A A A A A

Zizindikiro za Masamu: [Nambala 8]


CHIVUMBULUTSO 13:18
Pano pali nzeru. Iye wakukhala nacho chidziwitso awerenge chiwerengero cha chilombocho; pakuti chiwerengero chake ndi cha munthu; ndipo chiwerengero chake ndicho mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu ndi limodzi kudza zisanu ndi chimodzi.

DEUTERONOMO 6:4
Imvani, Israele; Yehova Mulungu wathu, Yehova ndiye mmodzi;

LEVITIKO 20:13
Munthu akagonana ndi mwamuna mnzake, monga amagonana ndi mkazi, achita chonyansa onse awiri; awaphe ndithu; mwazi wao ukhale pamtu pao.

1 AKORINTO 6:9-11
[9] Kapena simudziwa kuti osalungama sadzalandira ufumu wa Mulungu? Musasocheretsedwe; adama, kapena opembedza mafano, kapena achigololo, kapena olobodoka ndi zoipa, kapena akudziipsa ndi amuna,[10] kapena ambala, kapena osirira, kapena oledzera, kapena olalatira, kapena olanda, sadzalowa Ufumu wa Mulungu.[11] Ndipo ena a inu munali otere; koma munasambitsidwa, koma munayeretsedwa, koma munayesedwa olungama, m'dzina la Ambuye Yesu Khristu, ndi mwa Mzimu wa Mulungu wathu.

CHIVUMBULUTSO 11:2-3
[2] Ndipo bwalo la kunja kwa Kachisi ulisiye padera, osaliyesa; pakuti adapatsa ilo kwa amitundu; ndipo mzinda wopatulika adzaupondereza miyezi makumi anai mphambu iwiri.[3] Ndipo ndidzalamulira mboni zanga ziwiri, ndipo zidzanenera masiku chikwi chimodzi ndi mazana awiri amphambu makumi asanu ndi limodzi, zovala chiguduli.

LEVITIKO 20:27
Munthu wamwamuna kapena wamkazi wakubwebweta, kapena wanyanga, azimupha ndithu; aziwaponya miyala; mwazi wao ukhale pamtu pao.

DEUTERONOMO 18:10-12
[10] Asapezeke mwa inu munthu wakupitiriza mwana wake wamwamuna kapena mwana wake wamkazi ku moto wa ula, wosamalira mitambo, kapena wosamalira kulira kwa mbalame, kapena wanyanga.[11] Kapena wotsirika, kapena wobwebweta, kapena wopenduza, kapena wofunsira akufa.[12] Popeza aliyense wakuchita izi Yehova anyansidwa naye; ndipo chifukwa cha zonyansa izi Yehova Mulungu wanu awapirikitsa pamaso panu.

2 MAFUMU 21:6
Napititsa mwana wake pamoto, naombeza maula, nachita zanyanga, naika obwebweta ndi openda; anachita zoipa zambiri pamaso pa Yehova kuutsa mkwiyo wake.

MIKA 5:12
ndipo ndidzaononga zanyanga za m'dzanja lako; ndipo sudzakhalanso nao alosi;

YESAYA 47:12
Taima tsopano ndi maphendo ako, ndi unyinji wa matsenga ako, m'menemo iwe unagwira ntchito chiyambire ubwana wako; kuti kapena udzatha kupindula, kuti kapena udzapambana.

MACHITIDWE A ATUMWI 8:11-24
[11] Ndipo anamsamalira iye, popeza nthawi yaikulu adawadabwitsa iwo ndi matsenga ake.[12] Koma pamene anakhulupirira Filipo wakulalikira Uthenga Wabwino wa Ufumu wa Mulungu ndi dzina la Yesu Khristu, anabatizidwa, amuna ndi akazi.[13] Ndipo Simoni mwini wake anakhulupiriranso: ndipo m'mene anabatizidwa, anakhalira ndi Filipo; ndipo pakuona zizindikiro ndi mphamvu zazikulu zilikuchitika, anadabwa.[14] Koma pamene atumwi a ku Yerusalemu anamva kuti Samariya adalandira mau a Mulungu, anawatumizira Petro ndi Yohane;[15] amenewo, m'mene adatsikirako, anawapempherera, kuti alandire Mzimu Woyera:[16] pakuti kufikira pamenepo nkuti asanagwe pa wina mmodzi wa iwo; koma anangobatizidwa m'dzina la Ambuye Yesu.[17] Pamenepo anaika manja pa iwo, ndipo analandira Mzimu Woyera.[18] Koma pakuona Simoni kuti mwa kuika manja a atumwi anapatsidwa Mzimu Woyera, anawatengera ndalama,[19] nanena, Ndipatseni inenso ulamuliro umene, kuti amene aliyense ndikaika manja pa iye, alandire Mzimu Woyera.[20] Koma Petro anati kwa iye, Ndalama yako itayike nawe, chifukwa unalingirira kulandira mphatso ya Mulungu ndi ndalama.[21] Ulibe gawo kapena cholandira ndi mau awa; pakuti mtima wako suli wolunjika pamaso pa Mulungu.[22] Chifukwa chake lapa choipa chako ichi, pemphera Ambuye, kuti kapena akukhululukire iwe cholingirira cha mtima wako.[23] Pakuti ndiona kuti wagwidwa ndi ndulu yowawa ndi nsinga ya chosalungama.[24] Ndipo Simoni anayankha nati, Mundipempherere ine kwa Ambuye kuti zisandigwere izi mwanenazi.

GENESIS 1:24-31
[24] Ndipo adati Mulungu, Dziko lapansi libale zamoyo monga mwa mitundu yao, ng'ombe, ndi zokwawa, ndi zinyama za dziko lapansi monga mwa mitundu yao: ndipo kunatero.[25] Ndipo Mulungu anapanga zinyama za dziko lapansi monga mwa mitundu yao; ndi ng'ombe monga mwa mtundu wake, ndi zonse zokwawa pansi monga mwa mitundu yao; ndipo Mulungu anaona kuti kunali kwabwino.[26] Ndipo anati Mulungu, Tipange munthu m'chifanizo chathu, monga mwa chikhalidwe chathu: alamulire pa nsomba za m'nyanja, ndi pa mbalame za m'mlengalenga, ndi pa ng'ombe, ndi pa dziko lonse lapansi, ndi pa zokwawa zonse zakukwawa pa dziko lapansi.[27] Mulungu ndipo adalenga munthu m'chifanizo chake, m'chifanizo cha Mulungu adamlenga iye; adalenga iwo mwamuna ndi mkazi.[28] Mulungu ndipo anadalitsa iwo, ndipo adati kwa iwo, Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse: mulamulire pa nsomba za m'nyanja, ndi pa mbalame za m'mlengalenga, ndi zamoyo zonse zakukwawa pa dziko lapansi.[29] Ndipo anati Mulungu, Taonani, ndakupatsani inu therere lonse lakubala mbeu lili pa dziko lapansi, ndi mitengo yonse m'mene muli chipatso cha mtengo wakubala mbeu; chidzakhala chakudya cha inu:[30] ndiponso ndapatsa zinyama zonse za dziko lapansi, ndi mbalame zonse za m'mlengalenga, ndi zakukwawa zonse za dziko lapansi m'mene muli moyo, therere laliwisi lonse likhale chakudya: ndipo kunatero.[31] Ndipo anaziona Mulungu zonse zimene adazipanga, ndipo, taonani, zinali zabwino ndithu. Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku lachisanu ndi chimodzi.

1 AKORINTO 6:9
Kapena simudziwa kuti osalungama sadzalandira ufumu wa Mulungu? Musasocheretsedwe; adama, kapena opembedza mafano, kapena achigololo, kapena olobodoka ndi zoipa, kapena akudziipsa ndi amuna,

YOHANE 1:8
Iye sindiye kuunikaku, koma anatumidwa kukachita umboni wa kuunikaku.

CHIVUMBULUTSO 4:6-8
[6] ndipo kumpandowo, ngati nyanja yagalasi yonga krustalo; ndipo pakati pa mpandowo, ndi pozinga mpandowo, zamoyo zinai zodzala ndi maso kutsogolo ndi kumbuyo.[7] Ndipo chamoyo choyamba chinafanana nao mkango, ndi chamoyo chachiwiri chinafanana ndi mwanawang'ombe, ndi chamoyo chachitatu chinali nayo nkhope yake ngati ya munthu, ndi chamoyo chachinai chidafanana ndi chiombankhanga chakuuluka.[8] Ndipo zamoyozo zinai, chonse pa chokha chinali nao mapiko asanu ndi limodzi; ndipo zinadzala ndi maso pozinga ponse ndi m'katimo; ndipo sizipumula usana ndi usiku, ndi kunena, Woyera, woyera, woyera, Ambuye Mulungu Wamphamvuyonse, amene anali, amene ali, ndi amene alinkudza.

GENESIS 3:15
ndipo ndidzaika udani pakati pa iwe ndi mkaziyo, ndi pakati pa mbeu yako ndi mbeu yake; ndipo idzalalira mutu wako, ndipo iwe udzalalira chitende chake.

CHIVUMBULUTSO 13:5
Ndipo anachipatsa icho m'kamwa molankhula zazikulu ndi zamwano; ndipo anachipatsa ulamuliro wa kutero miyezi makumi anai ndi iwiri.

EKSODO 7:11
Pamenepo Farao anaitananso anzeru, ndi amatsenga; ndipo alembi a Aejipito, iwonso anachita momwemo ndi matsenga ao.

Chewa Bible 2014
Bible Society of Malawi