A A A A A

Good Character: [Hospitality]


AHEBRI 3:2
amene anakhala wokhulupirika kwa iye adamuikayo, monganso Mose m'nyumba yace yonse.

YESAYA 58:7
Kodi si ndiko kupatsa cakudya cako kwa anjala, ndi kuti ubwere nao kunyumba kwako aumphawi otayika? pakuona wamalisece kuti umbveke, ndi kuti usadzibisire wekha a cibale cako?

1 TIMOTEO 5:10
wa mbiri ya nchito zabwino; ngati walera ana, ngati wacereza alendo, ngati adasambitsa mapazi a nzera mtima, ngati wathapdiza osautsidwa, ngati anatsatadi nchito zonse zabwino.

TITO 1:8
komatu wokonda kucereza alendo, wokonda zokoma, wodziweruza, wolungama, woyera mtima, wodziletsa;

1 PETRO 4:8-9
[8] koposa zonse mukhale naco cikondano ceni ceni mwa inu nokha; pakuti cikondano cikwiriritsa unyinji wa macimo;[9] mucerezane wina ndi mnzace, osadandaula:

MACHITIDWE A ATUMWI 16:33-34
[33] Ndipo anawatenga ora lomwelo la usiku, natsuka mikwingwirima yao; nabatizidwa pomwepo, iye ndi a pabanja pace.[34] Ndipo anakwera nao kunka kunyumba kwace, nawakhazikira cakudya, nasangalala kwambiri, pamodzi ndi a pabanja pace, atakhulupirira Mulungu.

LEVITIKO 19:33-34
[33] Ndipo mlendo akagonera m'dziko mwanu, musamamsautsa.[34] Mlendo wakugonera kwa inu mumuyese pakati pa inu monga wa m'dziko momwemo; umkonde monga udzikonda wekha; popeza munali alendo m'dziko la Aigupto; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

LUKA 14:7-14
[7] Ndipo iye ananena fanizo kwa oitanidwa, popenya kuti amadzisankhira mipando yaulemu, nanena kwa iwo,[8] Pamene pali ponse waitanidwa iwe ndi munthu ku cakudya ca ukwati, usaseama pa mpando waulemu; kuti kapena wina waulemu wakuposa iwe akaitanidwe ndi iye,[9] ndipo pakufika iye amene adaitana iwe ndi uyu, adzati kwa iwe, Mpatse uyu malo; ndipo pomwepo udzayamba manyazi kukhala pa mpando wa kuthungo.[10] Koma pamene pali ponse waitanidwa iwe, pita nukhale pansi pa malo a kuthungo; kotero kuti pamene akadza iye anakuitana iwe, akanena ndi iwe, Bwenzi langa, sendera, kwera kuno; pomwepo udzakhala ndi ulemerero pamaso pa onse akuseama pacakudya pamodzi ndi iwe.[11] Cifukwa munthu ali yense wakudzikuza adzacepetsedwa; ndipo wakudzicepetsa adzakulitsidwa.[12] Ndipo ananenanso kwa iye amene adamuitana, Pamene ukonza cakudya ca pausana kapena ca madzulo, usaitane abwenzi ako, kapena abale ako, kapena a pfuko lako, kapena anansi ako eni cuma; kuti kapena iwonso angabwereze kuitana iwe, ndipo udzakhala nayo mphotho.[13] Koma pamene ukonza phwando uitane aumphawi, opunduka, otsimphina, akhungu;[14] ndipo udzakhala wodala; cifukwa iwo alibe cakubwezera iwe mphotho; pakuti idzabwezedwa mphotho pa kuuka kwa oiungama.

MATEYU 25:34-46
[34] Pomwepo Mfumuyo idzanena kwa iwo a ku dzanja lace lamanja, Idzani kuno inu odalitsika a Atate wanga, lowani mu Ufumu wokonzedwera kwa inu pa cikhazikiro cace ca dziko lapansi:[35] pakuti ndinali ndi njala, ndipo munandipatsa Ine kudya; ndinali ndi ludzu, ndipo munandimwetsa Ine; ndinali mlendo, ndipo munacereza Ine;[36] wamarisece Ine, ndipo munandibveka; ndinadwala, ndipo munadza kuceza ndi Ine; ndinali m'nyumba yandende, ndipo munadza kwa Ine.[37] Pomwepo olungama adzamyankha Iye kuti, Ambuye, tinakuonani Inu liti wanjala, ndi kukudyetsani? kapena waludzu, ndi kukumwetsani?[38] Ndipo tinaona Inu liti mlendo, ndi kukucerezani? kapena wamarisece, ndi kukubvekani?[39] Ndipo tinakuonani Inu liti wodwala, kapena m'nyumba yandende, ndipo tinadza kwa Inu?[40] Ndipo Mfumuyo idzayankha nidzati kwa iwo, Indetu ndinena kwa inu, Cifukwa munacitira ici mmodzi wa abale anga, ngakhale ang'onong'ono awa, munandicitira ici Ine.[41] Pomwepo Iye adzanena kwa iwo a ku dzanja lamanzere, Cokani kwa Ine otembereredwa inu, ku mota wa nthawi zonse wokolezedwera mdierekezi ndi amithenga ace:[42] pakuti ndinali ndi njala, ndipo simunandipatsa Ine kudya: ndinali ndi ludzu, ndipo simunandimwetsa Ine:[43] ndinali mlendo, ndipo simunandilandira Ine; wamarisece ndipo simunandibveka Ine; wodwala, ndi m'nyumba yandende, ndipo simunadza kundiona Ine.[44] Pomwepo iwonso adzayankha kuti, Ambuye, tinakuonani liti wanjala, kapena waludzu, kapena mlendo, kapena wamarisece, kapena m'nyumba yandende, ndipo ife sitinakutumikirani Inu?[45] Pomwepo Iye adzayankha iwo kuti, Indetu ndinena kwa inu, Cifukwa munalibe kucitira ici mmodzi wa awa ang'onong'ono, munalibe kundicitira ici Ine.[46] Ndipo amenewa adzacoka kumka ku cilango ca nthawi zonse; koma olungama ku moyo wa nthawi zonse.

AROMA 12:13-20
[13] Patsani zosowa oyera mtima; cerezani aulendo.[14] Dalitsani iwo akuzunza inu; dalitsani, musawatemberere.[15] Kondwani nao iwo akukondwera; lirani nao akulira.[16] Mukhale ndi mtima umodzi wina ndi mnzace. Musasamalire zinthu zazikuru, koma phatikanani nao odzicepetsa, Musadziyesere anzeru mwa inu nokha.[17] Musabwezere munthu ali yense coipa cosinthana ndi coipa. Ganiziranitu zinthu za ulemu pamaso pa anthu onse.[18] Ngati nkutheka, monga momwe mukhoza, khalani ndi mtendere ndi anthu onse.[19] Musabwezere coipa, okondedwa, koma patukani pamkwiyo; pakuti kwalembedwa, Kubwezera kuli kwanga, Ine ndidzabwezera, ati Ambuye.[20] Koma ngati mdani wako akumva njala, umdyetse, ngati akumva ludzu, ummwetse; pakuti pakutero udzaunjika makala a mota pamutu pace.

Chewa Bible (BL) 1992
Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society