A A A A A

Good Character: [Honor]


1 PETRO 2:17
Citirani ulemu anthu onse. Kondani abale. Opani Mulungu, Citirani mfumu ulemu.

AROMA 12:10
M'cikondano ca anzanu wina ndi mnzace mukondane ndi cikondi ceni ceni; mutsogolerane ndi kucitira wina mnzace ulemu;

1 TIMOTEO 5:17
Akuru akuweruza bwino ayesedwe oyenera ulemu wowirikiza, makamaka iwo akucititsa m'mau ndi m'ciphunzitso.

YOHANE 5:23
kuti onse akalemekeze Mwana, monga alemekeza Atate. Wosalemekeza Mwana salemekeza Atate amene anamtuma iye.

YOHANE 4:44
Pakuti Yesu mwini anacita umboni kuti, Mneneri alibe ulemu m'dziko la kwao.

1 TIMOTEO 1:17
Ndipo kwa Mfumu yosatha, yosabvunda, yosaoneka, Mulungu wa yekha, ukhale ulemu ndi ulemerero, kufikira nthawi za nthawi. Amen.

AROMA 13:1-7
[1] Anthu onse amvere maulamuliro a akulu; pakuti palibe ulamuliro wina koma wocokera kwa Mulungu; ndipo iwo amene alipo aikidwa ndi Mulungu.[2] Kotero kuti iye amene atsutsana nao ulamuliro, akaniza coikika ndi Mulungu; ndipo iwo akukaniza, adzadzitengera kulanga[3] Pakuti mafumu sakhala oopss nchito zabwino koma zoipa. Ndipo ufuna kodi kusaopa ulamuliro: Cita cabwino, ndipo udzalandirs kutama m'menemo:[4] pakuti ndiye mtumiki wa Mulungu, kucitira iwe zabwino. Koma ngati ucita coipa opatu, pakuti iye sagwira lupanga kwacabe; pakuti ndiye mtumiki wa Mulungu wakukwiyira ndi kubwe zera cilango wocita zoipa.[5] Cifukwa cace, kuyenera kuti mukhale omvera, si cifukwa ca mkwiyo woo kha, komanso cifukwa ca cikumbu mtima.[6] Pakuti cifukwa ca ici mupatsanso msonkho; pakuti iwo ndi wo atumiki a Mulungu akulabadira be cinthu cimeneci.[7] Perekani kwa anthu onse mangawa ao; msonkho kwa eni ace a msonkho; kuli pira kwa eni ace a kulipidwa; kuopa kwa eni ace a kuwaopa; ulemu kwe eni ace a ulemu.

AROMA 2:7
kwa iwo amene afunafuna ulemerero ndi ulemu ndi cisaonongeko, mwa kupirira pa nchito zabwino, adzabwezera moyo wosatha;

AHEBRI 13:4
Ukwati ucitidwe ulemu ndi onse, ndi pogona pakhale posadetsedwa; pakuti adama ndi acigololo adzawaweruza Mulungu.

YOHANE 12:26
Ngati wina anditumikira Ine, anditsate; ndipo kumene kuli Ine, komwekonso kudzakhala mtumiki wanga, Ngati wina anditumikira Ine, Atate adzamcitira ulemu iyeyu,

AEFESO 6:1-3
[1] Ananu, mverani akukubalani mwa Ambuye, pakuti ici ncabwino.[2] Lemekeza atate wako ndi amako (ndilo lamulo loyamba lokhala nalo lonjezano),[3] kuti kukhale bwino ndi iwe, ndi kuti ukhale wa nthawi yaikuru padziko.

AEFESO 6:2
Lemekeza atate wako ndi amako (ndilo lamulo loyamba lokhala nalo lonjezano),

YOHANE 5:22-23
[22] Pakuti Atate saweruza munthu ali yense, koma anapereka kuweruza konse kwa Mwana;[23] kuti onse akalemekeze Mwana, monga alemekeza Atate. Wosalemekeza Mwana salemekeza Atate amene anamtuma iye.

MATEYU 15:4
Pakuti Mulungu anati, Lemekeza atate wako ndi amako; ndipo, Wakunenera atate wace ndi amace zoipa, afe ndithu.

1 ATESALONIKA 4:4
yense wa inu adziwe kukhala naco cotengera cace m'ciyeretso ndi ulemu,

2 PETRO 1:17
Pakuti analandira kwa Mulungu Atate ulemu ndi ulemerero, pakumdzera iye mao otere ocokera ku ulemerero waukuru, Uyu ndi Mwana wanga wokondedwa, amene Ine ndikondwera naye;

CHIVUMBULUTSO 5:12-13
[12] akunena ndi mau akulu, Ayenera Mwanawankhosa, wophedwayo, kulandira cilimbiko, ndi cuma, ndi nzeru, ndi mphamvu, ndi ulemu, ndi ulemerero, ndi ciyamiko.[13] Ndipo colengedwa ciri conse ciri m'mwamba, ndi padziko, ndi pansi pa dziko, ndi m'nyanja, ndi zonse ziri momwemo, ndinazimva zirikunena, Kwa iye wakukhala pa mpando wacifumu, ndi kwa Mwanawankhosa zikhale ciyamiko, ndi ulemu, ndi ulemerero, ndi ufumu, kufikira nthawi za nthawi.

CHIVUMBULUTSO 7:12
ndi kunena, Amen: Thamo ndi ulemerero, ndi nzeru, ndi ciyamiko, ndi ulemu, ndi cilimbiko, ndi mphamvu zikhale kwa Mulungu wathu kufikira nthawi za nthawi. Amen.

1 AKORINTO 6:20
Pakuti munagulidwa ndi mtengo wace wapatali; cifukwa cace lemekezani Mulungu m'thupi lanu.

AEFESO 6:2-3
[2] Lemekeza atate wako ndi amako (ndilo lamulo loyamba lokhala nalo lonjezano),[3] kuti kukhale bwino ndi iwe, ndi kuti ukhale wa nthawi yaikuru padziko.

CHIVUMBULUTSO 4:9-11
[9] Ndipo pamene zamoyozo zipereka ulemerero ndi ulemu ndi uyamiko kwa iye wakukhala pa mpando wacifumu, kwa iye wakukhala ndi moyo kufikira nthawi za nthawi,[10] akulu makumi awiri mphambu anai amagwa pansi pamaso pa iye wakukhala pa mpando wacifumu, namlambira iye amene akhala ndi moyo kufikira nthawi za nthawi, ndipo aponya pansi akorona ao ku mpando wacifumu, ndi kunena,[11] Muyenera inu, Ambuye wathu, ndi Mulungu wathu, kulandira ulemerero ndi ulemu ndi mphamvu; cifukwa mudalenga zonse, ndipo mwa cifuniro canu zinakhala, nizinalengedwa.

MARKO 7:1-13
[1] Ndipo anasonkhana kwa Iye Afarisi, ndi alembi ena, akucokera ku Yerusalemu,[2] ndipo anaona kuti ophunzira ace ena anadya mkate ndi m'manja mwakuda, ndiwo osasamba.[3] Pakuti Afarisi, ndi Ayuda onse sakudya osasamba m'manja ao, kuti asungire mwambo wa akuru;[4] ndipo pakucoka kumsika, sakudya osasamba m'thupi; ndipo ziripo zinthu zina zambiri anazilandira kuzisunga, ndizo matsukidwe a zikho, ndi miphika, ndi zotengera zamkuwa.[5] Ndipo Afarisi ndi alembi anamfunsa Iye, kuti, Bwanji ophunzira anu satsata mwambo wa akuru, koma akudya mkate wao ndi m'manja mwakuda?[6] Ndipo Iye ananena nao, Yesaya ananenera bwino za inu onyenga, monga mwalembedwa, Anthu awa andilemekeza Ine ndi milomo yao, Koma mtima wao ukhala kutari ndi ine.[7] Koma andilambira Ine kwacabe, Ndi kuphunzitsa maphunzitso, malangizo a anthu.[8] Musiya lamulo la Mulungu, nimusunga mwambo wa anthu.[9] Ndipo ananena nao, Bwino mukaniza lamulo la Mulungu, kuti musunge mwambo wanu,[10] Pakuti Mose anati, Lemekeza atate wako ndi amako; ndipo iye wakunenera zotpa atate wace kapena amai wace, afe ndithu;[11] koma inu munena, Munthu akati kwa atate wace, kapena amai wace, Karban, ndiko kuti Mtulo, cimene ukadathandizidwa naco ndi ine,[12] simulolanso kumcitira kanthu atate wace kapena amai wace;[13] muyesa acabe mau a Mulungu mwa mwambo wanu, umene munaupereka: ndi zinthu zotere zambiri muzicita.

MATEYU 15:1-9
[1] Pomwepo anadza kwa Yesu Afarisi ndi alembi, ocokera ku Yerusalemu, nati,[2] Ophunzira anu alumphiranji miyambo ya makolo? pakuti sasamba manja pakudya.[3] Ndipo Iye anayankha, nati kwa iwo, Inunso mulumphiranji lamulo la Mulungu cifukwa ca miyambo yanu?[4] Pakuti Mulungu anati, Lemekeza atate wako ndi amako; ndipo, Wakunenera atate wace ndi amace zoipa, afe ndithu.[5] Koma inu munena, Amene ali yense anena kwa atate wace kapena kwa amace, Ico ukanathandizidwa naco, neoperekedwa kwa Mulungu;[6] iyeyo sadzalemekeza atate wace. Ndipo inu mupeputsa mau a Mulungu cifukwa ca miyambo yanu.[7] Onyenga inu! Yesaya ananenera bwino za inu, ndikuti,[8] Anthu awa andilemekeza Ine ndi milomo yao; Koma mtima wao uli kutari ndi Ine.[9] Koma andilambira Ine kwacabe, Ndi kuphunzitsa maphunzitso, malangizo a anthu.

LUKA 14:7-8
[7] Ndipo iye ananena fanizo kwa oitanidwa, popenya kuti amadzisankhira mipando yaulemu, nanena kwa iwo,[8] Pamene pali ponse waitanidwa iwe ndi munthu ku cakudya ca ukwati, usaseama pa mpando waulemu; kuti kapena wina waulemu wakuposa iwe akaitanidwe ndi iye,

2 AKORINTO 6:8
mwa ulemerero, mwa mnyozo, mwa mbiri yoipa ndi mbiri yabwino; mongaosoceretsa, angakhale ali oona;

CHIVUMBULUTSO 5:13
Ndipo colengedwa ciri conse ciri m'mwamba, ndi padziko, ndi pansi pa dziko, ndi m'nyanja, ndi zonse ziri momwemo, ndinazimva zirikunena, Kwa iye wakukhala pa mpando wacifumu, ndi kwa Mwanawankhosa zikhale ciyamiko, ndi ulemu, ndi ulemerero, ndi ufumu, kufikira nthawi za nthawi.

CHIVUMBULUTSO 4:11
Muyenera inu, Ambuye wathu, ndi Mulungu wathu, kulandira ulemerero ndi ulemu ndi mphamvu; cifukwa mudalenga zonse, ndipo mwa cifuniro canu zinakhala, nizinalengedwa.

1 TIMOTEO 6:16
amene iye yekha ali nao moyo wosatha, wakukhala m'kuunika kosakhozeka kufikako; amene munthu sanamuona, kapena sakhoza kumuona; kwa iye kukhale ulemu ndi mphamvu yosatha. Amen.

AHEBRI 5:4
Ndipo palibe munthu adzitengera ulemuwo mwini wace, komatu iye amene aitanidwa ndi Mulungu, monga momwenso Aroni.

MATEYU 15:8
Anthu awa andilemekeza Ine ndi milomo yao; Koma mtima wao uli kutari ndi Ine.

MATEYU 19:19
Lemekeza atate wako ndi amako, ndipo, Uzikonda mnzako monga udzikonda iwe mwini.

LUKA 18:20
Udziwa malamulo. Usacite cigololo, Usaphe, Usabe, Usacite umboni wonama, Lemekeza atate wako ndi amako.

MATEYU 13:57
Ndipo iwo anakhumudwa cifukwa ca Iye. Koma Yesu anati kwa iwo, 6 Mneneri sakhala wopanda ulemu koma ku dziko la kwao ndiko, ndi kubanja kwace.

MARKO 6:4
Ndipo Yesu ananena kwa iwo, Mneneri sakhala wopanda ulemu, koma m'dziko la kwao ndimo, ndi pakati pa abale ace, ndi m'nyumba yace.

YOHANE 12:23-26
[23] Koma Yesu anayankha iwo, nati, Yafika nthawi, kuti Mwana wa munthu alemekezedwe.[24] Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Ngati mbeu ya tirigu siigwa m'nthaka, nifa, ikhala pa yokha iyo; koma ngati ifa, ibala cipatso cambiri.[25] Iye wokonda moyo wace adzautaya; ndipo wodana ndi moyo wace m'dziko lino lapansi adzausungira ku moyo wosatha.[26] Ngati wina anditumikira Ine, anditsate; ndipo kumene kuli Ine, komwekonso kudzakhala mtumiki wanga, Ngati wina anditumikira Ine, Atate adzamcitira ulemu iyeyu,

AHEBRI 2:9
Koma timpenya iye amene adamcepsa pang'ono ndi angelo, ndiye Yesu, cifukwa ca zowawa za imfa, wobvala korona wa ulemerero ndi ulemu, kuti ndi cisomo ca Mulungu alawe imfa m'malo mwa munthu ali yense.

EKSODO 20:12
Uzilemekeza atate wako ndi amako; kuti acuruke masiku ako m'dziko limene Yehova Mulungu wako akupatsa iwe.

YESAYA 29:13
Ndipo Ambuye anati, Popeza anthu awa ayandikira ndi Ine ndi m'kamwa mwao, nandilemekeza ndi milomo yao, koma mtima wao uli kutari ndi Ine, ndi mantha ao akundiopa Ine, ndi lamulo la anthu analiphunzira;

1 SAMUELE 2:30
Cifukwa cace Yehova Mulungu wa Israyeli akuti, Ndinaterodi kuti banja lako ndi banja la kholo lako lidzayenda pamaso panga nthawi zonse; koma tsopano Yehova ati, Cikhale kutali ndi Ine; popeza amene andilemekeza Ine, Inenso ndidzawalemekeza iwowa, ndipo akundipeputsa Ine, adzapeputsidwa.

MIYAMBO 3:9
Lemekeza Yehova ndi cuma cako, Ndi zinthu zako zonse zoyambirira kuca;

DEUTERONOMO 5:16
Lemekeza atate wako ndi amako, monga Yehova Mulungu wako anakulamulira; kuti masiku ako acuruke, ndi kuti cikukomere, m'dziko limene Yehova Mulungu wako akupatsa iwe.

MIYAMBO 21:21
Wolondola cilungamo ndi cifundo Apeza moyo, ndi cilungamo, ndi ulemu.

MIYAMBO 22:4
Mphotho ya cifatso ndi kuopa, Yehova Ndiye cuma, ndi ulemu, ndi moyo.

MIYAMBO 14:31
Wotsendereza aumphawi atonza Mlengi wace; Koma wocitira wosauka cifundo amlemekeza.

MASALIMO 8:5-6
[5] Pakuti munamcepsa pang'ono ndi Mulungu, Munambveka iye korona wa ulemerero ndi ulemu.[6] Munamcititsa ufumu pa nchito za manja anu; Mudagonjetsa zonse pansi pa mapazi ace;

MIYAMBO 29:23
Kudzikuza kwa munthu kudzamcepetsa; Koma wokhala ndi mtima wodzicepetsa adzalemekezedwa.

MALAKI 1:6
Mwana alemekeza atate wace, ndi mnyamata mbuye wace; ngati Ine tsono ndine atate, uli kuti ulemu wanga? ngati Ine ndine mbuye, kundiopa kuli kuti? ati Yehova wa makamu kwa inu ansembe akupeputsa dzina langa. Ndipo mukuti, Tapeputsa dzina lanu motani?

1 TIMOTEO 5:3
Citira ulemu amasiye amene ali amasiye ndithu.

1 TIMOTEO 6:1
Onse amene ali akapolo a m'goli, ayesere ambuye a iwo okha oyenera ulemu wonse, kuti dzina la Mulungu ndi ciphunzitso zisacitidwe mwano.

Chewa Bible (BL) 1992
Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society