A A A A A

Moyo: [Kukongola]


1 PETRO 3:3-4
[3] Amene kukometsera kwanu kusakhale kwa kunja, kuluka tsitsi ndi kuvala za golide, kapena kuvala chovala;[4] koma kukhale munthu wobisika wamtima, m'chovala chosaola cha mzimu wofatsa ndi wachete, ndiwo wa mtengo wake wapatali pamaso pa Mulungu.

2 AKORINTO 4:16
Chifukwa chake sitifooka; koma ungakhale umunthu wathu wakunja uvunda, wa m'kati mwathu ukonzedwa kwatsopano tsiku ndi tsiku.

AEFESO 2:10
Pakuti ife ndife chipango chake, olengedwa mwa Khristu Yesu, kuchita ntchito zabwino, zimene Mulungu anazipangiratu, kuti tikayende m'menemo.

GENESIS 1:27
Mulungu ndipo adalenga munthu m'chifanizo chake, m'chifanizo cha Mulungu adamlenga iye; adalenga iwo mwamuna ndi mkazi.

YESAYA 40:8
Udzu unyala, duwa lifota, koma mau a Mulungu wathu adzakhala nthawi zachikhalire.

AFILIPI 4:8
Chotsalira, abale, zinthu zilizonse zoona, zilizonse zolemekezeka, zilizonse zolungama, zilizonse zoyera, zilizonse zokongola, zilizonse zimveka zokoma; ngati kuli chokoma mtima china, kapena chitamando china, zilingirireni izi.

MASALIMO 139:14
Ndikuyamikani chifukwa kuti chipangidwe changa nchoopsa ndi chodabwitsa; ntchito zanu nzodabwitsa; moyo wanga uchidziwa ichi bwino ndithu.

AROMA 8:6
pakuti chisamaliro cha thupi chili imfa; koma chisamaliro cha mzimu chili moyo ndi mtendere.

NYIMBO YA SOLOMONI 4:7
Wakongola monsemonse, wokondedwa wanga, namwaliwe, mulibe chilema mwa iwe.

MATEYU 6:28-29
[28] Ndipo muderanji nkhawa ndi chovala? Tapenyetsani maluwa a kuthengo, makulidwe ao; sagwiritsa ntchito, kapena sapota:[29] koma ndinena kwa inu, kuti angakhale Solomoni mu ulemerero wake wonse sanavale monga limodzi la amenewa.

1 TIMOTEO 2:9-10
[9] Momwemonso, akazi adziveke okha ndi chovala choyenera, ndi manyazi, ndi chidziletso; osati ndi tsitsi lake loluka, ndi golide kapena ngale, kapena malaya a mtengo wake wapatali;[10] komatu (umo mokomera akazi akuvomereza kulemekeza Mulungu), mwa ntchito zabwino.

1 SAMUELE 16:7
Koma Yehova ananena ndi Samuele, Usayang'ane nkhope yake, kapena kutalika kwa msinkhu wake, popeza Ine ndinamkana iye; pakuti Yehova saona monga aona munthu; pakuti munthu ayang'ana chooneka ndi maso, koma Yehova ayang'ana mumtima.

MLALIKI 3:11
Chinthu chilichonse anachikongoletsa pa mphindi yake; ndipo waika zamuyaya m'mitima yao ndipo palibe munthu angalondetse ntchito Mulungu wazipanga chiyambire mpaka chitsiriziro.

AGALATIYA 3:26-27
[26] Pakuti inu nonse muli ana a Mulungu, mwa chikhulupiriro cha mwa Khristu Yesu.[27] Pakuti nonse amene munabatizidwa kwa Khristu mudavala Khristu.

MIYAMBO 3:15-18
[15] Mtengo wake uposa ngale; ndipo zonse zikukondweretsa sizilingana naye.[16] Masiku ambiri ali m'dzanja lamanja lake; chuma ndi ulemu m'dzanja lake lamanzere.[17] Njira zake zili zokondweretsa, mayendedwe ake onse ndiwo mtendere.[18] Ndiyo mtengo wa moyo wa akuigwira; wakuiumirira ngwodala.

EZEKIELE 28:17-18
[17] Unadzikuza mtima chifukwa cha kukongola kwako, waipsa nzeru zako; chifukwa cha kuwala kwako ndakugwetsa pansi, ndakuika pamaso pa mafumu, kuti akupenye.[18] Mwa mphulupulu zako zochuluka ndi malonda ako osalungama waipsa malo ako opatulika; chifukwa chake ndatulutsa moto m'kati mwako wakunyeketsa iwe; ndipo ndakusandutsa mapulusa panthaka pamaso pa onse akuona.

YAKOBO 1:23
Pakuti ngati munthu ali wakumva mau, wosati wakuchita, iyeyu afanana ndi munthu wakuyang'anira nkhope yake ya chibadwidwe chake m'kalirole;

MATEYU 23:28
Chomwecho inunso muonekera olungama pamaso pa anthu, koma m'kati muli odzala ndi chinyengo ndi kusaweruzika.

MIYAMBO 31:30
Kukongola kungonyenga, maonekedwe okoma ndi chabe; koma mkazi woopa Yehova adzatamandidwa.

Chewa Bible 2014
Bible Society of Malawi