A A A A A

Machimo: [Kuchotsa mimba]


1 AKORINTO 1:27
koma 4 Mulungu anasankhula zopusa za dziko lapansi, kuti akacititse manyazi anzeru; ndipo zofoka za dziko lapansi Mulungu anazisankhula, kuti akacititse manyazi zamphamvu;

DEUTERONOMO 24:16
Atate asaphedwere ana, ndi ana asaphedwere atate; munthu yense aphedwere cimo lace lace.

DEUTERONOMO 30:19
Ndicititsa mboni lero kumwamba ndi dziko lapansi zitsutse inu; ndaika pamaso panu moyo ndi imfa, mdalitso ndi temberero; potero, sankhani moyo, kuti mukhale ndi moyo, inu ndi mbeu zanu;

AGALATIYA 1:15
Koma pamene padakondweretsa Mulungu, amene anandipatula, ndisanabadwe, nandiitana ine mwa cisomo cace,

YESAYA 43:25
Ine, Inedi, ndine amene ndifafaniza zolakwa zako, cifukwa ca Ine mwini; ndipo Ine sindidzakumbukira macimo ako.

YESAYA 44:24
Atero Yehova, Mombolo wako, ndi Iye amene anakuumba iwe m'mimba, Ine ndine Yehova, amene ndipanga zinthu zonse, ndi kufunyulula ndekha zakumwamba, ndi kuyala dziko lopansi; ndani ali ndi Ine?

AEFESO 1:7
Tiri ndi maomboledwe mwa mwazi wace, cikhululukiro ca zocimwa, monga mwa kulemera kwa cisomo cace,

EKSODO 4:11
Koma Yehova ananena naye, Anampangira munthu m'kamwa ndani? Kapena analenga munthu wosalankhula ndani, kapena wogontha, kapena wamaso, kapena wakhungu? Si ndine Yehova kodi?

YESAYA 64:8
Koma tsopano, Yehova, Inu ndinu Atate wathu; ife tiri dongo, ndipo Inu ndinu Muumbi wathu; ndipo ife tonse tiri nchito ya dzanja lanu.

YEREMIYA 1:5
Ndisanakulenge iwe m'mimba ndinakudziwa, ndipo usanabadwe ndinakupatula iwe; ndinakuika kuti ukhale mneneri wa mitundu ya anthu.

MASALIMO 100:3
Dziwani kuti Yehova ndiye Mulungu; Iyeyu anatilenga, ndipo ife ndife ace; Ndife anthu ace ndi nkhosa za pabusa pace.

MASALIMO 127:3
Taonani ana ndiwo colandira ca kwa Yehova; Cipatso ca m'mimba ndico mphotho yace.

LUKA 2:6-7
[6] Ndipo panali pokhaia iwo komweko, masiku ace a kubala anakwanira.[7] Ndipo iye anabala mwana wace wamwamuna woyamba; namkulunga iye m'nsaru, namgoneka modyera ng'ombe, cifukwa kuti anasowa malo m'nyumba ya alendo.

AEFESO 1:3-4
[3] Wolemekezeka Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Kristu, amene anatidalitsa ife ndi dalitso lonse la mzimu m'zakumwamba mwa Kristu;[4] monga anatisankha ife mwa iye, lisanakhazikike dziko lapansi, tikhale ife oyera mtima, ndi opanda cirema pamaso pace m'cikondi,

1 AKORINTO 6:19-20
[19] Kapena simudziwa kuti thupi lanu liri kacisi wa Mzimu Woyera, amene ali mwa inu, amene muli naye kwa Mulungu? Ndipo simukhala a inu nokha.[20] Pakuti munagulidwa ndi mtengo wace wapatali; cifukwa cace lemekezani Mulungu m'thupi lanu.

YESAYA 45:9-11
[9] Tsoka kwa iye amene akangana ndi Mlengi wace! phale mwa mapale a dziko lapansi! Kodi dongo linganene kwa iye amene aliumba, Kodi upanga ciani? pena nchito yako, Iye alibe manja?[10] Tsoka kwa iye amene ati kwa atate wace, Kodi iwe ubalanji? pena kwa mkazi, Ulikusauka ninji iwe?[11] Atero Yehova Woyera wa Israyeli ndi Mlengi wace, Ndifunse Ine za zinthu zimene zirinkudza; za ana anga amuna, ndi za nchito ya manja anga, ndilamulireni Ine.

EKSODO 21:22-25
[22] Akayambana amuna, nakakantha mkazi ali ndi pakati, kotero kuti abala, koma alibe kuphwetekwa; alipe ndithu, monga momwe amchulira mwamuna wa mkaziyo; apereke monga anena oweruza.[23] Koma ngati kuphweteka kukalipo, uzipereka moyo kulipa moyo,[24] diso kulipa diso, dzino kulipa dzino, dzanja kulipa dzanja, phazi kulipa phazi,[25] kutentha kulipa kutentha, bala kulipa bala, mkwapulo kulipa mkwapulo.

MASALIMO 139:13-16
[13] Pakuti Inu munalenga imso zanga; Munandiumba ndisanabadwe ine.[14] Ndikuyamikani cifukwa kuti cipangidwe canga ncoopsa ndi codabwiza; Nchito zanu nzodabwiza; Moyo wanga ucidziwa ici bwino ndithu.[15] Thupi langa silinabisikira Inu popangidwa ine mobisika, Poombedwa ine monga m'munsi mwace mwa dziko lapansi.[16] Ndisanaumbidwe ine maso anu anandipenya, Ziwalo zanga zonse zinalembedwa m'buku mwanu, Masiku akuti ziumbidwe, Pakalibe cimodzi ca izo.

LUKA 1:41-44
[41] Ndipo panali pamene Elisabeti anamva kulankhula kwace kwa Mariya, mwana wosabadwayo anatsalima m'mimba mwace; ndipo Elisabeti anadzazidwa ndi Mzimu Woyera;[42] nakweza mau ndi mpfuu waukuru, nati, 2 Wodalitsika iwe mwa akazi, ndipo codalitsika cipatso ca mimba yako,[43] Ndipo ici cicokera kuti kudza kwa ine, kuti adze kwa ine amace wa Ambuye wanga?[44] Pakuti ona, pamene mau a kulankhula kwako analowa m'makutu anga, mwana anatsalima ndi msangalalo m'mimba mwanga.

EKSODO 20:1-13
[1] Ndipo Mulungu ananena mau onse amenewa, nati:[2] INE ndine YEHOVA Mulungu wako, amene ndinaturutsa iwe ku dziko la Aigupto, ku nyumba ya akapolo.[3] Usakhale nayo milungu yina koma Ine ndekha.[4] Usadzipangire iwe wekha fano losema, kapena cifaniziro ciri conse ca zinthu za m'thambo la kumwamba, kapena za m'dziko lapansi, kapena za m'madzi a pansi pa dziko;[5] usazipembedzere izo, usazitumikire izo; cifukwa Ine Yehova Mulungu wako ndiri Mulungu wansanje, wakulanga ana cifukwa ca atate ao, kufikira mbadwo wacitatu ndi wacinai wa iwo amene akudana ndi Ine;[6] ndi kuwacitira cifundo anthu zikwizikwi a iwo amene akondana ndi Ine, nasunga malamulo anga.[7] Usaehule dzina la Yehova Mulungu wako pacabe; cifukwa Yehova sadzamuyesa iye wosacimwa, amene achula pacabe dzina lacelo.[8] Uzikumbukila tsiku la Sabata, likhale lopatulika.[9] Masiku asanu ndi limodzi uzigwira, ndi kumariza nchito zako zonse;[10] koma tsiku lacisanu ndi ciwiri ndilo Sabata la Yehova Mulungu wako; usagwire nchito iri yonse, kapena iwe wekha, kapena mwana wako wamwamuna, kapena mwana wako wamkazi, kapena wanchito wako wamwamuna, kapena wanchito wako wamkazi, kapena nyama zako, kapena mlendo amene ali m'mudzi mwako;[11] cifukwa masiku asanu ndi limodzi Yehova adamariza zakumwamba ndi zapansi, ndi nyanja, ndi zinthu zonse ziri m'menemo, napumula tsiku ladsanu ndi ciwiri; cifukwa cace Yehova anadalitsa tsiku la Sabata kuti likhale lopatulika.[12] Uzilemekeza atate wako ndi amako; kuti acuruke masiku ako m'dziko limene Yehova Mulungu wako akupatsa iwe.[13] Usaphe.

Chewa Bible (BL) 1992
Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society