A A A A A

Moyo: [Kukongola]


1 PETRO 3:3-4
[3] Amene kukometsera kwanu kusakhale kwa kunja, kuluka tsitsi ndi kubvala za golidi, kapena kubvala cobvala;[4] koma kukhale munthu wobisika wamtima, m'cobvala cosaola ca mzimu wofatsa ndi wacete, ndiwo wa mtengo wace wapatali pamaso pa Mulungu.

2 AKORINTO 4:16
Cifukwa cace sitifoka; koma ungakhale umunthu wathu wakunja ubvunda, wa m'kati mwathu ukonzedwa kwatsopano tsiku ndi tsiku.

AEFESO 2:10
Pakuti ife ndife cipango cace, olengedwa mwa Kristu Yesu, kucita nchito zabwino, zimene Mulungu anazipangiratu, kuti tikayende m'menemo.

GENESIS 1:27
Mulungu ndipo adalenga munthu m'cifanizo cace, m'cifanizo ca Mulungu adamlenga iye; adalenga iwo mwamuna ndi mkazi.

YESAYA 40:8
Udzu unyala, duwa lifota, koma mau a Mulungu wathu adzakhala nthawi zacikhalire.

AFILIPI 4:8
Cotsalira, abale, zinthu ziri zonse zoona, ziri zonse zolemekezeka, ziri zonse zolungama, ziri zonse zoyera, ziri zonse zokongola, ziri zonse zimveka zokoma; ngati kuli cokoma mtima cina, kapena citamando cina, zilingirireni izi.

MASALIMO 139:14
Ndikuyamikani cifukwa kuti cipangidwe canga ncoopsa ndi codabwiza; Nchito zanu nzodabwiza; Moyo wanga ucidziwa ici bwino ndithu.

AROMA 8:6
pakuti cisamaliro ca thupi ciri imfa; koma cisamaliro ca mzimu ciri moyo ndi mtendere.

NYIMBO YA SOLOMONI 4:7
Wakongola monse monse, wokondedwa wanga, namwaliwe, Mulibe cirema mwa iwe.

MATEYU 6:28-29
[28] Ndipo muderanji nkhawa ndi cobvala? Tapenyetsani maluwa a kuthengo, makulidwe ao; sagwiritsa nchito, kapena sapota:[29] koma ndinena kwa inu, kuti angakhale Solomo mu ulemerero wace wonse sanabvala monga limodzi la amenewa.

1 TIMOTEO 2:9-10
[9] Momwemonso, akazi adzibveke okha ndi cobvala coyenera, ndi manyazi, ndi cidziletso; osati ndi tsitsi lace loluka, ndi golidi kapena ngale, kapena maraya a mtengo wace wapatali;[10] komatu (umo mokomera akazi akubvomereza kulemekeza Mulungu), mwa nchito zabwino.

1 SAMUELE 16:7
Koma Yehova ananena ndi Samueli, Vsayang'ane nkhope yace, kapena kutalika kwa msinkhu wace, popeza Ine ndinamkana iye; pakuti Yehova saona monga aona munthu; pakuti munthu ayang'ana cooneka ndi maso, koma Yehova ayang'ana mumtima.

MLALIKI 3:11
Cinthu ciri conse anacikongoletsa pa mphindi yace; ndipo waika zamuyaya m'mitima yao ndipo palibe munthu angalondetse nchito Mulungu wazipanga ciyambire mpaka citsiriziro.

AGALATIYA 3:26-27
[26] 3 Pakuti inu nonse muli ana a Mulungu, mwa cikhulupiriro ca mwa Yesu Kristu.[27] 4 Pakuti nonse amene munabatizidwa kwa Kristu mudabvala Kristu.

MIYAMBO 3:15-18
[15] Mtengo wace uposa ngale; Ndipo zonse zikukondweretsa sizilingana naye.[16] Masiku ambiri ali m'dzanja lamanja lace; Cuma ndi ulemu m'dzanja lace lamanzere.[17] Njira zace ziri zokondweretsa, Mayendedwe ace onse ndiwo mtendere.[18] Ndiyo mtengo wa moyo wa akuigwira; Wakulumirira ngwodala.

EZEKIELE 28:17-18
[17] Unadzikuza mtima cifukwa ca kukongola kwako, waipsa nzeru zako; cifukwa ca kuwala kwako ndakugwetsa pansi, ndakuika pamaso pa mafumu, kuti akupenye.[18] Mwa mphulupulu zako zocuruka ndi malonda ako osalungama waipsa malo ako opatulika; cifukwa cace ndaturutsa moto m'kati mwako wakunyeketsa iwe; ndipo ndakusandutsa mapulusa panthaka pamaso pa onse akuona.

YAKOBO 1:23
Pakuti ngati munthu ali wakumva mau wosati wakucita, iyeyu afanana ndi munthu wakuyang'anira nkhope yace ya cibadwidwe cace m'kalirole;

MATEYU 23:28
Comweco inunso muonekera olungama pamaso pa anthu, koma m'kati muli odzala ndi cinyengo ndi kusayeruzika.

MIYAMBO 31:30
Kukongola kungonyenga, maonekedwe okoma ndi cabe; Koma mkazi woopa Yehova adzatamandidwa.

Chewa Bible (BL) 1992
Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society