A A A A A

Khalidwe Loipa: [Kudandaula]


MASALIMO 144:14
Kuti ng'ombe zathu zikhale zosenza katundu; ndi kuti pasakhale kupasula linga kapena kutulukamo, pasakhalenso kufuula m'makwalala athu.

NEHEMIYA 8:1
Ndipo anthu onse anasonkhana ngati munthu mmodzi kukhwalala lili ku Chipata cha Madzi, namuuza Ezara mlembi atenge buku la chilamulo cha Mose, chimene Yehova adalamulira Israele.

YESAYA 24:11
Muli mfuu m'makwalala chifukwa cha vinyo; kukondwa konse kwadetsedwa, kusangalala kwa dziko kwatha.

YEREMIYA 14:2
Yuda alira, ndipo zipata zake zilefuka, zikhala pansi zovekedwa ndi zakuda; mfuu wa Yerusalemu wakwera.

MIYAMBO 23:29
Ndani ali ndi chisoni? Ndani asauka? Ndani ali ndi makangano? Ndani ang'ung'udza? Ndani alasidwa chabe? Ndani afiira maso?

AFILIPI 4:6-7
[6] Musadere nkhawa konse; komatu m'zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu.[7] Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana chidziwitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.

Chewa Bible 2014
Bible Society of Malawi