A A A A A

Good Character: [Commitment]


1 YOHANE 4:20
Munthu akati, kuti, Ndikonda Mulungu, nadana naye mbale wace, ali wabodza: pakuti iye wosakonda mbale ware amene wamuona, sakhoza kukonda Mulungu amene sanamuona.

1 MAFUMU 8:61
Mitima yanu ikhale yangwiro ndi Yehova Mulungu wathu, kuyenda m'malemba ace ndi kusunga malamulo ace, monga lero lino.

2 TIMOTEO 1:12
Cifukwa ca ideo ndinamva zowawa izi; komatu sindicita manyazi; pakuti ndimdziwa iye amene ndamkhulupirira, ndipo ndikopeka mtima kuti ali wa mphamvu ya kudikira cosungitsa eangaeo kufikira tsiku lijalo.

2 TIMOTEO 2:15
Ucite cangu kudzionetsera kwa Mulungu wobvomerezeka, wanchito wopanda cifukwa ca kucita manyazi, wolunjika nao bwino mau a coonadi.

2 TIMOTEO 4:7
Ndalimbana nako kulimbana kwabwino, ndatsiriza njirayo, ndasunga cikhulupiriro:

MACHITIDWE A ATUMWI 2:42
Ndipo 4 anali cikhalire m'ciphunzitso ca atumwi ndi m'ciyanjano, m'kunyema mkate ndi mapemphero.

AKOLOSE 1:29
kucita ici ndidzibvutitsa ndi kuyesetsa 9 monga mwa macitidwe ace akucita mwa ine ndi mphamvu.

DEUTERONOMO 27:10
Potero muzimvera mau a Yehova Mulungu wanu, ndi kucita malamulo ace, ndi malemba ace, amene ndikuuzani lero lino.

DEUTERONOMO 6:5
ndipo muzikonda Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse, ndi mphamvu yanu yonse.

AGALATIYA 1:4
amene anadzipereka yekha cifukwa ca macimo athu, kuti akatilanditse ife m'nyengo ya pansi pano yino yoipa, monga mwa cifuniro ca Mulungu ndi Atate wathu;

AGALATIYA 6:9
Koma tisaleme pakucita zabwino pakuti pa nyengo yace tidzatuta tikapanda kufoka.

YOHANE 8:12
Pamenepo Yesu analankhulanso nao, nanena, Ine ndine kuunika kwa dziko lapansi; iye wonditsata ine sadzayenda mumdima, koma adzakhala nako kuunika kwa moyo.

YOHANE 9:62
Ena ananena, Mau awa sali a munthu wogwidwa ciwanda. Kodi ciwanda cikhoza kumtsegulira maso wosaona?

MATEYU 4:19
Ndipo Iye ananena nao, Tiyeni pambuyo panga, ndidzakusandutsani asodzi a anthu.

AFILIPI 3:13
Abale, ine sindiwerengera ndekha kuti ndatha kucigwira: koma cinthu cimodzi ndicicita; poiwaladi zam'mbuyo, ndi kutambalitsira zam'tsogolo,

MIYAMBO 16:3
Pereka zocita zako kwa Yehova, Ndipo zolingalira zako zidzakhazikika.

MIYAMBO 18:1
Wopanduka afunafuna niro cace, Nakangana ndi nzeru yonse yeniyeni.

MASALIMO 37:5
Pereka njira yako kwa Yehova; Khulupiriranso Iye, adzacicita.

Chewa Bible (BL) 1992
Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society