A A A A A

Good Character: [Contentment]


MATEYU 6:25-33
[25] Cifukwa cace ndinena kwa inu, Musadere nkhawa moyo wanu, cimene mudzadya ndi cimene mudzamwa; kapena thupi lanu, cimene mudzabvala. Kodi moyo suli woposa cakudya, ndi thupi loposa cobvala?[26] Yang'anirani mbalame za kumwamba, kuti sizimafesa ai, kapena sizimatema ai, kapena sizimatutira m'nkhokwe; ndipo Atate wanu wa Kumwamba azidyetsa. Nanga inu mulibe kusiyana nazo kuziposa kodi?[27] Ndipo ndani wa inu ndi kudera nkhawa angathe kuonjezera pa msinkhu wace mkono umodzi?[28] Ndipo muderanji nkhawa ndi cobvala? Tapenyetsani maluwa a kuthengo, makulidwe ao; sagwiritsa nchito, kapena sapota:[29] koma ndinena kwa inu, kuti angakhale Solomo mu ulemerero wace wonse sanabvala monga limodzi la amenewa.[30] Koma ngati Mulungu abveka cotero maudzu a kuthengo, akhala lero, ndi mawa oponyedwa pamoto, nanga si inu kopambana ndithu, inu akukhulupirira pang'ono?[31] Cifukwa cace musadere nkhawa, ndi kuti, Tidzadya ciani? kapena, Tidzamwa ciani? kapena, Tidzabvala ciani?[32] Pakuti anthu akunja azifunitsa zonse zimenezo; pakuti Atate wanu wa Kumwamba adziwa kuti musowa zonse zimenezo.[33] Koma muthange mwafuna Ufumu wace ndi cilungamo cace, ndipo zonse zimenezo zidzaonjezedwa kwa inu.

2 AKORINTO 11:23-25
[23] Kodi ali atumiki a Kristu? (ndilankhula monga moyaruka), makamaka ine; m'zibvutitso mocurukira, m'ndende mocurukira, m'mikwingwirima mosawerengeka, muimfa kawiri kawiri.[24] Kwa Ayuda ndinalandirakasanu mikwingwirima makumi anai kuperewera umodzi.[25] Katatu ndinamenyedwa ndi ndodo, kamodzi ndinaponyedwa miyala, katatu ndinatayika posweka combo, ndinakhala m'kuya tsiku limodzi usana ndi usiku;

AFILIPI 4:12-13
[12] Ndadziwa ngakhale kupeputsidwa, ndadziwanso kusefukira; konseko ndi m'zinthu zonse ndalowa mwambo wakukhuta, ndiponso wakumva njala; wakusefukira, ndiponso wakusowa.[13] Ndikhoza zonse mwa iye wondipatsa mphamvuyo.

AHEBRI 13:5
Mtima wanu ukhale wosakonda cuma; zimene muli nazo zikukwanireni; pakuti iye anati, Sindidzakusiya konse, kungakhale kukutaya, sindidzakutaya ndithu.

1 TIMOTEO 6:6-7
[6] Koma cipembedzo pamodzi ndi kudekha cipindulitsa kwakukuru;[7] pakuti sitinatenga kanthu polowa m'dziko lapansi, ndiponso sitikhoza kupita nako kanthu pocoka pano;

LUKA 12:15
Ndipo iye anati kwa iwo, Yang'anirani, mudzisungire kupewa msiriro uli wonse; cifukwa moyo wace wa munthu sulingana ndi kucuruka kwa zinthu zace ali nazo.

2 AKORINTO 12:10
Cifukwa cace ndisangalala m'tnaufoko, m'ziwawa, m'zikakamizo, m'mazunzo, m'zipsinjiko, cifukwa ca Kristu; pakuti pamene ndifoka, pamenepo ndiri wamphamvu.

MASALIMO 37:3-4
[3] Khulupirira Yehova, ndipo cita cokoma; Khala m'dziko, ndipo tsata coonadi.[4] Udzikondweretsenso mwa Yehova; Ndipo iye adzakupatsa zokhumba mtima wako.

1 TIMOTEO 6:10-11
[10] Pakuti muzu wa zoipa zonse ndiwo cikondi ca pa ndalama; cimene ena pocikhumba, anasocera, nataya cikhulupiriro, nadzipyoza ndi zowawa zambiri.[11] Koma iwe, munthu wa Mulungu iwe, thawa izi; nutsate cilungamo, cipembedzo, cikhulupiriro, cikondi, cipiriro, cifatso.

MIYAMBO 16:8
Zapang'ono, pokhala cilungamo, Ziposa phindu lalikuru lopanda ciweruzo.

MIYAMBO 28:6
Waumphawi woyenda mwangwiro Apambana ndi yemwe akhotetsa njira zace, angakhale alemera.

MLALIKI 3:13
Ndiponso kuti munthu yense adye namwe naone zabwino m'nchito zace zonse; ndiwo mtulo wa Mulungu.

Chewa Bible (BL) 1992
Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society