A A A A A

Zizindikiro za Masamu: [Nambala 8]


CHIVUMBULUTSO 13:18
Pano pali nzeru. Iye wakukhala naco cidziwitso awerenge ciwerengero ca ciromboco; pakuti ciwerengero cace ndi ca munthu; ndipo ciwerengero cace ndico mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu ndi limodzi kudza zisanu ndi cimodzi.

DEUTERONOMO 6:4
Imvani, Israyeli; Yehova Mulungu wathu, Yehova ndiye mmodzi;

LEVITIKO 20:13
Munthu akagonana ndi mwamuna mnzace, monga amagonana ndi mkazi, acita conyansa onse awiri; awaphe ndithu; mwazi wao ukhale pamtu pao.

1 AKORINTO 6:9-11
[9] Kapenasimudziwa kuti osalungama sadzalandira ufumu wa Mulungu? Musasoceretsedwe; adama, kapena opembedza mafano, kapena acigololo, kapena olobodoka ndi zoipa, kapena akudziipsa ndi amuna,[10] kapena ambala, kapena osirira, kapena oledzera, kapena olalatira, kapena olanda, sadzalowa Ufumu wa Mulungu.[11] Ndipo ena ainu munali otere; koma munasambitsidwa, koma munayeretsedwa, koma munayesedwa olungama, m'dzina la Ambuye Yesu Kristu, ndi mwa Mzimu wa Mulungu wathu.

CHIVUMBULUTSO 11:2-3
[2] Ndipo bwalo la kunja kwa Kacisi ulisiye padera, osaliyesa; pakuti adapatsa ilo kwa amitundu; ndipo mzinda wopatulika adzaupondereza miyezi makumi anai mphambu iwiri.[3] Ndipo ndidzalamulira mboni zanga ziwiri, ndipo zidzanenera masiku cikwi cimodzi ndi mazana awiri mphambu makumi asanu ndi limodzi, zobvala ciguduli.

LEVITIKO 20:27
Munthu wamwamuna kapena wamkazi wakubwebweta, kapena wanyanga, azimupha ndithu; aziwaponya miyala; mwazi wao ukhale pamtu pao.

DEUTERONOMO 18:10-12
[10] Asapezeke mwa inu munthu wakupitiriza mwana wace wamwamuna kapena mwana wace wamkazi ku mota wa ula, wosamalira mitambo, kapena wosamalira kulira kwa mbalame, kapena wanyanga.[11] Kapena wotsirika, kapena wobwebweta, kapena wopenduza, kapena wofunsira akufa.[12] Popeza ali yense wakucita izi Yehova anyansidwa naye; ndipo cifukwa ca zonyansa izi Yehova Mulungu wanu awapitikitsa pamaso panu.

2 MAFUMU 21:6
Napititsa mwana wace pamoto, naombeza maula, nacita zanyanga, naika obwebweta ndi openda; anacita zoipa zambiri pamaso pa Yehova kuutsa mkwiyo wace.

MIKA 5:12
ndipo ndidzaononga zanyanga za m'dzanja lako; ndipo sudzakhalanso nao alosi;

YESAYA 47:12
Taima tsopano ndi maphendo ako, ndi unyinji wa matsenga ako, m'menemo iwe unagwira nchito ciyambire ubwana wako; kuti kapena udzatha kupindula, kuti kapena udzapambana.

MACHITIDWE A ATUMWI 8:11-24
[11] Ndipo anamsamalira iye, popeza nthawi yaikuru adawadabwitsa iwo ndi matsenga ace.[12] Koma pamene anakhulupirira Filipo wakulalikira Uthenga Wabwinowa Ufumu wa Mulungu ndi dzina la Yesu Kristu, anabatizidwa, amuna ndi akazi.[13] Ndipo Simoni mwini wace anakhulupiranso: ndipo m'mene anabatizidwa, anakhalira ndi Filipo; ndipo pakuona zizindikilo ndi mphamvu zazikuru zirikucitika, anadabwa.[14] Koma pamene atumwi a ku Yerusalemu anamva kuti Samariya adalandira mau a Mulungu, anawatumizira Petro ndi Yohane;[15] amenewo, m'mene adatsikirako, anawapempherera, kuti alandire Mzimu Woyera:[16] pakuti kufikira pamenepo nkuti asanagwe pa wina mmodzi wa iwo; koma anangobatizidwam'dzina la Ambuye Yesu.[17] Pamenepo anaika manja pa iwo, ndipo analandira Mzimu Woyera.[18] Koma pakuona Simoni kuti mwa kuika manja a atumwi anapatsidwa Mzimu Woyera, anawatengera ndalama,[19] nanena, Ndipatseni inenso ulamuliro umene, kuti amene ali yense ndikaika manja pa iye, alandire Mzimu Woyera.[20] Koma Petro anati kwa iye, Ndalama yako itayike nawe, cifukwa unalingirira kulandira mphatso ya Mulungu ndi ndalama.[21] Ulibe gawo kapena colandira ndi mau awa; pakuti mtima wako suli wolunjika pamaso pa Mulungu.[22] Cifukwa: cace lapa coipa calm ici, pemphera Ambuye, kuti kapena akukhululukire iwe colingiriraca mtima wako.[23] Pakuti ndiona kuti wagwidwa ndi ndulu yowawa ndi nsinga ya cosalungama.[24] Ndipo Simoni anayankha nati, Mundipempherere ine kwa Ambuye kuti zisandigwere izi mwanenazi.

GENESIS 1:24-31
[24] Ndipo adati Mulungu, Dziko lapansi libale zamoyo monga mwa mitundu yao, ng'ombe, ndi zokwawa, ndi zinyama za dziko lapansi monga mwa mitundu yao: ndipo kunatero.[25] Ndipo Mulungu anapanga zinyama za dziko lapansi monga mwa mitundu yao; ndi ng'ombe monga mwa mtundu wace, ndi zonse zakukwawa pansi monga mwa mitundu yao; ndipo Mulungu anaona kuti kunali kwabwino.[26] Ndipo anati Mulungu, Tipange munthu m'cifanizo cathu, monga mwa cikhalidwe cathu: alamulire pa nsomba za m'nyanja, ndi pa mbalame za m'mlengalenga, ndi pa ng'ombe, ndi pa dziko lonse lapansi, ndi pa zokwawa zonse zakukwawa pa dziko lapansi.[27] Mulungu ndipo adalenga munthu m'cifanizo cace, m'cifanizo ca Mulungu adamlenga iye; adalenga iwo mwamuna ndi mkazi.[28] Mulungu ndipo anadalitsa iwo, ndipo adati kwa iwo, Mubalane, mucuruke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse: mulamulire pa nsomba za m'nyanja, ndi pa mbalame za m'mlengalenga, ndi pa zamoyo zonse zakukwawa pa dziko lapansi.[29] Ndipo anati Mulungu, Taonani, ndakupatsani inu therere lonse lakubala mbeu liri pa dziko lapansi, ndi mitengo yonse m'mene muli cipatso ca mtengo wakubala mbeu; cidzakhala cakudya ca inu:[30] ndiponso ndapatsa zinyama zonse za dziko lapansi, ndi mbalame zonse za m'mlengalenga, ndi zakukwawa zonse za dziko lapansi m'mene muli moyo, therere laliwisi lonse likhale cakudya: ndipo kunatero.[31] Ndipo anaziona Mulungu zonse zimene adazipanga, ndipo, taonani, zinali zabwino ndithu. Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku lacisanu ndi cimodzi.

1 AKORINTO 6:9
Kapenasimudziwa kuti osalungama sadzalandira ufumu wa Mulungu? Musasoceretsedwe; adama, kapena opembedza mafano, kapena acigololo, kapena olobodoka ndi zoipa, kapena akudziipsa ndi amuna,

YOHANE 1:8
iye sindiye kuunikaku, koma anatumidwa kukacita umboni wa kuunikaku.

CHIVUMBULUTSO 4:6-8
[6] ndipo ku mpandowo, ngati nyanja, yamandala yonga krustalo; ndipopakati pa mpandowo, ndi pozinga mpandowo, zamoyo zinai zodzaia ndi maso kutsogolo indi kumbuyo.[7] Ndipo camoyo coyamba cinafanana nao mkango, ndi camoyo caciwiri cinafanana ndi mwana wa ng'ombe, ndi camoyo cacitatu cinali nayo nkhope yace ngati ya munthu, ndi camoyo cacinai cidafanana ndi ciombankhanga cakuuluka.[8] Ndipo zamoyozo zinai, conse pa cokha cinali nao mapiko asanu ndi limodzi; ndipo zinadzala ndi maso pozinga ponse ndi m'katimo; ndipo sizipumula usana ndi usiku, ndi kunena, Woyera, woyera, woyera, Ambuye Mulungu Wamphamvuyonse, amene anali, amene ali, ndi amene alinkudza.

GENESIS 3:15
ndipo ndidzaika udani pakati pa iwe ndi mkaziyo, ndi pakati pa mbeu yako ndi mbeu yace; ndipo idzalalira mutu wako, ndipo iwe udzalalira citende cace.

CHIVUMBULUTSO 13:5
Ndipo anacipatsa ico m'kamwa molankhula zazikuru ndi zamwano; ndipo anacipatsa ulamuliro wa kutero miyezi makumi anai ndi iwiri.

EKSODO 7:11
Pamenepo Farao anaitananso anzeru, ndi amatsenga; ndipo alembi a Aigupto, iwonso anacita momwemo ndi matsenga ao.

Chewa Bible (BL) 1992
Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society