A A A A A

Khalidwe Labwino: [Kulimba Mtima]


MACHITIDWE A ATUMWI 4:29-31
[29] Ndipo tsopano Ambuye, penyani mau ao akuopsa, ndipo patsani kwa akapolo anu alankhule mau anu ndi kulimbika mtima konse,[30] m'mene mutambasula dzanja lanu kukaciritsa; ndi kuti zizindikilo ndi zozizwa zicitidwe mwa dzina la Mwana wanu wopatulika Yesu.[31] Ndipo m'mene adapemphera iwo, panagwedezeka pamalo pamene adasonkhanirapo; ndipo anadzazidwa onse ndi Mzimu Woyera, nalankhula mau a Mulungu molimbika mtima.

2 AKORINTO 3:12
Pokhala naco tsono ciyembekezo cotere, tilankhula ndi kukhazikika mtima kwakukuru,

MACHITIDWE A ATUMWI 14:3
Cifukwa cace anakhala nthawi yaikuru nanenetsa zolimba mtima mwa Ambuye, amene anacitira umboni mau a cisomo cace, napatsa zizindikiro ndi zozizwa kuti zicitidwe ndi manja ao.

MACHITIDWE A ATUMWI 13:46
Ndipo Paulo ndi Bamaba analimbika mtima ponena, nati, 9 Kunafunika kuti mau a Mulungu ayambe alankhulidwe kwa inu. 10 Popeza muwakankha, nimudziyesera nokha osayenera moyo wosatha, taonani, titembenukira kwa amitundu.

MACHITIDWE A ATUMWI 19:8
Ndipo iye analowa m'sunagoge, nanena molimba mtima, miyezi itatu, natsutsana ndi kukopa kunena za Ufumu wa Mulungu.

FILEMONI 1:8
Momwemo, ndingakhale ndiri nako kulimbika mtima kwakukuru m'Kristu kukulamulira cimene ciyenera,

MACHITIDWE A ATUMWI 18:26
ndipo iye anayamba kulankhula molimba mtima m'sunagoge, koma pamene anamumva iye Priskila ndi Akula, anamtenga, namfotokozera njira ya Mulungu mosamalitsa.

MARKO 15:43
anadzapo Y osefe wa ku Arimateya, mkulu wa mirandu womveka, amene yekha analikuyembekezera Ufumu wa Mulungu; nalimba mtima nalowa kwa Pilato, napempha mtembo wace wa Yesu.

MACHITIDWE A ATUMWI 28:31
ndi kulalikira Ufumu wa Mulungu, ndi kuphunzitsa za Ambuye Yesu Kristu ndi kulimbika konse, wosamletsa munthu.

MACHITIDWE A ATUMWI 4:29-30
[29] Ndipo tsopano Ambuye, penyani mau ao akuopsa, ndipo patsani kwa akapolo anu alankhule mau anu ndi kulimbika mtima konse,[30] m'mene mutambasula dzanja lanu kukaciritsa; ndi kuti zizindikilo ndi zozizwa zicitidwe mwa dzina la Mwana wanu wopatulika Yesu.

MIYAMBO 28:1
Woipaathawapalibewomthamangitsa; Koma olungama alimba mtima ngati mkango.

GENESIS 18:23-32
[23] Ndipo Abrahamu anayandikira nati, Kodi mudzaononga olungama pamodzi ndi oipa?[24] Kapena alipo olungama makumi asanu m'kati mwa mudzi; kodi mudzaononga, simudzasiya malowa cifukwa ca olungama makumi asanu ali momwemo?[25] Musamatero ai, kupha olungama pamodzi ndi oipa, kuta olungama akhale monga oipa; musamatero ai; kodi sadzacita zoyenera woweruza wa dziko lonse lapansi?[26] Ndipo anati Yehova, Ndikapeza m'Sodomu olungama makumi asanu m'kati mwa mudzi, ndidzasiya malo onse cifukwa ca iwo.[27] Ndipo anayankha Abrahamu nati, Taonanitu, ndadziyesera kunena kwa Ambuye, ine ndine pfumbi ndi phulusa:[28] kapena akaperewera asanu pa olungama makumi asanuwo; kodi mudzaononga mudzi wonse cifukwa ca kuperewera asanu? Ndipo anati, Ndikapeza makumi anai ndi asanu sindidzauononga.[29] Ndipo ananenanso kwa iye nati, Kapena akapezedwa makumi anai m'menemo. Ndipo anati, Sindidzacita cifukwa ca makumi anai.[30] Ndipo anati, Asakwiyetu Ambuye, ndipo ndidzanenanso: kapena akapezedwa makumi atatu m'menemo? Ndipo anati, Ndikapeza makumi atatu m'menemo sindidzacita.[31] Ndipo anati, Taonanitu, ndadziyesera kunena kwa Ambuye: kapena akapezedwa makumi awiri m'menemo. Ndipo anati, Sindidzacita cifukwa ca makumi awiri.[32] Ndipo anati, Asakwiyetu Ambuye, ndipo ndidzanena kamodzi aka kokha: kapena akapezedwakhumim'menemo: Ndipo anati, Sindidzacita cifukwa ca khumi.

MASALIMO 138:3
Tsiku loitana ine, munandiyankha, Munandilimbitsa ndi mphamvu m'moyo mwanga.

AEFESO 3:12
amene tiri naye cokhazikika mtima ndi ciyandiko eolimbika, mwa cikhulupiriro ca pa iye.

YOHANE 4:17
Mkazi anayankha nati kwa iye, Ndiribe mwamuna. Yesu ananena naye, Wanena bwino, kuti mwamuna ndiribe;

AHEBRI 10:19
Ndipo pokhala naco, abale, cilimbikitso cakulowa m'malo opatulika, ndi mwazi wa Yesu,

AHEBRI 4:16
Potero tilimbike mtima poyandikira mpando wacifumu wacisomo, kuti tilandire cifundo ndi kupeza cisomo ca kutithandiza nthawi yakusowa.

AHEBRI 13:6
Kotero kuti tinena molimbika mtima, Mthandizi wanga ndiye Ambuye; smdidzaopa; Adzandicitira ciani munthu?

AEFESO 6:19-20
[19] ndi ine ndemwe, kuti andipatse mau m'kunditsegulira m'kamwa molimbika, kuti ndizindikiritse anthu cinsinsico ca Uthenga Wabwino,[20] cifukwa ca umene 1 ndiri mtumiki wa m'unyolo, kuti m'menemo ndikalankhule molimbika, monga ndiyenera kulankhula.

MACHITIDWE A ATUMWI 4:13
Koma pakuona kulimbika mtima kwa Petro ndi Yohane, ndipo pozindikira kuti ndiwo anthu osaphunzira ndi opulukira, anazizwa ndipo anawazindikira, kuti adakhala pamodzi ndi Yesu.

1 TIMOTEO 3:13
Pakuti iwo akutumikira bwino adzitengera okha mbiri yabwino, ndi kulimbika kwakukuru m'cikhulupiriro ca mwa Kristu Yesu.

1 ATESALONIKA 2:2
koma tingakhale tidamva zowawa kale, ndipo anaticitira cipongwe, monga mudziwa, ku Filipi, tinalimbika pakamwa mwa Mulungu wathu kulankhula ndi inu Uthenga Wabwino wa Mulungu m'kutsutsana kwambiri.

AFILIPI 1:20
monga mwa kulingiriritsa ndi ciyembekezo canga, kuti palibe cinthu cidzandicititsa manyazi, komatu mwa kulimbika mtima konse, monga nthawi yonse, tsopanonso Kristu adzakuzidwa m'thupi langa, kapena mwamoyo, kapena mwa imfa.

2 TIMOTEO 1:7
Pakuti Mulungu sanatipatsa mzimu wa mantha; komatu wa mphamvu ndi cikondi ndi cidziletso.

1 AKORINTO 16:13
Dikirani, cirimikani m'cikhulupiriro; dzikhalitseni amuna, limbikani.

MIYAMBO 14:26
Wakuopa Yehova akhulupirira kolimba; Ndipo ana ace adzakhala ndi pothawirapo.

MASALIMO 27:14
Yembekeza Yehova: Limbika, ndipo Iye adzalimbitsa mtima wako; Inde, yembekeza Yehova.

AROMA 1:16
Pakuti Uthenga Wabwino sundicititsa manyazi; pakuti uti mphamvu ya Mulungu yakupulumutsa munthu ali yense wakukhulupira; kuyambira Myuda, ndiponso Mhelene.

1 MBIRI 28:20
Ndipo Davide anati kwa Solomo mwana wace, Limbika, nulimbe mtima, nucicite; usaopa, kapena kutenga nkhawa; pakuti Yehova Mulungu, ndiye Mulungu wanga, ali nawe; sadzakusowa kapena kukutaya mpaka zitatha nchito zonse za utumiki wa nyumba ya Yehova.

1 AKORINTO 15:58
Cifukwa cace, abale anga okondedwa, 24 khalani okhazikika, osasunthika, akucuruka mu ncbitoya Ambuye, nthawi zonse, podziwa kuti kucititsa kwanu sikuli cabe mwa Ambuye.

AEFESO 6:10
Cotsalira, tadzilimbikani mwa Ambuye, ndi m'kulimba kwa mphamvu yace.

YESAYA 54:4
Usaope, pakuti sudzakhala ndi manyazi; usasokonezedwe, pakuti sudzacitidwa manyazi; pakuti udzaiwala manyazi a ubwana wako, ndi citonzo ca umasiye wako sudzacikumbukiranso.

YOHANE 14:27
4 Mtendere ndikusiyirani inu, mtendere wanga ndikupatsani; Ine sindikupatsani inu monga dziko lapansi lipatsa. 5 Mtima wanu usabvutike, kapena usacite mantha.

MARKO 5:36
Koma Yesu wosasamala mau olankhulidwawo, ananena kwa mkuru wa sunagoge, Usaope, khulupirira kokha.

AFILIPI 1:28
osaopa adani m'kanthu konse, cimene ciri kwa iwowa cisonyezo ca cionongeko, koma kwa inu ca cipulumutso, ndico ca kwa Mulungu;

YOHANE 7:26
ndipo taona amalankhula poyera, ndipo sanena kanthu kwa iye. Kapena kodi akuru adziwa ndithu kuti ndiye Kristu ameneyo?

MACHITIDWE A ATUMWI 5:29
Ndipo anayankha Petro ndi atumwi, nati, Tiyenera kumvera Mulungu koposa anthu.

YOSWA 1:7
Komatu khala wamphamvu, nulimbike mtima kwambiri, kuti usamalire kucita monga mwa cilamulo conse anakulamuliraco Mose mtumiki wanga; usacipambukire ku dzanja lamanja kapena kulamanzere, kuti ukacite mwanzeru kuli konse umukako.

EZEKIELE 3:9
Ndalimbitsa mutu wako woposa mwala wolimbitsitsa, usawaopa kapena kutenga nkhawa pamaso pao; pakuti iwo ndiwo nyumba yopanduka.

MACHITIDWE A ATUMWI 9:29
nanena molimbika mtima m'dzina la Ambuye; ndipotu analankhula natsutsana ndi Aheleniste; koma anayesayesa kumupha iye.

AFILIPI 1:1
PAULO ndi Timoteo, akapolo a Yesu Kristu, kwa oyera mtima onse mwa Kristu Yesu, akukhala ku Filipi, pamodzi ndi oyang'anira ndi atumiki:

1 TIMOTEO 3:1
Mauwa ali okhulupirika, ngati munthu akhumba udindo wa woyang'anira, aifuna nchito yabwino.

1 AKORINTO 3:12
Koma ngati wina amanga pa mazikowo, golidi, siliva, miyala va mtengo wace, mtengo, maudzu, dziputu,

AHEBRI 10:1
mthunzi wa zokoma zirinkudza, osati cifaniziro ceni ceni ca zinthuzo, sicikhozatu, ndi nsembe zomwezi caka ndi caka, zimene azipereka kosalekeza, kuwayesera angwiro iwo akuyandikira.

1 PETRO 5:10
Ndipo Mulungu wa cisomo conse, amene adakuitanani kulowa ulemerero wace wosatha mwa Kristu, mutamva zowawa kanthawi, adzafikitsa inu opanda cirema mwini wace, adzakhazikitsa, adzalimbikitsa inu.

Chewa Bible (BL) 1992
Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society