A A A A A

Good Character: [Love]


1 AKORINTO 16:14
Zanu zonse zicitike m'cikondi.

1 YOHANE 4:8-18
[8] iye wosakonda sazindikira Mulungu; cifukwa Mulungu ndiye cikondi.[9] Umo cidaoneka cikondi ca Mulungu mwa ife, kuti Mulungu anamtuma Mwana wace wobadwa yekha alowe m'dziko lapansi, kuti tikhale ndi moyo mwa iye.[10] Umo muli cikondi, sikuti ife tinakonda Mulungu, koma kuti iye anatikonda ife, ndipo anatuma Mwana wace akhale ciombolo cifukwa ca macime athu.[11] Okondedwa, ngati Mulungu anatikonda ife kotero, ffenso tiyenera kukondana wina ndi mnzaceo[12] Palibe munthu adamuona Mulungu nthawi iri yonse; tikakondana wina ndi mnzace, Mulungu akhala mwa ife, ndi cikondi cace cikhala cangwiro mwa ife;[13] m'menemo tizindikira kuti tikhala mwa iye, ndi iye mwa ife, cifukwa anatipatsako Mzimu wace.[14] Ndipo ife tapenyera, ndipo ticita umboni kuti Atate anatuma Mwana akhale Mpulumutsi wa dziko lapansi.[15] Iye amene adzabvomereza kuti Yesu ali Mwana wa Mulungu, Mulungu akhala mwa iye, ndi iye mwa Mulungu.[16] Ndipo ife tazindikira, ndipo takhulupirira cikondico Mulungu ali naco pa ife. Mulungu ndiye cikondi, ndipo iye amene akhala m'cikondi akhala mwa Mulungu, ndipo Mulungu akhala mwa iye.[17] M'menemo cikondi cathu cikhala cangwiro kuti tikhale nako kulimbika mtima m'tsiku la mlandu; citukwa monga Iyeyuali, momwemo tiri ife m'dziko line lapansi.[18] Mulibe mantha m'cikondi; koma cikondi cangwiro citaya kunja mantha, popeza mantha ali naco cilango, ndipo wamanthayo sakhala wangwiro m'cikondi.

YOHANE 3:16
Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wace wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira iye asatayike, koma akhale nao moyo wosatha.

1 PETRO 4:8
koposa zonse mukhale naco cikondano ceni ceni mwa inu nokha; pakuti cikondano cikwiriritsa unyinji wa macimo;

AKOLOSE 3:14
koma koposa izi zonse khalani naco cikondano, ndico comangira ca mtima wamphumphu.

YOHANE 13:34-35
[34] Ndikupatsani inu lamulo latsopano, kuti mukondane wina ndi mnzace; monga ndakonda Inu, kuti inunso mukondane wina ndi mnzace.[35] 1 Mwa ici adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli naco cikondano wina ndi mnzace.

YOHANE 15:13
Palibe munthu ali naco cikondi coposa ici, cakuti munthu ataya moyo wace cifukwa ca abwenzi ace.

1 AKORINTO 13:13
Ndipo tsopano zitsala cikhulupiriro, dyembekezo, cikondi, zitatu izi; koma cacikuru ca izi ndico cikondi.

1 YOHANE 4:19
Tikonda ife, cifukwa anayamba iye kutikonda.

MIYAMBO 10:12
Udani upikisanitsa; Koma cikondi cikwirira zolakwa zonse.

1 YOHANE 4:7
Okondedwa, tikondane wins ndi mnzace: cifukwa kuti cikond cicokera kwa Mulungu, ndipo yense amene akonda, abadwa kucokera kwa Mulungu, namzindikira Mulungu,

Chewa Bible (BL) 1992
Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society