A A A A A

Good Character: [Cleanliness]


YESAYA 1:16
Sambani, dziyeretseni; cotsani macitidwe anu oipa pamaso panga; lekani kucita zoipa;

MASALIMO 51:7
Mundiyeretse ndi hisope ndipo ndidzayera; Munditsuke ndipo ndidzakhala wa mbu woposa matalala.

1 YOHANE 1:7-9
[7] koma ngati tiyenda m'kuunika, mongalye ali m'kuunika, tiyanjana wina ndi mnzace, ndipo mwazi wa Yesu Mwana wace utisambitsa kuticotsera ucimo wonse.[8] Tikati kuti tiribe ucimo, tidzinyenga tokha, ndipo mwa ife mulibe coonadi.[9] Ngati tibvomereza macimo athu, ali wokhulupirika ndi wolungama iye, kuti atikhululukire macimo athu, ndi kutisambitsa kuticotsera cosalungama ciri conse.

EZEKIELE 36:25
Ndipo ndidzakuwazani madzi oyera, ndipo mudzakhala oyera; ndidzakuyeretsani kukucotserani zodetsa zanu zonse, ndi mafano anu onse.

MASALIMO 51:10
Mundilengere mtima woyera, Mulungu; Mukonze mzimu wokhazikika m'kati mwanga.

MACHITIDWE A ATUMWI 9:1-31
[1] Koma Saulo, wosaleka kupumira pa akuphunzira a Ambuye kuopsya ndi kupha, ananka kwa mkulu wa ansembe,[2] napempha kwa iye akalata akunka nao ku Damasiko kumasunagoge, kuti akapeza ena otsata Njirayo, amuna ndi akazi, akawatenge kudza nao omangidwa ku Yerusalemu.[3] Ndipo poyenda ulendo wace, kunali kuti iye anayandikira Damasiko: ndipo mwadzidzidzi kudawala momzingira kuunika kocokera kumwamba;[4] ndipo anagwa pansi, namva mau akunena naye, Saulo, Saulo, Undilondalonderanji?[5] Koma anati, Ndiouyani Mbuye? Ndipo anati, Ndine Yesu amene umlondalonda;[6] komatu, uka, nulowe m'mudzi, ndipo kudzanenedwa kwa iwe cimene uyenera kucita.[7] Ndipo amunawo akumperekeza iye anaima du, atamvadi mau, koma osaona munthu.[8] Ndipo Saulo anauka; koma potseguka maso ace, sanapenya kanthu; ndipo anamgwira dzanja, namtenga nalowa naye ni'Damasiko.[9] Ndipo anakhala masiku atatu wosaona, ndipo sanadya kapena kumwa.[10] Koma ku Damasiko kunali wophunzira wina dzina lace Hananiya; ndipo Ambuye anati kwa iye m'masomphenya, Hananiya. Ndipo anati, Ndiri pano, Ambuye,[11] Ndipo Ambuye anati kwa iye, Tauka, pita ku khwalala lochedwa Lolunjika, ndipo m'nyumba ya Yuda ufunse za munthu dzina lace Saulo, wa ku Tariso: pakuti taona, alikupemphera[12] ndipo anaona mwamuna dzina, lace Hananiya, alikulowa, namuika manja, kuti apenyenso.[13] Ndipo Hananiya anayankha nati, Ambuye ndamva ndi ambiri za munthu uyu kuti anacitiradi coipa oyera mtima anu m'Yerusalemu;[14] ndi kuti pane ali nao ulamuliro wa kwa ansembe akulu wakumanga onse akuitana pa dzina lanu.[15] Koma Ambuye anat kwa iye, Pita; pakuti iye ndiye cotengera canga cosankhika, cakunyamula dzina langa pamaso pa amitundu ndi mafumu ndi ana a Israyeli;[16] pakuti Ine ndidzamuonetsa iye zinthu zambirl ayenera iye kuzimva kuwawa cifukwaca dzina langa.[17] Ndipo anacoka Hananiya, nalowa m'nyumbayo; ndipo anaika manja ace pa iye, nati, Saulo, mbale, Ambuye wandituma ine, ndiye Yesu amene anakuonekerani pa njira wadzerayo, kuti upenyenso, ndi kudzazidwa ndi Mzimu Woyera.[18] Ndipo pomwepo padagwa kucoka m'maso mwace ngati mamba, ndipo anapenyanso;[19] ndipo ananyamuka nabatizidwa; ndipo analandira cakudya, naona naco mphamvu. Ndipo anakhala pamodzi ndi akuphunzira a ku Damasiko masiku ena.[20] Ndipo pomwepo m'masunagoge analalikira Yesu, kuti iye ndiye Mwana wa Mulungu.[21] Ndipo onse amene anamva anadabwa, nanena, Suyu iye amene anaononga m'Yerusalemu onse akuitana pa dzina ili? Ndipo wadza kuno kudzatero, kuti amuke nao omangidwa kwa ansembe akuru.[22] Koma Saulo anakula makamaka mumphamvu, nadodometsa Ayuda akukhala m'Damasiko, nawatsimikizira kuti ameneyo ndi Kristu.[23] Ndipo atapita masiku ambiri, Ayuda anapangana kuti amuphe iye;[24] koma ciwembu cao cinadziwika ndi Saulo. Ndipo anadikiranso pazipata usana ndi usiku kuti amuphe;[25] koma ophunzira ace anamtenga usiku, nampyoletsa palinga, namtsitsa ndi mtanga,[26] Koma m'mene anafika ku Yerusalemu, anayesa kudziphatika kwa ophunzira; ndipo anamuopa iye onse, osakhulupirira kuti ali wophunzira.[27] Koma Bamaba anamtenga, napita naye kwa atumwi, nawafotokozera umo adaonera Ambuye m'njira, ndi kuti analankhula naye, ndi kuti m'Damasiko adanena molimbika mtima m'dzina la Yesu.[28] Ndipo anali pamodzi nao, nalowa naturuka ku Yerusalemu,[29] nanena molimbika mtima m'dzina la Ambuye; ndipotu analankhula natsutsana ndi Aheleniste; koma anayesayesa kumupha iye.[30] Koma m'mene abale anacidziwa, anapita naye ku Kaisareya, namtumiza acokeko kunka ku Tariso.[31] Pamenepo ndipo Mpingo wa m'Yudeya Ionse ndi Galileya ndi Samariya unali nao mtendere, nukhazikika; ndipo unayenda m'kuopa kwa Ambuye ndi m'citonthozo ca Mzimu Woyera, nucuruka.

DEUTERONOMO 23:12-14
[12] Mukhale nao malo kunja kwa cigono kumene muzimukako kuthengo;[13] nimukhale naco cokumbira mwa zida zanu; ndipo kudzali, pakukhala inu pansi kuthengo mukumbe naco, ndi kutembenuka ndi kufotsera cakuturukaco;[14] popeza Yehova Mulungu wanu ayenda pakati pa cigono canu, kukupulumutsani ndi kupereka adani anu pamaso panu; cifukwa cace cigono canu cikhale copatulika; kuti angaone kanthu kodetsa mwa inu, ndi kukupotolokerani.

MIYAMBO 20:9
Ndani anganene, Ndasambitsa mtima wanga, Ndayera opanda cimo?

AFILIPI 4:8
Cotsalira, abale, zinthu ziri zonse zoona, ziri zonse zolemekezeka, ziri zonse zolungama, ziri zonse zoyera, ziri zonse zokongola, ziri zonse zimveka zokoma; ngati kuli cokoma mtima cina, kapena citamando cina, zilingirireni izi.

MASALIMO 73:1
Indedi Mulungu acitira Israyeli zabwino, Iwo a mtima wa mbe.

CHIVUMBULUTSO 1:5
ndi kwa Yesu Kristu, mboli yokhulupirikayo, wobadwa woyanba wa akufa, ndi mkulu wa mafunu a dziko lapansi, Kwa iye ameieatikonda ife, natimasula ku macimo athu ndi mwazi wace;

2 AKORINTO 7:1
Pokhala nao tsono malonjezano amenewa, okondedwa, tidzikonzere tokha kuleka codetsa conse ca thupi ndi ca mzimu, ndi kutsirfza ciyero m'kuopa Mulungu.

LEVITIKO 19:28
Musamadziceka matupi anu cifukwa ca akufa, kapena kutema mpbini; Ine ndine Yehova.

LEVITIKO 20:13
Munthu akagonana ndi mwamuna mnzace, monga amagonana ndi mkazi, acita conyansa onse awiri; awaphe ndithu; mwazi wao ukhale pamtu pao.

2 PETRO 3:8
Koma ici cimodzi musaiwale, okondedwa inu, kuti tsiku limodzi likhala kwa Ambuye ngati zaka cikwi, ndi zaka cikwi ngati tsiku limodzi.

2 AKORINTO 5:17
Cifukwa cace ngati munthu ali yense ali mwa Kristu ali wolengedwa watsopano; zinthu zakale zapita, taonani, zakhala zatsopano,

MATEYU 23:25-28
[25] Tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! cifukwa mutsuka kunja kwace kwa cikho ndi mbale, koma m'katimo iwo adzala ndi kulanda ndi kusadziletsa.[26] Mfarisi iwe wakhungu, yambotsuka m'kati mwa cikho ndi mbale, kuti kunja kwace kukhalenso koyera.[27] Tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! cifukwa mufanafana ndi manda opaka njereza, amene aonekera okoma kunja kwace, koma adzala m'katimo ndi mafupa a anthu akufa ndi zonyansa zonse.[28] Comweco inunso muonekera olungama pamaso pa anthu, koma m'kati muli odzala ndi cinyengo ndi kusayeruzika.

LUKA 6:31
Ndipo monga mufuna inu kuti anthu adzakucitirani inu, muwacitire iwo motero inu momwe.

1 AKORINTO 10:13
Sicinakugwerani inu ciyeso koma ca umunthu; koma Mulungu ali wokhulupirika, amene sadzalola inu kuyesedwa koposa kumene mukhoza; koma pamodzi ndi ciyeso adzaikanso populumukirapo, kuti mudzakhoze kupirirako.

MATEYU 23:26
Mfarisi iwe wakhungu, yambotsuka m'kati mwa cikho ndi mbale, kuti kunja kwace kukhalenso koyera.

MATEYU 5:8
Odala ali oyera mtima; cifukwa adzaona Mulungu.

GENESIS 18:4
nditengetu madzi pang'ono, ndikusambitseni mapazi anu, mupumule pansi pa mtengo;

EKSODO 19:14
Ndipo Mose anatsika m'phiri kumka kwa anthu, nawapatulitsa anthu; natsuka iwo zobvala zao.

DEUTERONOMO 23:12
Mukhale nao malo kunja kwa cigono kumene muzimukako kuthengo;

AROMA 5:8
Koma g Mulungu atsimikiza kwa ife cikonai cace ca mwini yekha m'menemo, kuti pokhala ife cikhalire ocimwa, Kristu adatifera ife.

1 TIMOTEO 4:12
Munthu asapeputse ubwana wako; komatu khala citsanzo kwa iwo okhulupira, m'mau, m'mayendedwe, m'cikondi, m'cikhulupiriro, m'kuyera mtima.

2 AKORINTO 6:14-18
[14] Musakhale omangidwa m'goli ndi osakhulupira osiyana; pakuti cilungamo cigawanabwanji ndi cosalungama? Kapena kuunika kuyanjana bwanji nw mdima?[15] Ndipo Kristu abvomerezana bwanji ndi Beliyali? Kapena wokhulupira ali nalo gawo lanji pamodzi ndi wosakhulupira?[16] Ndipo ciphatikizo cace ncanji ndi kacisi wa Mulungu ndi wa mafano? Pakuti ife ndife kacisi wa, Mulungu wamoyo; monga Mulungu anati, Ndidzakhalitsa mwa iwo, ndipe ndidzayendayenda mwa iwo; ndipo ndidzakhala Mulungu wao, ndi iwo adzakhala anthu anga.[17] Cifukwa cace, Turukani pakati Pao, ndipo patukani, ati Ambuye, Ndipo musakhudza kanthu kosakonzeka; Ndipo Ine ndidzalandira inu,[18] Ndipo ndidzakhala kwa inu Atate, Ndi inu mudzakhala kwa Ine ana amunandi akazi, anena Ambuye Wamphamvuyonse.

MACHITIDWE A ATUMWI 9:1-20
[1] Koma Saulo, wosaleka kupumira pa akuphunzira a Ambuye kuopsya ndi kupha, ananka kwa mkulu wa ansembe,[2] napempha kwa iye akalata akunka nao ku Damasiko kumasunagoge, kuti akapeza ena otsata Njirayo, amuna ndi akazi, akawatenge kudza nao omangidwa ku Yerusalemu.[3] Ndipo poyenda ulendo wace, kunali kuti iye anayandikira Damasiko: ndipo mwadzidzidzi kudawala momzingira kuunika kocokera kumwamba;[4] ndipo anagwa pansi, namva mau akunena naye, Saulo, Saulo, Undilondalonderanji?[5] Koma anati, Ndiouyani Mbuye? Ndipo anati, Ndine Yesu amene umlondalonda;[6] komatu, uka, nulowe m'mudzi, ndipo kudzanenedwa kwa iwe cimene uyenera kucita.[7] Ndipo amunawo akumperekeza iye anaima du, atamvadi mau, koma osaona munthu.[8] Ndipo Saulo anauka; koma potseguka maso ace, sanapenya kanthu; ndipo anamgwira dzanja, namtenga nalowa naye ni'Damasiko.[9] Ndipo anakhala masiku atatu wosaona, ndipo sanadya kapena kumwa.[10] Koma ku Damasiko kunali wophunzira wina dzina lace Hananiya; ndipo Ambuye anati kwa iye m'masomphenya, Hananiya. Ndipo anati, Ndiri pano, Ambuye,[11] Ndipo Ambuye anati kwa iye, Tauka, pita ku khwalala lochedwa Lolunjika, ndipo m'nyumba ya Yuda ufunse za munthu dzina lace Saulo, wa ku Tariso: pakuti taona, alikupemphera[12] ndipo anaona mwamuna dzina, lace Hananiya, alikulowa, namuika manja, kuti apenyenso.[13] Ndipo Hananiya anayankha nati, Ambuye ndamva ndi ambiri za munthu uyu kuti anacitiradi coipa oyera mtima anu m'Yerusalemu;[14] ndi kuti pane ali nao ulamuliro wa kwa ansembe akulu wakumanga onse akuitana pa dzina lanu.[15] Koma Ambuye anat kwa iye, Pita; pakuti iye ndiye cotengera canga cosankhika, cakunyamula dzina langa pamaso pa amitundu ndi mafumu ndi ana a Israyeli;[16] pakuti Ine ndidzamuonetsa iye zinthu zambirl ayenera iye kuzimva kuwawa cifukwaca dzina langa.[17] Ndipo anacoka Hananiya, nalowa m'nyumbayo; ndipo anaika manja ace pa iye, nati, Saulo, mbale, Ambuye wandituma ine, ndiye Yesu amene anakuonekerani pa njira wadzerayo, kuti upenyenso, ndi kudzazidwa ndi Mzimu Woyera.[18] Ndipo pomwepo padagwa kucoka m'maso mwace ngati mamba, ndipo anapenyanso;[19] ndipo ananyamuka nabatizidwa; ndipo analandira cakudya, naona naco mphamvu. Ndipo anakhala pamodzi ndi akuphunzira a ku Damasiko masiku ena.[20] Ndipo pomwepo m'masunagoge analalikira Yesu, kuti iye ndiye Mwana wa Mulungu.

1 AKORINTO 15:29
Ngati si kutero, adzacita ciani iwo amene abatizidwa cifukwa ca akufa? Ngatiakufa saukitsidwa konse, abatizidwa cifukwa ninji cifukwa ca iwo?

LEVITIKO 18:22
Usamagonana ndi mwamuna, monga amagonana ndi mkazi; conyansa ici.

AROMA 1:26-27
[26] Cifukwa ca ici Mulungu anawapereka iwo 1 ku zilakolako za manyazi; pakuti angakhale akazi ao anasandutsa macitidwe ao a cibadwidwe akhale macitidwe osalingana ndi cibadwidwe:[27] ndipo cimodzimodzinso amuna anasiya macitidwe a cibadwidwe ca akazi, natenthetsana ndi colakalaka cao wina ndi mnzace, amuna okhaokha anacitirana camanyazi, ndipo analandira mwa iwo okha mphotho yakuyenera kulakwa kwao.

1 AKORINTO 14:40
Koma zonse zicitike koyenera ndi kolongosoka.

MATEYU 7:18-23
[18] Sungathe mtengo wabwino kupatsa zipatso zoipa, kapena mtengo wamphuci kupatsa zipatso zokoma.[19] Mtengo uli wonse wosapatsa cipatso cokoma, audula, nautaya kumoto.[20] Inde comweco pa zipatso zao mudzawazindikira iwo.[21] Si yense wakunena kwa Ine, Ambuye, Ambuye, adzalowa mu Ufumu wa Kumwamba; koma wakucitayo cifuniro ca Atate wanga wa Kumwamba.[22] Ambiri adzati kwa Ine tsiku lomwelo, Ambuye, Ambuye, kodi sitinanenera mau m'dzina lanu, ndi m'dzina lanunso kuturutsa mizimu yoipa, ndi kucita m'dzina lanunso zamphamvu zambiri?[23] Ndipo pamenepo ndidzafukulira iwo, Sindinakudziwani inu nthawi zonse; cokani kwa Ine, inu akucita kusayeruzika.

YOHANE 5:39-40
[39] 2 Musanthula m'malembo, popeza muyesa kuti momwemo muli nao moyo wosatha; ndipo akundicitira Ine umboni ndi iwo omwewo;[40] ndipo 3 simufuna kudza kwa Ine, kuti mukhale nao moyo.

Chewa Bible (BL) 1992
Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society