A A A A A

Mulungu: [Dalitso]

LUKA 6:38
6 Patsani, ndipo kudzapatsidwa kwa inu; muyeso wabwino, wotsendereka, wokucumuka, wosefukira, anthu adzakupatsani m'manja mwanu. Pakuti 7 kudzayesedwa kwa inu ndi muyeso womwewo muyesa nao inu.

MATEYU 5:4
Odala ali acisoni; cifukwa adzasangalatsidwa.

AFILIPI 4:19
Koma Mulungu wanga adzakwaniritsa cosowa canu ciri conse monga mwa cuma cace m'ulemerero mwa Kristu Yesu.

MASALIMO 67:7
Mulungu adzatidalitsa; Ndipo malekezero onse a dziko lapansi adzamuopa Iye,

NUMERI 6:24-25
[24] Yehova akudalitse iwe, nakusunge;[25] Yehova awalitse nkhope yace pa iwe, nakucitire cisomo;

AFILIPI 4:6-7
[6] Musadere nkhawa konse; komatu m'zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi ciyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu.[7] Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana cidziwitso conse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Kristu Yesu.

YAKOBO 1:17
Mphatso iri yonse yabwino, ndi cininkho ciri conse cangwiro zicokera Kumwamba, zotsika kwa Atate wa mauniko, amene alibe cisanduliko, kapena mthunzi wa citembenukiro.

YEREMIYA 17:7-8
[7] Wodala munthu amene akhulupirira Yehova, amene cikhulupiriro cace ndi Yehova.[8] Ndipo adzakhala ngati mtengo wooka kuti madzi, wotambalitsa mizu yace pamtsinje, wosaopa pofika nyengo yadzuwa, koma tsamba lace likhala laliwisi; ndipo subvutika cakaca cirala, suleka kubala zipatso.

YESAYA 41:10
usaope, pakuti Ine ndiri pamodzi ndi iwe; usaopsyedwe, pakuti Ine ndine Mulungu wako; ndidzakulimbitsa; inde, ndidzakuthangata; inde, ndidzakucirikiza ndi dzanja langa lamanja la cilungamo.

YOHANE 1:16
Cifukwa mwa kudzala kwace tinalandira ife tonse, cisomo cosinthana ndi cisomo.

GENESIS 22:16-17
[16] nati, Pa Ine ndekha ndalumbira, ati Yehova, popeza wadta ici, sunandikaniza mwana wako, mwana wako wa yekha,[17] kudalitsa ndidzakudalitsa iwe, kucurukitsa ndidzacurukitsa mbeu zako monga nyenyezi za kumwamba, monga mcenga wa m'mphepete mwa nyanja; ndipo mbeu zako zidzagonjetsa cipata ca adani ao;

GENESIS 27:28-29
[28] Mlungu akupatse iwe mame a kumwamba, Ndi zonenepa za dziko lapansi, Ndi tirigu wambiri ndi vinyo;[29] Anthu akutumikire iwe, Mitundu ikuweramire iwe; Ucite ufumu pa abale ako, Ana a amako akuweramire iwe; Wotemberereka ali yense akutemberera iwe, Wodalitsika ali yense akudalitsa iwe.

MASALIMO 1:1-3
[1] WODALA munthuyo wosayenda mu uphungu wa oipa, Kapena wosaimirira m'njira ya ocimwa, Kapena wosakhala pansi pa bwalo la onyoza.[2] Komatu m'cilamulo ca Yehova muli cikondwerero cace; Ndipo m'cilamulo cace amalingima usana ndi usiku.[3] Ndiye akunga mtengo wooka pa mitsinje ya madzi; Wakupatsa cipatso cace pa nyengo yace, Tsamba lace lomwe losafota; Ndipo zonse azicita apindula nazo.

MASALIMO 23:1-4
[1] Yehova ndiye mbusa wanga; sindidzasowa.[2] Andigonetsa ku busa lamsipu: Anditsogolera ku madzi ndikha.[3] Atsitsimutsa moyo wanga; Anditsogolera m'mabande a cilungamo, cifukwa ca dzina lace.[4] Inde, ndingakhale ndiyenda m'cigwa ca mthunzi wa Imfa, Sindidzaopa coipa; pakuti Inu muli ndi ine: Cibonga canu ndi ndodo yanu, izi zindisangalatsa ine,

2 SAMUELE 22:3-4
[3] Mulungu wa thanthwe langa, Iye ndidzamkhulupirira; Cikopa canga, ndi nyanga ya cipulumutso canga, nsanja yanga yaitali, ndi populumukirapo panga; Mpulumutsi wanga, mundipulumutsa kuciwawa.[4] Ndidzaitanakwa Yehovaamene ayenera timtamande; Comweco ndidzapulumutsidwa kwa adani anga.

1 YOHANE 5:18
Tidziwa kuti yense wobadwa kucokera mwa Mulungu sacimwa, koma iye wobadwa kucokera mwa Mulungu adzisunga yekha, ndipo woipayo samkhudza.

MASALIMO 138:7
Ndingakhale ndiyenda pakati pa nsautso, mudzandipatsa moyo; Mudzatambasula dzanja lanu pa mkwiyo wa adani anu, Ndipo dzanja lanu lamanja lidzandipulumutsa.

2 AKORINTO 9:8
Ndipo Mulungu akhoza kucurukitsira cisomo conse kwa inu; kuti inu, pokhala naco cikwaniro conse m'zinthu zonse, nthawi zonse, mukacurukire ku nchito yonse yabwino;

AFILIPI 4:7
Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana cidziwitso conse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Kristu Yesu.

Chewa Bible (BL) 1992
Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society