A A A A A

Khalidwe Labwino: [Kusamalira]


1 TIMOTEO 5:4
Koma ngati wamasiye wina ali nao ana kapena adzukulu, ayambe aphunzire iwo kucitira ulemu a m'banja lao, ndi kubwezera akuwabala; pakuti ici ncolandirika pamaso pa Mulungu.

1 TIMOTEO 3:15
kuti udziwe kuyenedwa kwace pokhala m'nyumba ya Mulungu, ndiye Eklesia wa Mulungu wamoyo, mzati ndi mcirikizo wa coonadi.

YOHANE 8:32
ndipo mudzazindikira coonadi, ndipo coonadi cidzakumasulani.

CHIVUMBULUTSO 17:5
ndipo pamphumi pace padalembedwa dzina, CINSINSI, BABULO WAUKURU AMAI WA ACIGOLOLO NDI WA ZONY ANSITSA ZA DZIKO.

YAKOBO 1:27
Mapembedzedwe oyera ndi osadetsa pamaso pa Mulungu ndi Atate ndiwo: z kuceza ndi ana amasiye ndi akazi amasiye m'cisautso cao, ndi 1 kudzisungira mwini wosacitidwa mawanga ndi dziko lapansi.

YOHANE 6:54
11 Iye wakudya thupi langa ndi kumwa mwazi wanga ali nao moyo wosatha; ndipo Ine ndidzamuukitsa iye tsiku lomariza.

MARKO 6:3
Si mmisiri wa mitengo uyu, mwana wa Mariya, mbale wao wa Yakobo, ndi Yose, ndi Yuda, ndi Simoni? Ndipo alongo ace sali nafe pano kodi? Ndipo anakhumudwa ndi Iye.

YOHANE 14:6
Yesu ananena naye, ine ndinenjira, ndi coonadi, ndi moyo. Palibe munthu adza kwa Atate, koma mwa Ine.

GENESIS 1:1-7
[1] PACIYAMBI Mulungu adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.[2] Dziko lapansi ndipo linali lopanda kanthu; ndipo mdima unali pamwamba pa nyanja; ndipo mzimu wa Mulungu unaliokufungatira pamwamba pa madzi.[3] Ndipo anati Mulungu, Kuyere; ndipo kunayera.[4] Ndipo anaona Mulungu kuti kuyerako kunali kwabino: ndipo Mulungu analekanitsa kuyera ndi mdima.[5] Ndipo Mulungu anacha kuyerako Usana, ndi mdimawo anaucha Usiku. Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku loyamba.[6] Ndipo anati Mulungu, Pakhale thambo pakati pa madzi, lilekanitse madzi ndi madzi.[7] Ndipo Mulungu anapanga thambo, nalekanitsa madzi anali pansi pa thambolo ndi madzi analf pamwamba pa thambolo: ndipo kunatero.

1 TIMOTEO 5:8
Koma ngati wina sadzisungiratu mbumba yace ya iye yekha, makamaka iwo a m'banja lace, wakana cikhulupiriro iye, ndipo aipa koposa wosakhulupira.

AGALATIYA 1:19
Koma wina wa atumwi sindinamuona, koma Yakobo mbale wa Ambuye.

MALAKI 1:11
Pakuti kuyambira koturukira dzuwa kufikira kolowera kwace dzina langa lidzakhala lalikuru mwa amitundu; ndipo m'malo monse adzaperekera dzina langa cofukiza ndi copereka coona; pakuti dzina langa lidzakhala lalikuru mwa amitundu, ati Yehova wa makamu.

GENESIS 2:7
Ndipo Yehova Mulungu anaumba munthu ndi dothi lapansi, nauzira mpweya wa moyo m'mphuno mwace; munthuyo nakhala wamoyo.

YOHANE 3:3-5
[3] Yesu anayankha nati kwa iye, Indetu, indetu, ndinena ndi iwe, Ngati munthu sabadwa mwatsopano, sakhoza kuona Ufumu wa Mulungu.[4] Nikodemoananena kwa iye, Munthu akhoza bwanji kubadwa atakalamba? Kodi akhoza kulowanso m'mimba ya amace ndi kubadwa?[5] Yesu anayankha, Indetu, indetu, ndinena ndi iwe, Ngati munthu sabadwa mwa madzi ndi Mzimu, sakhoza kulowa ufumu wa Mulungu.

AHEBRI 12:14
Londolani mtendere ndi anthu onse, ndi ciyeretso cimene, akapanda ici, palibe mmodzi adzaona Ambuye:

CHIVUMBULUTSO 17:18
Ndipo mkaziyo unamuona, ndiye mudzi waukuru, wakucita ufumu pa mafumu a dziko.

MATEYU 16:18
Ndiponso Ine ndinena kwa iwe, kuti iwe ndiwe Petro, ndipo pa thanthwe ili ndidzakhazika Mpingo wanga; ndipo makomo a dziko la akufa sadzaulaka uwo.

GENESIS 1:1
PACIYAMBI Mulungu adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.

EKSODO 15:3
Yehova ndiye wankhondo; Dzina lace ndiye Yehova.

CHIVUMBULUTSO 17:9
Pano pali mtima wakukhaia nayo nzeru. Mitu isanu ndi iwiri ndiyo mapiri asanu ndi awiri amene mkazi akhalapo;

AFILIPI 4:6-7
[6] Musadere nkhawa konse; komatu m'zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi ciyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu.[7] Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana cidziwitso conse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Kristu Yesu.

AGALATIYA 4:19
Tiana tanga, amene ndirikumvanso zowawa za kubala inu, kufikira Kristu aumbika mwa inu,

1 PETRO 3:15
koma mumpatulikitse Ambuye Kristu m'mitima yanu; okonzeka nthawi zonse kucita codzikanira pa yense wakukufunsani cifukwa ca ciyembekezo ciri mwa inu, komatu ndi cifatsondi mantha;

CHIVUMBULUTSO 17:1
Ndipo anadza mmodzi mwa angelo asanu ndi awiri akukhala nazo mbale zisanu ndi ziwiri, nalankhula ndi ine, nanena, Idza kuno, ndidzakuonetsa citsutso ca mkazi wacigololo wamkuru, wakukhala pa madzi ambiri,

MATEYU 18:15-18
[15] Ndipo ngati mbale wako akucimwira iwe, pita, numlangize pa nokha iwe ndi iye; ngati akumvera iwe, wambweza mbale wako.[16] Koma ngati samvera, onjeza kutenga ndi iwe wina mmodzi kapena awiri, kuti atsimikizidwe mau onse pakamwa pa mboni ziwiri kapena zitatu.[17] Ndipo ngati iye samvera iwo, uuze Mpingo; ndipo ngati iye samveranso Mpingowo, akhale kwa iwe monga wakunja ndi wamsonkho.[18] Indetu ndinena kwa inu, Ziri zonse mukazimanga pa dziko lapansi zidzakhala zomangidwa Kumwamba: ndipo ziri zonse mukazimasula pa dziko lapansi, zidzakhala zomasulidwa Kumwamba.

AEFESO 1:22-23
[22] ndipo 3 anakonza zonse pansi pa mapazi ace, nampatsa iye 4 akhale mutu pamtu pa zonse,[23] 5 kwa Eklesia amene ali thupi lace, 6 mdzazidwe wa iye amene adzazazonse m'zonse.

AEFESO 5:23
Pakuti mwamuna ndiye mutu wa mkazi, monganso Kristu ndiye mutu wa Eklesia, ali yekha Mpulumutsi wa thupilo.

MACHITIDWE A ATUMWI 4:32
Ndipo unyinji wa iwo akukhulupira anali wa mtima umodzi ndi moyo umodzi; ndipo sananena mmodzi kuti kanthu ka cuma anali naco ndi kace ka iye yekha; koma anali nazo zonse zodyerana.

1 AKORINTO 1:10
Koma ndikudandaulirani inu, abale, mwa dzina la Ambuye wathu Yesu Kristu, kuti munene cimodzimodzi inu nonse, ndi kuti pasakhale malekano pakati pa inu; koma mumangike mu mtima womwewo ndi m'ciweruziro comweco.

YOHANE 12:48
12 iye amene akaniza Ine, ndi kusalandira mau anga, ali naye womweruza iye; 13 mau amene ndalankhula, iwowa adzamweruza tsiku lomariza.

YOHANE 14:28
Mwamva kuti Ine ndinanena kwa inu, 6 Ndimuka, ndipo ndidza kwa inu. Mukadandikonda Ine, mukadakondwera kuti ndipita kwa Atate; 7 pakuti Atate ali wamkuru ndi Ine.

AHEBRI 1:14
Kodi siiri yonse mizimu yotumikira, yotumidwa kuti itumikire iwo amene adzalowa cipulumutso?

MATEYU 18:10
Yang'anirani kuti musanyoze mmodzi wa ang'ono awa; pakuti ndinena kwa inu, kuti angelo ao apenya cipenyere nkhope ya Atate wanga wa Kumwamba. [

AEFESO 6:12
Cifukwa kuti kulimbana kwathu sitilimbana nao mwazi ndi thupi, komatu nao maukulu, ndi maulamuliro, ndi akucita zolimbika a dziko lapansi a mdima uno, ndi a uzimu a coipa m'zakumwamba.

YOHANE 3:16
Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wace wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira iye asatayike, koma akhale nao moyo wosatha.

YOHANE 17:17
Patulani iwo m'coonadi; mau anu ndi coonadi.

CHIVUMBULUTSO 2:9
Ndidziwa cisautso cako, ndi umphawi wako (komatu uli wacuma), ndi mwano wa iwo akunena za iwo okha kuti ali Ayuda, osakhala Ayuda, komatu sunagoge wa Satana.

MASALIMO 68:5
Mulungu, mokhala mwace mayera, Ndiye Atate wa ana amasiye, ndi woweruza wa akazi amasiye.

MASALIMO 146:9
Yehova asunga alendo; Agwiriziza mwana wamasiye mkazi wamasiye; Koma akhotetsa njira ya oipa.

AGALATIYA 2:10
pokhapo kuti tikumbukile aumphawi; ndico comwe ndinafulumira kucicita.

AROMA 3:23
pakuti onse anacimwa, naperewera pa ulemerero wa Mulungu;

Chewa Bible (BL) 1992
Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society