A A A A A

Zowonjezera: [Kuchuluka]


1 TIMOTEO 5:8
Koma ngati wina sadzisungiratu mbumba yake ya iye yekha, makamaka iwo a m'banja lake, wakana chikhulupiriro iye, ndipo aipa koposa wosakhulupirira.

2 AKORINTO 9:8
Ndipo Mulungu akhoza kuchulukitsira chisomo chonse kwa inu; kuti inu, pokhala nacho chikwaniro chonse m'zinthu zonse, nthawi zonse, mukachulukire kuntchito yonse yabwino;

DEUTERONOMO 29:12
kuti mulowe chipangano cha Yehova Mulungu wanu, ndi lumbiriro lake, limene Yehova Mulungu wanu achita ndi inu lero lino;

AEFESO 3:20
Ndipo kwa Iye amene angathe kuchita koposaposatu zonse zimene tizipempha, kapena tiziganiza, monga mwa mphamvu ya kuchita mwa ife,

EKSODO 34:6
Ndipo Yehova anapita pamaso pake, nafuula, Yehova, Yehova, Mulungu wachifundo ndi wachisomo, wolekereza, ndi wa ukoma mtima wochuluka, ndi wachoonadi;

YAKOBO 1:17
Mphatso iliyonse yabwino, ndi chininkho chilichonse changwiro zichokera Kumwamba, zotsika kwa Atate wa mauniko, amene alibe chisanduliko, kapena mthunzi wa chitembenukiro.

YOHANE 10:10
Siikudza mbala, koma kuti ikabe, ndi kupha, ndi kuononga. Ndadza Ine kuti akhale ndi moyo, ndi kukhala nao wochuluka.

LUKA 6:38
Patsani, ndipo kudzapatsidwa kwa inu; muyeso wabwino, wotsendereka, wokuchumuka, wosefukira, anthu adzakupatsani m'manja mwanu. Pakuti kudzayesedwa kwa inu ndi muyeso womwewo muyesa nao inu.

LUKA 6:45
Munthu wabwino atulutsa zabwino m'chuma chokoma cha mtima wake; ndi munthu woipa atulutsa zoipa m'choipa chake: pakuti m'kamwa mwake mungolankhula mwa kuchuluka kwa mtima wake.

MATEYU 6:33
Koma muthange mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo zidzaonjezedwa kwa inu.

AFILIPI 4:19
Koma Mulungu wanga adzakwaniritsa chosowa chanu chilichonse monga mwa chuma chake m'ulemerero mwa Khristu Yesu.

MIYAMBO 3:5-10
[5] Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako;[6] umlemekeze m'njira zako zonse, ndipo Iye adzaongola mayendedwe ako.[7] Usadziyese wekha wanzeru; opa Yehova, nupatuke pazoipa;[8] mitsempha yako idzalandirapo moyo, ndi mafupa ako uwisi.[9] Lemekeza Yehova ndi chuma chako, ndi zinthu zako zonse zoyambirira kucha;[10] motero nkhokwe zako zidzangoti thee, mbiya zako zidzasefuka vinyo.

MASALIMO 23:5
Mundiyalikira gome pamaso panga m'kuona kwa adani anga; mwandidzoza mutu wanga mafuta; chikho changa chisefuka.

MASALIMO 36:8
Adzakhuta kwambiri ndi zonona za m'nyumba mwanu, ndipo mudzawamwetsa mu mtsinje wa zokondweretsa zanu.

MASALIMO 37:11
Koma ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nao mtendere wochuluka.

MASALIMO 65:11
Muveka chakachi ndi ukoma wanu; ndipo mabande anu akukha zakucha.

MASALIMO 72:16
M'dzikomo mudzakhala dzinthu dzochuluka pamwamba pa mapiri; zipatso zake zidzati waa, ngati za ku Lebanoni, ndipo iwo a m'mudzi adzaphuka ngati msipu wapansi.

AROMA 15:13
Ndipo Mulungu wa chiyembekezo adzaze inu ndi chimwemwe chonse ndi mtendere m'kukhulupirira, kuti mukachuluke ndi chiyembekezo, mu mphamvu ya Mzimu Woyera.

MASALIMO 66:8-12
[8] Lemekezani Mulungu wathu, mitundu ya anthu inu, ndipo mumveketse liu la chilemekezo chake.[9] Iye amene asunga moyo wathu tingafe, osalola phazi lathu literereke.[10] Pakuti munatiyesera, Mulungu, munatiyenga monga ayenga siliva.[11] Munapita nafe kuukonde; munatisenza chothodwetsa pamsana pathu.[12] Munapititsa anthu oberekeka pamwamba pamitu pathu; tinapyola moto ndi madzi; koma munatifikitsa potitsitsimutsa.

Chewa Bible 2014
Bible Society of Malawi