A A A A A

Good Character: [Mercy]


2 SAMUELE 24:14
Ndipo Davide ananena ndi Gadi, Ndipsinjika mtima kwambiri, tigwe m'dzanja la Yehova; pakuti zifundo zace nzazikuru; koma tisagwe m'dzanja la munthu.

MASALIMO 86:5
Pakuti fnu, Ambuye, ndinu wabwino, ndi wokhululukira, Ndi wa cifundo cocurukira onse akuitana Inu.

MASALIMO 145:9
Yehova acitira cokoma onse; Ndi nsoni zokoma zace zigwera nchito zace zonse.

LUKA 6:36
Khalani inu acifundo monga Atate wanu ali wacifundo. Ndipo musamaweruza, ndipo simudzaweruzidwa.

AEFESO 2:4
koma Mulungu, wolemera cifundo, cifukwa ca cikondi cace cacikuru cimene anatikonda naco,

TITO 3:5
zosati zocokera m'nchito za m'cilungamo, zimene tidazicita ife, komatu monga mwa cifundo cace anatipulumutsa ife, mwa kutsuka kwa kubadwanso ndi makonzedwe a Mzimu Woyera,

AHEBRI 4:16
Potero tilimbike mtima poyandikira mpando wacifumu wacisomo, kuti tilandire cifundo ndi kupeza cisomo ca kutithandiza nthawi yakusowa.

1 YOHANE 1:3
cimene tidaciona, ndipo tidacimva, tikulatikirani inunso, kuti inunso mukayaniane pamodzi ndi ife; ndipo ciyanjano cathu cirinso ndi Atate, ndipo ndi Mwana wace Yesu Kristu;

Chewa Bible (BL) 1992
Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society