A A A A A

Zinsinsi: [Chinjoka]


EZEKIELE 29:3
nena, uziti, Atero Ambuye Yehova, Taona nditsutsana nawe, Farao mfumu ya Aigupto, ng'ona yaikuru yakugona m'kati mwa mitsinje yace, imene ikuti, Mtsinje wanga ndi wangatu, ndadzipangira ndekha uwu.

EZEKIELE 32:2
Wobadwa ndi munthu iwe, takwezera Farao mfumu ya Aigupto nyimbo yamaliro; uziti naye, Unafanana nao msona wa mkango wa amitundu, unanga ng'ona ya m'nyanja, unabuka m'mitsinje mwako, nubvundulira madzi ndi mapazi ako, ndi kudetsa mitsinje yao.

YESAYA 27:1
Tsiku limenelo Yehova ndi lupanga lace lolimba ndi lalikuru ndi lamphamvu adzalanga nangumi njoka yotamanga, ndi nangumi njoka yopindika-pindika; nadzapha cing'ona cimene ciri m'nyanja.

YESAYA 51:9
Galamuka, galamuka, khala ndi mphamvu, mkono wa Yehova; galamuka monga masiku akale, mibadwo ya nthawi zakale. Kodi si ndiwe amene unadula Rahabu zipinjiri zipinjiri, amene unapyoza cinjoka cija?

YOBU 7:12
Ndine nyanja kodi, kapena cinjoka ca m'nyanja, Kuti Inu mundiikira odikira?

YOBU 41:18-21
[18] Pakuyetsemula ing'anipitsa kuunika, Ndi maso ace akunga zikope za m'mawa.[19] M'kamwa mwace muturuka miuni, Mbaliwali za moto zibukamo.[20] M'mphuno mwace muturuka utsi, Ngati nkhali yobwadamuka ndi moto wa zinyatsi.[21] Mpweya wace uyatsa makara, Ndi m'kamwa mwace muturuka lawi la moto.

MASALIMO 18:8
Unakwera utsi woturuka m'mphuno mwace: Ndi moto wa m'kamwa mwace unanyeka: Nuyakitsa makara.

MASALIMO 44:19
Mungakhale munatityola mokhala zirombo, Ndi kutiphimba nao mthunzi wa imfa.

MASALIMO 74:13
Mudagawa nyanja ndi mphamvu yanu; Mudaswa mitu ya zoopsa za m'madzi.

CHIVUMBULUTSO 1:7
Taonani, adza ndi mitambo; ndipo diso liri lonse lidzampenya iye, iwonso amene anampyoza; ndipo mafuko onse a pa dziko adzamlira iye. Terotu. Amen.

CHIVUMBULUTSO 11:7
Ndipo pamene zidatsiriza umboni wao cirombo eokwera kuturuka m'phompho cidzacita nazo nkhondo, nicidzazilaka, nicidzazipha izo.

DEUTERONOMO 32:33
Vinyo wao ndiwo ululu wa zinjoka, Ndi ululu waukali wa mphiri.

CHIVUMBULUTSO 13:8
Ndipo adzacilambira onse akukhala padziko, amene dzina lao silinalembedwa m'buku la moyo la Mwanawankhosa, wophedwa kuyambira makhazikidwe a dziko lapansi,

CHIVUMBULUTSO 16:13
Ndipo ndinaona moturuka m'kamwa mwa cinjoka, ndi m'kamwa mwa cirombo, ndi m'kamwa mwa mneneri wonyenga mizimu itatu yonyansa, ngati acule;

EKSODO 7:10-12
[10] Ndipo Mose ndi Aroni analowa kwa Farao, nacita monga momwe Yehova adawalamulira; ndipo Aroni anaponya pansi ndodo yace pamaso pa Farao, ndi pamaso pa anyamata ace, ndipo inasanduka cinjoka,[11] Pamenepo Farao anaitananso anzeru, ndi amatsenga; ndipo alembi a Aigupto, iwonso anacita momwemo ndi matsenga ao.[12] Pakuti yense anaponya pansi ndodo yace, ndipo zinasanduka zinjoka; koma ndodoya Aroni inameza ndodo zao,

YOBU 40:15-20
[15] Tapenya tsono mvuu ndinaipanga pamodzi ndi iwe, Ikudya udzu ngati ng'ombe.[16] Tapenya tsono, mphamvu yace iri m'cuuno mwace, Ndi kulimbalimba kwace kuli m'mitsempha ya m'mimba yace.[17] Igwedeza mcira wace ngati mkungudza; Mitsempha ya ncafu zace ipotana.[18] Mafupa ace akunga misiwe yamkuwa; Ziwalo zace zikunga zitsulo zamphumphu,[19] Iyo ndiyo ciyambi ca macitidwe a Mulungu; Wakuilenga anaininkha lupanga lace.[20] Pakuti mapiri aiphukitsira cakudya, Kumene zisewera nyama zonse za kuthengo,

CHIVUMBULUTSO 12:1-17
[1] Ndipo cizindikilo cacikuru cinaoneka m'mwamba; mkazi wobvekedwa dzuwa, ndi mwezi ku mapazi ace, ndi pamutu pace korona wa nyenyezi khumi ndi ziwiri;[2] ndipo anali ndi pakati; ndipo apfuula alimkubala, ndi kumva zowawa zakubala.[3] Ndipo cinaoneka cizindikilo cina m'mwamba, taonani, cinjoka cofiira, cacikuru, cakukhala nayo mitu isanu ndi iwiri, ndi nyanga khumi, ndi pamutu pace nduwira zacifumu zisanu ndi ziwiri.[4] Ndipo mcira wace uguza limodzi la magawo atatu a nyenyezi zam'mwamba, nuziponya padziko. Ndipo cinjoka cinaimirira pamaso pa mkazi akuti abale, kuti, akabala, ico cikalikwire mwana wace.[5] Ndipo anabala mwana wamwamuna, amene adzaweruza mitundu yonse ndi ndodo yacitsulo: ndipo anakwatulidwa mwana wace amuke kwa Mulungu, ndi ku mpando wacifumu wace.[6] Ndipo mkazi anathawira kucipululu, kumene ali nayo mbuto yokonzekeratu ndi Mulungu, kuti kumeneko akamdyetse masiku cikwi cimodzi ndi mazana awiri mphambu makumi asanu ndi limodzi.[7] Ndipo munali nkhondo m'mwamba. Mikayeli ndi angelo ace akucita nkhondo ndi cinjoka; cinjokanso ndi angelo ace cinacita nkhondo;[8] ndipo sicinalakika, ndipo sanapezekanso malo ao m'mwamba.[9] Ndipo cinaponyedwa pansi cinjoka cacikuru, njoka yokalambayo, iye wochedwa mdierekezi ndi Satana, wonyenga wa dziko lonse; cinaponyedwa pansi kudziko, ndi angelo ace anaponyedwa naye pamodzi.[10] Ndipo ndinamva mau akuru m'Mwamba, nanena, Tsopano zafika cipulumutso, ndi mphamvu, ndi ufumu za Mulungu wathu, ndi ulamuliro wa Kristu wace; pakuti wagwetsedwa wonenera wa abale athu, wakuwanenera pamaso pa Mulungu wathu usana ndi usiku.[11] Ndipo iwo anamlaka iye cifukwa ca mwazi wa Mwanawankhosa, ndi cifukwa ca mau a umboni wao; ndipo sanakonda moyo wao kungakhale kufikira imfa.[12] Cifukwa cace, kondwerani, miyamba inu, ndi inu akukhala momwemo. Tsoka mtunda ndi nyanja, cifukwa mdierekezi watsikira kwa inu, wokhala nao udani waukuru, podziwa kuti kamtsalira kanthawi.[13] Ndipo pamene cinjoka cinaonakuticinaponyedwa pansikudziko, cinazunza mkazi amene adabala mwana wamwamuna.[14] Ndipo anapatsa mkazi mapiko awiri a ciombankhanga cacikuru, kuti akaulukire kucipululu, ku mbuto yace, kumene adyetsedwako nthawi, ndi zinthawi, ndi nusu la nthawi, osapenya nkhope ya njoka.[15] Ndipo inalabvulira m'kamwa mwace, potsata mkazi, madzi ngati mtsinje, kuti akakokoleredwe mkazi nao.[16] Ndipo dziko linathandiza mkaziyo, ndi dziko linatsegula m'kamwa mwace, nilinameza madzi a mtsinje amene cinjoka cinalabvula m'kamwamwace.[17] Ndipo cinjoka cinakwiya ndi mkazi, nicinacoka kunka kucita nkhondondi otsala ambeu yace, amene asunga malamulo a Mulungu, nakhala nao umboni wa Yesu.

CHIVUMBULUTSO 13:1-18
[1] Ndipo ndinaimirira pa mcenga wa nyanja. Ndipo ndinaona cirombo cirinkuturuka m'nyanja, cakukhala nazo nyanga khumi, ndi mitu isanu ow iwiri, ndi pa nyanga zace nduwira zacifumu khumi, ndi pamitu pace maina a mwano.[2] Ndipo cirombo ndinacionaco cinafanana ndi nyalugwe, ndi mapazi ace ngati mapazi a fisi, ndi pakamwa pace ngati pakamwa pa mkango; ndipo cinjoka cinampatsa iye mphamvu yace, ndi mpando wacifumu wace, ndi ulamuliro waukuru.[3] Ndipo umodzi wa mitu yace unakhala ngati unalasidwa kufikira imfa; ndipo bala lace la kuimfa lidapola; ndipo dziko lonse linazizwa potsata ciromboco;[4] ndipo analambira cinjoka, cifukwa cinacipatsa ulamuliro ciromboco; ndipo analambira cirombo ndi kunena, Manana ndi cirombo ndani? Ndipo akhoza ndani kugwira nkhondo naco?[5] Ndipo anacipatsa ico m'kamwa molankhula zazikuru ndi zamwano; ndipo anacipatsa ulamuliro wa kutero miyezi makumi anai ndi iwiri.[6] Ndipo cinatsegula pakamwa pace kukanena zamwano pa Mulungu, kucitira mwano dzina lace, ndi cihema cace, ndi iwo akukhala m'Mwamba.[7] Ndipo anacipatsa ico kucita nkhondo ndi oyera mtima, ndi kuwalaka; ndipo anacipatsa ulamuliro wa pa pfuko liri lonse, ndi anthu, ndi manenedwe, ndi mitundu.[8] Ndipo adzacilambira onse akukhala padziko, amene dzina lao silinalembedwa m'buku la moyo la Mwanawankhosa, wophedwa kuyambira makhazikidwe a dziko lapansi,[9] N gati wina ali nalo khutu, amve.[10] N gati munthu alinga kundende, kundende adzamuka munthu akapha ndi lupanga, ayenera iyekuphedwa nalo lupanga, Pano pali cipiriro ndi cikhulupiriro ca oyera mtima.[11] Ndipo ndinaona cirombo cina cirikuturuka pansi; ndipo cinali nazo nyanga ziwiri ngati za mwana wa nkhosa, ndipo cinalankhula ngati cinjoka.[12] Ndipo cicita ulamuliro wonse wa cirombo coyamba pamaso pace. Ndipo cilambiritsa dziko ndi iwo akukhala momwemo cirombo coyamba, cimene bala lace la kuimfa lidapola.[13] Ndipo cicita zizindikilo zazikuru, kutinso citsitse moto ucokere m'mwamba nugwe padziko, pamaso pa anthu.[14] Ndipo cisokeretsa iwo akukhala padziko ndi zizindikilo zimene anacipatsa mphamvu yakuzicita pamaso pa cirombo, ndi kunena kwa iwo akukhala padziko, kuti apange fane la ciromboco, cimene cinali nalo bala la lupanga nicinakhalanso ndi moyo.[15] Ndipo anacipatsa mphamvu yakupatsa fano la cirombo mpweya, kutinso fane la cirombo Iilankhule, nilicite kuti onse osalilambira fane la cirombo aphedwe.[16] Ndipo cicita kuti onse, ang'ono ndi akuru, acuma ndi osauka, ndi mfulu ndi akapolo, alandire cilembo pa dzanja lao ndi pamphumi pao;[17] ndi kuti munthu sangakhoze kugula kapena kugulitsa, koma iye yekha wakukhala naco cilembo, ndilo dzina la cirombo, kapena ciwerengero ca dzina lace.[18] Pano pali nzeru. Iye wakukhala naco cidziwitso awerenge ciwerengero ca ciromboco; pakuti ciwerengero cace ndi ca munthu; ndipo ciwerengero cace ndico mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu ndi limodzi kudza zisanu ndi cimodzi.

CHIVUMBULUTSO 20:1-15
[1] Ndipo ndinaona mngelo anatsika Kumwamba, nakhala naco cifungulo ca phompho, ndi unyolo waukuru m'dzanja lace.[2] Ndipo anagwira cinjoka, njoka yakaleyo, ndiye mdierekezi ndi Satana, nammanga iye zaka cikwi,[3] namponya kuphompho, natsekapo, nasindikizapo cizindikilo pamwamba pace, kuti asanyengenso amitundu kufikira kudzatha zaka cikwi; patsogolo pace ayenera kumasulidwa iye kanthawi.[4] Ndipo ndinaona mipando yacifumu, ndipo anakhala pamenepo; ndipo anawapatsa ciweruziro; ndipo ndinaona mizimu ya iwo amene adawadula khosi cifukwa ca umboni wa Yesu, ndi cifukwa ca mau a Mulungu, ndi iwo amene sanalambira cirombo, kapena fano lace, nisanalandira lembalo pamphumi ndi pa dzanja lao; ndipo anakhala ndi moyo, nacita ufumu pamodzi ndi Kristu zaka cikwi.[5] Otsala a akufa sanakhalanso ndi moyo kufikira kudzatha zaka cikwi. Ndiko kuuka kwa akufa koyamba.[6] Wodala ndi woyera mtima ali iye amene acita nao pa kuuka koyamba; pa iwowa imfa yaciwiri iribe ulamuliro; komatu adzakhala ansembe a Mulungu ndi a Kristu, nadzacita ufumu pamodzi ndi iye zaka cikwizo.[7] Ndipo pamene zidzatha zaka cikwi, adzamasulidwa Satana m'ndende yace;[8] nadzaturuka kudzasokeretsa amitundu ali mu ngondya zinai za dziko, Gogo, ndi Magogo, kudzawasonkhanitsa acite nkhondo: ciwerengero cao ca iwo amene cikhala ngati mcenga wa kunyanja.[9] Ndipo anakwera nafalikira m'dziko, nazinga tsasa la oyera mtima ndi mudzi wokondedwawo: ndipo unatsika mota wakumwamba nuwanyeketsa.[10] Ndipo mdierekezi wakuwasokeretsa anaponyedwa m'nyanja ya mota ndi sulfure, kumeneko kulinso ciromboco ndi mneneri wonyengayo; ndipo adzazunzidwa usana ndi usiku ku nthawi za nthawi.[11] Ndipo ndinaona, mpando wacifumu waukuru woyera, ndi iye wakukhalapo, amene dziko ndi m'mwamba zinathawa pamaso pace, ndipo sanapezedwamalo ao.[12] Ndipo ndinaona akufa, akuru ndi ang'ono alinkuima ku mpando wacifumu; ndipo mabuku anatsegulidwa; ndipo buku lina Iinatsegulidwa, ndilo la moyo; ndipo akufa anaweruzidwa mwa zolembedwa m'mabuku, monga mwa nchito zao.[13] Ndipo nyanja inapereka akufawo anali momwemo, ndipo imfa ndi Hade zinapereka akufawo anali m'menemo; ndipo anaweruzidwa yense monga mwa nchito zace,[14] Ndipo imfa ndi Hade zinaponyedwa m'nyanja yamoto. Iyo ndiyo imfa yaciwiri, ndiyo nyanja yamoto.[15] Ndipo ngati munthu sanapezedwa wolembedwa m'buku la moyo, anaponyedwa m'nyanja yamoto.

Chewa Bible (BL) 1992
Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society