A A A A A

Good Character: [Confidence]


1 YOHANE 4:17
M'menemo cikondi cathu cikhala cangwiro kuti tikhale nako kulimbika mtima m'tsiku la mlandu; citukwa monga Iyeyuali, momwemo tiri ife m'dziko line lapansi.

1 YOHANE 5:14
Ndipo uku ndi kulimbika mrima kumene tiri nako kwa iye, kuti ngati tipempha kanthu monga mwa cifuniro cace, atimvera;

2 MBIRI 32:8
pamodzi ndi iye pali dzanja la thupi lanyama; koma pamodzi ndi ife pali Yehova Mulungu wathu, kutithandiza ndi kutigwirira nkhondo. Ndipo anthu anacirikizika ndi mau a Hezekiya mfumu ya Yuda.

AEFESO 3:12
amene tiri naye cokhazikika mtima ndi ciyandiko eolimbika, mwa cikhulupiriro ca pa iye.

AHEBRI 4:16
Potero tilimbike mtima poyandikira mpando wacifumu wacisomo, kuti tilandire cifundo ndi kupeza cisomo ca kutithandiza nthawi yakusowa.

YESAYA 32:17
Ndi nchito ya cilungamo idzakhala mtendere; ndi zotsata cilungamo zidzakhala mtendere, ndi kukhulupirika ku nthawi zonse.

YEREMIYA 17:7
Wodala munthu amene akhulupirira Yehova, amene cikhulupiriro cace ndi Yehova.

NEHEMIYA 6:16
Ndipo kunali atacimva adani athu onse, amitundu onse akutizinga anaopa, nagwadi nkhope; popeza anazindikira kuti nchitoyi inacitika ndi Mulungu wathu.

AFILIPI 1:6
pokhulupira pamenepo, kuti iye amene anayamba mwa inu nchito yabwino, adzaitsiriza kufikira tsiku la Yesu Kristu;

AFILIPI 4:13
Ndikhoza zonse mwa iye wondipatsa mphamvuyo.

MIYAMBO 3:26-32
[26] Pakuti Yehova adzalimbitsa mtima wako, Nadzasunga phazi lako lingakodwe.[27] Oyenera kulandira zabwino usawamane; Pokhoza dzanja lako kuwacitira zabwino.[28] Usanene kwa mnzako, Ukabwerenso, Ndipo mawa ndidzakupatsa; Pokhala uli nako kanthu.[29] Usapangire mnzako ciwembu; Popeza akhala nawe pafupi osatekeseka.[30] Usakangane ndi munthu cabe, Ngati sanakucitira coipa,[31] Usacitire nsanje munthu waciwawa; Usasankhe njira yace iri yonse.[32] Pakuti wamphulupulu anyansa Yehova; Koma cinsinsi cace ciri ndi oongoka.

MASALIMO 20:7
Ena atama magareca, ndi ena akavalo: Koma ife tidzachula dzina la Yehova Mulungu wathu.

AFILIPI 3:3-5
[3] pakuti ife ndife mdulidwe, akutumikira popembedza ndi Mzimu wa Mulungu, nadzitamandira mwa Yesu Kristu, osakhulupirira m'thupi;[4] ndingakhale inenso ndiri nako kakukhulupirira m'thupi; ngati wina yense ayesa kukhulupirira m'thupi, makamaka ineyu;[5] wodulidwa tsiku lacisanu ndi citatu, wa mbadwo wa Israyeli, wa pfuko la Benjamini, Mhebri wa mwa Ahebri; monga mwa lamulo, Mfarisi;

2 AKORINTO 3:1-4
[1] Kodi tirikuyambanso kudzibvomereza tokha? kapena kodi tisowa, monga ena, akalata otibvomerezetsa kwa inu, kapena ocokera kwa inu?[2] Inu ndinu kalata wathu, wolembedwa mu mitima yathu, wodziwika ndi wowerengedwa ndi anthu onse;[3] popeza mwaonetsedwa kuti muli kalata wa Kristu, wakumtumikira ndi ife, wosalembedwa ndi kapezi iai, koma ndi Mzimu wa Mulungu wamoyo; wosatim'magome amiyala, koma m'magome a mitima yathupi.[4] Ndipo kulimbika kotere kwa Mulungu tiri nako mwa Kristu:

Chewa Bible (BL) 1992
Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society