A A A A A

Machimo: [Kuledzera]


1 AKORINTO 10:13-14
[13] Sicinakugwerani inu ciyeso koma ca umunthu; koma Mulungu ali wokhulupirika, amene sadzalola inu kuyesedwa koposa kumene mukhoza; koma pamodzi ndi ciyeso adzaikanso populumukirapo, kuti mudzakhoze kupirirako.[14] Cifukwa cace, okondedwa anga, thawani kupembedza mafano.

1 YOHANE 2:16
Pakuti ciri conse ca m'dziko lapansi, cilakolakoca thupi ndi cilakolako ca maso, matamandidwe a moyo, sizicokera kwa Atate, koma ku dziko lapansi.

1 AKORINTO 15:33
Musanyengedwe; 5 mayanjano oipa aipsa makhalidwe okoma

YAKOBO 4:7
Potero mverani Mulungu; koma kanizani mdierekezi, ndipo adzakuthawani inu.

1 AKORINTO 6:12
Zinthu zonse ziloledwa kwa ine; koma si zonse zipindula, Zinthu zonse ziloledwa kwa ine, koma sindidzalamulidwa naco cimodzi.

1 PETRO 5:10
Ndipo Mulungu wa cisomo conse, amene adakuitanani kulowa ulemerero wace wosatha mwa Kristu, mutamva zowawa kanthawi, adzafikitsa inu opanda cirema mwini wace, adzakhazikitsa, adzalimbikitsa inu.

MASALIMO 50:15
Ndipo undiitane tsiku la cisautso: Ndidzakulanditsa, ndipo iwe udzandilemekeza.

AROMA 5:3-5
[3] Ndipo si cotero cokha, komanso tikondwera m'zisautso; podziwa ife kuti cisautso cicita cipiriro; ndi cipiriro cicita cizolowezi;[4] ndi cizolowezi cicita ciyembekezo:[5] ndipo ciyembekezo sicicititsa manyazi; cifukwa cikondi ca Mulungu cinatsanulidwa m'mitima mwathu mwa Mzimu Woyera, amene wapatsidwa kwa ife.

1 AKORINTO 6:9-11
[9] Kapenasimudziwa kuti osalungama sadzalandira ufumu wa Mulungu? Musasoceretsedwe; adama, kapena opembedza mafano, kapena acigololo, kapena olobodoka ndi zoipa, kapena akudziipsa ndi amuna,[10] kapena ambala, kapena osirira, kapena oledzera, kapena olalatira, kapena olanda, sadzalowa Ufumu wa Mulungu.[11] Ndipo ena ainu munali otere; koma munasambitsidwa, koma munayeretsedwa, koma munayesedwa olungama, m'dzina la Ambuye Yesu Kristu, ndi mwa Mzimu wa Mulungu wathu.

TITO 2:12
ndi kutiphunzitsa ife kuti, pokana cisapembedzo ndi zilakolako za dziko lapansi, tikhale ndi moyo m'dziko lino odziletsa, ndi olungama, ndi opembedza;

YAKOBO 1:2-3
[2] Muciyese cimwemwe cokha, abale anga, m'mene mukugwa m'mayesero a mitundu mitundu;[3] pozindikira kuti ciyesedwe ca cikhulupiriro canu cicita cipiriro.

AHEBRI 4:15-16
[15] Pakuti sitiri naye mkulu wa ansembe wosatha kumva cifundo ndi zofoka zathu; koma wayesedwa m'zonse monga momwe ife, koma wopanda ucimo.[16] Potero tilimbike mtima poyandikira mpando wacifumu wacisomo, kuti tilandire cifundo ndi kupeza cisomo ca kutithandiza nthawi yakusowa.

YOHANE 3:16-17
[16] Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wace wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira iye asatayike, koma akhale nao moyo wosatha.[17] Pakuti Mulungu sanatuma Mwana wace ku dziko lapansi, kuti akaweruze dziko lapansi, koma kuti dziko lapansi likapulumutsidwe ndi iye.

AFILIPI 4:13
Ndikhoza zonse mwa iye wondipatsa mphamvuyo.

MASALIMO 95:8
Musaumitse mitima yanu, ngati ku Meriba, Ngati tsiku la ku Masa m'cipululu;

MATEYU 6:13
Ndipo musatitengere kokatiyesa, koma mutipulumutse kwa woipayo.

MATEYU 26:41
Cezerani ndi kupemphera, kuti mungalowe m'kuyesedwa: mzimutu uti wakufuna, koma thupi liri lolefuka.

Chewa Bible (BL) 1992
Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society