A A A A A

Moyo: [Tsiku lobadwa]


AEFESO 2:10
Pakuti ife ndife chipango chake, olengedwa mwa Khristu Yesu, kuchita ntchito zabwino, zimene Mulungu anazipangiratu, kuti tikayende m'menemo.

YEREMIYA 29:11
Pakuti ndidziwa malingiriro amene ndilingiririra inu, ati Yehova, malingiriro a mtendere, si a choipa, akukupatsani inu adzukulu ndi chiyembekezero.

YOHANE 16:21
Mkazi pamene akuti abale ali nacho chisoni, chifukwa yafika nthawi yake; koma pamene wabala mwana, sakumbukiranso kusaukako, chifukwa cha chimwemwe kuti wabadwa munthu kudziko lapansi.

MIYAMBO 9:11
Pakuti mwa ine masiku ako adzachuluka, zaka za moyo wako zidzaonjezedwa.

MASALIMO 16:11
Mudzandidziwitsa njira ya moyo, pankhope panu pali chimwemwe chokwanira; m'dzanja lanu lamanja muli zokondweretsa zomka muyaya.

MASALIMO 20:4
likupatse cha mtima wako, ndipo likwaniritse upo wako wonse.

MASALIMO 27:4-7
[4] Chinthu chimodzi ndinachipempha kwa Yehova, ndidzachilondola ichi, Kuti ndikhalitse m'nyumba ya Yehova masiku onse a moyo wanga, kupenya kukongola kwake kwa Yehova ndi kufunsitsa m'Kachisi wake.[5] Chifukwa kuti pa tsiku la tsoka Iye adzandibisa mumsasa mwake, adzandibisa m'tsenjezi mwa chihema chake; pathanthwe adzandikweza.[6] Ndipo tsopano mutu wanga udzakwezeka pamwamba pa adani anga akundizinga; ndipo ndidzapereka m'chihema mwake nsembe za kufuula mokondwera; ndidzaimba, inde, ndidzaimbira Yehova zomlemekeza.[7] Imvani, Yehova, liu langa pofuula ine; mundichitirenso chifundo ndipo mundivomereze.

MASALIMO 90:12
Mutidziwitse kuwerenga masiku athu motero, kuti tikhale nao mtima wanzeru.

MASALIMO ๙๑:๑๑
Pakuti adzalamulira angelo ake za iwe, akusunge m'njira zako zonse.

MASALIMO ๙๑:๑๖
Ndidzamkhutitsa ndi masiku ambiri, ndi kumuonetsera chipulumutso changa.

MASALIMO 118:24
Tsiku ili ndilo adaliika Yehova; tidzasekera ndi kukondwera m'mwemo.

ZEFANIYA 3:17
Yehova Mulungu wako ali pakati pako, wamphamvu wakupulumutsa; adzakondwera nawe ndi chimwemwe, adzakhala wopanda thamo m'chikondi chake; adzasekerera nawe ndi kuimbirapo.

MASALIMO ๓๗:๔-๕
[๔] Udzikondweretsenso mwa Yehova; ndipo Iye adzakupatsa zokhumba mtima wako.[๕] Pereka njira yako kwa Yehova; khulupiriranso Iye, adzachichita.

MALIRO 3:22-23
[22] Chifukwa chakusathedwa ife ndicho chifundo cha Yehova, pakuti chisoni chake sichileka,[23] chioneka chatsopano m'mawa ndi m'mawa; mukhulupirika ndithu.

NUMERI 6:24-26
[24] Yehova akudalitse iwe, nakusunge;[25] Yehova awalitse nkhope yake pa iwe, nakuchitire chisomo;[26] Yehova akweze nkhope yake pa iwe, nakupatse mtendere.

MASALIMO 139:1-24
[1] Kwa Mkulu wa Nyimbo; Salimo la Davide. Munandisanthula, Yehova, nimundidziwa.[2] Inu mudziwa kukhala kwanga ndi kuuka kwanga, muzindikira lingaliro langa muli kutali.[3] Muyesa popita ine ndi pogona ine, ndi njira zanga zonse muzolowerana nazo.[4] Pakuti asanafike mau pa lilime langa, taonani, Yehova, muwadziwa onse.[5] Munandizinga kumbuyo ndi kumaso, nimunaika dzanja lanu pa ine.[6] Kudziwa ichi kundilaka ndi kundidabwitsa: Kundikhalira patali, sindifikirako.[7] Ndidzapita kuti kuzembera mzimu wanu? Kapena ndidzathawira kuti kuzembera nkhope yanu?[8] Ndikakwera kunka kumwamba, muli komweko; kapena ndikadziyalira ku Gehena, taonani, muli komweko.[9] Ndikadzitengera mapiko a mbandakucha, ndi kukhala ku malekezero a nyanja;[10] kungakhale komweko dzanja lanu lidzanditsogolera, nilidzandigwira dzanja lanu lamanja.[11] Ndipo ndikati, Koma mdima undiphimbe, ndi kuunika kondizinga kukhale usiku.[12] Ungakhale mdima sudetsa pamaso panu, koma usiku uwala ngati usana; mdima ukunga kuunika.[13] Pakuti Inu munalenga impso zanga; munandiumba ndisanabadwe ine.[14] Ndikuyamikani chifukwa kuti chipangidwe changa nchoopsa ndi chodabwitsa; ntchito zanu nzodabwitsa; moyo wanga uchidziwa ichi bwino ndithu.[15] Thupi langa silinabisikira Inu popangidwa ine mobisika, poombedwa ine monga m'munsi mwake mwa dziko lapansi.[16] Ndisanaumbidwe ine maso anu anandipenya, ziwalo zanga zonse zinalembedwa m'buku mwanu, masiku akuti ziumbidwe, pakalibe chimodzi cha izo.[17] Potero, Mulungu, ndiziyesa zolingalira zanu za mtengo wake ndithu! Mawerengedwe ake ndi ambirimbiri![18] Ndikaziwerenga zichuluka koposa mchenga: Ndikauka ndikhalanso nanu.[19] Indedi, mudzaomba woipa, Mulungu: Ndipo amuna inu okhumba mwazi, chokani kwa ine.[20] Popeza anena za Inu moipa, ndi adani anu atchula dzina lanu mwachabe.[21] Kodi sindidana nao iwo akudana ndi Inu, Yehova? Ndipo kodi sindimva nao chisoni iwo akuukira Inu?[22] Ndidana nao ndi udani weniweni, ndiwayesa adani.[23] Mundisanthule, Mulungu, nimudziwe mtima wanga; mundiyese nimudziwe zolingalira zanga.[24] Ndipo mupenye ngati ndili nao mayendedwe oipa, nimunditsogolere pa njira yosatha.

Chewa Bible 2014
Bible Society of Malawi