A A A A A

Good Character: [Honest]


2 AKORINTO 8:21
pakuti tikonzeratu zinthu zokoma, si pamaso pa Ambuye pokha, komanso pamaso pa anthu.

2 TIMOTEO 2:15
Ucite cangu kudzionetsera kwa Mulungu wobvomerezeka, wanchito wopanda cifukwa ca kucita manyazi, wolunjika nao bwino mau a coonadi.

AKOLOSE 3:9
musamanamizana wina ndi mnzace; popeza mudabvula munthu wakale pamodzi ndi nchito zace,

AEFESO 4:25
Mwa ici, mutataya zonama, 3 lankhulani zoona yense ndi mnzace; 4 pakuti tiri ziwalo wina ndi mnzace.

YAKOBO 1:26
Ngati wina adziyesera ali wopembedza Mulungu, ndiye wosamanga lilime lace, koma adzinyenga mtima wace, kupembedza kwace kwa munthuyu nkopanda pace.

YAKOBO 3:17
Koma nzeru yocokera kumwamba iyamba kukhala yoyera, nikhalanso yamtendere, yaulere, yomvera bwino, yodzala cifundo ndi zipatso zabwino, yopanda tsankhu, yosadzikometsera pamaso.

LUKA 6:31
Ndipo monga mufuna inu kuti anthu adzakucitirani inu, muwacitire iwo motero inu momwe.

MATEYU 5:8
Odala ali oyera mtima; cifukwa adzaona Mulungu.

MIYAMBO 10:9
Woyenda moongoka amayenda osatekeseka; Koma wokhotetsa njira zace adzadziwika.

MIYAMBO 11:3
Kuongoka mtima kwa olungama kuwatsogolera; Koma kukhota kwa aciwembu kudzawaononga.

MIYAMBO 12:17-22
[17] Wolankhula ntheradi aonetsa cilungamo; Koma mboni yonama imanyenga.[18] Alipo wonena mwansontho ngati kupyoza kwa lupanga; Koma lilime la anzeru lilamitsa.[19] Mlomo wa ntheradi ukhazikika nthawi zonse; Koma lilime lonama likhala kamphindi.[20] Cinyengo ciri m'mitima ya oganizira zoipa; Koma aphungu a mtendere amakondwa.[21] Palibe bvuto lidzagwera wolungama; Koma amphulupulu adzadzazidwa ndi zoipa,[22] Milomo yonama inyansa Yehova; Koma ocita ntheradi amsekeretsa.

MIYAMBO 14:5
Mboni yokhulupirika sidzanama; Koma mboni yonyenga imalankhula zonama.

MIYAMBO 21:3
Kucita cilungamo ndi ciweruzo Kupambana ndi nsembe kumkonda Yehova.

MIYAMBO 24:26
Wobwezera mau oongoka Apsompsona milomo.

MIYAMBO 28:18
Woyenda mwangwiro adzapulumuka; Koma wokhota m'mayendedwe ace adzagwa posacedwa.

MASALIMO 112:5
Wodala munthu wakudtira cifundo, nakongoletsa; Adzalimbika nao mlandu wace poweruzidwa.

1 MBIRI 29:17
Ndidziwanso, Mulungu wanga, kuti muyesa mtima, nimukondwera nako kuongoka. Kama ine, ndi mtima wanga woongoka ndapereka zonsezi mwaufulu; ndipo tsopano ndaona mokondwera anthu anu okhala pompano, napereka kwa Inu mwaufulu.

YOHANE 1:3
Zonse: zinalengedwa ndi iye; ndipo kopanda iye sikunalengedwa kanthu kali konse kolengedwa,

YOHANE 3:18
Wokhulupirira Iye saweruzidwa; wosakhulupira waweruzidwa ngakhale tsopano, cifukwa sanakhulupirira dzina la Mwana wobadwa yekha wa Mulungu.

AFILIPI 4:8-9
[8] Cotsalira, abale, zinthu ziri zonse zoona, ziri zonse zolemekezeka, ziri zonse zolungama, ziri zonse zoyera, ziri zonse zokongola, ziri zonse zimveka zokoma; ngati kuli cokoma mtima cina, kapena citamando cina, zilingirireni izi.[9] Zimenenso mudaziphunzira, ndi kuzilandira, ndi kuzimva, ndi kuziona mwa ine, zomwezo citani; ndipo Mulungu wa mtendere adzakhala pamodzi ndi inu.

1 PETRO 3:10-12
[10] Pakuti, iye wofuna kukonda moyo, Ndi kuona masiku abwino, Aletse lilime lace lisanene coipa, Ndi milomo yace isalankhule cinyengo;[11] j Ndipo apatuke pacoipa, nacite cabwino; Afunefune mtendere ndi kuulondola.[12] Pakuti maso a Ambuye ali pa olungama, Ndi makutu ace akumva rembedzo lao; Koma nkhope ya Ambuye iri pa ocita zoipa,

MIYAMBO 6:16-20
[16] Ziripo zinthu zisanu ndi cimodzi Mulungu azida; Ngakhale zisanu ndi ziwiri zimnyansa:[17] Maso akunyada, lilime lonama, Ndi manja akupha anthu osacimwa;[18] Mtima woganizira ziwembu zoipa, Mapazi akuthamangira mphulupulu mmangu mmangu;[19] Mboni yonama yonong'ona mabodza, Ndi wopikisanitsa abale.[20] Mwananga, sunga malangizo a atate wako, Usasiye malamulo a mako;

Chewa Bible (BL) 1992
Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society