A A A A A

Zowonjezera: [Mowa]


1 PETRO 4:3
Pakuti nthawi yapitayi idatifikira kuchita chifuno cha amitundu, poyendayenda ife m'kukhumba zonyansa, zilakolako, maledzero, madyerero, maimwaimwa, ndi kupembedza mafano kosaloleka;

1 TIMOTEO 5:23
Usakhalenso wakumwa madzi okha, komatu uchite naye vinyo pang'ono, chifukwa cha mimba yako ndi zofooka zako zobwera kawirikawiri.

MLALIKI 9:7
Tiye, idya zakudya zako mokondwa, numwe vinyo wako mosekera mtima; pakuti Mulungu wavomerezeratu zochita zako.

AEFESO 5:18
Ndipo musaledzere naye vinyo, m'mene muli chitayiko; komatu mudzale naye Mzimu,

MIYAMBO 20:1
Vinyo achita chiphwete, chakumwa chaukali chisokosa; wosochera nazo alibe nzeru.

MIYAMBO 23:31
Usayang'ane pavinyo alikufiira, alikung'azimira m'chikho, namweka mosalala.

AROMA 13:13
Tiyendeyende koyenera, monga usana; si m'madyerero ndi kuledzera ai, si m'chigololo ndi chonyansa ai, si mu ndeu ndi nkhwidzi ai.

MIYAMBO 31:4-5
[4] Mafumu, Lemuwele, mafumu sayenera kumwa vinyo; akalonga sayenera kunena, Chakumwa chaukali chili kuti?[5] Kuti angamwe, naiwale malamulo, naweruze mokhota anthu onse osautsidwa.

MASALIMO 104:14-15
[14] Ameretsa msipu ziudye ng'ombe, ndi zitsamba achite nazo munthu; natulutse chakudya chochokera m'nthaka;[15] ndi vinyo wokondweretsa mtima wa munthu, ndi mafuta akunyezimiritsa nkhope yake, ndi mkate wakulimbitsa mtima wa munthu.

1 AKORINTO 10:23-24
[23] Zinthu zonse ziloleka; koma sizipindula zonse. Zinthu zonse ziloleka; koma sizimanga zonse.[24] Munthu asafune zake za iye yekha, koma za mnzake.

YESAYA 62:8-9
[8] Yehova analumbira pa dzanja lake lamanja, ndi mkono wake wamphamvu, Zoonadi, sindidzaperekanso tirigu wako akhale chakudya cha adani ako, ndipo alendo sadzamwa vinyo wako amene iwe unagwirira ntchito;[9] koma iwo amene adzakolola adzadya ndi kutamanda Yehova; ndi iwo amene adzamtchera adzamumwa m'mabwalo a Kachisi wanga.

AGALATIYA 5:19-21
[19] Ndipo ntchito za thupi zionekera, ndizo dama, chodetsa, kukhumba zonyansa,[20] kupembedza mafano, nyanga, madano, ndeu, kaduka, zopsa mtima, zotetana, magawano, mipatuko,[21] njiru, kuledzera, mchezo, ndi zina zotere; zimene ndikuchenjezani nazo, monga ndachita, kuti iwo akuchitachita zotere sadzalowa Ufumu wa Mulungu.

1 AKORINTO 9:19-23
[19] Pakuti pokhala ndinali mfulu kwa onse, ndinadzilowetsa ndekha ukapolo kwa onse, kuti ndipindule ochuluka.[20] Ndipo kwa Ayuda ndinakhala monga Myuda, kuti ndipindule Ayuda; kwa iwo omvera lamulo monga womvera lamulo, ngakhale sindinakhala ndekha womvera lamulo, kuti ndipindule iwo omvera malamulo;[21] kwa iwo opanda lamulo monga wopanda lamulo, wosati wakukhala ine wopanda lamulo kwa Mulungu, koma womvera lamulo kwa Khristu kuti ndipindule iwo opanda lamulo.[22] Kwa ofooka ndinakhala ngati wofooka, kuti ndipindule ofooka. Ndakhala zonse kwa anthu onse, kuti paliponse ndikapulumutse ena.[23] Koma ndichita zonse chifukwa cha Uthenga Wabwino, kuti ndikakhale woyanjana nao.

AROMA 14:15-21
[15] Koma ngati iwe wachititsa mbale wako chisoni ndi chakudya, pamenepo ulibe kuyendayendanso ndi chikondano. Usamuononga ndi chakudya chako, iye amene Khristu adamfera.[16] Chifukwa chake musalole chabwino chanu achisinjirire.[17] Pakuti ufumu wa Mulungu sukhala chakudya ndi chakumwa, koma chilungamo, ndi mtendere, ndi chimwemwe mwa Mzimu Woyera.[18] Pakuti iye amene atumikira Khristu mu izi akondweretsa Mulungu, navomerezeka ndi anthu.[19] Chifukwa chake tilondole zinthu za mtendere, ndi zinthu zakulimbikitsana wina ndi mnzake.[20] Usapasule ntchito ya Mulungu chifukwa cha chakudya. Zinthu zonse zili zoyera; koma kuli koipa kwa munthu amene akudya ndi kukhumudwa.[21] Kuli kwabwino kusadya nyama, kapena kusamwa vinyo, kapena kusachita chinthu chilichonse chakukhumudwitsa mbale wako.

YOHANE 2:3-11
[3] Ndipo pakutha vinyo, amake wa Yesu ananena naye, Alibe vinyo.[4] Yesu nanena naye, Mkazi, ndili ndi chiyani ndi inu? Nthawi yanga siinafike.[5] Amake ananena kwa atumiki, Chimene chilichonse akanena kwa inu, chitani.[6] Ndipo panali pamenepo mitsuko yamiyala isanu ndi umodzi yoikidwako monga mwa mayeretsedwe a Ayuda, yonse ya miyeso iwiri kapena itatu.[7] Yesu ananena nao, Dzazani mitsukoyo ndi madzi. Naidzaza, ndendende.[8] Ndipo ananena nao, Tungani tsopano, mupite nao kwa mkulu wa phwando. Ndipo anapita nao.[9] Koma pamene mkuluyo analawa madzi osanduka vinyowo, ndipo sanadziwe kumene anachokera (koma atumiki amene adatunga madzi anadziwa), mkuluyo anaitana mkwati,[10] nanena naye, Munthu aliyense amayamba kuika vinyo wokoma; ndipo anthu atamwatu, pamenepo wina wosakoma; koma iwe wasunga vinyo wokoma kufikira tsopano lino.[11] Chiyambi ichi cha zizindikiro zake Yesu anachita m'Kana wa m'Galileya naonetsera ulemerero wake; ndipo ophunzira ake anakhulupirira Iye.

Chewa Bible 2014
Bible Society of Malawi