A A A A A

Good Character: [Patience]


1 AKORINTO 13:4
Cikondi cikhala cilezere, ciri cokoma mtima; cikondi sicidukidwa; cikondi sicidziwa kudzitamanda, sicidzikuza,

AFILIPI 4:6
Musadere nkhawa konse; komatu m'zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi ciyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu.

MLALIKI 7:9
Usakangaze mumtima mwako kukwiya; pakuti mkwiyo ugona m'cifuwa ca zitsiru.

AROMA 12:12
kondwerani m'ciyembekezo, pirirani m'masautso; limbikani cilimbikire m'kupemphera,

AEFESO 4:2
ndi kuonetsera kudzicepetsa konse, ndi cifatso, ndi kuonetsera cipiriro, ndi kulolerana wina ndi mnzace, mwa cikondi;

AGALATIYA 6:9
Koma tisaleme pakucita zabwino pakuti pa nyengo yace tidzatuta tikapanda kufoka.

GENESIS 29:20
Ndipo Yakobo anamtumikira zaka zisanu ndi ziwiri cifukwa ca Rakele; koma zidamuonekera iye ngati masiku owerengeka cifukwa ca cikondi cimene anamkonda iye naco.

MIYAMBO 15:18
Munthu wozaza aputa makani; Koma wosakwiya msanga atonthoza makangano.

YEREMIYA 29:11
Pakuti ndidziwa malingiriro amene ndilingiririra inu, ati Yehova, malingiriro a mtendere, si a coipa, akukupatsani inu adzukulu ndi ciyembekezero.

1 SAMUELE 13:8-14
[8] Ndipo iye anatsotsa masiku asanu ndi awiri, monga nthawi anampanga Samueli; koma Samueli sanafika ku Giligala, ndipo anthu anabalalika namsiya Sauli.[9] Pamenepo Sauli anati, Andipatsire kuno nsembe yopsereza, ndi nsembe zoyamika. Ndipo iye anapereka nsembe yopserezayo.[10] Ndipo kunali kuti pakutsiriza iye kupereka nsembe yopserezayo, pomwepo, onani, Samueli anafika. Ndipo Sauli anamcingamira kukamlankhula iye.[11] Ndipo Samueli anati, Mwacitanji? Nati Sauli, Cifukwa ndinaona kuti anthuwo alinkubalalika kundisiya ine, ndi kuti inu simunafika masiku aja tinapangana, ndi kuti Afilisti anasonkhana ku Mikimasi;[12] cifukwa cace ndinati, Afilisti adzatitsikira pane pa Giligala, ndisanapembedze Yehova; potero ndinadzifulumiza, ndi kupereka nsembe yopsereza.[13] Ndipo Samueli ananena ndi Sauli, Munacita kopusa; simunasunga lamulo la Yehova Mulungu wanu, limene iye anakulamulirani; mwenzi Yehova atakhazikitsa nthawi yino ufumu wanu, ukhale pa Israyeli nthawi yosatha.[14] Koma tsopano ufumu wanu sudzakhala cikhalire; Yehova wadzifunira munthu wa pamtima pace; ndipo Yehova wamuika iye akhale mtsogoleri wa anthu ace, cifukwa inu simunasunga cimene Yehova anakulamulirani.

LUKA 15:11-24
[11] Ndipo iye anati, Munthu wina anali ndi ana amuna awiri;[12] ndipo wamng'onoyo anati kwa atate wace, Atate, ndigawirenitu zanga za pa cuma canu. Ndipo iye anawagawira za moyo wace.[13] Ndipo pakupita masiku owerengekamwana wamng'onoyo anasonkhanitsa zonse, napita ulendo wace ku dziko lakutari; ndipo komweko anamwaza cuma cace ndi makhalidwe a citayiko.[14] Ndipo pamene anatha zace zonse, panakhala njala yaikuru m'dziko muja, ndipo iye anayamba kusowa.[15] Ndipo anamuka nadziphatikiza kwa mfulu imodzi ya dziko lija; ndipo uyu anamtumiza kubusa kwace kukaweta nkhumba.[16] Ndipo analakalaka kukhutitsa mimba yace ndi makoko amene nkhumba rimadya, ndipo palibe munthu anamninkha kanthu.[17] Koma m'mene anakumbukila mumtima, anati, Anchito olipidwa ambiri a atate wanga ali naco cakudya cocuruka, ndipo ine ndionongeke kuno ndi njala?[18] Ndidzanyamuka ndipite kwa atate wanga, ndipo ndidzanena nave, Atate, ndinacimwira Kumwamba ndi pamaso panu;[19] sindiyeneranso konse kuchulidwa mwana wanu; mundiyese ine ngati mmodzi wa anchito anu.[20] Ndipo iye ananyamuka, nadza kwa atate wace. Koma pakudza iye kutali, atate wace anamuona, nagwidwa cifundo, nathamanga, namkupatira pakhosi pace, nampsompsonetsa.[21] Ndipo mwanayo anati kwa iye, Atate ndinacimwira Kumwamba ndi pamaso panu, sindiyeneranso konse kuchulidwa mwana wanu.[22] Koma atateyo ananena kwaakapolo ace, Turutsani msanga mwinjiro wokometsetsa, nimumbveke; ndipo mpatseni phete ku dzanja lace ndi nsapato ku apazi ace;[23] ndipo idzani naye mwana wa ng'ombe wonenepa, mumuphe, ndipo tidye, tisekere;[24] cifukwa mwana wanga uyu anali wakufa, ndipo akhalanso wamoyo; anali wotayika, ndipo wapezedwa. Ndipo anayamba kusekera.

MASALIMO 37:7-9
[7] Khala cete mwa Yehova, numlindirire Iye: Usabvutike mtima cifukwa ca iye wolemerera m'njira yace, Cifukwa ca munthu wakucita ciwembu.[8] Leka kupsa mtima, nutaye mkwiyo: Usabvutike mtima ungacite coipa,[9] Pakuti ocita zoipa adzadulidwa: Koma iwo akuyembekeza Yehova, iwowa adzalandira dziko lapansi.

AROMA 8:24-30
[24] Pakuti ife tinapolumutsidwa ndi ciyembekezo; koma ciyembekezo cimene cioneka si ciri ciyembekezo ai; pa kuti ayembekezera ndani cimene acipenya?[25] Koma ngati tiyembekezera cimene: siticipenya, pomwepo ticilindirira ndi cipiriro.[26] Ndipo momwemonso Mzimu athandiza kufoka kwathu; pakuti cimene tizipempha monga ciyenera, sitidziwa; koma Mzimu mwiniatipempherera ndi zobuula zosatheka kuneneka;[27] ndipo iye amene asanthula m'mitima adziwa cimene acisamalira Mzimu, cifukwa apempherera oyera mtima monga mwa cifuno ca Mulungu.[28] Ndipo tidziwa kuti amene akonda Mulungu zinthu zonse zithandizana kuwacitira ubwino, ndiwo amene aitanidwa monga mwa kutsimikiza kwa mtima wace.[29] Cifukwa kuti iwo 1 amene iye anawadziwiratu, 2 iwowa anawalamuliratu 3 afanizidwe ndi cifaniziro ca Mwana wace, kuti 4 iye akakhale mwana woyamba wa abale ambiri;[30] ndipo amene iye anawalamuliratu, iwo anawaitananso; ndimo iwo amene iye anawaitana, iwowa anawayesanso olungama; ndi iwo amene iye anawayesa olungama, 5 iwowa anawapatsanso olemerero.

2 ATESALONIKA 1:4-5
[4] kotero kuti ife tokha tidzitamandira za inu m'Mipingo ya Mulungu, cifukwa ca cipiriro canu, ndi cikhulupiriro canu, m'mazunzo anu onse ndi zisautsozo muzimva;[5] ndico citsimikizo ca ciweruziro colungama ca Mulungu; kuti mu-kawerengedwe oyenera ufumu wa Mulungu, umenenso mumvera zowawa;

AHEBRI 11:13-16
[13] Iwo onse adamwalira m'cikhulupiriro, osalandira malonjezano, komatu adawaona ndi kuwalankhula kutali, nabvomereza kuti ali alendo ndi ogonera padziko.[14] Pakuti wo akunena zotere aonetserapo kuti alikufuna dziko likhale lao.[15] Ndipotu akadakumbukila lijalo adaturukamo akadaona njira yakubwera nayo.[16] Koma tsopano akhumba lina loposa, ndilo la m'Mwamba; mwa ici Mulungu sacita manyazi nao poitanidwa Mulungu wao; pakuti adawakonzera mudzi.

GENESIS 29:20-28
[20] Ndipo Yakobo anamtumikira zaka zisanu ndi ziwiri cifukwa ca Rakele; koma zidamuonekera iye ngati masiku owerengeka cifukwa ca cikondi cimene anamkonda iye naco.[21] Ndipo Yakobo anati kwa Labani, Undipatse Ine mkazi wanga, cifukwa masiku anga atha, kuti ndilowe kwa iye.[22] Ndipo Labani anasonkhanitsa anthu onse a kumeneko nakonzera madyerero.[23] Ndipo panali madzulo Labani anatenga Leya mwana wace wamkazi, nadza naye kwa Yakobo, ndipo iye analowa kwa mkaziyo.[24] Ndipo Labani anampatsa mwana wace wamkazi Leya Zilipa mdzakazi wace kuti akhale mdzakazi wa Leya.[25] Ndipo panali m'mamawa, anaona kuti ndi Leya; ndipo anati kwa Labani, Ciani wandicitira ine? Kodi sindinakutumikira iwe cifukwa ca Rakele? wandinyenga ine bwanji?[26] Ndipo Labani anati, Satero kwathu kuno, kupatsa wamng'ono asanapatse wamkuru.[27] Umarize sabata lace la uyu, ndipo ndidzakupatsa uyonso cifukwa ca utumiki umene udzanditumikirawo kuonjezera zaka zina zisanu ndi ziwiri.[28] Yakobo ndipo anacita cotero namariza sabata lace; ndipo Labani anampatsa iye Rakele mwana wace wamkazi kuti akwatire iyenso.

2 SAMUELE 5:4-5
[4] Davide anali ndi zaka makumi atatu polowa iye ufumu wace, nakhala mfumu zaka makumi anai.[5] Ku Hebroni anacita ufumu pa Yuda zaka zisanu ndi ziwiri kudza miyezi isanu ndi umodzi; ndi ku Yerusalemu anacita ufumu pa Aisrayelionse ndi Ayuda omwe zaka makumi atatu mphambu zitatu.

MASALIMO 75:2
Pakuona nyengo yace ndidzaweruza molunjika.

HABAKUKU 2:3
Pakuti masomphenyawo alindira nyengo yoikidwiratu, ndipo afulumirira potsirizira pace, osanama; akacedwa uwalindirire; popeza afika ndithu, osazengereza.

AROMA 5:2-4
[2] amene ife tikhoza kulowa naye ndi cikhulupiriro m'cisomo ici m'mene tirikuunamo; ndipo tikondwera m'ciyembekezo ca ulemerero wa Mulungu.[3] Ndipo si cotero cokha, komanso tikondwera m'zisautso; podziwa ife kuti cisautso cicita cipiriro; ndi cipiriro cicita cizolowezi;[4] ndi cizolowezi cicita ciyembekezo:

CHIVUMBULUTSO 6:9-11
[9] Ndipo pamene adamasula cizindikilo cacisanu, ndinaona pansi pa guwa la nsembe mizimu ya iwo adaphedwa cifukwa ca mau a Mulungu, ndi cifukwa ca umboni umene anali nao:[10] ndipo anapfuula ndi mau akulu, ndi kunena, Kufikira liti, Mfumu yoyera ndi yoona, muleka kuweruza ndi kubwezera cilango cifukwa ca mwazi wathu, pa iwo akukhala padziko?[11] Ndipo anapatsa yense wa iwo mwinjiro woyera; nanena kwa iwo, kuti apumulebe kanthawi, kufikira atakwaniranso akapolo anzao, ndi abale ao amene adzaphedwa monganso iwo eni.

Chewa Bible (BL) 1992
Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society