A A A A A

Zizindikiro za Masamu: [Nambala 5]


CHIVUMBULUTSO 13:5-18
[5] Ndipo anachipatsa icho m'kamwa molankhula zazikulu ndi zamwano; ndipo anachipatsa ulamuliro wa kutero miyezi makumi anai ndi iwiri.[6] Ndipo chinatsegula pakamwa pake kukanena zamwano pa Mulungu, kuchitira mwano dzina lake, ndi chihema chake, ndi iwo akukhala m'Mwamba.[7] Ndipo anachipatsa icho kuchita nkhondo ndi oyera mtima, ndi kuwalaka; ndipo anachipatsa ulamuliro wa pa fuko lililonse, ndi anthu, ndi manenedwe, ndi mitundu.[8] Ndipo adzachilambira onse akukhala padziko, amene dzina lao silinalembedwa m'buku la moyo la Mwanawankhosa, wophedwa kuyambira makhazikidwe a dziko lapansi.[9] Ngati wina ali nalo khutu, amve.[10] Ngati munthu alinga kundende, kundende adzamuka; munthu akapha ndi lupanga, ayenera iye kuphedwa nalo lupanga. Pano pali chipiriro ndi chikhulupiriro cha oyera mtima.[11] Ndipo ndinaona chilombo china chilikutuluka pansi; ndipo chinali nazo nyanga ziwiri ngati za mwanawankhosa, ndipo chinalankhula ngati chinjoka.[12] Ndipo chichita ulamuliro wonse wa chilombo choyamba pamaso pake. Ndipo chilambiritsa dziko ndi iwo akukhala momwemo chilombo choyamba, chimene bala lake la kuimfa lidapola.[13] Ndipo chichita zizindikiro zazikulu, kutinso chitsitse moto uchokere m'mwamba nugwe padziko, pamaso pa anthu.[14] Ndipo chisokeretsa iwo akukhala padziko ndi zizindikiro zimene anachipatsa mphamvu yakuzichita pamaso pa chilombo, ndi kunena kwa iwo akukhala padziko, kuti apange fano la chilombocho, chimene chinali nalo bala la lupanga nichinakhalanso ndi moyo.[15] Ndipo anachipatsa mphamvu yakupatsa fano la chilombo mpweya, kutinso fano la chilombo lilankhule, nilichite kuti onse osalilambira fano la chilombo aphedwe.[16] Ndipo chichita kuti onse, ang'ono ndi akulu, achuma ndi osauka, ndi mfulu ndi akapolo, alandire chilembo pa dzanja lao ndi pamphumi pao;[17] ndi kuti munthu sangakhoze kugula kapena kugulitsa, koma iye yekha wakukhala nacho chilembo, ndilo dzina la chilombo, kapena chiwerengero cha dzina lake.[18] Pano pali nzeru. Iye wakukhala nacho chidziwitso awerenge chiwerengero cha chilombocho; pakuti chiwerengero chake ndi cha munthu; ndipo chiwerengero chake ndicho mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu ndi limodzi kudza zisanu ndi chimodzi.

MATEYU 19:9
Ndipo Ine ndinena kwa inu, Amene aliyense akachotsa mkazi wake, kosakhala chifukwa cha chigololo, nadzakwatira wina, achita chigololo: ndipo iye amene akwatira wochotsedwayo, achita chigololo.

CHIVUMBULUTSO 11:2-3
[2] Ndipo bwalo la kunja kwa Kachisi ulisiye padera, osaliyesa; pakuti adapatsa ilo kwa amitundu; ndipo mzinda wopatulika adzaupondereza miyezi makumi anai mphambu iwiri.[3] Ndipo ndidzalamulira mboni zanga ziwiri, ndipo zidzanenera masiku chikwi chimodzi ndi mazana awiri amphambu makumi asanu ndi limodzi, zovala chiguduli.

MATEYU 5:32
koma Ine ndinena kwa inu, kuti yense wakuchotsa mkazi wake, kosati chifukwa cha chigololo, amchititsa chigololo: ndipo amene adzakwata wochotsedwayo achita chigololo.

2 TIMOTEO 3:16
Lemba lililonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa pa chiphunzitso, chitsutsano, chikonzero, chilangizo cha m'chilungamo:

CHIVUMBULUTSO 4:6-8
[6] ndipo kumpandowo, ngati nyanja yagalasi yonga krustalo; ndipo pakati pa mpandowo, ndi pozinga mpandowo, zamoyo zinai zodzala ndi maso kutsogolo ndi kumbuyo.[7] Ndipo chamoyo choyamba chinafanana nao mkango, ndi chamoyo chachiwiri chinafanana ndi mwanawang'ombe, ndi chamoyo chachitatu chinali nayo nkhope yake ngati ya munthu, ndi chamoyo chachinai chidafanana ndi chiombankhanga chakuuluka.[8] Ndipo zamoyozo zinai, chonse pa chokha chinali nao mapiko asanu ndi limodzi; ndipo zinadzala ndi maso pozinga ponse ndi m'katimo; ndipo sizipumula usana ndi usiku, ndi kunena, Woyera, woyera, woyera, Ambuye Mulungu Wamphamvuyonse, amene anali, amene ali, ndi amene alinkudza.

NUMERI 5:11-31
[11] Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,[12] Nena ndi ana a Israele, nuti nao, Mkazi wa mwini akapatukira mwamuna wake, nakamchitira mosakhulupirika,[13] ndi munthu akagona naye, koma kumbisikira maso a mwamuna wake, ndi kumng'unira; nadetsedwa mkaziyo, koma palibe mboni yomtsutsa, kapena sanamgwire alimkuchita;[14] ndipo ukamgwira mwamuna mtima wansanje, kuti achitire nsanje mkazi wake, popeza wadetsedwa; kapena ukamgwira mtima wansanje, kuti amchitire mkazi wake nsanje angakhale sanadetsedwe;[15] pamenepo mwamunayo azidza naye mkazi wake kwa wansembe, nadze nacho chopereka chake, limodzi la magawo khumi la efa wa ufa wabarele; asathirepo mafuta, kapena kuikapo lubani; popeza ndiyo nsembe yaufa yansanje, nsembe yaufa yachikumbutso, yakukumbutsa mphulupulu.[16] Ndipo wansembe abwere naye, namuike pamaso pa Yehova;[17] natenge madzi opatulika m'mbale yadothi wansembeyo, natengeko fumbi lili pansi m'Kachisi, wansembeyo nalithire m'madzimo.[18] Pamenepo wansembeyo aike mkaziyo pamaso pa Yehova, navula mutu wa mkaziyo, naike nsembe yaufa yachikumbutso m'manja mwake, ndiyo nsembe yaufa yansanje; ndipo m'manja mwake mwa wansembe muzikhala madzi owawa akudzetsa temberero.[19] Ndipo wansembe amlumbiritse, nanene kwa mkazi, Ngati sanagone nawe munthu mmodzi yense, ngati sunapatukira kuchidetso, pokhala ndiwe wa mwamuna wako, upulumuke ku madzi owawa awa akudzetsa temberero.[20] Koma iwe, ngati wapatukira mwamuna wako, ngati wadetsedwa, kuti wagona nawe munthu, wosati mwamuna wako;[21] pamenepo wansembe alumbiritse mkazi lumbiro lakutemberera, ndi wansembe anene kwa mkazi, Yehova akuike ukhale temberero ndi lumbiro pakati pa anthu a mtundu wako, pakuondetsa Yehova m'chuuno mwako, ndi kukutupitsa thupi lako;[22] ndipo madzi awa akudzetsa temberero adzalowa m'matumbo mwako, nadzakutupitsa thupi lako ndi kuondetsa m'chuuno mwako; ndipo mkaziyo aziti, Amen, Amen.[23] Ndipo wansembe alembere matemberero awa m'buku, ndi kuwafafaniza ndi madzi owawawa.[24] Ndipo amwetse mkaziyo madzi owawa akudzetsa temberero; ndi madzi odzetsa temberero adzalowa mwa iye nadzamwawira.[25] Ndipo wansembe atenge nsembe yaufa yansanje m'manja mwa mkazi, naweyule nsembe yaufa pamaso pa Yehova, nabwere nayo ku guwa la nsembe.[26] Wansembe atengekonso nsembe yaufa wodzala manja, chikumbutso chake, nachitenthe pa guwa la nsembe; ndipo atatero amwetse mkazi madziwo.[27] Ndipo atammwetsa madziwo, kudzatero, ngati wadetsedwa, nachita mosakhulupirika pa mwamuna wake, madzi odzetsa tembererowo adzalowa mwa iye nadzamwawira, nadzamtupitsa thupi lake, ndi m'chuuno mwake mudzaonda; ndi mkaziyo adzakhala temberero pakati pa anthu a mtundu wake.[28] Koma ngati mkazi sanadetsedwe, nakhala woyera, pamenepo adzapulumuka, nadzaima.[29] Ichi ndi chilamulo cha nsanje, pamene mkazi, pokhala naye mwamuna wake, ampatukira nadetsedwa;[30] kapena pamene mtima wansanje umgwira mwamuna, ndipo achitira mkazi wake nsanje; pamenepo aziika mkazi pamaso pa Yehova, ndipo wansembe amchitire chilamulo ichi chonse.[31] Mwamunayo ndiye wosachita mphulupulu, koma mkazi uyo asenze mphulupulu yake.

1 MAFUMU 7:23
Ndipo anayenganso thawale lamkuwa, kukamwa kwake kunali kwa mikono khumi, linali lozunguniza, ndi msinkhu wake unali mikono isanu; ndi chingwe cha mikono makumi atatu chinalizungulira.

DEUTERONOMO 6:4
Imvani, Israele; Yehova Mulungu wathu, Yehova ndiye mmodzi;

MALAKI 3:10
Mubwere nalo limodzilimodzi lonse la khumi, kunyumba yosungiramo, kuti m'nyumba mwanga mukhale chakudya; ndipo mundiyese nako tsono, ati Yehova wa makamu, ngati sindikutsegulirani mazenera a kumwamba, ndi kukutsanulirani mdalitso wakuti adzasoweka malo akuulandira.

MASALIMO 104:9
Munaika malire kuti asapitirireko; kuti asabwererenso kuphimba dziko lapansi.

GENESIS 6:12
Ndipo Mulungu anaona dziko lapansi, ndipo taonani, linavunda; pakuti anthu onse anavunditsa njira yao pa dziko lapansi.

GENESIS 7:20
Madzi anapambana ndithu nakwera mikono khumi ndi isanu: namizidwa mapiri.

GENESIS 8:5-9
[5] Ndipo madzi analinkuchepa kufikira mwezi wakhumi; mwezi wakhumi tsiku loyamba mwezi ndipo padaoneka mitu ya mapiri.[6] Ndipo panali atapita masiku makumi anai, Nowa anatsegula pa zenera la chingalawa limene analipanga:[7] ndipo anatulutsa khungubwi, ndipo anatuluka kunka kwina ndi kwina kufikira adaphwa madzi pa dziko lapansi.[8] Ndipo anatulutsa njiwa imchokere, kuti aone kapena madzi anaphwa pamwamba pa dziko lapansi;[9] koma njiwayo siinapeza popondapo phazi lake, nibwera kwa iye kuchingalawako, pakuti madzi analipo pa dziko lonse lapansi; ndipo anatulutsa dzanja lake, naitenga, nailowetsa kwa iye m'chingalawamo.

GENESIS 9:11
Ndipo ndidzakhazikitsa pangano langa pamodzi ndi inu; zamoyo zonse sizidzamalizidwanso konse ndi madzi a chigumula; ndipo sikudzakhalanso konse chigumula cha kuononga dziko lapansi.

GENESIS 1:31
Ndipo anaziona Mulungu zonse zimene adazipanga, ndipo, taonani, zinali zabwino ndithu. Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku lachisanu ndi chimodzi.

GENESIS 3:15
ndipo ndidzaika udani pakati pa iwe ndi mkaziyo, ndi pakati pa mbeu yako ndi mbeu yake; ndipo idzalalira mutu wako, ndipo iwe udzalalira chitende chake.

1 AKORINTO 10:13
Sichinakugwerani inu chiyeso koma cha umunthu; koma Mulungu ali wokhulupirika, amene sadzalola inu kuyesedwa koposa kumene mukhoza; koma pamodzi ndi chiyeso adzaikanso populumukirapo, kuti mudzakhoze kupirirako.

EKSODO 20:13
Usaphe.

Chewa Bible 2014
Bible Society of Malawi