A A A A A

Good Character: [Humble / Humility]


AKOLOSE 3:12
Cifukwa cace bvalani, monga osankhika a Mulungu, oyera mtima ndi okondedwa, mtima wacifundo, kukoma mtima, kudzicepetsa, cifatso, kuleza mtima;

AEFESO 4:2
ndi kuonetsera kudzicepetsa konse, ndi cifatso, ndi kuonetsera cipiriro, ndi kulolerana wina ndi mnzace, mwa cikondi;

YAKOBO 4:6-10
[6] Koma apatsa cisomo coposa. Potero anena malembo, Mulungu akaniza odzikuza, koma apatsa cisomo odzicepetsa.[7] Potero mverani Mulungu; koma kanizani mdierekezi, ndipo adzakuthawani inu.[8] Yandikirani kwa Mulungu, ndipo adzayandikira kwa inu, Sambani m'manja, ocimwa inu; yeretsani mitima, a mitima iwiri inu.[9] Khalani osautsidwa, lirani, lirani misozi; kuseka kwanu kusanduke kulira, ndi cimwemwe canu cisanduke cisoni.[10] Dzicepetseni pamaso pa Ambuye, ndipo adzakukwezani.

1 PETRO 5:5
Koma nonsenu mubvale kudzicepetsa kuti mutumikirane; pakuti Mulungu akaniza odzikuza, koma apatsa cisomo kwa odzicepetsa.

2 MBIRI 7:14
ndipo anthu anga ochedwa dzina langa akadzicepetsa, nakapemphera, nakafuna nkhope yanga, nakatembenuka kuleka njira zao zoipa; pamenepo ndidzamvera m'Mwamba, ndi kukhululukira coipa cao, ndi kuciritsa dziko lao.

LUKA 14:11
Cifukwa munthu ali yense wakudzikuza adzacepetsedwa; ndipo wakudzicepetsa adzakulitsidwa.

MIKA 6:8
Iye anakuuza, munthuwe, comwe ciri cokoma; ndipo Yehova afunanji nawe koma kuti ucite colungama, ndi kukonda cifundo ndi kuyenda modzicepetsa ndi Mulungu wako?

MIYAMBO 3:3-4
[3] Cifundo ndi coonadi zisakusiye; Uzimange pakhosi pako; Uzilembe pamtima pako;[4] Motero udzapezakisomo ndi nzeru yabwino, Pamaso pa Mulungu ndi anthu.

MIYAMBO 11:2
Pakudza kudzikuza padzanso manyazi; Koma nzeru iri ndi odzicepetsa,

MIYAMBO 12:15
Njira ya citsiru nlolungama pamaso pace pace; Koma wanzeru amamvera uphungu.

MIYAMBO 15:33
Kuopa Yehova ndiko mwambo wanzeru; Ndipo cifatso citsogolera ulemu.

MIYAMBO 18:12
Mtima wa munthu unyada asanaonongeke; Koma cifatso citsogolera ulemu.

MIYAMBO 22:4
Mphotho ya cifatso ndi kuopa, Yehova Ndiye cuma, ndi ulemu, ndi moyo.

MIYAMBO 27:2
Wina akutame, si m'kamwamwako ai; Mlendo, si milomo ya iwe wekha.

MASALIMO 25:9
Adzawatsogolera ofatsa m'ciweruzo: Ndipo adzaphunzitsa ofatsa njira yace.

MASALIMO 149:4
Popeza Yehova akondwera nao anthu ace; Adzakometsa ofatsa ndi cipulumutso,

AROMA 12:3
Pakuti ndi cisomo capatsidwa kwa ine, ndiuza munthu ali yense wa inu, kuti asadziyese koposa kumene ayenera kudziyesa; koma aganize modziletsa yekha, monga, Mulungu anagawira kwa munthu ali yense muyeso wa cikhulupiriro,

AROMA 12:16
Mukhale ndi mtima umodzi wina ndi mnzace. Musasamalire zinthu zazikuru, koma phatikanani nao odzicepetsa, Musadziyesere anzeru mwa inu nokha.

2 AKORINTO 12:9-10
[9] Ndipo ananena kwa ine, Cisomo canga cikukwanira; pakuti mphamvu yanga ithedwa m'ufoko. Cifukwa cace makamaka ndidzadzitamandira rriokondweratu m'maufoko anga, kuti mphamvu ya Kristu ikhale pa ine.[10] Cifukwa cace ndisangalala m'tnaufoko, m'ziwawa, m'zikakamizo, m'mazunzo, m'zipsinjiko, cifukwa ca Kristu; pakuti pamene ndifoka, pamenepo ndiri wamphamvu.

AFILIPI 2:3-4
[3] musacite kanthu monga mwa cotetana, kapena monga mwa ulemerero wopanda pace, komatu ndi kudzicepetsa mtima, yense ayese anzace omposa iye mwini;[4] munthu yense asapenyerere zace za iye yekha, koma yense apenyererenso za mnzaceo

MATEYU 23:10-12
[10] Ndipo musachedwa atsogoleri, pakuti alipo mmodzi Mtsogoleri wanu, ndiye Kristu.[11] Koma wamkuru wopambana wa inu adzakhala mtumiki wanu.[12] Ndipo amene ali yense akadzikuza yekha adzacepetsedwa; koma amene adzicepetsa mwini yekha adzakulitsidwa.

YAKOBO 4:14-16
[14] inu amene simudziwa cimene cidzagwa mawa. Moyo wanu uli wotani? Pakuti muli utsi, wakuonekera kanthawi, ndi pamenepo ukanganuka.[15] Mukadanena inu, Akalola Mulungu, ndipo tikakhala ndi moyo, tidzacita kakuti kakuti.[16] Koma tsopano mudzitamandira m'kudzikuza kwanu; kudzitamandira kuli konse kotero nkoipa.

AFILIPI 2:5-8
[5] Mukhale nao mtima m'kati mwanu umene unalinso mwa Kristu Yesu,[6] ameneyo, pokhala nao maonekedwe a Mulungu, sanaciyesa colanda kukhala wofana ndi Mulungu,[7] koma anadzikhuthula yekha, natenga maonekedwe akapolo, nakhala m'mafanizidwe a anthu;[8] ndipo popezedwa m'maonekedwe ngati munthu, anadzicepetsa yekha, nakhala womvera kufikira imfa, ndiyo imfa ya pamtanda.

Chewa Bible (BL) 1992
Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society