A A A A A

Khalidwe Loipa: [Mkwiyo]


AEFESO 4:26-31
[26] Kwiyani, koma musachimwe; dzuwa lisalowe muli chikwiyire,[27] ndiponso musampatse malo mdierekezi.[28] Wakubayo asabenso; koma makamaka agwiritse ntchito, nagwire ntchito yokoma ndi manja ake, kuti akhale nacho chakuchereza wosowa.[29] Nkhani yonse yovunda isatuluke m'kamwa mwanu, koma ngati pali ina yabwino kukumangirira monga mofunika ndiyo, kuti ipatse chisomo kwa iwo akumva.[30] Ndipo musamvetse chisoni Mzimu Woyera wa Mulungu, amene munasindikizidwa chizindikiro mwa Iye, kufikira tsiku la maomboledwe.[31] Chiwawo chonse, ndi kupsa mtima, ndi mkwiyo, ndi chiwawa, ndi mwano zichotsedwe kwa inu, ndiponso choipa chonse.

YAKOBO 1:19-20
[19] Mudziwa, abale anga okondedwa, kuti munthu aliyense akhale wotchera khutu, wodekha polankhula, wodekha pakupsa mtima.[20] Pakuti mkwiyo wa munthu suchita chilungamo cha Mulungu.

MIYAMBO 29:11
Chitsiru chivumbulutsa mkwiyo wake wonse; koma wanzeru auletsa nautontholetsa.

MLALIKI 7:9
Usakangaze mumtima mwako kukwiya; pakuti mkwiyo ugona m'chifuwa cha zitsiru.

MIYAMBO 15:1
Mayankhidwe ofatsa abweza mkwiyo; koma mau owawitsa aputa msunamo.

MIYAMBO 15:18
Munthu wozaza aputa makani; koma wosakwiya msanga atonthoza makangano.

AKOLOSE 3:8
Koma tsopano tayani inunso zonsezi: mkwiyo, kupsa mtima, dumbo, mwano, zonyansa zotuluka m'kamwa mwanu:

YAKOBO 4:1-2
[1] Zichokera kuti nkhondo, zichokera kuti zolimbana mwa inu? Kodi sizichokera kuzikhumbitso zanu zochita nkhondo m'ziwalo zanu?[2] Mulakalaka, ndipo zikusowani; mukupha, nimuchita kaduka, ndipo simukhoza kupeza; mulimbana, nimuchita nkhondo; mulibe kanthu, chifukwa simupempha.

MIYAMBO 16:32
Wosakwiya msanga aposa wamphamvu; wolamulira mtima wake naposa wolanda mudzi.

MIYAMBO 22:24
Usayanjane ndi munthu wokwiya msanga; ngakhale kupita ndi mwamuna waukali;

MATEYU 5:22
koma Ine ndinena kwa inu, kuti yense wokwiyira mbale wake wopanda chifukwa adzakhala wopalamula mlandu; ndipo amene adzanena ndi mbale wake, Wopanda pake iwe, adzakhala wopalamula mlandu wa akulu: koma amene adzati, Chitsiru iwe: adzakhala wopalamula Gehena wamoto.

MASALIMO 37:8-9
[8] Leka kupsa mtima, nutaye mkwiyo; usavutike mtima ungachite choipa.[9] Pakuti ochita zoipa adzadulidwa; koma iwo akuyembekeza Yehova, iwowa adzalandira dziko lapansi.

MASALIMO 7:11
Mulungu ndiye Woweruza wolungama, ndiye Mulungu wakukwiya masiku onse.

2 MAFUMU 11:9-10
[9] Ndipo atsogoleri a mazana anachita monga mwa zonse anawalamulira Yehoyada wansembe, natenga yense anthu ake olowera pa Sabata, ndi otulukira pa Sabata, nafika kwa Yehoyada wansembeyo.[10] Ndipo wansembeyo anapereka kwa atsogoleri a mazana mikondo ndi zikopa, zinali za mfumu Davide, zosungika m'nyumba ya Yehova.

2 MAFUMU 17:18
Chifukwa chake Yehova anakwiya naye Israele kwakukulu, nawachotsa pamaso pake osatsala mmodzi, koma fuko la Yuda lokha.

MIYAMBO 14:29
Wosakwiya msanga apambana kumvetsa; koma wansontho akuza utsiru.

Chewa Bible 2014
Bible Society of Malawi