A A A A A

Good Character: [Sanctification]


2 ATESALONIKA 2:13
Koma tiyenera ife tiziyamika Mulungu nthawi zonse cifukwa: ca inu, abale okondedwa ndi Ambuye, kuti Mulungu anakusankhani inu kuyambira paciyambi, mulandire cipulumutso mwa ciyeretso ca Mzimu ndi cikhulupiriro ca coonadi;

2 TIMOTEO 2:21
Ngati tsono munthu adziyeretsa yekha pa izi, adzakhala cotengera ca kuulemu, copatulidwa, coyenera kucita naco Mbuye, cokonzera nchito yonse yabwino.

MACHITIDWE A ATUMWI 26:18
kukawatsegulira maso ao, kuti atembenuke kucokera kumdima, kulinga kukuunika, ndi kucokera ulamuliro wa Satana kulinga kwa Mulungu, kuti alandire iwo cikhululukiro ca macimo, ndi colowa mwa iwo akuyeretsedwa ndi cikhulupiriro ca mwa Ine.

AKOLOSE 2:11
amenenso munadulidwa mwa iye ndi mdulidwe wosacitika ndi manja, m'mabvulidwe a thupi, mu mdulidwe wa Kristu;

AKOLOSE 3:1-5
[1] Cifukwa cace ngati munaukitsidwa pamodzi ndi Kristu, funani zakumwamba, kumene kuli Kristu wokhala pa dzanja lamanja la Mulungu.[2] Lingalirani zakumwamba osati za padziko ai.[3] Pakuti munafa, ndipo moyo wanu wabisika pamodzi ndi Kristu mwa Mulungu,[4] Pamene Kristu adzaoneka, ndiye moyo wathu, pamenepo inunso mudzaonekera pamodzi ndi iye m'ulemerero.[5] Cifukwa cace fetsani ziwalozo ziri padziko; dama, cidetso, cifunitso ca manyazi, cilakolako coipa, nelicisiriro, cimene ciri kupembedza mafano;

AEFESO 1:13
Mwa Iyeyo inunso, mutamva mau a coonadi, Uthenga Wabwino wa cipulumutso canu; ndi kumkhulupirira iye, munasindikizidwa cizindikilo ndi Mzimu Woyera wa lonjezano,

EKSODO 13:2
Ndipatulire Ine yense woyamba kubadwa, wotsegulira pa amace mwa ana a Israyeli, mwa anthu ndi mwa zoweta; ndiwo anga.

EKSODO 31:13
Koma iwe, lankhula ndi ana a Israyeli, ndi kuti, Muzisunga masabata anga ndithu; pakuti ndiwo cizindikilo pakati pa Ine ndi inu mwa mibadwo yanu; kuti mudziwe kuti Ine ndine Yehova wakukupatulani.

AGALATIYA 2:20
Ndinapacikidwa ndi Kristu; koma ndiri ndi mayo; wosatinso ine ai, koma Kristu ali ndi moyo mwa ine; koma moyo umene ndiri nao: tsopano m'thupi, ndiri nao m'cikhulupiriro ca Mwana wa Mulungu, amene anandikonda, nadzipereka yekha cifukwa ca ine.

AHEBRI 2:11
Pakuti iye wakuyeretsa ndi iwo akuyeretsedwa acokera onse mwa mmodzi; cifukwa ca ici alibe manyazi kuwacha iwo abale,

AHEBRI 9:14
koposa kotani nanga mwazi wa Kristu amene anadzipereka yekha wopanda cirema kwa Mulungu mwa Mzimu wosatha, udzayeretsa cikumbu mtima canu kucisiyanitsa ndi nchito zakufa, kukatumikira Mulungu wamoyo?

AHEBRI 10:10-14
[10] Ndi cifuniro cimeneco tayeretsedwa mwa copereka ca thupi la Yesu Kristu, kamodzi, kwatha.[11] Ndipotu wansembe ali yenseamaima tsiku ndi tsiku, natumikira, napereka nsembe zomwezi kawiri kawiri, zimene sizikhoza konse kucotsa macimo;[12] koma iye, m'mene adapereka nsembe imodzi cifukwa ca macimo, anakhala pa dzanja lamanja la Mulungu cikhalire;[13] kuyambira pomwepo alindirira, kufikira adani ace aikidwa akhale mpando ku mapazi ace.[14] Pakuti ndi cipereko cimodzi anawayesera angwiro cikhalire iwo oyeretsedwa.

AHEBRI 12:10-14
[10] Pakutitu iwo anatilanga masiku owerengeka monga kudawakomera; koma iye atero, kukatipindulitsa, kuti tikalandirane nao pa ciyero cace.[11] Chango ciri conse, pakucitika, sicimveka cokondwetsa, komatu cowawa; koma citatha, cipereka cipatso ca mtendere, kwa iwo ozoloweretsedwa naco, ndico ca cilungamo.[12] Mwa ici limbitsani manja ogooka, ndi maondo olobodoka;[13] ndipo lambulani miseu yolunjika yoyendamo mapazi anu, kuti cotsimphinaco cisapatulidwe m'njira, koma ciciritsidwe.[14] Londolani mtendere ndi anthu onse, ndi ciyeretso cimene, akapanda ici, palibe mmodzi adzaona Ambuye:

AHEBRI 13:12
Mwa ici Yesunso, kuti akayeretse anthuwo mwa mwazi wa iye yekha, adamva cowawa kunja kwa cipata.

1 AKORINTO 1:2
kwa Mpingo wa Mulungu wakukhala m'Korinto, ndiwo oyeretsedwa mwa Kristu Yesu, oitanidwa akhale oyera mtima, pamodzi ndi onse akuitana pa dzina la Ambuye wathu Yesu Kristu, m'malo monse, ndiye wao, ndi wathu:

1 AKORINTO 6:11
Ndipo ena ainu munali otere; koma munasambitsidwa, koma munayeretsedwa, koma munayesedwa olungama, m'dzina la Ambuye Yesu Kristu, ndi mwa Mzimu wa Mulungu wathu.

1 YOHANE 1:9
Ngati tibvomereza macimo athu, ali wokhulupirika ndi wolungama iye, kuti atikhululukire macimo athu, ndi kutisambitsa kuticotsera cosalungama ciri conse.

1 YOHANE 3:9
Yense wobadwa kucokera mwa Mulungu sacita cimo, cifukwa mbeu yace ikhala mwa iye; ndipo sakhoza kucimwa, popeza wabadwa kucokera mwa Mulungu.

1 PETRO 1:2
monga mwa kudziwiratu kwa Mulungu Atate, m'ciyeretso ca Mzimu, cocitira cimvero, ndi kuwaza kwa mwazi wa Yesu Kristu: Cisomo, ndi mtendere zicurukire inu.

1 ATESALONIKA 4:3
Pakuti ici ndi cifuniro ca Mulungu, ciyeretso canu, kuti mudzipatule kudama;

1 ATESALONIKA 5:23
Ndipo Mulungu wa mtendere yekha ayeretse inu konsekonse; ndipo mzimu wanu ndi moyo wanu ndi thupi lanu zisungidwe zamphumphu, zopanda cirema pa kudza kwace kwa: Ambuye wathu Yesu Kristu.

2 AKORINTO 5:17
Cifukwa cace ngati munthu ali yense ali mwa Kristu ali wolengedwa watsopano; zinthu zakale zapita, taonani, zakhala zatsopano,

1 ATESALONIKA 4:3
Pakuti ici ndi cifuniro ca Mulungu, ciyeretso canu, kuti mudzipatule kudama;

1 ATESALONIKA 5:23
Ndipo Mulungu wa mtendere yekha ayeretse inu konsekonse; ndipo mzimu wanu ndi moyo wanu ndi thupi lanu zisungidwe zamphumphu, zopanda cirema pa kudza kwace kwa: Ambuye wathu Yesu Kristu.

2 AKORINTO 5:17
Cifukwa cace ngati munthu ali yense ali mwa Kristu ali wolengedwa watsopano; zinthu zakale zapita, taonani, zakhala zatsopano,

2 AKORINTO 12:21
kuti pakudzanso ine, Mulungu wanga angandicepse pa inu, ndipo ndingalirire ambiri 1 a iwo amene adacimwa kale, osalapa pa codetsa, ndi cigololo, ndi kukhumba zonyansa zimene anacita.

YOHANE 17:17-19
[17] Patulani iwo m'coonadi; mau anu ndi coonadi.[18] Monga momwe munandituma Ine ku dziko lapansi, Inenso ndinatuma iwo ku dziko lapansi,[19] Ndipo cifukwa ca iwo Ine ndidzipatula ndekha kuti iwonso akhale opatulidwa m'coonadi.

AFILIPI 1:6
pokhulupira pamenepo, kuti iye amene anayamba mwa inu nchito yabwino, adzaitsiriza kufikira tsiku la Yesu Kristu;

AFILIPI 2:13
pakuti wakucita mwa inu kufuna ndi kucita komwe, cifukwa ca kukoma mtima kwace, ndiye Mulungu,

AROMA 6:6
podziwa ici, kuti umunthu wathu wakale unapacikidwa pamodzi ndi iye, kuti thupilo la ucimo likaonongedwe, kuti ife tisakhalenso akapolo a ucimo;

AROMA 15:16
kuti ndikhale mtumiki wa Yesu Kristu kwa anthu amitundu, wakutumikira Uthenga Wabwino wa Mulungu, kuti kupereka kwace kwa anthu amitundu kulandirike, koyeretsedwa ndi Mzimu Woyera.

2 PETRO 1:2-4
[2] Cisomo kwa inu ndi mtendere zicurukitsidwe m'cidziwitso ca Mulungu ndi Yesu Ambuye wathu.[3] Popeza mphamvu ya umulungu wace idatipatsa ife zonse za pamoyo ndi cipembedzo, mwa cidziwitso ca iye amene adatiitana ife ndi ulemerero ndi ukoma wace wa iye yekha;[4] mwa izi adatipatsa malonjezano a mtengo wace ndi akuru ndithu; kuti mwa izi mukakhale oyanjana nao umulungu wace, mutapulumuka ku cibvundi ciri pa dziko lapansi m'cilakolako.

1 ATESALONIKA 4:3-5
[3] Pakuti ici ndi cifuniro ca Mulungu, ciyeretso canu, kuti mudzipatule kudama;[4] yense wa inu adziwe kukhala naco cotengera cace m'ciyeretso ndi ulemu,[5] kosati m'eiliro ca cilakolako conyansa, monganso amitundu osadziwa Mulungu;

YOHANE 15:1-4
[1] Ine ndine mpesa weniweni, ndipo Atate wanga ndiye wam'munda.[2] Nthambi iri yonse ya mwa Ine yosabala cipatso, aicotsa; ndi iri y'onse yakubala cipatso, aisadza, kuti ikabale cipatso cocuruka.[3] Mwakhala okonzeka tsopano inu cifukwa ca mau amene ndalankhula ndi inu,[4] Khalani mwa Ine, ndi Ine mwa inu. Monga nthambi siingathe kubala cipatso pa yokha, ngati siikhala mwampesa; motere mulibe inunso ngati simukhala mwa Ine.

AROMA 6:1-23
[1] Cifukwa cace tidzatani? Tidzakhalabe m'ucimo kodi, kuti cisomo cicuruke?[2] Msatero ai. Ife amene tiri akufa ku ucimo, tidzakhala bwanji cikhalire m'menemo?[3] Kapena kodi simudziwa kuti ife tonse amene tinabatizidwa mwa Kristu Yesu; tinabatizidwa mu imfa yace?[4] Cifukwa cace tinaikldwa m'manda pamodzi ndi iye mwa ubatizo kulowa muimfa; kuti monga Kristu anaukitsidwa kwa akufa mwa ulemerero wa Atate, cotero ifenso tikayende m'moyo watsopano.[5] Pakuti ngati ife tinakhala olumikizidwa ndi iye m'cifanizidwe ca imfa yace, koteronso tidzakhala m'cifani'Zidwe ca kuuka kwace;[6] podziwa ici, kuti umunthu wathu wakale unapacikidwa pamodzi ndi iye, kuti thupilo la ucimo likaonongedwe, kuti ife tisakhalenso akapolo a ucimo;[7] pakuti iye amene anafa anamasulidwa kuucimo.[8] Koma ngati ife tinafa ndi Kristu, tikhulupirira kuti tidzakhalanso amoyo ndi iye;[9] podziwa kuti Kristu anaukitsidwa kwa akufa, sadzafanso; imfa siicitanso ufumu pa Iye.[10] Pakuti pakufa iye, atafa ku ucimo kamodzi; ndipo pakukhala iye wamoyo, akhala wamoyo kwa Mulungu.[11] Cotero inunso mudziwerengere inu nokha ofafa ku ucimo, koma amoyo kwa Mulungu mwa Kristu Yesu.[12] Cifukwa cace musamalola ucimo ucite ufumu m'thupi lanu la imfa kumvera zofuna zace:[13] ndipo musapereke ziwalo zanu kuucimo, zikhale zida za cosalungama; koma mudzipereke inu nokha kwa Mulungu, monga amoyo ataturuka mwa akufa, ndi ziwalo zanu kwa Mulungu zikhale zida za cilungamo,[14] Pakuti ucimo sudzacita ufumu pa inu; popeza simuli a lamulo koma a cisomo.[15] Ndipo ciani tsono? Tidzacimwa kodi cifukwa sitiri a lamulo, koma a cisomo? Msatero ai.[16] Kodi simudziwa kuti kwa iye amene mudzipereka eni nokha kukhala akapolo ace akumvera iye, mukhalatu akapolo ace a yemweyo mulikumvera iye; kapena a ucimo kulinga kuimfa, kapena a umvero kulinga kucilungamo?[17] Koma ayamikidwe Mulungu, kuti ngakhale mudakhala akapolo a ucimo, tsopano mwamvera ndi mtima makhalidwe aja a ciphunzitso cimene munaperekedweraco;[18] ndipo pamene munamasulidwa kuucimo, munakhala akapolo a cilungamo,[19] Ndilankhula manenedwe a anthu, cifukwa ca kufoka kwa thupi lanu; pakuti monga inu munapereka ziwalo zanu zikhale akapolo a conyansa ndi a kusayeruzika kuti zicite kusayeruzika, inde kotero tsopano perekani ziwalo zanu zikhale akapolo a cilungamo kuti zicite ciyeretso.[20] Pakuti pamene inu munali aka polo a ucimo, munali osatumikira cilungamo.[21] Ndipo munali nazo zobala zanji nthawi ija, m'zinthu zimene mucita nazo manyazi tsopano? pakuti cimariziro ca zinthu izi ciri imfa.[22] Koma tsopano, pamene munamasulidwa kuucimo, ndi kukhala akapolo a Mulungu, muli naco cobala canu cakufikira ciyeretso, ndi cimariziro cace moyo wosatha.[23] Pakuti mphotho yace ya ucimo ndi imfa; koma mphatso yaulere ya Mulungu ndiyo moyo wosatha wa mwa Kristu Yesu Ambuye wathu.

Chewa Bible (BL) 1992
Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society