A A A A A

Good Character: [Integrity]


MIYAMBO 11:3
Kuongoka mtima kwa olungama kuwatsogolera; Koma kukhota kwa aciwembu kudzawaononga.

MIYAMBO 28:6
Waumphawi woyenda mwangwiro Apambana ndi yemwe akhotetsa njira zace, angakhale alemera.

1 PETRO 3:16
ndi kukhala naco cikumbu mtima cabwino, kuti umo akunenerani, iwo akunenera konama mayendedwe anu abwino m'Kristu akacitidwe manyazi.

MIYAMBO 12:22
Milomo yonama inyansa Yehova; Koma ocita ntheradi amsekeretsa.

MIYAMBO 21:3
Kucita cilungamo ndi ciweruzo Kupambana ndi nsembe kumkonda Yehova.

2 AKORINTO 8:21
pakuti tikonzeratu zinthu zokoma, si pamaso pa Ambuye pokha, komanso pamaso pa anthu.

YOHANE 14:6
Yesu ananena naye, ine ndinenjira, ndi coonadi, ndi moyo. Palibe munthu adza kwa Atate, koma mwa Ine.

MIYAMBO 4:25-27
[25] Maso ako ayang'ane m'tsogolo, Zikope zako zipenye moongoka,[26] Sinkasinkha bwino mayendedwe a mapazi ako; Njira zako zonse zikonzeke.[27] Usapatuke ku dzanja lamanja kapena kulamanzere; Suntha phazi lako kusiya zoipa.

AHEBRI 13:18
Mutipempherere ife; pakuti takopeka mtima kuti tiri naco cikumbu mtima cokoma m'zonse, pofuna kukhala nao makhalidwe abwino.

LUKA 6:31
Ndipo monga mufuna inu kuti anthu adzakucitirani inu, muwacitire iwo motero inu momwe.

MASALIMO 41:11-12
[11] Umo ndidziwa kuti mukondwera ndi ine, Popeza mdani wanga sandiseka.[12] Ndipo ine, mundigwirizize m'ungwiro wanga, Ndipo mundiike pankhope panu ku nthawi yamuyaya.

AFILIPI 4:8
Cotsalira, abale, zinthu ziri zonse zoona, ziri zonse zolemekezeka, ziri zonse zolungama, ziri zonse zoyera, ziri zonse zokongola, ziri zonse zimveka zokoma; ngati kuli cokoma mtima cina, kapena citamando cina, zilingirireni izi.

YESAYA 26:7
Njira ya wolungama iri njira yoongoka; Inu amene muli woongoka, mukonza njira ya wolungama.

Chewa Bible (BL) 1992
Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society