A A A A A

Good Character: [Kindness]


1 AKORINTO 13:4-7
[4] Cikondi cikhala cilezere, ciri cokoma mtima; cikondi sicidukidwa; cikondi sicidziwa kudzitamanda, sicidzikuza,[5] sicicita zosayenera, sicitsata za mwini yekha, sicipsa mtima, sicilingirira zoipa;[6] sicikondwera ndi cinyengo, koma cikondwera ndi coonadi;[7] cikwirira zinthu zonse, cfkhulupirira zinthu zonse, ciyembekeza zinthu zonse, cipirira zinthu zonse.

AEFESO 4:29
8 Nkhani yonse yobvunda isaturuke m'kamwa mwanu, koma ngati pali yina yabwino kukumangirira monga mofunika ndiyo, 9 kuti ipatse cisomo kwa iwo akumva.

MIKA 6:8
Iye anakuuza, munthuwe, comwe ciri cokoma; ndipo Yehova afunanji nawe koma kuti ucite colungama, ndi kukonda cifundo ndi kuyenda modzicepetsa ndi Mulungu wako?

AKOLOSE 3:12
Cifukwa cace bvalani, monga osankhika a Mulungu, oyera mtima ndi okondedwa, mtima wacifundo, kukoma mtima, kudzicepetsa, cifatso, kuleza mtima;

AEFESO 2:7
kuti akaonetsere m'nyengo zirinkudza cuma coposa ca cisomo cace, m'kukoma mtima kwa pa ife mwa Kristu Yesu.

MATEYU 5:24
usiye pomwepo mtulo wako kuguwako, nucoke, nuyambe kuyanjana ndi mbale wako, ndipo pamenepo idza nupereke mtulo wako.

AROMA 2:4
Kapena upeputsa kodi kulemera kwa ubwino wace, ndi cilekerero ndi cipiriro cace, wosadziwa kuti ubwino wa Mulungu ukubwezera kuti ulape?

AGALATIYA 5:22
Koma cipatso ca Mzimu ndico cikondi, cimwemwe, mtendere, kuleza mtima, cifundo, kukoma mtima, icikhulupirtro,

MASALIMO 141:5
Akandipanda munthu wolungama ndidzati ncifundo: Akandidzudzula, ndidzakuyesa mafuta a pamutu; Mutu wanga usakane: Pakuti pangakhale posautsidwa iwo ndidzawapempherera.

YESAYA 54:8
M'kukwiya kwa kusefukira ndinakubisira nkhope yanga kamphindi; koma ndi kukoma mtima kwa cikhalire ndidzakucitira cifundo, ati Yehova Mombolo wako.

MIYAMBO 19:22
Cotikondetsa munthu ndico kukoma mtima kwace; Ndipo wosauka apambana munthu wonama.

1 PETRO 4:8
koposa zonse mukhale naco cikondano ceni ceni mwa inu nokha; pakuti cikondano cikwiriritsa unyinji wa macimo;

2 PETRO 1:5-7
[5] Ndipo mwa ici comwe, pakutengeraponso cangu conse, muonjezerapo ukoma pa cikhulupiriro canu, ndi paukoma cizindikiritso; ndi pacizindikiritso codziletsa;[6] ndi pacodziletsa cipiriro;[7] ndi pacipiriro zipembedzo; ndi pactpembedzo cikondi ca pa abale; ndi pacikondi ca pa abale cikondi.

ESTERE 2:9
Ndipo namwaliyo anamkomera, namcitira cifundo; ndipo anafulumira kumpatsa zace zomyeretsa, ndi magawo ace, ndi anamwali asanu ndi awiri oyenera kumpatsa ocokera m'nyumba ya mfumu; ndipo anamsuntha iye ndi anamwali ace akhale m'malo okometsetsa m'nyumba ya akazi.

AEFESO 4:32
Koma 12 mukhalirane okoma wina ndi mnzace, a mtima wacifundo, akukhululukirana nokha, 13 monganso Mulungu mwa Kristu anakhululukira inu.

AGALATIYA 6:10
Cifukwa cace, monga tiri nayo nyengo, ticitire onse cokoma, koma makamaka iwo a pa banja la cikhulupiriro.

LUKA 6:35
Koma 3 takondanani nao adani anu, ndi kuwacitira zabwino, ndipo kongoletsani osayembekeza kanthu konse, ndipo mphotho yanu idzakhala yaikuru, ndipo 4 inu mudzakhala ana a Wamkurukuruyo; cifukwa iye acitira zokoma anthu osayamika ndi oipa.

MIYAMBO 31:26
Atsegula pakamwa pace ndi nzeru, Ndipo cilangizo ca cifundo ciri pa lilime lace.

1 PETRO 3:9
osabwezera coipa ndi coipa, kapena cipongwe ndi cipongwe, koma penatu madalitso; pakuti kudzatsata ici mwaitanidwa, kuti mukalandire dalitso.

RUTE 2:20-21
[20] Nati Naomi kwa mpongozi wace, Yehova amdalitse amene sanaleka kuwacitira zokoma amoyo, ndi akufa. Ndipo Naomi ananena baye, Munthuyu ndiye mbale wathu, ndiye mmodzi wa iwo otiombolera colowa.[21] Ndipo Rute Mmoabu anati, Ananenanso nane ndithu, Uwaumirire anyamata anga, mpaka atatha kuceka zanga zonse za m'minda.

RUTE 3:10
Nati iye, Yehova akudalitse, mwana wanga. Cokoma cako wacicita potsiriza pano, ciposa cakuyamba cija, popeza sunatsata anyamata, angakhale osauka angakhale acuma.

NEHEMIYA 9:17
nakana kumvera, osakumbukilansozodabwiza zanu munazicita pakati pao; koma anaumitsa khosi lao, ndipo m'kupanduka kwao anaika mtsogoleri abwerere kumka ku ukapolo wao; koma Inu ndinu Mulungu wokhululukira, wacisomo, ndi wansoni, wolekereza, ndi wocuruka cifundo; ndipo simunawasiya.

MASALIMO 31:21
Wolemekezeka Yehova: Pakuti anandicitira cifundo cace codabwiza m'mudzi walinga.

MASALIMO 117:1-2
[1] Lemekezani Yehova, amitundu onse; Myimbireni, anthu onse.[2] Pakuti cifundo cace ca pa ife ndi cacikuru; Ndi coonadi ca Yehova ncosatha. Haleluya.

MASALIMO 119:76
Cifundo canu cikhaletu cakunditonthoza, ndikupemphani, Monga mwa mau anu kwa mtumiki wanu.

YESAYA 54:10
Pakuti mapiri adzacoka, ndi zitunda zidzasunthika; koma kukoma mtima kwanga sikudzakucokera iwe, kapena kusunthika cipangano canga ca mtendere, ati Yehova amene wakucitira iwe cifundo.

YEREMIYA 2:2
Pita nupfuule n'makutu a Yerusalemu, kuti, Yehova atero, Ndikumbukira za iwe kukoma mtima kwa ubwana wako, cikondi ca matomedwe ako; muja unanditsata m'cipululu m'dziko losabzya lamo.

YOWELE 2:13
ndipo ng'ambani mitima yanu, si zobvala zanu ai; ndi kurembenukira kwa Yehova Mulungu wanu; pakuti Iye ndiye wacisomo, ndi wodzala cifundo, wosapsa mtima msanga, ndi wocuruka kukoma mtima, ndi woleka coipaco.

YONA 4:2-3
[2] Ndipo anapemphera kwa Yehova, nati, Ha, Yehova! si ndiwo mau anga ndikali m'dziko langa? cifukwa cace ndinafulumira kuthawira ku Tarisi, pakuti ndinadziwa kuti Inu ndinu Mulungu wacisomo ndi wodzala cifundo, wolekerera ndi wokoma mtima mocuruka, ndi woleka coipaco.[3] Ndipo tsopano, Yehova, mundicotseretu moyo wanga, kundikomera ine kufa, osakhala ndi moyo ai.

MACHITIDWE A ATUMWI 28:2
Ndipo akunja anaticitira zokoma zosacitika pena ponsepo; pakuti anasonkha moto, natilandira ife tonse, cifukwa ca mvula inalinkugwa, ndi cifukwa ca cisanu.

GENESIS 24:14
ndipo pakhale kuti namwali amene ndidzati kwa iye, Tulatu mtsuko wako, ndimwe; ndipo iye adzati, Imwa, ndipo ndidzamwetsanso ngamila zako; yemweyo akhale mkazi wosankhira mnyamata wanu Isake; ndipo cotero ndidzadziwa kuti mwamcitira mbuyanga ufulu.

YOSWA 2:12
Ndipo tsopano, mundilumbiriretu kwa Yehova, popeza ndakucitirani cifundo, kuti inunso mudzacitira cifundo a m'nyumba ya atate wanga ndi kundipatsa cizindikilo coona,

2 AKORINTO 6:6
m'mayeredwe, m'cidziwitso, m'cilekerero, m'kukoma mtima, mwa Mzimu Woyera, m'cikondi cosanyenga;

TITO 3:4
Koma pamene kukoma mtima, ndi cikondi ca pa anthu, ca Mpulumutsi wathu Mulungu zidaoneka,

GENESIS 24:12
Ndipo anati, Yehova, Mulungu wa mbuyanga Abrahamu mundiyendetse ine bwino lero lino, mumcitire ufulu mbuyanga Abrahamu,

Chewa Bible (BL) 1992
Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society