Instagram
English
A A A A A

Khalidwe Labwino: [Kulandila]
1 AKORINTO 5:11-13
[11] koma tsopano ndalembera inu kuti musayanjane naye, ngati wina wotchedwa mbale ali wachigololo, kapena wosirira, kapena wopembedza mafano, kapena wolalatira, kapena woledzera, kapena wolanda, kungakhale kukadya naye wotere, iai.[12] Pakuti nditani nao akunja kukaweruza iwo? Kodi amene ali m'katimo simuwaweruza ndi inu,[13] koma akunja awaweruza Mulungu? Chotsani woipayo pakati pa inu nokha.

1 YOHANE 1:9
Ngati tivomereza machimo athu, ali wokhulupirika ndi wolungama Iye, kuti atikhululukire machimo athu, ndi kutisambitsa kutichotsera chosalungama chilichonse.

1 PETRO 3:8-9
[8] Chotsalira, khalani nonse a mtima umodzi, ochitirana chifundo, okondana ndi abale, achisoni, odzichepetsa;[9] osabwezera choipa ndi choipa, kapena chipongwe ndi chipongwe, koma penatu madalitso; pakuti kudzatsata ichi mwaitanidwa, kuti mukalandire dalitso.

YOHANE 3:16
Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakhulupirira Iye asatayike, koma akhale nao moyo wosatha.

MIYAMBO 13:20
Ukayenda ndi anzeru udzakhala wanzeru: koma mnzao wa opusa adzaphwetekedwa.

AROMA 2:11
pakuti Mulungu alibe tsankho.

AROMA 5:8
Koma Mulungu atsimikiza kwa ife chikondi chake cha mwini yekha m'menemo, kuti pokhala ife chikhalire ochimwa, Khristu adatifera ife.

AROMA 8:31
Ndipo tidzatani ndi zinthu izi? Ngati Mulungu ali ndi ife, adzatikaniza ndani?

AROMA 14:1-2
[1] Ndipo iye amene ali wofooka m'chikhulupiriro, mumlandire, koma si kuchita naye makani otsutsana ai.[2] Munthu mmodzi akhulupirira kuti adye zinthu zonse, koma wina wofooka angodya zitsamba.

AHEBRI 10:24-25
[24] ndipo tiganizirane wina ndi mnzake kuti tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino,[25] osaleka kusonkhana kwathu pamodzi, monga amachita ena, komatu tidandaulirane, ndiko koposa monga momwe muona tsiku lilikuyandika.

YOHANE 6:35-37
[35] Yesu anati kwa iwo, Ine ndine mkate wamoyo; iye amene adza kwa Ine sadzamva njala, ndi iye amene akhulupirira Ine sadzamva ludzu nthawi zonse.[36] Koma ndinati kwa inu, kuti mungakhale mwandiona, simukhulupirira.[37] Chinthu chonse chimene anandipatsa Ine Atate chidzadza kwa Ine; ndipo wakudza kwa Ine sindidzamtaya iye kunja.

AKOLOSE 3:12-14
[12] Chifukwa chake valani, monga osankhika a Mulungu, oyera mtima ndi okondedwa, mtima wachifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, chifatso, kuleza mtima;[13] kulolerana wina ndi mnzake, ndi kukhululukirana eni okha, ngati wina ali nacho chifukwa pa mnzake; monganso Ambuye anakhululukira inu, teroni inunso;[14] koma koposa izi zonse khalani nacho chikondano, ndicho chomangira cha mtima wamphumphu.

MATEYU 5:38-42
[38] Munamva kuti kunanenedwa, Diso kulipa diso, ndi dzino kulipa dzino:[39] koma ndinena kwa inu, Musakanize munthu woipa; koma amene adzakupanda iwe pa tsaya lako lamanja, umtembenuzire linanso.[40] Ndipo kwa iye wofuna kupita nawe kumlandu ndi kutenga malaya ako, umlolezenso chofunda chako.[41] Ndipo amene akakukakamiza kumperekeza njira imodzi, upite naye ziwiri.[42] Kwa iye wopempha iwe umpatse, ndipo kwa iye wofuna kukukongola usampotolokere.

MATEYU 25:34-40
[34] Pomwepo Mfumuyo idzanena kwa iwo a kudzanja lake lamanja, Idzani kuno inu odalitsika a Atate wanga, lowani mu Ufumu wokonzedwera kwa inu pa chikhazikiro chake cha dziko lapansi:[35] pakuti ndinali ndi njala, ndipo munandipatsa Ine kudya; ndinali ndi ludzu, ndipo munandimwetsa Ine; ndinali mlendo, ndipo munachereza Ine;[36] wamaliseche Ine, ndipo munandiveka; ndinadwala, ndipo munadza kucheza ndi Ine; ndinali m'nyumba yandende, ndipo munadza kwa Ine.[37] Pomwepo olungama adzamyankha Iye kuti, Ambuye, tinakuonani Inu liti wanjala, ndi kukudyetsani? Kapena waludzu, ndi kukumwetsani?[38] Ndipo tinaona Inu liti mlendo, ndi kukucherezani? Kapena wamaliseche, ndi kukuvekani?[39] Ndipo tinakuonani Inu liti wodwala, kapena m'nyumba yandende, ndipo tinadza kwa Inu?[40] Ndipo Mfumuyo idzayankha nidzati kwa iwo, Indetu ndinena kwa inu, Chifukwa munachitira ichi mmodzi wa abale anga, ngakhale ang'onong'ono awa, munandichitira ichi Ine.

AROMA 15:1-7
[1] Ndipo ife amene tili olimba tiyenera kunyamula zofooka za opanda mphamvu, ndi kusadzikondweretsa tokha.[2] Yense wa ife akondweretse mnzake, kumchitira zabwino, zakumlimbikitsa.[3] Pakuti Khristunso sanadzikondweretsa yekha; koma monga kwalembedwa, Minyozo ya iwo amene anakunyoza iwe inagwa pa Ine.[4] Pakuti zonse zinalembedwa kale zinalembedwa kutilangiza, kuti mwa chipiriro ndi chitonthozo cha malembo, tikhale ndi chiyembekezo.[5] Ndipo Mulungu wa chipiriro ndi wa chitonthozo apatse inu kuti mukhale ndi mtima umodzi wina ndi mnzake, monga mwa Khristu Yesu;[6] kuti nonse pamodzi, m'kamwa mmodzi, mukalemekeze Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu.[7] Chifukwa chake mulandirane wina ndi mnzake, monganso Khristu anakulandirani inu, kukachitira Mulungu ulemerero.

AROMA 14:10-19
[10] Koma iwe uweruziranji mbale wako? Kapena iwenso upeputsiranji mbale wako? Pakuti ife tonse tidzaimirira kumpando wakuweruza wa Mulungu.[11] Pakuti kwalembedwa, Pali moyo wanga, ati Ambuye, mabondo onse adzagwadira Ine, ndipo malilime onse adzavomereza Mulungu.[12] Chotero munthu aliyense wa ife adzadziwerengera mlandu wake kwa Mulungu.[13] Chifukwa chake tisaweruzanenso wina mnzake; koma weruzani ichi makamaka, kuti munthu asaike chokhumudwitsa pa njira ya mbale wake, kapena chomphunthwitsa.[14] Ndidziwa, ndipo ndakhazikika mtima mwa Ambuye Yesu, kuti palibe chinthu chonyansa pa chokha; koma kwa ameneyo achiyesa chonyansa, kwa iye chikhala chonyansa.[15] Koma ngati iwe wachititsa mbale wako chisoni ndi chakudya, pamenepo ulibe kuyendayendanso ndi chikondano. Usamuononga ndi chakudya chako, iye amene Khristu adamfera.[16] Chifukwa chake musalole chabwino chanu achisinjirire.[17] Pakuti ufumu wa Mulungu sukhala chakudya ndi chakumwa, koma chilungamo, ndi mtendere, ndi chimwemwe mwa Mzimu Woyera.[18] Pakuti iye amene atumikira Khristu mu izi akondweretsa Mulungu, navomerezeka ndi anthu.[19] Chifukwa chake tilondole zinthu za mtendere, ndi zinthu zakulimbikitsana wina ndi mnzake.

Chewa Bible 2014
Bible Society of Malawi