monga mwa mitundu yao; ndipo Mulungu anaona kuti kunali kwabwino.[26] Ndipo anati Mulungu, Tipange munthu m'chifanizo chathu, monga mwa chikhalidwe chathu: alamulire pa nsomba za m'nyanja, ndi pa mbalame za m'mlengalenga, ndi pa ng'ombe, ndi pa dziko lonse lapansi, ndi pa zokwawa zonse zakukwawa pa dziko lapansi.[27] Mulungu ndipo adalenga munthu m'chifanizo chake, m'chifanizo cha Mulungu adamlenga iye; adalenga iwo mwamuna ndi mkazi.[28] Mulungu ndipo anadalitsa iwo, ndipo adati kwa iwo, Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse: mulamulire pa nsomba za m'nyanja, ndi pa mbalame za m'mlengalenga, ndi zamoyo zonse zakukwawa pa dziko lapansi.[29] Ndipo anati Mulungu, Taonani, ndakupatsani inu therere lonse lakubala mbeu lili pa dziko lapansi, ndi mitengo yonse m'mene muli chipatso cha mtengo wakubala mbeu; chidzakhala chakudya cha inu:[30] ndiponso ndapatsa zinyama zonse za dziko lapansi, ndi mbalame zonse za m'mlengalenga, ndi zakukwawa zonse za dziko lapansi m'mene muli moyo, therere laliwisi lonse likhale chakudya: ndipo kunatero.[31] Ndipo anaziona Mulungu zonse zimene adazipanga, ndipo, taonani, zinali zabwino ndithu. Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku lachisanu ndi chimodzi.

YOBU 40:15-24
[15] Tapenya tsono mvuu ndinaipanga pamodzi ndi iwe, ikudya udzu ngati ng'ombe.[16] Tapenya tsono, mphamvu yake ili m'chuuno mwake, ndi kulimbalimba kwake kuli m'mitsempha ya m'mimba yake.[17] Igwedeza mchira wake ngati mkungudza; mitsempha ya ntchafu zake ipotana.[18] Mafupa ake akunga misiwe yamkuwa; ziwalo zake zikunga zitsulo zamphumphu.[19] Iyo ndiyo chiyambi cha machitidwe a Mulungu; wakuilenga anaininkha lupanga lake.[20] Pakuti mapiri aiphukitsira chakudya, kumene zisewera nyama zonse za kuthengo.[21] Igona pansi patsinde pa mitengo yamthunzi, pobisala pabango ndi pathawale.[22] Mitengo yamthunzi iiphimba ndi mthunzi wao, misondodzi ya kumtsinje iizinga.[23] Taona madzi a mumtsinje akakula, siinjenjemera; ilimbika mtima, ngakhale Yordani atupa mpaka pakamwa pake.[24] Ikakhala maso, munthu adzaigwira kodi? Kapena kuboola m'mphuno mwake ili m'khwekhwe?

YOBU 41:1-10
[1] Kodi ukhoza kukoka Leviyatani ndi mbedza? Kapena kukanikiza kalandira wake ndi chingwe?[2] Kodi ukhoza kumanga m'mphuno ndi mlulu? Kapena kuboola nsagwada wake ndi mbedza?[3] Kodi idzachulukitsa mau akukupembedza? Kapena idzanena nawe mau ofatsa?[4] Kodi idzapangana ndi iwe, kuti uitenge ikhale kapolo wako wachikhalire?[5] Kodi udzasewera nayo ngati mbalame? Kapena udzaimangira anamwali ako kuti aiwete?[6] Kodi opangana malonda adzaitsatsa? Adzaigawana eni malonda?[7] Kodi udzadzaza khungu lake ndi ntchetho, kapena mutu wake ndi miomba?[8] Isanjike dzanja lako; ukakumbukira nkhondoyi, sudzateronso.[9] Taona, chiyembekezo chako cha pa iyo chipita pachabe. Kodi sadzatenga nkhawa munthu pakungoiona?[10] Palibe wolimba mtima kuti adzaiputa. Ndipo ndaniyo adzaima pamaso pa Ine?

YOSWA 10:1-10
[1] Ndipo kunali, pamene Adoni-Zedeki mfumu ya Yerusalemu anamva kuti Yoswa adalanda Ai, ndi kumuononga konse; nachitira Ai ndi mfumu yake monga adachitira Yeriko ndi mfumu yake; ndi kuti nzika za Gibiyoni zinachitirana mtendere ndi Israele, nizikhala pakati pao;[2] anaopa kwambiri, popeza Gibiyoni ndi mudzi waukulu, monga wina wa midzi yachifumu, popezanso unaposa Ai kukula kwake, ndi amuna ake onse ndiwo amphamvu.[3] Chifukwa chake Adoni-Zedeki mfumu ya Yerusalemu anatuma kwa Hohamu, mfumu ya Hebroni, ndi kwa Piramu mfumu ya Yaramuti, ndi kwa Yafiya mfumu ya Lakisi, ndi kwa Debiri mfumu ya Egiloni, ndi kuti,[4] Kwerani kwanga kuno, ndi kundithandiza kuti tikanthe Gibiyoni, pakuti unachitirana mtendere ndi Yoswa ndi ana a Israele.[5] Pamenepo mafumu asanu a Aamori, ndiwo mfumu ya ku Yerusalemu, mfumu ya ku Hebroni, mfumu ya ku Yaramuti, mfumu ya ku Lakisi, mfumu ya ku Egiloni anasonkhana, nakwera iwo ndi makamu ao onse namanga misasa pa Gibiyoni, nauthira nkhondo.[6] Ndipo amuna a ku Gibiyoni anatumira Yoswa mau kuchigono ku Giligala, ndi kuti, Musalekerere akapolo anu; mutikwerere msanga, ndi kutipulumutsa, ndi kutithandiza; pakuti mafumu onse a Aamori, akukhala kumapiri atisonkhanira.[7] Pamenepo Yoswa anakwera kuchokera ku Giligala, iye ndi anthu onse a nkhondo pamodzi naye, ndi ngwazi zonse.[8] Ndipo Yehova ananena ndi Yoswa, Usawaope, pakuti ndawapereka m'dzanja lako; palibe mmodzi wa iwo adzaima pamaso pako.[9] Ndipo Yoswa anawadzidzimukitsa; popeza anakwera kuchokera ku Giligala usiku wonse.[10] Ndipo Yehova anawamwaza pamaso pa Israele, ndipo anawakantha makanthidwe akulu ku Gibiyoni, nawapirikitsa pa njira yokwera pa Betehoroni, nawakantha mpaka Azeka, ndi mpaka Makeda.

Chewa Bible 2014
Bible Society of Malawi