A A A A A

Good Character: [Grateful]


AKOLOSE 4:2
Citani khama m'kupemphera, nimudikire momwemo ndi ciyamiko;

2 AKORINTO 2:14-15
[14] Koma ayamikike Mulungu, amene atitsogolera m'cigonjetso mwa Kristu, namveketsa pfungo la cidziwitso cace mwa ife pamalo ponse.[15] Pakuti ife ndife pfungo labwino la Kristu, kwa Mulungu, mwa iwo akupulumutsidwa, ndi mwa iwo akuonongeka; kwa ena pfungo la imfa kuimfa;

YONA 2:9
Koma ine ndidzakupherani Inu nsembe ndi mau akuyamika, Ndidzakwaniritsacowindacanga. Cipulumutso nca Yehova.

1 ATESALONIKA 5:18
M'zonse yamikani; pakuti ici ndi cifuniro ca Mulungu ca kwa inu, mwa Kristu Yesu.

AKOLOSE 3:15-17
[15] Ndipo mtendere wa Kristu ucite ufumu m'mitima yanu, kulingakonso munaitanidwa m'thupi limodzi; ndipo khalani akuyamika.[16] Mau a Knstu akhalitse mwa inu cicurukire mu nzeru yonse, ndi kuphunzitsa ndi kuyambirirana eni okha ndi masalmo, ndimayamiko ndi nyimbo zauzimu, ndi kuyimbira Mulungu ndi cisomo mumtima mwanu.[17] Ndipo ciri conse mukacicita m'mau kapena muncbito, citani zonse m'dzina la Ambuye Yesu, ndi kuyamika Mulungu Atate mwa iye.

1 AKORINTO 15:57
koma 23 ayamikike Mulungu, amene atipatsa ife cigonjetso mwa Ambuye wathu Yesu Kristu.

MASALIMO 100:4
Lowani ku zipata zace ndi ciyamiko, Ndi ku mabwalo ace ndi cilemekezo: Myamikeni; lilemekezeni dzina lace.

1 MBIRI 16:34
Yamikani Yehova; pakuti iye ndiye wabwino; Pakuti cifundo cace ncosatha.

AROMA 1:21
cifukwa kuti, ngakhale anadziwa Mulungu, sanamcitira ulemu wakuyenera Mulungu, ndipo sanamyamika; koma anakhala opanda pace m'maganizo ao, ndipo unada mtima wao wopulukira,

AFILIPI 4:6
Musadere nkhawa konse; komatu m'zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi ciyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu.

MASALIMO 69:30
Ndidzalemekeza dzina la Mulungu ndi kuliyimbira, Ndipo ndidzambukitsa ndi kumyamika.

2 AKORINTO 9:15
Ayamikike Mulungu cifukwa ca mphatso yace yace yosatheka kuneneka.

1 ATESALONIKA 5:16-18
[16] Kondwerani nthawi zonse;[17] Pempherani kosaleka;[18] M'zonse yamikani; pakuti ici ndi cifuniro ca Mulungu ca kwa inu, mwa Kristu Yesu.

AFILIPI 4:6-7
[6] Musadere nkhawa konse; komatu m'zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi ciyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu.[7] Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana cidziwitso conse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Kristu Yesu.

AKOLOSE 1:12
ndi kuyamika Atate, amene anatiyeneretsa ife kulandirana nao colowa ca oyera mtima m'kuunika;

YAKOBO 1:17
Mphatso iri yonse yabwino, ndi cininkho ciri conse cangwiro zicokera Kumwamba, zotsika kwa Atate wa mauniko, amene alibe cisanduliko, kapena mthunzi wa citembenukiro.

AEFESO 5:4
kapena cinyanso, ndi kulankhula zopanda pace, kapena zopusa zimene siziyenera; koma makamaka ciyamiko.

LEVITIKO 22:29
Ndipo mukamaphera Yehova nsembe yoyamika, muiphere kuti mulandirike.

MASALIMO 103:2
Lemekeza Yehova, moyo wanga, Ndi kusaiwala zokoma zace zonse aticitirazi:

DANIELE 6:10
Ndipo podziwa Danieli kuti adatsimikiza colembedwaco, analowa m'nyumba mwace, m'cipinda mwace, cimene mazenera ace anatseguka oloza ku Yerusalemu; ndipo anagwadamaondo ace tsiku limodzi katatu, napemphera, nabvomereza pamaso pa Mulungu wace monga umo amacitira kale lonse.

MASALIMO 107:1
Yamikani Yehova pakuti Iye ndiye wabwino; Pakuti cifundo cace ncosatha.

AEFESO 5:20
ndi kuyamika Mulungu Atate masiku onse, cifukwa ca zonse, m'dzina la Ambuye wathu Yesu Kristu;

MASALIMO 9:1
Ndidzayamika Yehova ndi mtima wanga wonse; Ndidzawerengera zodabwiza zanu zonse.

YOHANE 3:16
Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wace wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira iye asatayike, koma akhale nao moyo wosatha.

AKOLOSE 3:2
Lingalirani zakumwamba osati za padziko ai.

AKOLOSE 3:16
Mau a Knstu akhalitse mwa inu cicurukire mu nzeru yonse, ndi kuphunzitsa ndi kuyambirirana eni okha ndi masalmo, ndimayamiko ndi nyimbo zauzimu, ndi kuyimbira Mulungu ndi cisomo mumtima mwanu.

MASALIMO 107:8
Ayamike Yehova cifukwa ca cifundo cace, Ndi zodabwiza zace za kwa ana a anthu!

MASALIMO 119:62
Pakati pa usiku ndidzauka kukuyamikani Cifukwa ca maweruzo anu olungama.

CHIVUMBULUTSO 11:17
nati, Tikuyamikani, Ambuye Mulungu, Wamphamvuyonse, amene muli, nimunali; popeza mwadzitengera mphamvu yanu yaikuru, ndipo mwacita ufumu.

AKOLOSE 3:15-17
[15] Ndipo mtendere wa Kristu ucite ufumu m'mitima yanu, kulingakonso munaitanidwa m'thupi limodzi; ndipo khalani akuyamika.[16] Mau a Knstu akhalitse mwa inu cicurukire mu nzeru yonse, ndi kuphunzitsa ndi kuyambirirana eni okha ndi masalmo, ndimayamiko ndi nyimbo zauzimu, ndi kuyimbira Mulungu ndi cisomo mumtima mwanu.[17] Ndipo ciri conse mukacicita m'mau kapena muncbito, citani zonse m'dzina la Ambuye Yesu, ndi kuyamika Mulungu Atate mwa iye.

MASALIMO 106:1
Haleluya. Yamikani Yehova; pakuti Iye ndiye wabwino: Pakuti cifundo cace ncosatha.

AHEBRI 12:28
Mwa ici polandira ufumu wosagwedezeka, tikhale naco cisomo, cimene tikatumikire naco Mulungu momkondweretsa, ndi kumcitira ulemu ndi mantha.

MASALIMO 107:1-2
[1] Yamikani Yehova pakuti Iye ndiye wabwino; Pakuti cifundo cace ncosatha.[2] Atere oomboledwa a Yehova, Amene anawaombola m'dzanja la wosautsa;

2 SAMUELE 22:49
Amene anditurutsa kwa adani anga; Inde mundikweza ine pamwamba pa iwo akundiukira; Mundipulumutsa kwa munthu waciwawa.

1 ATESALONIKA 1:2
Tiyamika Mulungu nthawi zonse cifukwa ca inu nonse, ndi kukumbukila inu m'mapemphero athu;

1 TIMOTEO 2:1-2
[1] Ndidandaulira tsono, poyambayamba, kuti acitike mapembedzo, mapemphero, mapembedzero, mayamiko, cifukwa ca anthu onse;[2] cifukwa ca mafumu ndi onse akucita ulamuliro kuti m'moyo mwathu tikakhale odika mtima, ndi acete m'kulemekeza Mulungu, ndi m'kulemekezeka monse.

YOHANE 11:41
Pomwepo anacotsa mwala. Kama Yesu anakweza maso ace kupenya kumwamba nati, Atate, ndiyamika Inu kuti munamva Ine.

MASALIMO 118:1-18
[1] Yamikani Yehova; pakuti Iye ndiye wabwino; Pakuti cifundo cace ncosatha.[2] Anene tsono Israyeli, Kuti cifundo cace ncosatha.[3] Anene tsono nyumba ya Aroni, Kuti cifundo cace ncosatha.[4] Anene tsono iwo akuopa Yehova, Kuti cifundo cace ncosatha.[5] M'mene ndinasautsika ndinaitanira pa Yehova; Anandiyankha Dandiika motakasuka Yehova.[6] Yehova ndi wanga; sindidzaopa; Adzandicitanji munthu?[7] Yehova ndi wanga, mwa iwo akundithandiza; M'mwemo ndidzaona cofuna ine pa iwo akundida,[8] Kuthawira kwa Yehova nkokoma Koposa kukhulupirira munthu.[9] Kuthawira kwa Yehova nkokoma Koposa kukhulupirira akulu,[10] Amitundu onse adandizinga, Zedi, m'dzina la Yehova ndidzawaduladula.[11] Adandizinga, inde, adandizinga: Indedi, m'dzinala Yehova ndidzawaduladula.[12] Adandizinga ngati njuci; Anazima ngati moto waminga; Indedi, m'dzina la Yehova ndidzawaduladula.[13] Kundikankha anandikankha ndikadagwa; Koma Yehova anandithandiza.[14] Yehova ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga; Ndipo anakhala cipulumutso canga.[15] M'mahema a olungama muli liu lakupfuula mokondwera ndi la cipulumutso:[16] Dzanja lamanja la Yehova licita mwamphamvu.[17] Sindidzafa koma ndidzakhala ndi moyo, Ndipo ndidzafotokozera nchito za Yehova.[18] Kulanga anandilangadi Yehova: Koma sanandipereka kuimfa ai.

MASALIMO 20:4
Likupatse ca mtima wako, Ndipo likwaniritse upo wako wonse.

MASALIMO 30:12
Kuti ulemu wanga uyimbire Inu, wosakhala cete. Yehova Mulungu wanga, ndidzakuyamikani nthawi zonse.

MASALIMO 95:2
Tidze naco ciyamiko pamaso pace, Timpfuulire Iye mokondwera ndi masalmo.

2 AKORINTO 9:11
polemeretsedwa inu m'zonse ku kuolowa manja konse, kumene kucita mwa ife ciyamiko ca kwa Mulungu,

2 AKORINTO 2:14
Koma ayamikike Mulungu, amene atitsogolera m'cigonjetso mwa Kristu, namveketsa pfungo la cidziwitso cace mwa ife pamalo ponse.

AFILIPI 4:19
Koma Mulungu wanga adzakwaniritsa cosowa canu ciri conse monga mwa cuma cace m'ulemerero mwa Kristu Yesu.

AROMA 11:36
Cifukwa 7 zinthu zonse zicokera kwa iye, zicitika mwa iye, ndi kufikira kwa iye. 8 K wa Iyeyo ukhale ulemerero ku nthawi zonse. Amen.

MASALIMO 105:1
Yamikani Yehova, itanirani pa dzina lace; Bukitsani mwa mitundu ya anthu zocita Iye.

MACHITIDWE A ATUMWI 16:40
Ndipo anaturukam'ndendemo, nalowa m'nyumba ya Lidiya: ndipo pamene anaona abale, anawasangalatsa, namuka.

Chewa Bible (BL) 1992
Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society