A A A A A

Angelo ndi Ziwanda: [Belezebule]


MATEYU 12:24
Koma Afarisi pakumva, anati, Uyu samatulutsa ziwanda koma ndi mphamvu yake ya Belezebulu, mkulu wa ziwanda.

MARKO 3:22
Ndipo alembi amene adatsika ku Yerusalemu ananena kuti, Ali naye Belezebulu, ndipo, Ndi mkulu wao wa ziwanda atulutsa ziwanda.

MATEYU 10:25
Kumkwanira wophunzira kuti akhale monga mphunzitsi wake, ndi kapolo monga mbuye. Ngati anamutcha mwini banja Belezebulu, sadzaposa kodi kuwatero apabanja ake?

MATEYU 12:27
Ndipo ngati Ine ndimatulutsa ziwanda ndi mphamvu yake ya Belezebulu, ana anu amazitulutsa ndi mphamvu ya yani? Chifukwa chake iwo adzakhala oweruza anu.

LUKA 11:15-19
[15] Koma ena mwa iwo anati, Ndi Belezebulu mkulu wa ziwanda amatulutsa ziwanda.[16] Koma ena anamuyesa, nafuna kwa Iye chizindikiro chochokera Kumwamba.[17] Koma Iye, podziwa zolingirira zao, anati kwa iwo, Ufumu uliwonse wogawanika m'kati mwake upasuka; ndipo nyumba ikagawanika m'kati mwake igwa.[18] Ndiponso ngati Satana agawanika kudzitsutsa mwini, udzaimika bwanji ufumu wake? Popeza munena kuti nditulutsa ziwanda ndi Belezebulu.[19] Koma ngati Ine ndimatulutsa ziwanda ndi Belezebulu, ana anu azitulutsa ndi yani? Mwa ichi iwo adzakhala oweruza anu.

2 MAFUMU 1:1-3
[1] Ndipo atamwalira Ahabu, Mowabu anapandukana ndi Israele.[2] Ndipo Ahaziya anagwa kuchokera pamwamba pa chipinda chake chosanja chinali ku Samariya, nadwala, natuma mithenga, nanena nayo, Mufunsire kwa Baala-Zebubi mulungu wa ku Ekeroni ngati ndidzachira nthenda iyi.[3] Koma mthenga wa Yehova anati kwa Eliya wa ku Tisibe, Nyamuka, kwera kukomana ndi mithenga ya mfumu ya Samariya, nunene nayo, Kodi ndi popeza palibe Mulungu mwa Israele, kuti mukafunsira kwa Baala-Zebubi mulungu wa ku Ekeroni?

LUKA 11:18
Ndiponso ngati Satana agawanika kudzitsutsa mwini, udzaimika bwanji ufumu wake? Popeza munena kuti nditulutsa ziwanda ndi Belezebulu.

MARKO 3:20-30
[20] Ndipo anthu ambiri anasonkhananso, kotero kuti sanathe iwo konse kudya.[21] Ndipo pamene abale ake anamva, anadza kudzamgwira Iye; pakuti anati adayaluka.[22] Ndipo alembi amene adatsika ku Yerusalemu ananena kuti, Ali naye Belezebulu, ndipo, Ndi mkulu wao wa ziwanda atulutsa ziwanda.[23] Ndipo m'mene adawaitana iwo, ananena nao m'mafanizo, Satana angathe bwanji kutulutsa Satana?[24] Ndipo ufumu ukagawanika pa uwu wokha, sukhoza kukhazikika.[25] Ndipo nyumba ikagawanika pa iyo yokha, sikhoza kukhazikika nyumbayo,[26] Ndipo Satana akadziukira mwini yekha, nagawanika, sakhoza kukhazikika, koma atsirizika.[27] Komatu palibe munthu akhoza kulowa m'nyumba ya mwini mphamvu, ndi kufunkha akatundu ake, koma athange wamanga mwini mphamvuyo; ndipo pamenepo adzafunkha za m'nyumba mwake.[28] Indetu, ndinena ndi inu, Adzakhululukidwa machimo onse a ana a anthu, ndi zamwano zilizonse adzachita mwano nazo;[29] koma aliyense adzachitira Mzimu Woyera mwano alibe kukhululukidwa nthawi yonse, koma anapalamuladi tchimo losatha;[30] pakuti adanena, Ali ndi mzimu wonyansa.

2 MAFUMU 1:16
Ndipo ananena nayo, Atero Yehova, Popeza watuma mithenga kukafunsira kwa Baala-Zebubi mulungu wa ku Ekeroni, kodi ndi popeza palibe Mulungu mwa Israele kufunsira mau ake? Chifukwa chake sudzatsika pakama pamene wakwerapo, koma udzafa ndithu.

GENESIS 1:1
Pachiyambi Mulungu adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.

MATEYU 9:34
Koma Afarisi analinkunena, Atulutsa ziwanda ndi mphamvu zake za mfumu ya ziwanda.

CHIVUMBULUTSO 21:20
achisanu, ndi sardonu; achisanu ndi chimodzi, ndi sardiyo; achisanu ndi chiwiri, ndi krusolito; achisanu ndi chitatu, ndi berulo; achisanu ndi chinai, ndi topaziyo; akhumi, ndi krusoprazo; akhumi ndi achimodzi, ndi huakinto; akhumi ndi chiwiri, ndi ametusto.

YOBU 2:11
Atamva tsono mabwenzi atatu a Yobu za choipa ichi chonse chidamgwera, anadza, yense kuchokera kwao, Elifazi wa ku Temani, ndi Bilidadi Msuki, ndi Zofari wa ku Naama, napangana kudzafika kumlirira ndi kumsangalatsa.

2 MAFUMU ൧:൬
Ndipo inanena naye, Munthu anakwera kukomana nafe, nati kwa ife, Kabwerereni kwa mfumu imene inakutumani inu, nimunene nayo, Atero Yehova, Kodi ndi popeza palibe Mulungu mwa Israele, kuti ulikutuma kukafunsira kwa Baala-Zebubi mulungu wa ku Ekeroni? Chifukwa chake sudzatsika pakama pamene wakwerapo, koma udzafa ndithu.

YOHANE 1:1
Pachiyambi panali Mau, ndipo Mau anali kwa Mulungu, ndipo Mau ndiye Mulungu.

LUKA 11:19
Koma ngati Ine ndimatulutsa ziwanda ndi Belezebulu, ana anu azitulutsa ndi yani? Mwa ichi iwo adzakhala oweruza anu.

EKSODO 6:23
Ndipo Aroni anadzitengera Eliseba, mwana wamkazi wa Aminadabu, mlongo wake wa Nasoni, akhale mkazi wake; ndipo anambalira Nadabu ndi Abihu, Eleazara ndi Itamara.

LUKA 3:1
Ndipo pa chaka chakhumi ndi chisanu cha ufumu wa Tiberio Kaisara, pokhala Pontio Pilato kazembe wa Yudeya, ndi Herode chiwanga cha Galileya, ndi Filipo mbale wake chiwanga cha dziko la Itureya ndi la Trakoniti, ndi Lisaniasi chiwanga cha Abilene;

GENESIS 10:10
Ndipo kuyamba kwake kwa ufumu wake kunali Babiloni, ndi Ereke, ndi Akadi, ndi Kaline, m'dziko la Sinara.

GENESIS 14:1
Ndipo panali masiku a Amurafere mfumu ya Sinara, ndi Ariyoki mfumu ya Elasara, ndi Kedorilaomere mfumu ya Elamu, ndi Tidala mfumu ya Goimu,

DEUTERONOMO 14:5
ngondo, ndi nswala ndi mphoyo, ndi mphalapala, ndi ngoma, ndi nyumbu, ndi mbalale.

RUTE 1:2
Dzina la munthuyo ndiye Elimeleki, ndi dzina la mkazi wake ndiye Naomi, ndi maina a ana ake awiri ndiwo Maloni, ndi Kilioni; ndiwo Aefurati a ku Betelehemu-Yuda. Iwowa ndipo analowa m'dziko la Mowabu, nakhala komweko.

NEHEMIYA 1:1
Mau a Nehemiya mwana wa Hakaliya. Kunali tsono mwezi wa Kisilevi, chaka cha makumi awiri, pokhala ine ku Susa kunyumba ya mfumu,

ESTERE 1:1
Izi zinachitika masiku a Ahasuwero, ndiye Ahasuweroyo anachita ufumu kuyambira Indiya kufikira Kusi, pa maiko zana limodzi mphambu makumi awiri kudza asanu ndi awiri.

1 MAFUMU 1:2
Pamenepo anyamata ake ananena naye, Amfunire mbuye wanga mfumu namwali, aimirire pamaso pa mfumu namsunge; nagone m'mfukato mwanu, kuti mbuye mfumu yanga afundidwe.

CHIVUMBULUTSO 16:16
Ndipo anawasonkhanitsira kumalo otchedwa m'Chihebri Armagedoni.

YESAYA 34:14
Ndipo zilombo za m'chipululu zidzakomana ndi mimbulu, tonde adzaitana mnzake; inde manchichi adzatera kumeneko, nadzapeza popumira.

MATEYU 22:37
Ndipo Yesu anati kwa iye, Uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse.

MARKO 3:1-6
[1] Ndipo analowanso m'sunagoge; ndipo munali munthu m'menemo ali ndi dzanja lake lopuwala.[2] Ndipo anamuyang'anira Iye, ngati adzamchiritsa tsiku la Sabata; kuti ammange mlandu.[3] Ndipo ananena ndi munthu ali ndi dzanja lopuwala, Taimirira pakati.[4] Ndipo ananena kwa iwo, Kodi nkuloledwa tsiku la Sabata kuchita zabwino, kapena zoipa? Kupulumutsa moyo kapena kupha? Koma anakhala chete.[5] Ndipo m'mene anawaunguza ndi mkwiyo, ndi kumva chisoni chifukwa cha kuuma kwa mitima yao, ananena kwa munthuyo, Tambasula dzanja lako. Ndipo analitambasula; ndipo linachira dzanja lake.[6] Ndipo Afarisi anatuluka, ndipo pomwepo anamkhalira upo ndi Aherode, wakumuononga Iye.

MARKO 10:46-52
[46] Ndipo iwo anafika ku Yeriko; ndipo m'mene Iye analikutuluka m'Yeriko, ndi ophunzira ake, ndi khamu lalikulu la anthu, mwana wa Timeo, Baratimeo, wopempha wakhungu, analikukhala pansi m'mbali mwa njira.[47] Ndipo pamene anamva kuti ndi Yesu wa ku Nazarete, anayamba kufuula, ndi kunena, Yesu, Inu Mwana wa Davide, mundichitire ine chifundo.[48] Ndipo ambiri anamulamula kuti atonthole: koma makamaka anafuulitsa kuti, Inu mwana wa Davide, mundichitire chifundo.[49] Ndipo Yesu anaima, nati, Mwitaneni. Ndipo anaitana wakhunguyo, nanena naye, Limba mtima; nyamuka, akuitana.[50] Ndipo iye anataya chofunda chake, nazunzuka, nadza kwa Yesu.[51] Ndipo Yesu anamyankha, nati, Ufuna kuti ndikuchitire chiyani? Ndipo wakhunguyo anati kwa Iye, Raboni, ndilandire kuona kwanga.[52] Ndipo Yesu anati kwa iye, Muka; chikhulupiriro chako chakupulumutsa iwe. Ndipo pomwepo anapenyanso; namtsata Iye panjira.

DANIELE 1:7
Ndi mkulu wa adindo anawapatsa maina ena; Daniele anamutcha Belitesazara; ndi Hananiya, Sadrake; ndi Misaele, Mesaki; ndi Azariya, Abedenego.

OWERUZA 4:6
Ndipo anatuma, naitana Baraki mwana wa Abinowamu, achoke m'Kedesi-Nafutali; nanena naye, Kodi Yehova Mulungu wa Israele sanalamulire ndi kuti, Muka, nulunjike kuphiri la Tabori, nuwatenge, apite nawe anthu zikwi khumi a ana a Nafutali ndi ana a Zebuloni?

2 MAFUMU 19:37
Ndipo kunali popembedza iye m'nyumba ya Nisiroki mulungu wake, Adrameleki ndi Sarezere anamkantha ndi lupanga; napulumukira ku dziko la Ararati. Ndipo Esarahadoni mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake.

EZEKIELE 23:4
Ndipo maina ao ndiwo Ohola wamkulu, ndi Oholiba mng'ono wake; nakhala anga, nabala ana aamuna ndi aakazi. Ndipo maina ao, Samariya ndiye Ohola, ndi Yerusalemu ndiye Oholiba.

YEREMIYA 1:1
Mau a Yeremiya mwana wa Hilikiya, wa ansembe amene anali ku Anatoti m'dziko la Benjamini;

GENESIS 10:22
Ana amuna a Semu; Elamu, ndi Asiriya, ndi Aripakisadi, ndi Ludi, ndi Aramu.

EZARA 4:7
Ndipo masiku a Arita-kisereksesi Bisilamu, Mitiredati, Tabeele, ndi anzao otsala, analembera kwa Arita-kisereksesi mfumu ya Persiya; ndi chilembedwe chake cha kalatayo anamlemba m'Chiaramu, namsanduliza m'Chiaramu.

MATEYU 10:3
Filipo, ndi Bartolomeo; Tomasi, ndi Mateyu wamsonkhoyo; Yakobo mwana wa Alifeyo, ndi Tadeyo;

MACHITIDWE A ATUMWI 2:9
Aparti ndi Amedi, ndi Aelamu, ndi iwo akukhala m'Mesopotamiya, m'Yudeya, ndiponso m'Kapadokiya, m'Ponto, ndi m'Asiya;

LEVITIKO 11:5
Ndi mbira, ingakhale ibzikula koma yosagawanika chiboda, muiyese yodetsedwa.

MLALIKI 1:1
Mau a Mlaliki, mwana wa Davide, mfumu ya m'Yerusalemu.

EKSODO 30:34
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Udzitengere zonunkhira, natafi, ndi sekeleti, ndi kelebuna; zonunkhira pamodzi ndi lubani loona; miyeso yofanana;

YOBU 9:9
Wolenga Mlalang'amba, Akamwiniatsatana, ndi Nsangwe, ndi Kumpotosimpita.

MACHITIDWE A ATUMWI 6:5
Ndipo mau amene anakonda unyinji wonse; ndipo anasankha Stefano, ndiye munthu wodzala ndi chikhulupiriro ndi Mzimu Woyera, ndi Filipo, ndi Prokoro, ndi Nikanore ndi Timoni, ndi Parmenasi, ndi Nikolasi, ndiye wopinduka wa ku Antiokeya:

CHIVUMBULUTSO 1:11
ndi kuti, Chimene upenya, lemba m'buku, nulitumize kwa Mipingo isanu ndi iwiri, ku Efeso, ndi ku Smirina, ndi ku Pergamo, ndi ku Tiatira, ndi ku Sardi, ndi ku Filadelfiya, ndi ku Laodikea.

1 MAFUMU 8:13
Ine ndakumangirani ndithu nyumba yokhalamo Inu, ndiyo malo okhalamo Inu nthawi zosatha.

MARKO 3:23
Ndipo m'mene adawaitana iwo, ananena nao m'mafanizo, Satana angathe bwanji kutulutsa Satana?

YOSWA 24:15
Ndipo ngati kutumikira Yehova kukuipirani mudzisankhire lero amene mudzamtumikira, kapena milungu imene anaitumikira makolo anu okhala tsidya lija la mtsinje, kapena milungu ya Aamori amene mukhala m'dziko lao; koma ine, ndi a m'nyumba yanga, tidzatumikira Yehova.

Ukrainian Bible HOM 1963
Public Domain: 1963