A A A A A

Good Character: [Courage / Brave]


1 MBIRI 28:20
Ndipo Davide anati kwa Solomo mwana wace, Limbika, nulimbe mtima, nucicite; usaopa, kapena kutenga nkhawa; pakuti Yehova Mulungu, ndiye Mulungu wanga, ali nawe; sadzakusowa kapena kukutaya mpaka zitatha nchito zonse za utumiki wa nyumba ya Yehova.

1 AKORINTO 15:58
Cifukwa cace, abale anga okondedwa, 24 khalani okhazikika, osasunthika, akucuruka mu ncbitoya Ambuye, nthawi zonse, podziwa kuti kucititsa kwanu sikuli cabe mwa Ambuye.

DEUTERONOMO 31:6-8
[6] Khalani amphamvu, limbikani mitima, musamacita mantha, kapena kuopsedwa cifukwa ca iwowa; popeza Yehova Mulungu wanu ndiye amene amuka nanu; iye sadzakusowani, kapena irukusiyani.[7] Ndipo Mose anaitana Yoswa, nati naye pamaso pa Israyeli wonse, Khala wamphamvu, nulimbe mtima; pakuti udzalowa nao anthu awa m'dziko limene Yehova analumbirira makolo ao kuwapatsa ilo; ndipo iwe udzawalandiritsa ilo.[8] Ndipo Yehova, iye ndiye amene akutsogolera; iye adzakhala ndi iwe, iye sadzakusowa kapena kukusiya; usamacita mantha, usamatenga nkhawa.

AEFESO 6:10
Cotsalira, tadzilimbikani mwa Ambuye, ndi m'kulimba kwa mphamvu yace.

YESAYA 54:4
Usaope, pakuti sudzakhala ndi manyazi; usasokonezedwe, pakuti sudzacitidwa manyazi; pakuti udzaiwala manyazi a ubwana wako, ndi citonzo ca umasiye wako sudzacikumbukiranso.

YOHANE 14:27
4 Mtendere ndikusiyirani inu, mtendere wanga ndikupatsani; Ine sindikupatsani inu monga dziko lapansi lipatsa. 5 Mtima wanu usabvutike, kapena usacite mantha.

MASALIMO 27:1
Yehova ndiye kuunika kwanga ndi cipulumutso canga; ndidzaopa yani? Yehova ndiye mphamvu ya moyo wanga; ndidzacita mantha ndi yani?

MASALIMO 56:3-4
[3] Tsiku lakuopa ine, Ndidzakhulupirira Inu.[4] Mwa Mulungu ndidzalemekeza mau ace: Ndakhulupirira Mulungu, sindidzaopa; Anthu adzandicitanji?

2 TIMOTEO 1:7
Pakuti Mulungu sanatipatsa mzimu wa mantha; komatu wa mphamvu ndi cikondi ndi cidziletso.

YOSWA 1:9-11
[9] Kodi sindinakulamulira iwe? Khala wamphamvu, nulimbike mtima, usaope, kapena kutenga nkhawa, pakuti Yehova Mulungu wako ali ndi iwe kuli konse umukako.[10] Pamenepo Yoswa analamulira akapitao a anthu, ndi kuti,[11] Pitani pakati pa cigono, nimulamulire anthu, ndi kuti, Mudzikonzeretu kamba, pakuti asanapite masiku atatu mudzaoloka Yordano uyu, kulowa ndi kulandira dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani, likhale lanu lanu.

YESAYA 41:10-13
[10] usaope, pakuti Ine ndiri pamodzi ndi iwe; usaopsyedwe, pakuti Ine ndine Mulungu wako; ndidzakulimbitsa; inde, ndidzakuthangata; inde, ndidzakucirikiza ndi dzanja langa lamanja la cilungamo.[11] Taona, onse amene akukwiyira iwe adzakhala ndi manyazi, nasokonezedwa; iwo amene akangana ndi iwe adzakhala ngati cabe, nadzaonongeka.[12] Iwe udzawafuna osawapeza, ngakhale iwo amene akangana ndi iwe; ocita nkhondo ndi iwe, adzakhala ngati cabe, ndi monga kanthu kopanda pace.[13] Pakuti Ine Yehova Mulungu wako ndidzagwira dzanja lako lamanja, ndi kunena kwa iwe, Usaope ndidzakuthandiza iwe.

1 AKORINTO 16:13
Dikirani, cirimikani m'cikhulupiriro; dzikhalitseni amuna, limbikani.

MASALIMO 27:14
Yembekeza Yehova: Limbika, ndipo Iye adzalimbitsa mtima wako; Inde, yembekeza Yehova.

MIYAMBO 3:5-6
[5] Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, Osacirikizika pa luntha lako;[6] Umlemekeze m'njira zako zonse, Ndipo Iye adzaongola mayendedwe ako.

MASALIMO 23:1-4
[1] Yehova ndiye mbusa wanga; sindidzasowa.[2] Andigonetsa ku busa lamsipu: Anditsogolera ku madzi ndikha.[3] Atsitsimutsa moyo wanga; Anditsogolera m'mabande a cilungamo, cifukwa ca dzina lace.[4] Inde, ndingakhale ndiyenda m'cigwa ca mthunzi wa Imfa, Sindidzaopa coipa; pakuti Inu muli ndi ine: Cibonga canu ndi ndodo yanu, izi zindisangalatsa ine,

MARKO 5:36
Koma Yesu wosasamala mau olankhulidwawo, ananena kwa mkuru wa sunagoge, Usaope, khulupirira kokha.

AFILIPI 1:28
osaopa adani m'kanthu konse, cimene ciri kwa iwowa cisonyezo ca cionongeko, koma kwa inu ca cipulumutso, ndico ca kwa Mulungu;

MASALIMO 112:7
Sadzaopa mbiri yoipa; Mtima wace ngwokhazikika, wakhulupirira Yehova.

YOSWA 1:6
Khala wamphamvu, nulimbike mtima, pakuti udzagawira anthu awa dzikoli likhale colowa cao, ndilo limene ndinalumbirira makolo ao kuwapatsa.

MASALIMO 31:24
Limbikani, ndipo Iye adzalimbitsa mtima wanu, Inu nonse akuyembekeza Yehova.

Chewa Bible (BL) 1992
Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society