MLALIKI 6:10 |
Comwe cinalipo cachedwa dzina lace kale, cidziwika kuti ndiye munthu; sakhoza kulimbana ndi womposa mphamvu. |
|
HABAKUKU 2:3 |
Pakuti masomphenyawo alindira nyengo yoikidwiratu, ndipo afulumirira potsirizira pace, osanama; akacedwa uwalindirire; popeza afika ndithu, osazengereza. |
|
YESAYA 46:10 |
ndilalikira za cimariziro kuyambira paciyambi, ndi kuyambira nthawi zakale ndinena zinthu zimene zisanacitidwe; ndi kunena, Uphungu wanga udzakhala, ndipo ndidzacita zofuna zanga zonse; |
|
YESAYA 55:11 |
momwemo adzakhala mau anga amene aturuka m'kamwa mwanga, sadzabwerera kwa Ine cabe, koma adzacita cimene ndifuna, ndipo adzakula m'mene ndinawatumizira. |
|
YEREMIYA 1:5 |
Ndisanakulenge iwe m'mimba ndinakudziwa, ndipo usanabadwe ndinakupatula iwe; ndinakuika kuti ukhale mneneri wa mitundu ya anthu. |
|
YEREMIYA 17:10 |
Ine Yehova ndisanthula mtima, ndiyesa imso, kuti ndimpatse munthu yense monga mwa njira zace, monga zipatso za nchito zace. |
|
YOHANE 16:33 |
Zinthu izi ndalankhula ndi inu, kuti mwa Ine mukakhale nao mtendere. M'dziko lapansi mudzakhala naco cibvuto, koma limbikani mtima; ndalilaka dziko lapansi Ine. |
|
NUMERI 23:19 |
Mulungu sindiye munthu, kuti aname; Kapena mwana wa munthu, kuti aleke; Kodi anena, osacita? |
|
MIYAMBO 16:3 |
Pereka zocita zako kwa Yehova, Ndipo zolingalira zako zidzakhazikika. |
|
MIYAMBO 19:20-24 |
[20] Tamvera uphungu, nulandire mwambo, Kuti ukhale wanzeru pa cimariziro cako,[21] Muli zolingalira zambiri m'mtima mwa munthu; Koma uphungu wa Yehova ndiwo udzaimika.[22] Cotikondetsa munthu ndico kukoma mtima kwace; Ndipo wosauka apambana munthu wonama.[23] Kuopa Yehova kupatsa moyo; Wokhala nako adzakhala wokhuta; Zoipa sizidzamgwera.[24] Wolesi alonga dzanja lace m'mbale, Osalibwezanso kukamwa kwace. |
|
MASALIMO 37:37 |
Tapenya wangwiro, ndipo taona woongoka mtima! Pakuti ku matsiriziro ace a munthuyo kuti mtendere. |
|
MASALIMO 138:8 |
Yehova adzanditsirizira za kwa ine: Cifundo canu, Yehova, cifikira ku nthawi zonse: Musasiye nchito za manja anu. |
|
CHIVUMBULUTSO 20:12 |
Ndipo ndinaona akufa, akuru ndi ang'ono alinkuima ku mpando wacifumu; ndipo mabuku anatsegulidwa; ndipo buku lina Iinatsegulidwa, ndilo la moyo; ndipo akufa anaweruzidwa mwa zolembedwa m'mabuku, monga mwa nchito zao. |
|
AROMA 12:2 |
Ndipo musafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano: koma mukhale osandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wanu, kuti mukazindikire cimene ciri cifuno ca Mulungu, cabwino, ndi cokondweretsa, ndi cangwiro. |
|
AROMA 8:28-29 |
[28] Ndipo tidziwa kuti amene akonda Mulungu zinthu zonse zithandizana kuwacitira ubwino, ndiwo amene aitanidwa monga mwa kutsimikiza kwa mtima wace.[29] Cifukwa kuti iwo 1 amene iye anawadziwiratu, 2 iwowa anawalamuliratu 3 afanizidwe ndi cifaniziro ca Mwana wace, kuti 4 iye akakhale mwana woyamba wa abale ambiri; |
|
AEFESO 2:8-9 |
[8] Pakuti muli opulumutsidwa ndi cisomo cakucita mwa cikhulupiriro, ndipo ici cosacokera kwa inu: ciri mphatso ya Mulungu;[9] cosacokera kunchito, kuti asadzitamandire munthu ali yense. |
|
1 PETRO 2:8-9 |
[8] ndipo, Mwala wakukhumudwa nao, ndi thanthwe lopunthwitsa; kwa iwo akukhumudwa ndi mau, pokhala osamvera, kumenekonso adaikidwako.[9] Koma inu ndinu mbadwa yosankhika, ansembe acifumu, mtundu woyera mtima, anthu a mw ni wace, kotero kuti mukalakire zoposazo za iye amene anakuitanani muturuke mumdima, mulowe kuunika kwace kodabwitsa; |
|
1 AKORINTO 2:7-9 |
[7] koma tilankhula nzeru ya Mulungu m'cinsinsi, yobisikayo, imene Mulungu anaikiratu, pasanakhale nyengo za pansi pano, ku ulemerero wathu,[8] imene saidziwa mmodzi wa akulu a nthawi a pansi pano; pakuti akadadziw sakadapaeika Mbuye wa ulemerero[9] koma monga kulembedwa, Zimene diso silinaziona, ndi khutu silinazimva, Nisizinalowa mu mtima wa munthu, Zimene ziri zonse Mulungi anakonzereratu iwo aku mkonda iye. |
|
YEREMIYA 29:11-14 |
[11] Pakuti ndidziwa malingiriro amene ndilingiririra inu, ati Yehova, malingiriro a mtendere, si a coipa, akukupatsani inu adzukulu ndi ciyembekezero.[12] Pamenepo mudzandiitana Ine, ndipo mudzanka ndi kupemphera kwa Ine, ndipo ndidzakumverani inu.[13] Ndipo mudzandifuna Ine, ndi kundipeza, pamene mundifuna ndi mtima wanu wonse.[14] Ndipo ndidzapezedwa ndi inu, ati Yehova, ndidzabwezanso undende wanu, ndipo ndidzasonkhanitsa inu kwa mitundu yonse, ndi kumalo konse kumene ndinakupitikitsirani inu, ati Yehova; ndipo ndidzakubwezeraninso kumalo kumene ndinakutengani inu andende. |
|
Chewa Bible (BL) 1992 |
Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society |