A A A A A

Zizindikiro za Masamu: [Nambala 5]


CHIVUMBULUTSO 13:5-18
[5] Ndipo anacipatsa ico m'kamwa molankhula zazikuru ndi zamwano; ndipo anacipatsa ulamuliro wa kutero miyezi makumi anai ndi iwiri.[6] Ndipo cinatsegula pakamwa pace kukanena zamwano pa Mulungu, kucitira mwano dzina lace, ndi cihema cace, ndi iwo akukhala m'Mwamba.[7] Ndipo anacipatsa ico kucita nkhondo ndi oyera mtima, ndi kuwalaka; ndipo anacipatsa ulamuliro wa pa pfuko liri lonse, ndi anthu, ndi manenedwe, ndi mitundu.[8] Ndipo adzacilambira onse akukhala padziko, amene dzina lao silinalembedwa m'buku la moyo la Mwanawankhosa, wophedwa kuyambira makhazikidwe a dziko lapansi,[9] N gati wina ali nalo khutu, amve.[10] N gati munthu alinga kundende, kundende adzamuka munthu akapha ndi lupanga, ayenera iyekuphedwa nalo lupanga, Pano pali cipiriro ndi cikhulupiriro ca oyera mtima.[11] Ndipo ndinaona cirombo cina cirikuturuka pansi; ndipo cinali nazo nyanga ziwiri ngati za mwana wa nkhosa, ndipo cinalankhula ngati cinjoka.[12] Ndipo cicita ulamuliro wonse wa cirombo coyamba pamaso pace. Ndipo cilambiritsa dziko ndi iwo akukhala momwemo cirombo coyamba, cimene bala lace la kuimfa lidapola.[13] Ndipo cicita zizindikilo zazikuru, kutinso citsitse moto ucokere m'mwamba nugwe padziko, pamaso pa anthu.[14] Ndipo cisokeretsa iwo akukhala padziko ndi zizindikilo zimene anacipatsa mphamvu yakuzicita pamaso pa cirombo, ndi kunena kwa iwo akukhala padziko, kuti apange fane la ciromboco, cimene cinali nalo bala la lupanga nicinakhalanso ndi moyo.[15] Ndipo anacipatsa mphamvu yakupatsa fano la cirombo mpweya, kutinso fane la cirombo Iilankhule, nilicite kuti onse osalilambira fane la cirombo aphedwe.[16] Ndipo cicita kuti onse, ang'ono ndi akuru, acuma ndi osauka, ndi mfulu ndi akapolo, alandire cilembo pa dzanja lao ndi pamphumi pao;[17] ndi kuti munthu sangakhoze kugula kapena kugulitsa, koma iye yekha wakukhala naco cilembo, ndilo dzina la cirombo, kapena ciwerengero ca dzina lace.[18] Pano pali nzeru. Iye wakukhala naco cidziwitso awerenge ciwerengero ca ciromboco; pakuti ciwerengero cace ndi ca munthu; ndipo ciwerengero cace ndico mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu ndi limodzi kudza zisanu ndi cimodzi.

MATEYU 19:9
Ndipo Ine ndinena kwa inu, Amene ali yense akacotsa mkazi wace, kosakhala cifukwa ca cigololo, nadzakwatira wina, acita cigololo: ndipo iye amene akwatira wocotsedwayo, acita cigololo.

CHIVUMBULUTSO 11:2-3
[2] Ndipo bwalo la kunja kwa Kacisi ulisiye padera, osaliyesa; pakuti adapatsa ilo kwa amitundu; ndipo mzinda wopatulika adzaupondereza miyezi makumi anai mphambu iwiri.[3] Ndipo ndidzalamulira mboni zanga ziwiri, ndipo zidzanenera masiku cikwi cimodzi ndi mazana awiri mphambu makumi asanu ndi limodzi, zobvala ciguduli.

MATEYU 5:32
koma Ine ndinena kwa inu, kuti 4 yense wakucotsa mkazi wace, kosati cifukwa ca cigololo, amcititsa cigololo: ndipo amene adzakwata wocotsedwayo acita cigololo.

2 TIMOTEO 3:16
Lemba liri lonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa pa ciphunzitso, citsutsano, cikonzero, cilangizo ca m'cilungamo:

CHIVUMBULUTSO 4:6-8
[6] ndipo ku mpandowo, ngati nyanja, yamandala yonga krustalo; ndipopakati pa mpandowo, ndi pozinga mpandowo, zamoyo zinai zodzaia ndi maso kutsogolo indi kumbuyo.[7] Ndipo camoyo coyamba cinafanana nao mkango, ndi camoyo caciwiri cinafanana ndi mwana wa ng'ombe, ndi camoyo cacitatu cinali nayo nkhope yace ngati ya munthu, ndi camoyo cacinai cidafanana ndi ciombankhanga cakuuluka.[8] Ndipo zamoyozo zinai, conse pa cokha cinali nao mapiko asanu ndi limodzi; ndipo zinadzala ndi maso pozinga ponse ndi m'katimo; ndipo sizipumula usana ndi usiku, ndi kunena, Woyera, woyera, woyera, Ambuye Mulungu Wamphamvuyonse, amene anali, amene ali, ndi amene alinkudza.

NUMERI 5:11-31
[11] Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,[12] Nena ndi ana a Israyeli, nuti nao, Mkazi wa mwini akapatukira mwamuna wace, nakamcitira mosakhulupirika,[13] ndi munthu akagona naye, koma kumbisikira maso a mwamuna wace, ndikumng'unira; nadetsedwa mkaziyo, koma palibe mboni yomtsutsa, kapena sanamgwira alimkucita;[14] ndipo ukamgwira mwamuna mtima wansanje, kuti acitire nsanje mkazi wace, popeza wadetsedwa; kapena ukamgwira mtima wansanje, kuti amcitire mkazi wace nsanje angakhale sanadetsedwa;[15] pamenepo mwamunayo azidza naye mkazi wace kwa wansembe, nadze naco copereka cace, limodzi la magawo khumi la efa wa ufa wabarele; asathirepo mafuta, kapena kuikapo libano; popeza ndiyo nsembe yaufa yansanje, nsembe yaufa yacikumbutso, yakukumbutsa mphulupulu.[16] Ndipo wansembe abwere naye, namuike pamaso pa Yehova;[17] natenge madzi opatulika m'mbale yadothi wansembeyo, natengeko pfumbi liri pansi m'kacisi, wansembeyo nalithire m'madzimo.[18] Pamenepo wansembeyo aike mkaziyo pamaso pa Mulungu, nabvula mutu wa mkaziyo, naike nsembe yaufa yacikumbutso m'manja mwace, ndiyo nsembe yaufa yansanje; ndipo m'manja mwace mwa wansembe muzikhala madzi owawa akudzetsa temberero.[19] Ndipo wansembe amlumbiritse, nanene kwa mkazi, Ngati sanagona nawe munthu mmodzi yense, ngati sunapatukira kucidetso, pokhala ndiwe wa mwamuna wako, upulumuke ku madzi owawa awa akudzetsa temberero.[20] Koma iwe, ngati wapatukira mwamuna wako, ngati wadetsedwa, kuti wagona nawe munthu, wosati mwamuna wako;[21] pamenepo wansembe alumbiritse mkazi lumbiro lakutemberera, ndi wansembe anene kwa mkazi, Yehova akuike ukhale temberero ndi lumbiro pakati pa anthu a mtundu wako, pakuondetsa Yehova m'cuuno mwako, ndi kukutupitsa mbulu;[22] ndipo madzi awa akudzetsa temberero adzalowa m'matumbo mwako, nadzakutupitsa mbulu ndi kuondetsa m'cuuno mwako; ndipo mkaziyo aziti, Amen, Amen.[23] Ndipo wansembe alembere matemberero awa m'buku, ndi kuwafafaniza ndi madzi owawawa.[24] Ndipo amwetse mkaziyo madzi owawa akudzetsa temberero; ndi madzi odzetsa temberero adzalowa mwa iye nadzamwawira.[25] Ndipo wansembe atenge nsembe yaufa m'manja mwa mkazi, naweyule nsembe yaufa pamaso pa Yehova, nabwere nayo ku guwa la nsembe.[26] Wansembe atengekonso nsembe yaufa wodzala manja, cikumbutso cace, nacitenthe pa guwa la nsembe; ndipo atatero amwetse mkazi madziwo.[27] Ndipo atammwetsa madziwo, kudzatero, ngati wadetsedwa, nacita mosakhulupitika pa mwamuna wace, madzi odzetsa tembererowo adzalowa mwa iye nadzamwawira, nadzamtupitsa mbulu, ndi m'cuuno mwace mudzaonda; ndi mkaziyo adzakhala temberero pakati pa anthu a mtundu wace.[28] Koma ngati mkazi sanadetsedwa, nakhala woyera, pamenepo adzapulumuka, nadzaima.[29] Ici ndi cilamulo ca nsanje, pamene mkazi, pokhala naye mwamuna wace, ampatukira nadetsedwa;[30] kapena pamene mtima wansanje umgwira mwamuna, ndipo acitira mkazi wace nsanje; pamenepo aziika mkazi pamaso pa Yehova, ndipo wansembe amcitire cilamulo ici conse.[31] Mwamunayo ndiye wosacita mphulupulu, koma mkazi uyo asenze mphulupulu yace.

1 MAFUMU 7:23
Ndipo anayenganso thawale lamkuwa, kukamwa kwace kunali kwa mikono khumi, linali lozunguniza, ndi msinkhu wace unali mikono isanu; ndi cingwe ca mikono makumi atatu cinalizungulira.

DEUTERONOMO 6:4
Imvani, Israyeli; Yehova Mulungu wathu, Yehova ndiye mmodzi;

MALAKI 3:10
Mubwere nalo limodzi limodzi lonse la khumi, ku nyumba yosungiramo, kuti m'nyumba mwanga mukhale cakudya; ndipo mundiyese nako tsono, ati Yehova wa makamu, ngati sindikutsegulirani mazenera a kumwamba, ndi kukutsanulirani mdalitso wakuti adzasoweka malo akuulandira.

MASALIMO 104:9
Munaika malire kuti asapitirireko; Kuti asabwererenso kuphimba dziko lapansi.

GENESIS 6:12
Ndipo Mulungu anaona dziko lapansi, ndipo taonani, linabvunda; pakuti anthu onse anabvunditsa njira yao pa dziko lapansi.

GENESIS 7:20
Madzi anapambana ndithu nakwera mikono khumi ndi isanu: namizidwa mapiri,

GENESIS 8:5-9
[5] Ndipo madzi analinkucepa kufikira mwezi wakhumi; mwezi wakhumi tsiku loyamba mwezi ndipo padaoneka mitu ya mapiri.[6] Ndipo panali atapita masiku makumi anai, Nowa anatsegula pa zenera la cingalawa limene analipanga:[7] ndipo anaturutsa khungubwe, ndipo anaturuka kunka kwina ndi kwina kufikira adaphwa madzi pa dziko lapansi,[8] Ndipo anaturutsa njiwa imcokere, kuti aone kapena madzi anaphwa pamwamba pa dziko lapansi;[9] koma njiwayo siinapeza popondapo phazi lace, nibwera kwa iye kucingalawako, pakuti madzi analipo pa dziko lonse lapansi; ndipo anaturutsa dzanja lace, naitenga, nailowetsa kwa iye m'cingalawamo.

GENESIS 9:11
Ndipo ndidzakhazikitsa pangano langa pamodzi ndi inu; zamoyo zonse sizidzamarizidwanso konse ndi madzi a cigumula; ndipo sikudzakhalanso konse cigumula cakuononga dziko lapansi.

GENESIS 1:31
Ndipo anaziona Mulungu zonse zimene adazipanga, ndipo, taonani, zinali zabwino ndithu. Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku lacisanu ndi cimodzi.

GENESIS 3:15
ndipo ndidzaika udani pakati pa iwe ndi mkaziyo, ndi pakati pa mbeu yako ndi mbeu yace; ndipo idzalalira mutu wako, ndipo iwe udzalalira citende cace.

1 AKORINTO 10:13
Sicinakugwerani inu ciyeso koma ca umunthu; koma Mulungu ali wokhulupirika, amene sadzalola inu kuyesedwa koposa kumene mukhoza; koma pamodzi ndi ciyeso adzaikanso populumukirapo, kuti mudzakhoze kupirirako.

EKSODO 20:13
Usaphe.

Chewa Bible (BL) 1992
Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society