A A A A A

Good Character: [Modesty]


1 AKORINTO 12:23
ndipo zimene tiziyesa Zocepa ulemum'thupi, pa izi tiika ulemu wocuruka woposa; ndi zinthu zosakoma zikhala naco cokometsera coposa,

1 TIMOTEO 2:8-10
[8] Cifukwa cace ndifuna kuti amunawo apemphere pamalo ponse, ndi kukweza manja oyera, opanda mkwiyo ndi makani.[9] Momwemonso, akazi adzibveke okha ndi cobvala coyenera, ndi manyazi, ndi cidziletso; osati ndi tsitsi lace loluka, ndi golidi kapena ngale, kapena maraya a mtengo wace wapatali;[10] komatu (umo mokomera akazi akubvomereza kulemekeza Mulungu), mwa nchito zabwino.

1 PETRO 3:3-4
[3] Amene kukometsera kwanu kusakhale kwa kunja, kuluka tsitsi ndi kubvala za golidi, kapena kubvala cobvala;[4] koma kukhale munthu wobisika wamtima, m'cobvala cosaola ca mzimu wofatsa ndi wacete, ndiwo wa mtengo wace wapatali pamaso pa Mulungu.

AROMA 12:2
Ndipo musafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano: koma mukhale osandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wanu, kuti mukazindikire cimene ciri cifuno ca Mulungu, cabwino, ndi cokondweretsa, ndi cangwiro.

MATEYU 5:28
koma Ine ndinena kwa inu, kuti yense wakuyang'ana mkazi kumkhumba, pamenepo watha kucita naye cigololo mumtima mwace.

DEUTERONOMO 22:5
Mkazi asabvale cobvala ca mwa muna, kapena mwamuna asabvale cobvala ca mkazi; pakuti ali yense wakucita izi Yehova Mulungu wanu anyansidwa naye.

1 PETRO 3:3
Amene kukometsera kwanu kusakhale kwa kunja, kuluka tsitsi ndi kubvala za golidi, kapena kubvala cobvala;

1 SAMUELE 16:7
Koma Yehova ananena ndi Samueli, Vsayang'ane nkhope yace, kapena kutalika kwa msinkhu wace, popeza Ine ndinamkana iye; pakuti Yehova saona monga aona munthu; pakuti munthu ayang'ana cooneka ndi maso, koma Yehova ayang'ana mumtima.

1 AKORINTO 6:19-20
[19] Kapena simudziwa kuti thupi lanu liri kacisi wa Mzimu Woyera, amene ali mwa inu, amene muli naye kwa Mulungu? Ndipo simukhala a inu nokha.[20] Pakuti munagulidwa ndi mtengo wace wapatali; cifukwa cace lemekezani Mulungu m'thupi lanu.

1 AKORINTO 10:31
Cifukwa cace 2 mungakhale mudya, mungakhale mumwa, mungakhale mucita kanthu kena, citani zonse ku ulemerero wa Mulungu.

MIYAMBO 7:10
Ndipo taona, mkaziyo anamcingamira, Atabvala zadama wocenjera mtima,

MIYAMBO 31:30
Kukongola kungonyenga, maonekedwe okoma ndi cabe; Koma mkazi woopa Yehova adzatamandidwa.

1 TIMOTEO 3:2
Ndipo kuyenera woyang'anira akhale wopanda cirema, mwamuna wa mkazi mmodzi, wodzisunga, wodziletsa, wolongosoka, wokonda kucereza alendo, wokhoza kuphunzitsa;

LUKA 17:1
Ndipo anati kwa ophunzira ace, Sikutheka kuti zolakwitsa zisadze; koma tsoka iye amene adza nazo.

MIYAMBO 11:22
Monga cipini cagolidi m'mphuno ya nkhumba, Momwemo mkazi wokongola wosasinkhasinkha bwino.

AEFESO 2:10
Pakuti ife ndife cipango cace, olengedwa mwa Kristu Yesu, kucita nchito zabwino, zimene Mulungu anazipangiratu, kuti tikayende m'menemo.

AROMA 14:13
Cifukwa cace risaweruzanenso wina mnzace; koma weruzani ici makamaka, kuti munthu asaike cokhumudwitsa pa njira ya mbale wace, kapena compunthwitsa.

1 PETRO 3:3-5
[3] Amene kukometsera kwanu kusakhale kwa kunja, kuluka tsitsi ndi kubvala za golidi, kapena kubvala cobvala;[4] koma kukhale munthu wobisika wamtima, m'cobvala cosaola ca mzimu wofatsa ndi wacete, ndiwo wa mtengo wace wapatali pamaso pa Mulungu.[5] Pakuti koteronso kale akazi oyera mtima, akuyembekezera Mulungu, anadzikometsera okha, namvera amuna ao a iwo okha;

1 PETRO 1:14
monga ana omvera osadzifanizitsanso ndi zilakolako zakale, pokhala osadziwa inu;

1 SAMUELE 9:21
Ndipo Sauli anayankha nati, Sindiri Mbenjamini kodi, wa pfuko laling'ono mwa Israyeli? Ndiponso banja lathu nlocepa pakati pa mabanja onse a pfuko la Benjamini? Potero mulankhula bwanji mau otere ndi ine?

ESTERE 1:11-12
[11] abwere naye Vasiti mkazi wamkuru pamaso pa mfumu ndi korona wacifumu, kuonetsa anthu ndi akuru kukoma kwace; popeza anali wokongola maonekedwe ace.[12] Koma Vasiti mkazi wamkuruyo anakana kudza pa mau a mfumu adamuuza adindowo; potero mfumu idapsa mtima ndithu, ndi mkwiyo wace unatentha m'kati mwace.

YOBU 32:4-7
[4] Ndipo Elihu analindira kulankhula ndi Yobu, popeza akulu misinkhu ndi iwowa.[5] Koma pakuona Elihu kuti anthu atatuwa anasowa poyankha pakamwa pao anapsa mtima.[6] Ndipo Elihu mwana wa Barakeli wa ku Buzi anayankha, nati, Ine ndine mnyamata, inu ndinu okalamba; Cifukwa cace ndinadziletsa, ndi kuopa kukuonetsani monga umo ndayesera ine.[7] Ndinati, Amisinkhu anene, Ndi a zaka zocuruka alangize nzeru.

1 PETRO 3:1-4
[1] Momwemonso, akazi inu, mverani amuna anu ainu nokha; kuti, ngatinso ena samvera mau, akakodwe opanda mau mwa mayendedwe a akazi;[2] pakuona mayendedwe anu oyera ndi kuopa kwanu.[3] Amene kukometsera kwanu kusakhale kwa kunja, kuluka tsitsi ndi kubvala za golidi, kapena kubvala cobvala;[4] koma kukhale munthu wobisika wamtima, m'cobvala cosaola ca mzimu wofatsa ndi wacete, ndiwo wa mtengo wace wapatali pamaso pa Mulungu.

1 YOHANE 2:16
Pakuti ciri conse ca m'dziko lapansi, cilakolakoca thupi ndi cilakolako ca maso, matamandidwe a moyo, sizicokera kwa Atate, koma ku dziko lapansi.

AROMA 12:1
Cifukwa cace ndikupemphani inu, abale, mwa zifundo za Mulungu, kuti mupereke matupi anu nsembe yamoyo, yopatulika, yokondweretsa, Mulungu, ndiko kupembedza kwanu koyenera.

MIYAMBO 31:25
Abvala mphamvu ndi ulemu; Nangoseka nthawi ya m'tsogolo.

1 TIMOTEO 4:8
pakuti cizolowezi ca thupi cipindula pang'ono, koma cipembedzo cipindula zonse, popeza cikhala nalo Lonjezano la ku moyo uno, ndi la moyo ulinkudza.

AFILIPI 2:5
Mukhale nao mtima m'kati mwanu umene unalinso mwa Kristu Yesu,

1 PETRO 3:4
koma kukhale munthu wobisika wamtima, m'cobvala cosaola ca mzimu wofatsa ndi wacete, ndiwo wa mtengo wace wapatali pamaso pa Mulungu.

1 TIMOTEO ۲:۱۰
komatu (umo mokomera akazi akubvomereza kulemekeza Mulungu), mwa nchito zabwino.

Chewa Bible (BL) 1992
Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society