A A A A A

Khalidwe Labwino: [Kusamalira]


1 TIMOTEO 5:4
Koma ngati wamasiye wina ali nao ana kapena adzukulu, ayambe aphunzire iwo kuchitira ulemu a m'banja lao, ndi kubwezera akuwabala; pakuti ichi ncholandirika pamaso pa Mulungu.

MASALIMO 146:9
Yehova asunga alendo; agwiriziza mwana wamasiye ndi mkazi wamasiye; koma akhotetsa njira ya oipa.

YOHANE 8:32
ndipo mudzazindikira choonadi, ndipo choonadi chidzakumasulani.

CHIVUMBULUTSO 17:5
ndipo pamphumi pake padalembedwa dzina, CHINSINSI, BABILONI WAUKULU, AMAI WA ACHIGOLOLO NDI WA ZONYANSITSA ZA DZIKO.

YAKOBO 1:27
Mapembedzedwe oyera ndi osadetsa pamaso pa Mulungu ndi Atate ndiwo: kucheza ndi ana amasiye ndi akazi amasiye m'chisautso chao, ndi kudzisungira mwini wosachitidwa mawanga ndi dziko lapansi.

YOHANE 6:54
Iye wakudya thupi langa ndi kumwa mwazi wanga ali nao moyo wosatha; ndipo Ine ndidzamuukitsa iye tsiku lomaliza.

MARKO 6:3
Si mmisiri wa mitengo uyu, mwana wa Maria, mbale wao wa Yakobo, ndi Yose, ndi Yudasi, ndi Simoni? Ndipo alongo ake sali nafe pano kodi? Ndipo anakhumudwa ndi Iye.

YOHANE 14:6
Yesu ananena naye, Ine ndine njira, ndi choonadi, ndi moyo. Palibe munthu adza kwa Atate, koma mwa Ine.

GENESIS 1:1-7
[1] Pachiyambi Mulungu adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.[2] Dziko lapansi ndipo linali lopanda kanthu; ndipo mdima unali pamwamba pa nyanja; ndipo mzimu wa Mulungu unalinkufungatira pamwamba pa madzi.[3] Ndipo anati Mulungu, Kuyere; ndipo kunayera.[4] Ndipo anaona Mulungu kuti kuyerako kunali kwabwino; ndipo Mulungu analekanitsa kuyera ndi mdima.[5] Ndipo Mulungu anacha kuyerako Usana, ndi mdimawo anautcha Usiku. Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku loyamba.[6] Ndipo anati Mulungu, Pakhale thambo pakati pamadzi, lilekanitse madzi ndi madzi.[7] Ndipo Mulungu anapanga thambo, nalekanitsa madzi anali pansi pa thambolo ndi madzi anali pamwamba pa thambolo; ndipo kunatero.

1 TIMOTEO 5:8
Koma ngati wina sadzisungiratu mbumba yake ya iye yekha, makamaka iwo a m'banja lake, wakana chikhulupiriro iye, ndipo aipa koposa wosakhulupirira.

AGALATIYA 1:19
Koma wina wa atumwi sindinamuona, koma Yakobo mbale wa Ambuye.

MALAKI 1:11
Pakuti kuyambira kotulukira dzuwa kufikira kolowera kwake dzina langa lidzakhala lalikulu mwa amitundu; ndipo m'malo monse adzaperekera dzina langa chofukiza ndi chopereka choona; pakuti dzina langa lidzakhala lalikulu mwa amitundu, ati Yehova wa makamu.

GENESIS 2:7
Ndipo Yehova Mulungu anaumba munthu ndi dothi lapansi, nauzira mpweya wa moyo m'mphuno mwake; munthuyo nakhala wamoyo.

YOHANE 3:3-5
[3] Yesu anayankha nati kwa iye, Indetu, indetu, ndinena ndi iwe, Ngati munthu sabadwa mwatsopano, sakhoza kuona Ufumu wa Mulungu.[4] Nikodemo ananena kwa Iye, Munthu akhoza bwanji kubadwa atakalamba? Kodi akhoza kulowanso m'mimba ya amake ndi kubadwa?[5] Yesu anayankha, Indetu, indetu, ndinena ndi iwe, Ngati munthu sabadwa mwa madzi ndi Mzimu, sakhoza kulowa ufumu wa Mulungu.

AHEBRI 12:14
Londolani mtendere ndi anthu onse, ndi chiyeretso chimene, akapanda ichi, palibe mmodzi adzaona Ambuye:

CHIVUMBULUTSO 17:18
Ndipo mkaziyo unamuona, ndiye mudzi waukulu, wakuchita ufumu pa mafumu a dziko.

MATEYU 16:18
Ndiponso Ine ndinena kwa iwe, kuti iwe ndiwe Petro, ndipo pa thanthwe ili ndidzakhazika Mpingo wanga; ndipo makomo a dziko la akufa sadzagonjetsa uwo.

GENESIS 1:1
Pachiyambi Mulungu adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.

EKSODO 15:3
Yehova ndiye wankhondo; dzina lake ndiye Yehova.

CHIVUMBULUTSO 17:9
Pano pali mtima wakukhala nayo nzeru. Mitu isanu ndi iwiri ndiyo mapiri asanu ndi awiri amene mkazi akhalapo;

AFILIPI 4:6-7
[6] Musadere nkhawa konse; komatu m'zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu.[7] Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana chidziwitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.

AGALATIYA 4:19
Tiana tanga, amene ndilikumvanso zowawa za kubala inu, kufikira Khristu aumbika mwa inu,

1 PETRO 3:15
koma mumpatulikitse Ambuye Khristu m'mitima yanu; okonzeka nthawi zonse kuchita chodzikanira pa yense wakukufunsani chifukwa cha chiyembekezo chili mwa inu, komatu ndi chifatso ndi mantha;

CHIVUMBULUTSO 17:1
Ndipo anadza mmodzi mwa angelo asanu ndi awiri akukhala nazo mbale zisanu ndi ziwiri, nalankhula ndi ine, nanena, Idza kuno, ndidzakuonetsa chitsutso cha mkazi wachigololo wamkulu, wakukhala pa madzi ambiri,

MATEYU 18:15-18
[15] Ndipo ngati mbale wako akuchimwira iwe, pita, numlangize pa nokha iwe ndi iye; ngati akumvera iwe, wambweza mbale wako.[16] Koma ngati samvera, onjeza kutenga ndi iwe wina mmodzi kapena awiri, kuti atsimikizidwe mau onse pakamwa pa mboni ziwiri kapena zitatu.[17] Ndipo ngati iye samvera iwo, uuze Mpingo; ndipo ngati iye samveranso Mpingowo, akhale kwa iwe monga wakunja ndi wamsonkho.[18] Indetu ndinena kwa inu, Zilizonse mukazimanga pa dziko lapansi zidzakhala zomangidwa Kumwamba: ndipo zilizonse mukazimasula pa dziko lapansi, zidzakhala zomasulidwa Kumwamba.

AEFESO 1:22-23
[22] ndipo anakonza zonse pansi pa mapazi ake, nampatsa Iye akhale mutu pamtu pa zonse, kwa Mpingo[23] amene ali thupi lake, mdzazidwe wa Iye amene adzaza zonse m'zonse.

AEFESO 5:23
Pakuti mwamuna ndiye mutu wa mkazi, monganso Khristu ndiye mutu wa Mpingo, ali yekha Mpulumutsi wa thupilo.

MACHITIDWE A ATUMWI 4:32
Ndipo unyinji wa iwo akukhulupirira anali wa mtima umodzi ndi moyo umodzi; ndipo sananena mmodzi kuti kanthu ka chuma anali nacho ndi kake ka iye yekha; koma anali nazo zonse zodyerana.

1 AKORINTO 1:10
Koma ndikudandaulirani inu, abale, mwa dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu, kuti munene chimodzimodzi inu nonse, ndi kuti pasakhale malekano pakati pa inu; koma mumangike mu mtima womwewo ndi m'chiweruziro chomwecho.

YOHANE 12:48
Iye amene akaniza Ine, ndi kusalandira mau anga, ali naye womweruza iye, mau amene ndalankhula, iwowa adzamweruza tsiku lomaliza.

YOHANE 14:28
Mwamva kuti Ine ndinanena kwa inu, Ndimuka, ndipo ndidza kwa inu. Mukadandikonda Ine, mukadakondwera kuti ndipita kwa Atate; pakuti Atate ali wamkulu ndi Ine.

AHEBRI 1:14
Kodi siili yonse mizimu yotumikira, yotumidwa kuti itumikire iwo amene adzalowa chipulumutso?

MATEYU 18:10
Yang'anirani kuti musanyoze mmodzi wa ang'ono awa; pakuti ndinena kwa inu, kuti angelo ao apenya chipenyere nkhope ya Atate wanga wa Kumwamba.

AEFESO 6:12
Chifukwa kuti kulimbana kwathu sitilimbana nao mwazi ndi thupi, komatu nao maukulu, ndi maulamuliro, ndi akuchita zolimbika a dziko lapansi a mdima uno, ndi auzimu a choipa m'zakumwamba.

YOHANE 3:16
Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakhulupirira Iye asatayike, koma akhale nao moyo wosatha.

YOHANE 17:17
Patulani iwo m'choonadi; mau anu ndi choonadi.

CHIVUMBULUTSO 2:9
Ndidziwa chisautso chako, ndi umphawi wako (komatu uli wachuma), ndi mwano wa iwo akunena za iwo okha kuti ali Ayuda, osakhala Ayuda, komatu sunagoge wa Satana.

MASALIMO 68:5
Mulungu, mokhala mwake moyera, ndiye Atate wa ana amasiye, ndi woweruza wa akazi amasiye.

MASALIMO 146:9
Yehova asunga alendo; agwiriziza mwana wamasiye ndi mkazi wamasiye; koma akhotetsa njira ya oipa.

AGALATIYA 2:10
pokhapo kuti tikumbukire aumphawi; ndicho chomwe ndinafulumira kuchichita.

AROMA 3:23
pakuti onse anachimwa, naperewera pa ulemerero wa Mulungu;

Chewa Bible 2014
Bible Society of Malawi